Kodi Ndinu Wochitiridwa Tsankhu?
KODI nkufanana kotani kumene kuli pakati pa chiwawa cha mtundu, tsankhu la fuko, kusankhana, kupatulana, ndi kupululutsa fuko lonse? Zonsezo ndi zipatso za chikhoterero chofala chaumunthu—tsankhu!
Kodi tsankhu nchiyani? Insaikulopediya ina imatanthauzira liwulo kukhala “lingaliro loumbidwa popanda kupatula nthaŵi ya kugamula bwino kapena popanda kusamala.” Monga anthu opanda ungwiro, tili ndi chikhoterero cha kukhala atsankhu linalake. Mwinamwake mungathe kukumbukira za nthaŵi ina pamene munagamula nkhani popanda umboni wake wonse. Baibulo limasiyanitsa malingaliro atsankhuwo ndi mmene Yehova Mulungu amagamulira zinthu. Limati: “Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:7.
Tsankhu Lingavulaze
Mosakayikira aliyense walingaliridwapo molakwa ndi munthu wina panthaŵi ina. (Yerekezerani ndi Mlaliki 7:21, 22.) Mwachidziŵikire, tonsefe ena amatichitira tsankhu. Komabe, pamene athetsedwa msanga, mwachionekere malingaliro a tsankhu adzavulaza munthu pang’ono kapena sadzamvulaza. Kusunga malingaliro amenewo nkumene kungavulaze. Kungatinamize kuyamba kukhulupirira bodza. Mwachitsanzo, anthu ena osonkhezeredwa ndi tsankhu amakhulupiriradi kuti munthu angathe kukhala waumbombo, waulesi, chitsiru, kapena wonyada kokha chifukwa chakuti ndi wachipembedzo chinachake, mtundu, kapena fuko lina.
M’zochitika zambiri kugamula zinthu molakwa kumeneko kumayambitsa kuchitira ena mosayenera, kutukwana, kapena ngakhale kuchitira ena chiwawa. Miyandamiyanda ya anthu ataya miyoyo yawo m’kuphedwa kwankhanza, kupululutsa, kuphana kwa mitundu, ndi mitundu ina ya tsankhu loipitsitsa.
Kuzungulira dziko lonse, maboma alimbana ndi tsankhu mwa kukhazikitsa mwalamulo zoyenera zamphamvu za ufulu, chisungiko, ndi kulingana. Ngati muŵerenga konsichushoni kapena mpambo wofunika wa malamulo a dziko lanu, mosakayikira mudzapezamo mawu kapena mfundo zokonzedwanso zolinganizidwa kutetezera zoyenera za nzika zonse, mosasamala kanthu za fuko lawo, mwamuna kapena mkazi, kapena chipembedzo. Komabe, tsankhu nlofala padziko lonse.
Kodi amakuchitirani tsankhu? Kodi mwatchedwa waumbombo, waulesi, chitsiru, kapena wonyada kokha chifukwa cha fuko lanu, msinkhu, kukhala kwanu mwamuna kapena mkazi, mtundu, kapena zikhulupiriro zachipembedzo? Kodi mukumanidwa mwaŵi wa maphunziro oyenera, ntchito, nyumba, ndi mautumiki ena a m’chitaganya chifukwa cha tsankhu? Ngati zili choncho, kodi mungapirire motani?
[Chithunzi patsamba 3]
Kukulitsa tsankhu kumabala udani wamafuko
[Mawu a Chithunzi]
Nina Berman/Sipa Press