Kutsatira Chilamulo cha Kristu
“Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.”—AGALATIYA 6:2.
1. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chilamulo cha Kristu chili mphamvu yaikulu yosonkhezera kuchita chabwino lerolino?
KU Rwanda, Mboni za Yehova zachihutu ndi zachitutsi zinaika moyo wawo pangozi kuti zitetezerane wina ndi mnzake ku kuphana kwa mafuko kumene kunasesa dzikolo posachedwapa. Mboni za Yehova ku Kobe, Japan, zimene zinataya apabanja awo m’chivomezi chosakaza zinasweka mtima ndi kutayikidwako. Komabe, izo zinachitapo kanthu mofulumira kupulumutsa anthu ena. Inde, zitsanzo zolimbikitsa mtima kuchokera padziko lonse zimasonyeza kuti chilamulo cha Kristu chikugwira ntchito lerolino. Ndicho mphamvu yosonkhezera kuchita chabwino.
2. Kodi Dziko Lachikristu lalephera motani kumvetsa chilamulo cha Kristu, ndipo tiyenera kuchitanji kuti tifitse chilamulocho?
2 Panthaŵi imodzimodzi, ulosi wa Baibulo wonena za “masiku otsiriza” ano oŵaŵitsa ukukwaniritsidwa. Ambiri ali “nawo maonekedwe a chipembedzo” koma “mphamvu yake adaikana.” (2 Timoteo 3:1, 5) Makamaka m’Dziko Lachikristu, chipembedzo nthaŵi zambiri chimangokhala chachiphamaso, chosachokera mumtima. Kodi zili choncho chifukwa chakuti nkovuta kwambiri kutsatira chilamulo cha Kristu? Iyayi. Yesu sangatipatse chilamulo chimene sichingatsatirike. Dziko Lachikristu langolephera kumvetsa chilamulocho. Lalephera kulabadira mawu awa ouziridwa: “Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.” (Agalatiya 6:2) ‘Timafitsa chilamulo cha Kristu’ mwa kunyamulirana zothodwetsa, osati mwa kutsanzira Afarisi ndipo mosayenerera kuwonjezera katundu wa abale athu.
3. (a) Kodi malamulo ena amene ali m’chilamulo cha Kristu ndi otani? (b) Kodi nchifukwa ninji kungakhale kulakwa kuganiza kuti mpingo wachikristu suyenera kukhala ndi malamulo ena alionse kusiyapo malamulo operekedwa ndi Kristu mwini?
3 Chilamulo cha Kristu chimaphatikizapo malamulo onse a Kristu Yesu—kaya kulalikira ndi kuphunzitsa, kukhala ndi diso loyera ndi lakumodzi, kulimbikira kukhala pamtendere ndi mnansi wathu, kapena kuchotsa chodetsa mumpingo. (Mateyu 5:27-30; 18:15-17; 28:19, 20; Chivumbulutso 2:14-16) Inde, Akristu ali ndi thayo la kusunga malamulo onse omwe ali m’Baibulo operekedwa kwa otsatira a Kristu. Ndipo palinso zina. Gulu la Yehova, ndiponso mpingo umodzi ndi umodzi, lakhazikitsa malamulo ofunika ndi malangizo kuti pakhale dongosolo labwino. (1 Akorinto 14:33, 40) Ndipotu, Akristu sakanasonkhana pamodzi ngati analibe malamulo onena za nthaŵi, malo, ndi mmene misonkhano yotero iyenera kuchitikira! (Ahebri 10:24, 25) Kumvera malangizo oyenera operekedwa ndi aja okhala ndi udindo m’gulu kulinso mbali ya kufitsa chilamulo cha Kristu.—Ahebri 13:17.
4. Kodi chimene chimasonkhezera kulambira koyera nchiyani?
4 Ngakhale zili choncho, Akristu oona samalola kulambira kwawo kukhala kakonzedwe kopanda tanthauzo ka malamulo. Samatumikira Yehova chabe chifukwa chakuti munthu wina kapena gulu lawauza kuchita zimenezo. M’malo mwake, chimene chimasonkhezera kulambira kwawo ndi chikondi. Paulo analemba kuti: ‘Chikondi cha Kristu chitikakamiza.’ (2 Akorinto 5:14) Yesu analamula otsatira ake kukondana wina ndi mnzake. (Yohane 15:12, 13) Chikondi chodzimana ndicho maziko a chilamulo cha Kristu, ndipo chimakakamiza kapena kusonkhezera Akristu oona kulikonse, m’banja ndi mumpingo momwe. Tiyeni tione mmene chimachitira zimenezo.
M’Banja
5. (a) Kodi makolo angafitse motani chilamulo cha Kristu panyumba? (b) Kodi ana amafunanji kwa makolo awo, ndipo ndi zopinga zina ziti zimene makolo ayenera kugonjetsa kuti achisonyeze?
5 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5:25) Pamene mwamuna atsanzira Kristu nachita ndi mkazi wake mwachikondi ndi mwachifundo, amafitsa mbali yofunika kwambiri ya chilamulo cha Kristu. Ndiponso, Yesu anasonyeza chikondi poyera kwa tiana, akumatiyangata, kuika manja ake pa ito, ndi kutidalitsa. (Marko 10:16) Makolo amene amafitsa chilamulo cha Kristu amasonyezanso chikondi kwa ana awo. Zoona, alipo makolo ena amene kumawavuta kutsanzira chitsanzo cha Yesu pambaliyi. Ena mwachibadwa satha kusonyeza poyera chikondi chawo. Makolonu, musalole malingaliro otero kukuletsani kusonyeza ana anu chikondi chimene muli nacho pa iwo! Sikuli kokwanira kwa inu kudziŵa kuti mumakonda ana anu. Iwo ayeneranso kudziŵa. Ndipo iwo sadzadziŵa kusiyapo ngati mupeza njira yosonyezera chikondi chanu.—Yerekezerani ndi Marko 1:11.
6. (a) Kodi ana amafunikira malamulo a makolo, ndipo mukuyankhiranji choncho? (b) Kodi chifukwa chachikulu cha malamulo a m’banja chimene ana afunikira kudziŵa nchiyani? (c) Kodi ndi ngozi zotani zimene zimapeŵedwa pamene m’banja muli chilamulo cha Kristu?
6 Panthaŵi imodzimodzi, ana amafunikira malire, kutanthauza kuti makolo awo afunikira kukhazikitsa malamulo ndipo nthaŵi zina kusungitsa malamulo ameneŵa mwa kupereka chilango. (Ahebri 12:7, 9, 11) Ngakhale zili choncho, ana ayenera kuthandizidwa pang’onopang’ono kuona chifukwa chachikulu chimene malamulo ameneŵa akhalirako: kuti makolo awo amawakonda. Ndipo ayenera kudziŵa kuti chikondi ndicho chifukwa chabwino koposa chimene iwo ayenera kukhalira omvera makolo awo. (Aefeso 6:1; Akolose 3:20; 1 Yohane 5:3) Cholinga cha kholo lozindikira ndicho kuphunzitsa ana kugwiritsira ntchito ‘mphamvu yawo ya kulingalira’ kotero kuti m’kupita kwa nthaŵi azipanga zosankha zabwino paokha. (Aroma 12:1, NW; yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:11.) Komabe, malamulowo asakhale ochulukitsa kapena chilangocho chisakhale chaukali koposa. Paulo akuti: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21; Aefeso 6:4) Pamene m’banja muli chilamulo cha Kristu, malo samapezeka operekera chilango ndi mkwiyo wosalamulirika kapena a kutonyola kopweteka. M’nyumba yotero, ana amamva kukhala otetezereka ndi omangiriridwa, osati olemetsedwa kapena oluluzidwa.—Yerekezerani ndi Salmo 36:7.
7. Kodi ndi motani mmene nyumba za Beteli zingaperekere chitsanzo ponena za kukhazikitsa malamulo panyumba?
7 Ena amene achezerapo nyumba za Beteli kuzungulira dziko lonse amati izo zili zitsanzo zabwino za kusapambanitsa pankhani ya malamulo a banja. Ngakhale kuti kuli achikulire, malo amenewo amakhaladi ngati banja.a Ntchito za pa Beteli nzovuta kwambiri ndipo zimafuna malamulo ochulukirapo—ndithudi oposa a banja wamba. Ngakhale zili choncho, akulu otsogolera m’nyumba za Beteli, m’maofesi, ndi pantchito za m’fakitale amayesayesa kugwiritsira ntchito chilamulo cha Kristu. Amaliona kukhala thayo lawo osati kungolinganiza ntchito komanso kulimbikitsa kukula msinkhu kwauzimu ndi “chimwemwe cha Yehova” pakati pa antchito anzawo. (Nehemiya 8:10) Chifukwa chake, amayesayesa kuchita zinthu m’njira yabwino ndi yolimbikitsa ndipo amayesetsa kukhala ololera. (Aefeso 4:31, 32) Nchifukwa chake mabanja a Beteli amadziŵika ndi mzimu wawo wa chimwemwe!
Mumpingo
8. (a) Kodi cholinga chathu nthaŵi zonse mumpingo chiyenera kukhala chotani? (b) Kodi ndi m’mikhalidwe ina yotani imene ena afunsira zigamulo kapena ayesa kupanga malamulo?
8 Mumpingo chimakhalanso cholinga chathu kumangirirana wina ndi mnzake mumzimu wa chikondi. (1 Atesalonika 5:11) Chotero Akristu onse ayenera kusamala kuti asawonjezere zothodwetsa za ena mwa kuyesa kuumiriza malingaliro awoawo pa nkhani zaumwini. Nthaŵi zina, ena amalembera Watch Tower Society kuipempha kupereka chigamulo pa nkhani zonena za mmene ayenera kuonera mafilimu akutiakuti, mabuku, ndipo ngakhale zoseŵeretsa ana. Komabe, Sosaite ilibe mphamvu ya kuyang’anitsitsa zinthu zotero ndi kupereka zigamulo pa izo. Kaŵirikaŵiri, zimenezi ndi nkhani zimene munthu aliyense kapena mutu wa banja ayenera kusankha, malinga ndi kukonda kwake mapulinsipulo a Baibulo. Ena amatenga malingaliro ndi zitsogozo za Sosaite nkuzisandutsa malamulo. Mwachitsanzo, m’kope la Nsanja ya Olonda ya March 15, 1996, munali nkhani yabwino yolimbikitsa akulu kupanga maulendo aubusa nthaŵi zonse kwa ziŵalo za mpingo. Kodi chifuno chake chinali kukhazikitsa malamulo? Iyayi. Ngakhale kuti aja amene akhoza kutsatira malingalirowo amapeza mapindu ambiri, akulu ena sakhoza kuchita zimenezo. Mofananamo, nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” m’kope la Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995, inachenjeza za kululuza ulemu wake wa chochitika cha ubatizo mwa kuchita zinthu zomkitsa, monga chikondwerero chosalamulirika kapena kuchita mapwando. Ena autenga mopambanitsa uphungu wauchikulire umenewu, akumapanga ndi lamulo lakuti kutumiza khadi lachilimbikitso panthaŵiyi nkulakwa!
9. Kodi nchifukwa ninji nkofunika kuti tipeŵe kukhala osuliza kwambiri ndi okonda kuweruzana wina ndi mnzake?
9 Talingaliraninso kuti ngati ‘lamulo langwiro, laufulu’ liti likhale pakati pathu, tiyenera kuvomereza kuti zikumbumtima zonse za Akristu zimasiyana. (Yakobo 1:25) Kodi tiyenera kukulitsa nkhani ngati anthu ali ndi zosankha zaumwini zimene sizikuswa mapulinsipulo a m’Malemba? Iyayi. Kuchita kwathu zimenezo kungadzetse malekano. (1 Akorinto 1:10) Paulo, potichenjeza za kuweruza Mkristu mnzathu, anati: “Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti [Yehova, NW] ali wamphamvu kumuimiritsa.” (Aroma 14:4) Timakhala pangozi ya kusakondweretsa Mulungu ngati timanenerana pankhani zimene ziyenera kusiyidwira chikumbumtima cha munthu.—Yakobo 4:10-12.
10. Kodi ndani amene amaikidwa kuyang’anira mpingo, ndipo tiyenera kuwachirikiza motani?
10 Tikumbukirenso kuti akulu aikidwa kuyang’anira gulu la nkhosa la Mulungu. (Machitidwe 20:28) Alipo kuti apereke thandizo. Tiyenera kukhala aufulu kuwafikira kaamba ka uphungu, pakuti iwo ali ophunzira Baibulo ndipo amadziŵa zimene zafotokozedwa m’mabuku a Watch Tower Society. Pamene akulu aona khalidwe limene lingachititse kuswa mapulinsipulo a Malemba, iwo mopanda mantha amapereka uphungu wofunikira. (Agalatiya 6:1) Ziŵalo za mpingo zimatsatira chilamulo cha Kristu mwa kumvera abusa okondedwa ameneŵa, otsogolera pakati pawo.—Ahebri 13:7.
Akulu Gwiritsirani Ntchito Chilamulo cha Kristu
11. Kodi akulu mumpingo amagwiritsira ntchito motani chilamulo cha Kristu?
11 Akulu amalakalaka kufitsa chilamulo cha Kristu mumpingo. Amatsogolera pa kulalikira uthenga wabwino, amagwiritsira ntchito Baibulo pophunzitsa kuti afike mitima ndipo, monga abusa achikondi ndi ofatsa, amalankhula kwa “amantha mtima.” (1 Atesalonika 5:14) Amapeŵa mzimu umene suuli wachikristu wopezeka m’zipembedzo zambiri za Dziko Lachikristu. Zoona, dzikoli likunyonyotsoka mofulumira, ndipo monga Paulo, akulu angade nkhaŵa kaamba ka gulu la nkhosa; koma amakhalabe osapambanitsa posamalira zodetsa nkhaŵa zimenezo.—2 Akorinto 11:28, NW.
12. Pamene Mkristu afika kwa mkulu kaamba ka thandizo, kodi mkuluyo angachite motani?
12 Mwachitsanzo, Mkristu angafune kufunsa mkulu za nkhani yofunika imene sikutchulidwa mwachindunji m’Malemba kapena imene ikufuna kugwiritsira ntchito bwino mapulinsipulo osiyana achikristu. Mwinamwake wapatsidwa mwaŵi wa kukwezedwa pantchito yamalipiro okulirapo komanso yathayo kwambiri. Kapena tate wosakhulupirira wa Mkristu wachichepere angakhale akufuna zopambanitsa kwa mwana wake zimene zingakhudze utumiki wake. M’mikhalidwe yotero mkulu amapeŵa kupereka malingaliro akeake. M’malo mwake, iye mosakayikira adzatsegula Baibulo ndi kuthandiza munthuyo kulingalira pa mapulinsipulo oyenera. Angagwiritsire ntchito Watch Tower Publications Index, ngati ali nayo, kuti apeze zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wanena pankhaniyo mu Nsanja ya Olonda ndi zofalitsa zina. (Mateyu 24:45) Nanga bwanji ngati Mkristuyo pambuyo pake wapanga chosankha chooneka ngati chopanda nzeru kwa mkuluyo? Ngati chosankhacho mosakayikira sichikuswa mapulinsipulo kapena malamulo a Baibulo, Mkristuyo adzapeza kuti mkuluyo amazindikira kuyenera kwa munthuyo kupanga chosankha chimenecho, podziŵa kuti “yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” Komabe, Mkristuyo ayenera kukumbukira kuti “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:5, 7.
13. M’malo mopereka mayankho achindunji pa mafunso kapena kupereka malingaliro awoawo, kodi nchifukwa ninji akulu amathandiza ena kulingalira pankhaniyo?
13 Kodi nchifukwa ninji mkulu wachidziŵitsoyo amachita motere? Pali zifukwa ziŵiri. Choyamba, Paulo anauza mpingo wina kuti sanali ‘kuchita ufumu pa chikhulupiriro chawo.’ (2 Akorinto 1:24) Mkuluyo, pothandiza mbale wake kulingalira pa Malemba ndi kudzipangira chosankha akudziŵa bwino zimene akuchita, amatsanzira mzimu wa Paulo. Amazindikira kuti ulamuliro wake uli ndi malire, monga momwedi Yesu anazindikirira kuti ulamuliro wake unali ndi malire. (Luka 12:13, 14; Yuda 9) Panthaŵi imodzimodzi, akulu sazengereza kupereka thandizo, ngakhale uphungu wamphamvu wa m’Malemba pamene ufunikira. Chachiŵiri, amakhala akuphunzitsa Mkristu mnzake. Mtumwi Paulo anati: “Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14) Chifukwa chake, kuti tikule msinkhu, tifunikira kugwiritsira ntchito mphamvu zathuzathu zakuzindikira, osati nthaŵi zonse kumadalira wina kuti atipatse mayankho. Mkuluyo, mwa kusonyeza Mkristu mnzake mmene angalingalirire pa Malemba, akumthandiza mwa njira imeneyi kupita patsogolo.
14. Kodi akulu msinkhu angasonyeze motani kuti amakhulupirira Yehova?
14 Tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova Mulungu mwa mzimu wake woyera amasonkhezera mitima ya olambira oona. Chotero, Akristu akulu msinkhu amakopa mitima ya abale awo, kuwadandaulira, monga momwe anachitira mtumwi Paulo. (2 Akorinto 8:8; 10:1; Filemoni 8, 9) Paulo anadziŵa kuti makamaka ndi osalungama, osati olungama, amene amafunikira malamulo ambirimbiri kuti iwo akhale olongosoka. (1 Timoteo 1:9) Anasonyeza chikhulupiriro mwa abale ake, osati chikayikiro kapena kusawakhulupirira. Ku mpingo wina iye analemba kuti: “Tikhulupirira mwa Ambuye za inu.” (2 Atesalonika 3:4) Chikhulupiriro cha Paulo, ndi chidaliro chake zinathandiza kwambiri kusonkhezera Akristu amenewo. Akulu ndi oyang’anira oyendayenda lerolino ali ndi cholinga chofanana. Amuna okhulupirika ameneŵa ali otsitsimula chotani nanga, pamene mwachikondi aŵeta gulu la nkhosa!—Yesaya 32:1, 2; 1 Petro 5:1-3.
Kutsatira Chilamulo cha Kristu
15. Kodi ndi mafunso ena otani amene tingadzifunse kuona ngati tikugwiritsira ntchito chilamulo cha Kristu pa unansi wathu ndi abale athu?
15 Ife tonse tifunikira kudzipenda nthaŵi zonse kuona ngati tikutsatira chilamulo cha Kristu ndi kuchichirikiza. (2 Akorinto 13:5) Ndithudi, tonsefe tingapindule mwa kufunsa kuti: ‘Kodi ndine womangirira kapena wosuliza? Kodi ndine wosapambanitsa kapena wopambanitsa? Kodi ndimalingalira za ena kapena kuumirira pa zoyenera zanga?’ Mkristu samayesa kuuza mbale wake zochita kapena zosayenera kuchita pankhani zimene Baibulo silimatchula mwachindunji.—Aroma 12:1; 1 Akorinto 4:6.
16. Kodi tingawathandize motani aja amene ali ndi malingaliro olakwa ponena za iwo eni, motero tikumafitsa mbali yofunika kwambiri ya chilamulo cha Kristu?
16 M’nthaŵi zino zoŵaŵitsa, nkofunika kwa ife kufunafuna njira zolimbikitsirana wina ndi mnzake. (Ahebri 10:24, 25; yerekezerani ndi Mateyu 7:1-5.) Pamene tiyang’ana abale athu ndi alongo, kodi sitimafuna kusumika maganizo pa mikhalidwe yawo yabwino kuposa zofooka zawo? Kwa Yehova, aliyense ali wamtengo wapatali. Nzachisoni kuti si onse amene amaganiza motero, ngakhale ponena za iwo eni. Ambiri amakonda kungoyang’ana pa zolakwa zawo ndi zophophonya. Kuti tilimbikitse otero—ndi ena—kodi tingayese kulankhula kwa munthu mmodzi kapena aŵiri pamsonkhano uliwonse, kuwadziŵitsa chifukwa chake timaŵerengera kukhalapo kwawo ndi chichirikizo chofunika chimene amapereka mumpingo? Nkosangalatsa chotani nanga kuwapeputsira chothodwetsa mwa njira imeneyi ndipo kotero kufitsa chilamulo cha Kristu!—Agalatiya 6:2.
Chilamulo cha Kristu Chikugwira Ntchito!
17. Kodi ndi m’njira zosiyanasiyana zotani zimene mumaoneramo chilamulo cha Kristu chikugwira ntchito mumpingo wanu?
17 Chilamulo cha Kristu chikugwira ntchito mumpingo wachikristu. Timachiona masiku onse—pamene Mboni mofunitsitsa ziuza ena uthenga wabwino, pamene zitonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake, pamene zilimbikira kutumikira Yehova mosasamala kanthu za zothetsa nzeru zovuta kwambiri, pamene makolo ayesetsa kulera ana awo kuti akonde Yehova ndi mtima wachimwemwe, pamene oyang’anira aphunzitsa Mawu a Mulungu mwachikondi ndi mwaubwenzi, kusonkhezera gulu la nkhosa kukhala ndi changu chamoto cha kutumikira Yehova kosatha. (Mateyu 28:19, 20; 1 Atesalonika 5:11, 14) Pamene ife aliyense payekha tigwiritsira ntchito chilamulo cha Kristu m’moyo wathu, mtima wa Yehova umakondwera chotani nanga! (Miyambo 23:15) Iye amafuna kuti onse okonda chilamulo chake changwiro akakhale ndi moyo wosatha. M’Paradaiso alinkudza, tidzakhala m’nthaŵi imene anthu adzakhala angwiro, nthaŵi yopanda akuswa malamulo, ndipo nthaŵi pamene ndingaliro zilizonse za mtima wathu zidzalamulirika. Ndi mfupo yaulemerero chotani nanga kaamba ka kutsatira chilamulo cha Kristu!
[Mawu a M’munsi]
a Nyumba zotero sizili ngati nyumba za amonke za Dziko Lachikristu. Kulibe ma “abbot,” kapena “atate,” m’lingaliro limenelo. (Mateyu 23:9) Abale athayo amapatsidwa ulemu, koma utumiki wawo umatsogozedwa ndi mapulinsipulo amodzimodzi amene amatsogoza akulu onse.
Kodi Mukuganiza Bwanji?
◻ Kodi nchifukwa ninji Dziko Lachikristu silinamvetse chilamulo cha Kristu?
◻ Kodi tingachigwiritsire ntchito motani chilamulo cha Kristu m’banja?
◻ Kuti tigwiritsire ntchito chilamulo cha Kristu mumpingo, kodi tiyenera kupeŵanji, ndipo tiyenera kuchitanji?
◻ Kodi akulu angamvere motani chilamulo cha Kristu pochita ndi mpingo?
[Chithunzi patsamba 23]
Chimene mwana wanu amafuna koposa ndi chikondi
[Chithunzi patsamba 24]
Abusa athu achikondi ngotsitsimula chotani nanga!