Aliyense Amalimbikitsidwa
1. Kodi maulendo ochezera mipingo a oyang’anira oyendayenda amatipatsa mwayi wapadera wotani?
1 Mtumwi Paulo analembera mpingo wa ku Roma kuti: “Ndikulakalaka kukuonani, kuti ndikugawireni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba; kapena kuti tidzalimbikitsane mwa chikhulupiriro cha wina ndi mnzake, ponse pawiri chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Masiku anonso maulendo ochezera mipingo a oyang’anira oyendayenda amatipatsa mwayi wolimbikitsana.
2. Kodi n’chifukwa chiyani amatiuziratu kuti kudzabwera woyang’anira dera?
2 Mpingo: Nthawi zambiri mpingo umauzidwa kuti kudzabwera woyang’anira dera kutatsala miyezi itatu. Izi zimatipatsa nthawi yosintha zochita zathu kuti tidzapindule mokwanira. (Aef. 5:15, 16) Ngati mumagwira ntchito, mwina mungapemphe tchuthi kuti mudzalowe nawo mu utumiki wakumunda mlungu umene muli ndi woyang’anira dera. Ena amakonza zochita upainiya wothandiza mwezi umenewo. Ngati mwakonza zodzachokapo, kodi mungasinthe kuti mlunguwo mudzakhalepo?
3. Kodi aliyense angachite chiyani kuti alimbikitsidwe ndi woyang’anira dera?
3 Cholinga chenicheni chimene woyang’anira dera amafikira pa mpingo ndi kulimbikitsa ndi kuphunzitsa anthu utumiki wakumunda. Kodi mungamupemphe kuti muyende naye mu ulaliki kapena kuti muyende ndi mkazi wake ngati ndi wokwatira? Woyang’anira dera amasangalala kuyenda ndi ofalitsa osiyanasiyana, monga amene sanazolowere kulalikira kapenanso amene akufuna kuwonjezera luso lawo mu utumiki. Onse angaphunzire mmene iye akulalikirira ndipo angagwiritse ntchito malangizo aliwonse amene iye angawapatse. (1 Akor. 4:16, 17) Kumuitana kuti mudzadye naye chakudya kudzakupatsani mwayi winanso wolimbikitsana pamene mukucheza. (Aheb. 13:2) Popeza kuti nkhani zake amazikonza mogwirizana ndi mpingowo, tifunika kumvetsera mwatcheru.
4. Kodi tingamulimbikitse bwanji woyang’anira dera wathu?
4 Woyang’anira Dera: Mtumwi Paulo sanali wosiyana ndi abale ena onse mu mpingo. Iye ankakumana ndi mavuto ndiponso ankakhala ndi nkhawa, moti ankafunikira kulimbikitsidwa ndipo ena akamulimbikitsa, ankayamikira kwambiri. (2 Akor. 11:26-28) Mpingo wa ku Roma utamva kuti Paulo, yemwe panthawiyi anali mkaidi, tsopano akubwera ku mpingowo, anthu ena anayenda ulendo wa makilomita 74 kukamuchingamira ku Msika wa Apiyo. “Mmene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimba mtima.” (Mac. 28:15) Inunso mungalimbikitse woyang’anira dera wanu. M’patseni “ulemu wowirikiza” mwa kuchirikiza ndi mtima wonse zochitika za mlungu wapaderawo. (1 Tim. 5:17) Muuzeni ndipo sonyezani kuti mukuyamikira kwambiri zimene akukuchitirani. Iye ndi mkazi wake amasangalala akamaona chikhulupiriro chanu, chikondi chanu, ndi kupirira kwanu.—2 Ates. 1:3, 4.
5. N’chifukwa chiyani masiku ano aliyense amafunika kulimbikitsidwa?
5 ‘M’nthawi yovuta’ ino, kodi ndani safuna kulimbikitsidwa? (2 Tim. 3:1) Choncho, tsimikizani mtima kuchita nawo zonse pa mlungu wapadera. Tonsefe, oyang’anira oyendayenda ndi ofalitsa omwe, tingasangalale kwambiri polimbikitsana. Tikatero ‘tidzapitiriza kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake.’—1 Ates. 5:11.