Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 January tsamba 7
  • ‘Paulo Anayamika Mulungu, Ndipo Analimba Mtima’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Paulo Anayamika Mulungu, Ndipo Analimba Mtima’
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Aliyense Amalimbikitsidwa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Amachita Khama Kuti Atitumikire
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Oyang’anira Oyendayenda—Mphatso mwa Amuna
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 January tsamba 7
Paulo akuthokoza Mulungu chifukwa cha abale amene anapita kukamuchingamira

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

‘Paulo Anayamika Mulungu, Ndipo Analimba Mtima’

Akhristu a mpingo wa ku Roma atamva kuti Paulo akubwera, gulu la abale linayenda ulendo wa makilomita 64 kukamuchingamira. Kodi chikondi chimene abalewa anasonyeza chinamukhudza bwanji Paulo? Iye “atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:15) Ngakhale kuti Paulo ankalimbikitsa mipingo imene ankaichezera, pa nthawi imeneyi pamene anali mkaidi, iyeyo ndi amene analimbikitsidwa.​—2 Akor. 13:10.

Masiku ano oyang’anira dera amayendera mipingo kuti alimbikitse abale ndi alongo. Mofanana ndi atumiki enanso a Mulungu, nawonso nthawi zina amatopa, amakhala ndi nkhawa komanso amafooka. Ulendo wina woyang’anira dera ndi mkazi wake akamadzachezera mpingo wanu, kodi mungadzachite chiyani kuti mumulimbikitse pamene nayenso akukulimbikitsani?​—Aroma 1:11, 12.

  • Woyang’anira dera akuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki

    Muzipezeka pamsonkhano wokonzekera utumiki. Woyang’anira dera amalimbikitsidwa akamaona ofalitsa akusiya zinthu zina n’cholinga choti achirikize mokwanira mlungu wapadera. (1 Ates. 1:2, 3; 2:20) Mungachite bwino kudzachita upainiya wothandiza pa nthawi imeneyi. Kodi mungakonde kudzalowa mu utumiki ndi woyang’anira dera kapena mkazi wake, mwinanso kupita naye ku phunziro lanu la Baibulo? Woyang’anira dera ndi mkazi wake amasangalala kwambiri kulalikira ndi ofalitsa osiyanasiyana kuphatikizapo amene angoyamba kumene kulalikira kapenanso amene alibe luso lolalikira.

  • Woyang’anira dera ndi mkazi wake akulandiridwa mwansangala ndi banja lina

    Muzikhala ochereza. Kodi n’zotheka kumuitana kuti adzadye kunyumba kwanu kapena kumupatsa malo ogona? Zimenezi zingachititse woyang’anira dera ndi mkazi wake kuona kuti mumawakonda. Si kuti amayembekezera kuti muwapangire zinthu zimene simungakwanitse.​—Luka 10:38-42.

  • Woyang’anira dera akuchititsa msonkhano wa akulu

    Muzimvera komanso kugwiritsa ntchito malangizo amene mwapatsidwa. Woyang’anira dera amatithandiza kuona zimene tingachite kuti tizichita zambiri potumikira Yehova. Nthawi zina angafunike kutipatsa malangizo amphamvu. (1 Akor. 5:1-5) Woyang’anira dera amasangalala kwambiri akaona kuti tikutsatira zimene watiuza.​—Aheb. 13:17.

  • Mpingo ukuyamikira woyang’anira dera ndi mkazi wake

    Muziwayamikira. Muziuza woyang’anira dera ndi mkazi wake mmene mwapindulira ndi khama lawo. Mukhoza kuwauza pamasom’pamaso, kuwalembera kalata kapena khadi.​—Akol. 3:15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena