Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 15-19
  • Mmene Oyang’anira Oyendayenda Amatumikirira Monga Adindo Okhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Oyang’anira Oyendayenda Amatumikirira Monga Adindo Okhulupirika
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyamikira Utumiki Wawo
  • Kuchita Udindo Wawo Mwachipambano
  • Mikhalidwe Ina Yofunika Kwambiri
  • Mphotho za Ntchito Yawo Yosangalatsa
  • Oyang’anira Oyendayenda—Mphatso mwa Amuna
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kodi Oyang’anira Dera Amatithandiza Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Aliyense Amalimbikitsidwa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 15-19

Mmene Oyang’anira Oyendayenda Amatumikirira Monga Adindo Okhulupirika

“Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu.”​—1 PETRO 4:10.

1, 2. (a) Kodi mungamasulire motani liwu lakuti “mdindo”? (b) Kodi ndani amene akuphatikizidwa pakati pa adindo ogwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu?

YEHOVA amagwiritsira ntchito Akristu onse okhulupirika monga adindo. Mdindo nthaŵi zambiri amakhala kapolo woyang’anira nyumba. Iye angayang’anirenso chuma cha mbuyake. (Luka 16:1-3; Agalatiya 4:1, 2) Yesu anatcha kagulu kake ka odzozedwa okhulupirika padziko lapansi “mdindo wokhulupirika.” Kwa mdindo ameneyu iye wapereka “zonse ali nazo,” kuphatikizapo ntchito yolalikira Ufumu.​—Luka 12:42-44; Mateyu 24:14, 45.

2 Mtumwi Petro ananena kuti Akristu onse ali adindo a chisomo cha Mulungu cha mitundumitundu. Mkristu aliyense ali ndi malo ake amene angachitiremo udindo wokhulupirika. (1 Petro 4:10) Akulu oikidwa achikristu ali adindo, ndipo pakati pawo pali oyang’anira oyendayenda. (Tito 1:7) Kodi akulu oyendayenda ameneŵa ayenera kuonedwa motani? Kodi iwo ayenera kukhala ndi mikhalidwe ndi zolinga zotani? Ndipo angadzetse motani mapindu ochuluka?

Kuyamikira Utumiki Wawo

3. Kodi nchifukwa ninji oyang’anira oyendayenda angatchedwe “adindo okoma”?

3 Polembera woyang’anira woyendayenda ndi mkazi wake, Akristu ena aŵiri okwatirana anati: “Tikufuna kukuthokozani kaamba ka nthaŵi yonse ndi chikondi chimene mwatisonyeza. Ife monga banja, tapindula kwambiri ndi chilimbikitso chanu chonse ndi uphungu. Tikudziŵa kuti tifunikira kupitirizabe kukula mwauzimu, koma mothandizidwa ndi Yehova ndi abale ndi alongo onga inuyo, zovuta pa kukulako zimapepuka.” Mawu onga ameneŵa ngofala chifukwa chakuti oyang’anira oyendayenda amasonyeza chidwi mwa wokhulupirira mnzawo aliyense payekha, monga momwedi mdindo wabwino amasamalirira bwino zofunika za panyumba. Ena ali odziŵa kukamba nkhani bwino koposa. Ambiri ndi akatswiri m’ntchito yolalikira, pamene ena amadziŵika chifukwa cha ubwenzi wawo ndi chifundo. Mwa kukulitsa ndi kugwiritsira ntchito mphatso zotero potumikira ena, oyang’anira oyendayenda angatchedwedi “adindo okoma.”

4. Kodi ndi funso lotani limene lidzapendedwa tsopano?

4 “Pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika,” mtumwi Paulo analemba motero. (1 Akorinto 4:2) Kutumikira Akristu anzawo m’mipingo yosiyanasiyana mlungu ndi mlungu ndiko mwaŵi wapadera ndi wosangalatsa. Komabe, kulinso thayo lalikulu. Pamenepa, kodi ndi motani mmene oyang’anira oyendayenda angachitire udindo wawo mokhulupirika ndi mwachipambano?

Kuchita Udindo Wawo Mwachipambano

5, 6. Kodi nchifukwa ninji kudalira Yehova mwapemphero kuli kofunika kwambiri m’moyo wa woyang’anira woyendayenda?

5 Kudalira Yehova mwapemphero nkofunika kuti oyang’anira oyendayenda akhale adindo achipambano. Chifukwa cha ndandanda yawo ndi mathayo ambiri, iwo nthaŵi zina angathodwe. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:4.) Chotero afunikira kuchita mogwirizana ndi nyimbo ya wamasalmo Davide nyimbo yakuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Otonthozanso ndi mawu a Davide akuti: “Wolemekezeka Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu.”​—Salmo 68:19.

6 Kodi Paulo anapeza kuti mphamvu yosamalirira mathayo ake auzimu? “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo,” analemba motero. (Afilipi 4:13) Inde, Yehova Mulungu anali Magwero a mphamvu ya Paulo. Mofananamo, Petro analangiza kuti: “Wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu.” (1 Petro 4:11) Mbale wina amene anali woyang’anira woyendayenda kwa zaka zambiri anagogomezera kufunika kwa kudalira pa Mulungu, akumati: “Nthaŵi zonse yang’anani kwa Yehova posamalira mavuto, ndipo funafunani thandizo la gulu lake.”

7. Kodi kumathandiza motani pa ntchito ya woyang’anira woyendayenda kuchita zinthu molinganiza?

7 Woyang’anira woyendayenda wachipambano amafunikira kukhala wochita zinthu molinganiza. Monga Akristu ena, amayesayesa “kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.” (Afilipi 1:10, NW)a Pamene akulu akumaloko ali ndi mafunso pankhani ina yake, kuli kwanzeru kufunsa woyang’anira dera amene akuwachezetsa. (Miyambo 11:14; 15:22) Nkotheka kuti malingaliro ake oyenera ndi uphungu wa m’Malemba zidzakhala zothandiza kwambiri pamene akulu apitiriza kusamalira nkhaniyo iye atachoka pampingopo. M’njira yofananayo, Paulo anauza Timoteo kuti: “Zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziŵa kuphunzitsa enanso.”​—2 Timoteo 2:2.

8. Kodi nchifukwa ninji phunziro la Baibulo, kufufuza, ndi kusinkhasinkha zili zofunika?

8 Kuphunzira Malemba, kufufuza, ndi kusinkhasinkha nzofunika pa kupereka uphungu wabwino. (Miyambo 15:28) Woyang’anira chigawo wina anati: “Pokumana ndi akulu, sitiyenera kuwopa kuvomereza kuti sitikudziŵa yankho la funso lina lake.” Kuyesayesa kukhala ndi “mtima wa Kristu” pankhani yakutiyakuti kumatheketsa kuti uphungu wozikidwa pa Baibulo, umene udzathandiza ena kuchita chifuniro cha Mulungu, uperekedwe. (1 Akorinto 2:16) Nthaŵi zina woyang’anira woyendayenda amafunikira kulembera Watch Tower Society kaamba ka chitsogozo. Mulimonse mmene zingakhalire, chikhulupiriro mwa Yehova ndi kukonda choonadi nzofunika kwambiri kuposa chithunzi chimene tingapereke kwa ena kapena kudziŵa kulankhula. M’malo mofika ndi “kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru,” Paulo anayamba utumiki wake ku Korinto “mofooka ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri.” Kodi zimenezo zinamchititsa kukhala wosagwira mtima? Ayi, zinathandiza Akorinto kukhala ndi chikhulupiriro, ‘chosakhala m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.’​—1 Akorinto 2:1-5.

Mikhalidwe Ina Yofunika Kwambiri

9. Kodi nchifukwa ninji akulu oyendayenda amafunika kumvera chisoni?

9 Kumvera chisoni kumathandiza oyang’anira oyendayenda kupeza zotulukapo zabwino. Petro analimbikitsa Akristu onse ‘kuchitirana chifundo,’ kapena kukhala “omvera chisoni.” (1 Petro 3:8, NW, mawu amtsinde) Woyang’anira dera wina akuona kuti nkofunika ‘kukhala wokondwera ndi aliyense mumpingo ndi kukhala wotcheradi khutu.’ Ndi mzimu wofananawo, Paulo analemba kuti: “Kondwani nawo iwo akukondwera, lirani nawo akulira.” (Aroma 12:15) Maganizo otero amasonkhezera oyang’anira oyendayenda kuyesetsa kumvetsa mavuto ndi mikhalidwe ya okhulupirira anzawo. Ndiyeno akhoza kupereka uphungu womangirira wa m’Malemba umene ungadzetsedi mapindu ngati autsatira. Woyang’anira dera wopambana pa kumvera chisoni analandira kalata yotsatirayi kuchokera ku mpingo wina pafupi ndi Turin, Italy: “Ngati ufuna kuti ukhale wokondweretsa, kondweretsedwa ndi ena; ngati ufuna kuti ukhale wosangalatsa, sangalatsidwa ndi ena; ngati ufuna kukondedwa, ukhale wokondeka; ngati ufuna thandizo, ukhale wokonzekera kuthandiza ena. Nzimene taphunzira kwa inu!”

10. Kodi oyang’anira madera ndi a zigawo anenanji pa kukhala wodzichepetsa, ndipo Yesu anapereka chitsanzo chotani pankhaniyi?

10 Kukhala odzichepetsa ndi ofikirika kumathandiza oyang’anira oyendayenda kudzetsa mapindu ochuluka. Woyang’anira dera wina anati: “Nkofunika koposa kusunga mzimu wodzichepetsa.” Iye ankachenjeza oyang’anira dera atsopano kuti: “Musalole abale achuma kukusonkhezerani mosayenera chifukwa cha zimene angakuchitireni, kapena kukhala mabwenzi kwa amenewo okha, koma yesetsani nthaŵi zonse kuchita ndi ena mosakondera.” (2 Mbiri 19:6, 7) Ndipo woyang’anira woyendayenda wodzichepetsadi sangakhale wodzikweza monga woimira Sosaite. Woyang’anira chigawo wina moyenerera anati: “Khalani wodzichepetsa ndi wofuna kumvetsera kwa abale. Khalani wofikirika nthaŵi zonse.” Monga munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, Yesu Kristu akanachititsa anthu kutekeseka, koma anali wodzichepetsa ndi wofikirika kwakuti ngakhale ana anali omasuka kukhala naye. (Mateyu 18:5; Marko 10:13-16) Oyang’anira oyendayenda amafuna kuti ana, achinyamata, okalamba​—inde, aliyense mumpingo​—akhale womasuka kuwafikira.

11. Pamene kuli kofunikira, kodi kupepesa kungakhale ndi chiyambukiro chotani?

11 Zoonadi, “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri,” ndipo palibe woyang’anira woyendayenda amene salakwa. (Yakobo 3:2) Pamene iwo alakwa, kupepesa moona mtima kumapatsa akulu enawo chitsanzo cha kudzichepetsa. Malinga ndi kunena kwa Miyambo 22:4, “mphotho ya chifatso ndi kuwopa Yehova [koyenera] ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” Ndipo kodi atumiki onse a Mulungu safunikira ‘kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wawo’? (Mika 6:8) Atafunsidwa kuti ndi uphungu wotani umene angapatse mkulu woyendayenda watsopano, woyang’anira dera wina anati: “Khalani ndi ulemu waukulu kwa abale onse, ndi kuwaona kukhala abwino kwambiri kuposa inu. Mudzaphunzira zambiri kwa abale. Khalani wodzichepetsa. Khalani mmene mulili. Musadzikweze.”​—Afilipi 2:3.

12. Kodi nchifukwa ninji changu cha utumiki wachikristu chili chofunika kwambiri?

12 Changu cha utumiki wachikristu chimachititsa mawu a woyang’anira woyendayenda kukhala amphamvu. Kwenikweni, pamene iye ndi mkazi wake apereka chitsanzo cha changu m’ntchito yolalikira, akulu, akazi awo, ndi ena onse mumpingo amalimbikitsidwa kuchita changu mu utumiki wawo. “Khalani achangu mu utumiki,” analimbikitsa motero woyang’anira dera wina. Anawonjezera kuti: “Nthaŵi zambiri ndapeza kuti pamene mpingo uli wachangu kwambiri mu utumiki, umakhala ndi zothetsa nzeru zoŵerengeka.” Woyang’anira dera wina anati: “Ndikhulupirira kuti ngati akulu agwira ntchito m’munda ndi abale ndi alongo ndi kuwathandiza kusangalala ndi utumiki, zimenezi zidzadzetsa mtendere wa maganizo ndi chikhutiro chachikulu koposa potumikira Yehova.” Mtumwi Paulo ‘analimbika pakamwa kulankhula ndi Atesalonika uthenga wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.’ Nchifukwa chake iwo anali kukumbukira kwambiri ulendo wake ndi ntchito yolalikira nalakalaka kumuonanso iye!​—1 Atesalonika 2:1, 2; 3:6.

13. Kodi woyang’anira woyendayenda amalingalira za chiyani pogwira ntchito ndi Akristu anzake mu utumiki wakumunda?

13 Pogwira ntchito ndi Akristu anzake mu utumiki wakumunda, woyang’anira woyendayenda amalingalira za mikhalidwe yawo ndi zolephera zawo. Ngakhale kuti malingaliro ake angakhale othandiza, amadziŵa kuti ena amachita mantha polalikira ndi mkulu wachidziŵitso. Chifukwa chake, chilimbikitso nthaŵi zina chingakhale chothandiza kwambiri kuposa uphungu. Pamene atsagana ndi ofalitsa kapena apainiya ku phunziro la Baibulo, iwo angafune kuti iye achititse. Zimenezi kwenikweni zili kaamba kakuti iwo adziŵe njira zina zowongolera kaphunzitsidwe kawo.

14. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti oyang’anira oyendayenda achangu amasonkhezera changu mwa ena?

14 Oyang’anira oyendayenda achangu amasonkhezera changu mwa ena. Woyang’anira dera wina ku Uganda anadutsa m’nkhalango yoŵirira kwa ola limodzi potsagana ndi mbale wina ku phunziro la Baibulo limene silinali kupita patsogolo kwenikweni. Paulendo wawowo kunagwa mvula yaikulu kwakuti anafika atavumbwa. Pamene banja la anthu asanu ndi mmodzi linadziŵa kuti mlendoyo anali woyang’anira woyendayenda, linachita chidwi kwambiri. Linadziŵa kuti abusa a tchalitchi chawo sakanasonyeza nkhosa zawo chikondi chotero. Mlungu wotsatira pa Sande, iwo anapezeka pamsonkhano wawo woyamba ndipo anasonyeza chikhumbo cha kukhala Mboni za Yehova.

15. Kodi ndi chokumana nacho chotani chimene woyang’anira dera wina wachangu ku Mexico anali nacho?

15 M’boma la Oaxaca ku Mexico, woyang’anira dera wina anachita zimene sanamyembekezere kuchita. Anapanga makonzedwe akuti agone m’lumande masiku anayi kuti achezetse kagulu ka akaidi asanu ndi aŵiri amene anakhala ofalitsa a Ufumu. Kwa masiku angapo anatsagana ndi akaidi ameneŵa pamene iwo anali kuchitira umboni kulumande ndi lumande ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Chifukwa cha chidwi chosonyezedwa, ena a maphunziro ameneŵa anapitiriza mpaka usiku. “Pamapeto pa kuchezetsako, ineyo ndi akaidiwo tinadzala ndi chimwemwe chifukwa cha kulimbikitsana,” akulemba motero woyang’anira dera wachangu ameneyu.

16. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa pamene oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo apereka chilimbikitso?

16 Oyang’anira oyendayenda amayesa kukhala olimbikitsa. Pamene Paulo anachezetsa mipingo ku Makedoniya, ‘anawalimbikitsa ndi mawu ambiri.’ (Machitidwe 20:1, 2, NW) Mawu olimbikitsa angakhale othandiza kwambiri potsogoza achichepere ndi achikulire omwe kulinga ku zonulirapo zauzimu. Pa ofesi yanthambi ina yaikulu ya Watch Tower Society, kufufuza kwachisawawa kunasonyeza kuti oyang’anira madera analimbikitsa pafupifupi 20 peresenti ya antchito odzifunira kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse. Mwa chitsanzo chake chabwino monga wolengeza Ufumu wa nthaŵi zonse, mkazi wa woyang’anira woyendayenda amakhaladi woperekanso chilimbikitso.

17. Kodi woyang’anira dera wina wachikulire amaganiza motani ponena za mwaŵi wake wa kuthandiza ena?

17 Okalamba ndi opsinjika mtima amafunikira chilimbikitso kwambiri. Woyang’anira dera wina wachikulire akulemba kuti: “Mbali ya ntchito yanga imene imandipatsa chimwemwe chosaneneka ndiyo mwaŵi wa kupereka thandizo kwa ofooka ndi olefuka pakati pa gulu la nkhosa la Mulungu. Mawu a Aroma 1:11, 12 ali ndi tanthauzo lapadera kwa ine, pakuti ndimapeza chilimbikitso chachikulu ndi nyonga ‘pogaŵira kwa iwo mtulo wina wauzimu, kuti iwo akhazikike.’”

Mphotho za Ntchito Yawo Yosangalatsa

18. Kodi ndi zolinga za m’Malemba zotani zimene oyang’anira oyendayenda ali nazo?

18 Oyang’anira oyendayenda amafunira ubwino okhulupirira anzawo. Amafuna kulimbitsa mipingo ndi kuimangirira mwauzimu. (Machitidwe 15:41) Woyang’anira woyendayenda wina amalimbikira “kupereka chilimbikitso, kupereka mpumulo, ndi kusonkhezera chikhumbo cha kukwaniritsa utumiki ndi kupitiriza kulondola choonadi.” (3 Yohane 3) Winanso amayesayesa kulimbitsa okhulupirira anzake m’chikhulupiriro. (Akolose 2:6, 7) Kumbukirani kuti woyang’anira woyendayenda ali ‘mnzanu wa m’goli woona,’ osati mfumu pa chikhulupiriro cha ena. (Afilipi 4:3; 2 Akorinto 1:24) Ulendo wake umakhala nthaŵi ya chilimbikitso ndi ntchito yowonjezereka, limodzinso ndi mwaŵi wakuti bungwe la akulu lipende kupita patsogolo kumene kwachitidwa ndi kulingalira zonulirapo zamtsogolo. Mwa mawu ake ndi chitsanzo, ofalitsa a mpingo, apainiya, atumiki otumikira, ndi akulu angayembekezere kumangiriridwa ndi kusonkhezeredwa kaamba ka ntchito yamtsogolo. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:11.) Chotero, pamenepa, chirikizani ndi mtima wonse kuchezetsa kwa woyang’anira dera, ndipo gwiritsirani ntchito mokwanira utumiki wochitidwa ndi woyang’anira chigawo.

19, 20. Kodi oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo afupidwa motani kaamba ka utumiki wawo wokhulupirika?

19 Oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo amafupidwa kwambiri chifukwa cha utumiki wawo wokhulupirika, ndipo angakhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzawadalitsa pa zokoma zimene amachita. (Miyambo 19:17; Aefeso 6:8) Georg ndi Magdalena ali okwatirana okalamba amene anatumikira zaka zambiri m’ntchito yoyendayenda. Pamsonkhano wachigawo ku Luxembourg, munthu wina amene Magdalena anamlalikira zaka zoposa 20 kumbuyoko anamfikira. Chidwi cha choonadi cha mkazi wachiyuda ameneyu chinadzutsidwa ndi mabuku a Baibulo omwe Magdalena anamsiyira, ndipo m’kupita kwa nthaŵi anabatizidwa. Georg anafikiridwa ndi mlongo wina wauzimu amene anakumbukira kucheza kwake kunyumba kwawo pafupifupi zaka 40 zapitazo. Kulalikira kwake uthenga wabwino mwachangu potsirizira pake kunachititsa iye ndi mwamuna wake kulandira choonadi. Ndithudi, Georg ndi Magdalena anakondwera kwambiri.

20 Utumiki wokhulupirika wa Paulo ku Efeso unampatsa chimwemwe ndipo ungakhale utamsonkhezera kugwira mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Popeza kuti ntchito yoyendayenda imaphatikizapo kupatsa kosalekeza, awo amene amaichita amapeza chimwemwe, makamaka pamene aona zotulukapo zabwino za ntchito yawo. Woyang’anira dera wina amene anathandiza mkulu wolefuka anauzidwa m’kalata kuti: “Mwakhala ‘chonditonthoza mtima’ kwambiri m’moyo wanga wauzimu​—kuposa mmene mukudziŵira. . . . Simudzadziŵa konse mmene mwathandizira Asafu wamakono, amene ‘mapazi ake akadaterereka.’”​—Akolose 4:11; Salmo 73:2.

21. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti 1 Akorinto 15:58 amakhudza ntchito ya oyang’anira oyendayenda?

21 Mkristu wina wokalamba amene anali m’ntchito ya dera zaka zambiri amakonda kulingalira za 1 Akorinto 15:58, pamene Paulo analimbikitsa kuti: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” Ndithudi oyang’anira oyendayenda ali ndi zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye. Ndipo tikuthokoza chotani nanga kuti iwo akutumikira mwachimwemwe kwambiri monga adindo okhulupirika a chisomo cha Yehova!

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Kodi Mungakondwere ndi Zochita Zambiri?” mu Nsanja ya Olonda, May 15, 1991, masamba 28-31.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji oyang’anira oyendayenda angaonedwe monga “adindo okoma”?

◻ Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimathandiza oyang’anira madera ndi a zigawo kuchita zokoma zochuluka?

◻ Kodi nchifukwa ninji kudzichepetsa ndi changu zili zofunika kwambiri kwa awo ochita ntchito yoyendayenda?

◻ Kodi ndi zolinga zabwino zotani zimene oyang’anira oyendayenda ali nazo?

[Chithunzi patsamba 16]

Oyang’anira oyendayenda amafuna kulimbikitsa okhulupirira anzawo

[Zithunzi patsamba 17]

Achichepere ndi achikulire omwe angapindule mwa kuyanjana ndi oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo

[Chithunzi patsamba 18]

Utumiki wachangu wa woyang’anira woyendayenda umasonkhezera changu mwa ena

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena