“Tiphunzitseni Ife Kupemphera”
“AMBUYE, tiphunzitseni ife kupemphera.” Limenelo linali pempho la mmodzi wa ophunzira a Yesu Kristu. (Luka 11:1) Mwachionekere, wophunzira amene sanatchulidwe dzina ameneyo anali munthu woliyamikira kwambiri pemphero. Mofananamo Akristu oona lerolino amazindikira kufunika kwake. Kwenikweni, pemphero ndilo njira imene timalankhuliramo ndi Munthu Wapamwamba Koposa m’chilengedwe chonse! Ndipo tangoganizirani! “Wakumva Pemphero” amapereka chisamaliro chaumwini pa zofuna zathu ndi nkhaŵa zathu. (Salmo 65:2) Chofunika kwambiri ndicho chakuti mwa pemphero, timayamika ndi kutamanda Mulungu.—Afilipi 4:6.
Ngakhale zili choncho, mawuwo “tiphunzitseni ife kupemphera” amadzutsa mafunso ofunika. M’dziko lonse zipembedzo zosiyanasiyana zimagwiritsira ntchito njira zambiri zolankhulira ndi Mulungu. Koma kodi pali njira yabwino ndi yolakwika yopempherera? Kuti tiyankhe, tiyeni choyamba tione miyambo yotchuka yachipembedzo ya kupemphera. Tidzasumika maganizo pa imene amachita ku Latin America.
Mafano ndi “Atetezi Oyera Mtima”
Kunena mwachisawawa, maiko a ku Latin America ngachipembedzo kwambiri. Mwachitsanzo, m’Mexico yense munthu atha kuona chizoloŵezi chotchuka cha kupemphera kwa “atetezi oyera mtima.” Zoonadi, ndi mwambo kuti matauni ku Mexico azikhala ndi “atetezi oyera mtima” amene amawachitira mapwando masiku akutiakuti. Akatolika a ku Mexico amapempheranso kwa mafano osiyanasiyana ambiri. Komabe, “woyera mtima” amene munthu amapembedza amadziŵika ndi chimene wolambirayo akufuna kupempha. Ngati munthu akufunafuna woti akwatire, akhoza kuyatsira kandulo Anthony “Woyera Mtima.” Munthu amene akufuna kuyenda ulendo wa pagalimoto akhoza kudzipereka m’manja mwa Christopher “Woyera Mtima,” mtetezi wa apaulendo, makamaka a pagalimoto.
Komabe, kodi miyambo yotereyi inachokera kuti? Mbiri imasonyeza kuti pamene Aspanya anafika m’Mexico, anapeza kuti anthu ambiri anali odzipereka pa kulambira milungu yachikunja. M’buku lake lakuti Los Aztecas, Hombre y Tribu (Aaziteki, Munthu ndi Mtundu), Victor Wolfgang von Hagen akuti: “Panali milungu yaumwini, chomera chilichonse chinali ndi mulungu wake, ntchito iliyonse inali ndi mulungu wake wamwamuna kapena wamkazi, ngakhale kudzipha kunali ndi mulungu wake. Yacatecuhtli anali mulungu wa amalonda. M’dziko lino la milungu yambiri, milungu yonse inali ndi mikhalidwe yake ndi ntchito zodziŵika bwino.”
Kufanana kwa milungu imeneyi ndi “oyera mtima” a Akatolika kunali koonekera kwambiri kwakuti pamene ogonjetsa achispanya anayesa ‘kuloŵetsa’ eni dzikowo mu ‘Chikristu,’ iwo anangosintha kudzipereka kwawo ku mafano awo nadzipereka kwa “oyera mtima” a tchalitchi. Nkhani ina ya mu The Wall Street Journal inavomereza kuti Chikatolika chochitidwa m’mbali zina za Mexico chili ndi mizu yachikunja. Inanena kuti ku dera lina, ochuluka a “oyera mtima” 64 olambiridwa ndi anthu ambiri amafanana ndi “milungu yodziŵika ya Amaya.”
New Catholic Encyclopedia imanena kuti “pakati pa woyera mtima ndi awo amene ali padziko lapansi pali chomangira cha ubwenzi wodalirika, . . . chomangira chimene chimakulitsa ndi kulimbitsa unansi ndi Kristu ndi Mulungu, m’malo mwa kuuwononga.” Koma kodi chomangira chimene moonekeratu chinachokera ku chikunja chingakulitse motani unansi wa munthu ndi Mulungu woona? Kodi mapemphero amene amaperekedwa kwa “oyera mtima” ameneŵa amakondweretsadi Mulungu?
Chiyambi cha Korona
Mwambo wina wofala ndiwo kugwiritsira ntchito korona. Diccionario Enciclopédico Hispano-Americano (Hispanic-American Encyclopedic Dictionary) imafotokoza korona kukhala “chingwe chokhala ndi mikanda makumi asanu kapena zana limodzi ndi makumi asanu wokhala m’timagulu ta khumi tolekanitsidwa ndi mkanda wina waukulupo ndipo cholumikizidwa ndi mtanda, pakali pano woyambiriridwa ndi mikanda itatu.”
Pofotokoza mmene amagwiritsirira ntchito korona, chofalitsa china chachikatolika chimati: “Korona Woyera ndi mtundu wa pemphero la mawu ndi la mumtima lokhudza Zinsinsi za kuomboledwa kwathu. Ali ndi mbali khumi ndi zisanu. Mbali iliyonse imaphatikizapo kutchula mawu a Pemphero la Ambuye kamodzi, Tikuoneni Mariya nthaŵi khumi ndi Gloria Patri kamodzi. Pambali iliyonse pamakhala kusinkhasinkha za chinsinsicho.” Zinsinsi zimenezo ndi ziphunzitso zimene Akatolika amayenera kudziŵa, panopo kunena za moyo, kuvutika, ndi imfa ya Kristu Yesu.
The World Book Encyclopedia imati: “Njira zoyambirira za kupemphera ndi korona zinayambira m’Chikristu m’Nyengo Zapakati, koma zinangofala m’ma 1400 ndi 1500.” Kodi ndi Akatolika okha amene amagwiritsira ntchito korona? Ayi. Diccionario Enciclopédico Hispano-Americano ikuti: “Mikanda yonga imeneyo imagwiritsiridwa ntchito m’kulambira kwa Chisilamu, Chilama ndi Chibuda.” Inde, Encyclopedia of Religion and Religions imati: “Kwalingaliridwa kuti okhulupirira Muhammad anatengera Korona kwa Abuda, ndipo Akristu kwa okhulupirira Muhammad panthaŵi ya Nkhondo za Mtanda.”
Ena amanena kuti korona amangokhala ngati chokumbutsa pamene wina akufuna kubwereza mapemphero angapo. Koma kodi Mulungu amakondwera ndi ntchito yake?
Sitifunikira kuyerekeza kapena kukangana ponena zakuti kaya miyambo imeneyi ili yoyenera kapena yoona. Yesu anapereka yankho lophunzitsa pamene anapemphedwa kuphunzitsa otsatira ake kupemphera. Zimene ananena zidzatsegula maso oŵerenga ena kapena ngakhale kuwadabwitsa.
[Zithunzi patsamba 3]
Akatolika ambiri amagwiritsira ntchito mikanda ya korona. Kodi inachokera kuti?