Kubwerera Kufumbi—Motani?
“NDIWE fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” Pamene munthu woyamba, Adamu, anamva mawu amenewo, anadziŵa zimene zidzamchitikira. Anapangidwa ndi dothi lapansi ndipo anali kudzabwerera kufumbi komweko. Anayembekezera kufa chifukwa sanamvere Mlengi wake, Yehova Mulungu.—Genesis 2:7, 15-17; 3:17-19.
Baibulo limasonyeza kuti anthu anapangidwa ndi dothi. Limanenanso kuti: “Sou imene ichimwa—imeneyo ndiyo idzafa.” (Ezekieli 18:4, NW; Salmo 103:14) Imfa yadzetsa chisoni kwa anthu mamiliyoni ambiri ndipo mobwerezabwereza yabutsa mafunso onena za katayidwe ka mtembo wa munthu.
Miyambo Yakale ndi Yamakono
Kodi anthu a Mulungu akale anali kutaya motani mitembo ya anthu? M’masamba ake oyambirira, Baibulo limatchula njira zosiyanasiyana zochitira ndi akufa, kuphatikizapo kuwakwirira pansi. (Genesis 35:8) Kholo Abrahamu ndi mkazi wake, Sara, limodzi ndi mwana wawo Isake ndi mdzukulu wawo Yakobo anaikidwa m’phanga la Makipela. (Genesis 23:2, 19; 25:9; 49:30, 31; 50:13) Oweruza a Israyeli Gideoni ndi Samsoni anaikidwa ‘m’manda a atate wawo.’ (Oweruza 8:32; 16:31) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu a Mulungu akale anakonda kukhala ndi manda a banja. Pamene Yesu Kristu anafa m’zaka za zana loyamba C.E., mtembo wake unaikidwa m’manda atsopano osemedwa m’mwala. (Mateyu 27:57-60) Chotero, mitembo ya anthu nthaŵi zambiri inali kuikidwa m’nthaka kapena m’manda osemedwa m’miyala. Zimenezi zidakachitikabe kumadera ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi.
Komabe, kumbali zina za dziko lerolino kusoŵa kwa malo ndi kukwera mtengo kwa malo kukuchititsa kupeza manda kukhala kovuta kwambiri. Chifukwa chake, anthu ena akulingalira za njira zina zotayira mitembo ya anthu.
Kumwaza phulusa pambuyo pa kutentha mtembo wa munthu kukufalikira kwambiri. Ku England pafupifupi 40 peresenti ya akufa tsopano akutayidwa mwanjira imeneyi. Ku Sweden, kumene akufa oposa 80 peresenti a m’madera a m’tauni amatenthedwa, nkhalango zina zimasankhidwa kukhala komwazira phulusa. Ndipo ku Shanghai ndi kumizinda ina ingapo ya kumadzi ya ku China, maboma a mizindayo amachirikiza kumwaza phulusa lochuluka m’nyanja nthaŵi zingapo pachaka.
Kodi phulusa lingamwazidwire kuti? Si paliponse ayi. Ena angawope kuti kumwaza phulusa kungawononge malo okhala. Komabe, kwenikweni ngozi iliyonse ya miliri imene ingakhalepo imathetsedwa mwa kutentha mtembowo. Kumanda ena ku England ndi ku United States malo a kapinga kapena minda ya maluŵa yasankhidwa monga komwazira phulusa. Ndithudi, Akristu amafuna kudziŵa makamaka lingaliro la Malemba ponena za kutentha mtembo ndi kumwaza phulusa lake.
Kodi Lingaliro la Malemba Nlotani?
Polengeza chiweruzo pa “mfumu ya ku Babulo,” mneneri Yesaya anati: “Watayidwa kunja kwa manda ako.” (Yesaya 14:4, 19) Kodi kumwaza phulusa kuyenera kufanizidwa ndi mchitidwe umenewo woluluza? Ayi, pakuti sakutchula za kutentha mtembo ndi kusunga kapena kumwaza phulusa lake lotsala.
Yesu Kristu analankhula za chiukiriro cha padziko lapansi cha akufa chimene chidzachitika mu Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi pamene anati: “Onse ali m’manda adzamva mawu [anga] nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Komabe, kusafunikira kwenikweni kwa manda enieni kuti munthu aukitsidwe kukusonyezedwa ndi mafotokozedwa ena a ulosi wa chiukiriro. Chivumbulutso 20:13 chimati: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo.” Chotero, chofunika si malo kapena njira imene munthu ‘adzabwerera nayo kufumbi.’ M’malo mwake, ndicho chakuti kaya munthuyo Mulungu akumkumbukira ndipo waukitsidwa. (Yobu 14:13-15; yerekezerani ndi Luka 23:42, 43.) Ndithudi Yehova samafunikira manda apadera kuti amthandize kukumbukira anthu. Kutentha mtembo sikumaletsa chiukiriro cha munthu. Ndipo ngati kumwaza phulusako kuchitidwa ndi cholinga chabwino ndipo popanda madzoma a chipembedzo chonyenga, sikungakhale kosemphana ndi Malemba.
Amene asankha kumwaza phulusa afunikira kusamala malamulo a dzikolo. Kulinso bwino kwa iwo kulingalira zimene ofedwa ndi ena angaganize. Atumiki a Yehova angachite bwino kusamala kuti kusonyeza ufulu wawo wa Malemba sikukudzetsa chitonzo pa dzina labwino limene Akristu ali nalo. Zimenezi nzofunika makamaka m’maiko kumene boma limalola kutentha mtembo ndi kumwaza phulusa komano anthu sanalandire zimenezi kwenikweni. Ndithudi, Mkristu amapeŵa madzoma kapena miyambo iliyonse yozikidwa pa chikhulupiriro cha kusafa kwa sou ya munthu.
Kumasukiratu ku Manda!
Ena amene amachirikiza kumwaza phulusa amanena kuti kumapereka chimasuko ku kuikidwa m’manda. Komabe, chimene chidzadzetsa mpumulo waukulu koposa ndicho kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Baibulo lakuti “mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.”—1 Akorinto 15:24-28.
Zimenezi zikutanthauza kuti manda, malithinda, ngakhale kutentha mtembo ndi kumwaza phulusa, zidzakhala zinthu zakale. Inde, imfa sidzakhalakonso. Mouziridwa ndi Mulungu mtumwi Yohane analemba kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Zonsezi zidzachitika pamene imfa yaumunthu yodzetsedwa ndi uchimo wa Adamu idzathetsedweratu mu Ufumu wa Mulungu. Panthaŵiyo anthu omvera sadzayang’anizana ndi chiyembekezo cha kubwerera kufumbi.
[Zithunzi patsamba 29]
Njira zofala zosamalirira mtembo wa munthu
[Chithunzi patsamba 31]
Kumwaza phulusa ku Sagami Bay, Japan
[Mawu a Chithunzi]
Mwa Chilolezo cha Koueisha, Tokyo