Mulungu, Boma, ndi Inuyo
“Tchalitchi ndi Boma Zilimbana m’Mavoti a Chisudzulo ku Ireland”
MUTU wa nkhani umenewu wa mu The New York Times ukusonyeza mmene anthu lerolino angafunikire kusankha pakati pa chimene Boma likufuna ndi chimene tchalitchi chawo chimaphunzitsa.
Nkhaniyo inati: “Kutatsala pafupifupi mwezi kuti achite voti lofuna kuchotsa lamulo lake loletsa chisudzulo, Ireland wodzala Aroma Katolika akuona kulimbana kosachitikapo kwa atsogoleri ake a Boma ndi aja a tchalitchi chake.” Boma linati lichotse lamulo loletsa chisudzulo, pamene Tchalitchi cha Katolika chimatsutsa zolimba chisudzulo ndi kukwatiranso. Akatolika achiairishi anafunikira kusankha Tchalitchi kapena Boma. Malinga ndi zotulukapo zake, Boma linapambana ndi mlingo waung’ono.
Chodabwitsa kwambiri nchakuti, kwa zaka zambiri, anthu ku Northern Ireland akhala ndi mkangano wowopsa wokhudza ulamuliro wa dziko lawo. Ambiri aphedwa. Aroma Katolika ndi Aprotesitanti akhala osiyana malingaliro ponena za Boma limene akanagonjera: ulamuliro wopitiriza wachibritishi m’Northern Ireland kapena boma lakumaloko lolamulira Ireland yense.
Momwemonso, m’dziko lomwe kale linali Yugoslavia, olamulira afuna kuti anthu a zipembedzo zosiyanasiyana, kuphatikizapo Akatolika ndi Aorthodox, amenye nkhondo kuti atetezere dziko lawo. Kodi thayo loyamba la nzika wamba linali kwa yani? Kodi zinafunikira kutsatira aja amene anati anali kuimira Boma, kapena kodi zinayenera kumvera Mulungu, amene amati: “Usaphe . . . Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha”?—Aroma 13:9.
Mungaganize kuti mkhalidwe wotere sungakukhudzeni konse. Koma ukhoza kutero. Kwenikweni, ukukukhudzani ngakhale tsopano. M’buku lake lakuti The State in the New Testament, katswiri wa zaumulungu Oscar Cullmann akulankhula za “kusankha moyo kapena imfa kumene Akristu amakono ayenera kuchita kapena kumene angafunikire kuchita m’mikhalidwe yovuta pamene awopsezedwa ndi maboma otsendereza.” Komabe, akulankhulanso za “thayo lenileni ndi lofunikanso la Mkristu aliyense—ndiponso Mkristu wokhala m’mikhalidwe yotchedwa ‘yabwino’ ndi ‘yamasiku onse’—la kuyang’anizana ndi kulimbana ndi vuto lalikulu limene amakumana nalo chifukwa chabe chakuti ndi Mkristu.”
Choncho kodi Akristu lerolino ayenera kufuna kudziŵa za unansi wa chipembedzo ndi Boma? Ayeneradi kutero. Kuyambira kale, Akristu ayesa kukhala ndi lingaliro loyenera kulinga kwa olamulira a dziko. Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu, anaweruzidwa, kutsutsidwa, ndi kuphedwa ndi Boma la Roma. Ophunzira ake anafunikira kulinganiza mathayo awo achikristu ndi mangawa awo kulinga ku Ufumu wa Roma. Chotero, kupenda unansi wawo ndi olamulira kudzapereka zitsogozo za Akristu lerolino.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Tom Haley/Sipa Press