Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsamba 9
  • Amachita Khama Kuti Atitumikire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amachita Khama Kuti Atitumikire
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Muziyamikira Amuna Amene Yehova Watipatsa Mumpingo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Aliyense Amalimbikitsidwa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • ‘Paulo Anayamika Mulungu, Ndipo Analimba Mtima’
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Oyang’anira Oyendayenda—Mphatso mwa Amuna
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 July tsamba 9
Zithunzi zosonyeza woyang’anira dera pa nthawi imene akuchezera mpingo: 1. Akuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki. 2. Ali pa msonkhano ndi bungwe la akulu. 3. Ali ndi m’bale wachinyamata mu utumiki.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Amachita Khama Kuti Atitumikire

Oyang’anira madera ndi akazi awo amasonyeza chikondi chololera kuvutikira anthu amene amawatumikira. Mofanana ndi ena tonse, nawonso amafunikira zinthu zina, nthawi zina amatopa, amafooka komanso amakhala ndi nkhawa. (Yak 5:17) Komabe, mlungu uliwonse iwo amaganizira mmene angalimbikitsire abale ndi alongo a mumpingo umene akuchezera. Kunena zoona, oyang’anira dera amafunika “apatsidwe ulemu waukulu.”​—1Ti 5:17.

Pamene mtumwi Paulo ankakonzekera kupita ku Roma kuti ‘akagawire abale a mpingo wa kumeneko mphatso inayake yauzimu,’ ankayembekezera mwachidwi kuti akalimbikitsane nawo mwa ‘chikhulupiriro chake ndi chawo.’ (Aro 1:11, 12) Kodi munaganizirapo za mmene mungalimbikitsire woyang’anira dera ndi mkazi wake, ngati ali wokwatira?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MOYO WA WOYANG’ANIRA DERA AMENE AMATUMIKIRA MADERA A KU MIDZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi oyang’anira madera ndi akazi awo amasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena m’njira ziti?

  • Kodi zomwe amachita zakuthandizani bwanji?

  • Kodi tingawalimbikitse bwanji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena