Muzimvetsera Mwachidwi Kuti Mupeze Mayankho a Mafunso Awa:
Kodi “chilamulo cha Khristu” n’chiyani? (Agal. 6:2)
Kodi tingakwaniritse bwanji chilamulo cha Khristu ngakhale pamene anthu ena sakutiona? (1 Akor. 10:31)
Kodi timakwaniritsa bwanji chilamulo cha Khristu tikamalalikira? (Luka 16:10; Mat. 22:39; Mac. 20:35)
N’chifukwa chiyani tinganene kuti chilamulo cha Khristu ndi chabwino kwambiri kuposa Chilamulo cha Mose? (1 Pet. 2:16)
Kodi anthu apabanja komanso makolo angatani kuti azikwaniritsa chilamulo cha Khristu m’banja mwawo? (Aef. 5:22, 23, 25; Aheb. 5:13, 14)
Kodi mungatani kuti muzikwaniritsa chilamulo cha Khristu mukakhala kusukulu? (Sal. 1:1-3; Yoh. 17:14)
Kodi tingatani kuti tizikondana ngati mmene Yesu anatikondera? (Agal. 6:1-5, 10)