Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 25-27
  • Kodi Mukutsanzira Mulungu Wathu Wopanda Tsankhu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukutsanzira Mulungu Wathu Wopanda Tsankhu?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri ya Yehova ya Kupanda Tsankhu
  • Kuphunzirapo Pa Kupanda Tsankhu Kwa Yehova
  • Makhalidwe a Yehova Ndi Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Muzitsanzira Yehova Yemwe Ndi Wosakondera
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Tsanzirani Yehova, Mulungu Wathu Wopanda Tsankho
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mulungu Alibe Tsankho
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 25-27

Kodi Mukutsanzira Mulungu Wathu Wopanda Tsankhu?

KUPANDA tsankhu​—kodi kungapezeke kuti? Pali Wina amene ali wopandiratu tsankhu, wopanda kukondera, ndi wosapatula ena. Ameneyo ndiye Yehova Mulungu, Mlengi wa mtundu wa anthu. Komabe, ponena za anthu, mlembi wachingelezi wa m’zaka za zana la 19 Charles Lamb moona mtima analemba kuti: “kunena mosavuta, Ine ndangokhala phukusi la malingaliro a tsankhu basi​—ndili ndi zokonda zanga ndi zodana nazo.”

Kunena za kupanda tsankhu, uli mkhalidwe wopereŵera kwambiri pakati pa anthu m’maunansi awo. Zaka mazana ambiri zapitazo Mfumu yanzeru ya Israyeli Solomo anazindikira kuti: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Udani wafuko, nkhondo zautundu, ndi mikangano yam’banja zikupitirizabe kuwonjezeka. Chotero, kodi nkwanzeru kukhulupirira kuti, mwa iwo okha, anthu angathe kupanga chitaganya chopanda tsankhu?

Kuyesayesa modzipenda nkofunika kuti tilamulire maganizo athu ndi kuchotsa malingaliro a tsankhu ali onse okhomerezeka. (Aefeso 4:22-24) Mosazindikira, tingakhale ndi mikhalidwe imene inaumbika mwa mayanjano athu ndi mkhalidwe wakusukulu ndi imene inali yozama m’banja lathu, fuko ndi mtundu. Zikhoterero zooneka ngati zazing’ono zimenezi kaŵirikaŵiri zimadzazama ndipo zimakulitsa mkhalidwe wa tsankhu. Woweruza ndi mlembi wa ku Scotland Lord Francis Jeffrey anavomereza kuti: “Palibe kanthu kena kamene munthu amakhala wosakazindikira kwa nthaŵi yaitali, monga mlingo ndi mphamvu ya malingaliro ake atsankhu.”

Lenaa ndi munthu wina amene akuvomereza kuti kuyesayesa modzipenda nkofunika kuti tilimbane ndi chikhoterero cha kukhala watsankhu. Kuletsa malingaliro a tsankhu mwa munthu mwiniwe, iye akutero, “ndi ntchito yaikulu chifukwa kaleredwe nchisonkhezero champhamvu.” Lena amazindikiranso kuti zikumbutso zakaŵirikaŵiri nzofunika.

Mbiri ya Yehova ya Kupanda Tsankhu

Yehova ali chitsanzo changwiro cha kupanda tsankhu. M’masamba oyambirira a Baibulo, timaŵerenga za mmene iye anasonyezera kupanda tsankhu kwake m’zochita zake ndi anthu. Tingathe kuphunzira zochuluka m’zitsanzo ndi zikumbutso zopambana zimenezi.

Yehova anasonyeza kupanda tsankhu posintha zinthu kotero kuti mtumwi wachiyudayo Petro analengeza uthenga wabwino kwa Korneliyo ndi Akunja ena mu 36 C.E. Pa nthaŵi imeneyo Petro anati: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye”​—Machitidwe 10:34, 35.

M’zochita zake zonse ndi banja la anthu, Yehova mosasintha wasonyeza kupanda tsankhu kwake. Kristu Yesu anati ponena za Atate wake: “Iye amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:45) Poonjezera kutamanda Yehova monga Mulungu wopanda tsankhu, Petro anachitira umboni kuti: “Aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”​—2 Petro 3:9.

M’tsiku la Nowa, pamene “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha,” Yehova analamulira chiwonongeko cha dziko limenelo la mtundu wa anthu. (Genesis 6:5-7, 11, 12) Komabe, mwa lamulo la Mulungu ndipo moonedwa bwino lomwe ndi anthu a m’nthaŵi yake, Nowa anakhoma chingalawa. Pamene iye ndi ana ake anali kupanga chingalawacho, Nowa analinso “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Mosasamala kanthu za kudziŵa chikhoterero cha mtima woipa wa mbadwo umenewo, Yehova mopanda tsankhu anawatumizira uthenga womvekera bwino. Iye anawadandaulira mosonkhezera maganizo ndi mitima mwa kupangitsa Nowa kukhoma ndi kulalikira. Anali ndi mwaŵi wonse wakulabadira, koma m’malo mwake “iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.”​—Mateyu 24:39.

Nchitsanzo chabwino koposa chotani nanga cha kupanda tsankhu kwa Yehova! M’masiku oŵaŵitsa otsiriza ano, kumene kumasonkhezera atumiki a Mulungu kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanda tsankhu kumodzimodziko. Ndiponso, saaleka kulengeza tsiku la kubwezera la Yehova. Moonedwa ndi onse, iwo amapereka uthenga wa Yehova mopanda kusankha kuti onse amve.​—Yesaya 61:1, 2.

Malonjezo a Yehova kwa makolowo Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anaonetsa kuti Yehova ali Mulungu wopanda tsankhu. Kupyolera m’mzera wawo wa banja wosankhidwa, Woikidwayo mwa amene ‘mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa’ anali kudzadza. (Genesis 22:18; 26:4; 28:14) Kristu Yesu anatsimikizira kukhala Woikidwa ameneyo. Mwa njira ya imfa ndi chiukiriro cha Yesu, Yehova anapereka njira ya chipulumutso kwa anthu onse omvera. Inde, mapindu a nsembe ya dipo ya Kristu ali opezeka popanda kusankha.

M’masiku a Mose, kupanda tsankhu kwa Yehova kunaonekera kokha m’njira yokondweretsa yokhudza ana aakazi a Tselofekadi. Akazi asanu ameneŵa anayang’anizana ndi chothetsa nzeru chokhudza choloŵa cha atate wawo m’Dziko Lolonjezedwa. Izi zinali choncho chifukwa unali mwambo mu Israyeli kuti choloŵa cha munda chiperekedwe kwa ana aamuna a munthu. Komabe, Tselofekadi anafa wopanda kusiya mwana wamwamuna kuti alandire choloŵa. Motero, ana aakazi asanu a Tselofekadi anabwera ndi pempho lawo kuti achitiridwe mopanda tsankhu pamaso pa Mose, akumati: “Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu.” Yehova anamvetsera kuchonderera kwawo ndipo analangiza Mose kuti: “Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, choloŵa chake achilandire mwana wake wamkazi.”​—Numeri 27:1-11.

Nchitsanzo chotani nanga cha kupanda tsankhu kwachikondi! Kuti atsimikizire kuti choloŵa cha fuko chisapatsidwe ku fuko lina pamene ana aakaziwo anakwatiwa, iwo anafunikira kukwatiwa kokha “m’fuko la banja la atate wawo.”​—Numeri 36:5-12.

Timadziŵa zoonjezereka za kupanda tsankhu kwa Yehova popenda masiku a woweruza ndi mneneri Samueli. Yehova anampatsa ntchito yoti adzoze mfumu yatsopano m’fuko la Yuda m’banja la Jese wa ku Betelehemu. Koma Jese anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Kodi ndani yemwe anayenera kudzozedwa monga mfumu? Samueli anachita chidwi ndi maonekedwe a thupi a Eliyabu. Komabe, Yehova samatengeka ndi maonekedwe akunja. Anamuuza Samueli kuti: “Usayang’ane nkhope yake kapena kutalika kwa msinkhu wake, . . . pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” Davide, mwana wamng’onong’ono wa Jese, anasankhidwa.​—1 Samueli 16:1, 6-13.

Kuphunzirapo Pa Kupanda Tsankhu Kwa Yehova

Akulu achikristu angachite bwino kutsanzira Yehova mwa kuyang’ana mikhalidwe yauzimu ya wokhulupirira mnzawo. Kuli kokhweka kuweruza munthu wina mwa miyezo yathuyathu, tikumalola malingaliro aumwini kuphimba kuzindikira kwathu. Monga momwe mkulu wina ananenera kuti, “Ndimayesa kuchita ndi ena m’njira imene imakondweretsa Yehova, osati yozikidwa pa malingaliro ongodziganizira ndekha.” Nkopindulitsa chotani nanga kuti atumiki onse a Yehova agwiritsire ntchito mawu Ake monga muyezo wawo!

Zitsanzo za m’Baibulo zimene zangotchulidwazo zimatithandiza kulimbana ndi malingaliro okhalitsa a tsankhu la fuko kapena utundu. Mwa kutsanzira kupanda tsankhu kwa Yehova, timatetezera mpingo wachikristu ku tsankhu, kupatula ena, ndi kukondera.

Mtumwi Petro anaphunzira kuti “Mulungu alibe tsankhu.” (Machitidwe 10:34) Kukondera ndi mdani wa kupanda tsankhu ndipo kumaononga mapulinsipulo a chikondi ndi umodzi. Yesu anasamalira osauka, ofooka, ndi amphaŵi, ndipo anapepuza mtolo wawo. (Mateyu 11:28-30) Iye anachita mosiyana kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo achiyudawo, amene anachita umbuye pa anthu, akumaŵasenza katundu wolemera wa malamulo. (Luka 11:45, 46) Kuchita izi ndi kusonyeza mzimu wokondera kwa otchuka sikunagwirizane ndi ziphunzitso za Kristu.​—Yakobo 2:1-4, 9.

Lerolino, akulu achikristu amadzigonjetsera ku umutu wa Kristu ndipo amasonyeza kupanda tsankhu kwa anthu odzipatulira onse a Yehova. Mmene iwo ‘akuŵeta gulu la Mulungu lili mwa iwo,’ amapewa kusonyeza mzimu wokondera chifukwa cha chuma cha munthu, kusamvana, kapena chibale. (1 Petro 5:2) Mwa kutsanzira Mulungu wopanda tsankhuyo ndi kulabadira chenjezo lake lotsutsa machitidwe a kukondera, akulu achikristu amakulitsa mzimu wa kupanda tsankhu mumpingo.

Mpingo wachikristu wa Mboni za Yehova ndiwo ubale wa padziko lonse. Uli umboni wooneka wakuti chitaganya chopanda tsankhu chingathe kukhala chothekera motsogoleredwa ndi Yesu Kristu. Mbonizo ‘zavala umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa [chifuniro cha, NW] Mulungu, m’chilungamo ndi m’chiyero cha choonadi [“kukhulupirika,” NW].’ (Aefeso 4:24) Inde, iwo akuphunzira pa chitsanzo changwiro cha Mulungu wopanda tsankhuyo, Yehova, ndipo ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano lopanda tsankhu konse.​—2 Petro 3:13.

[Mawu a M’munsi]

a Dzina lasinthidwa.

[Chithunzi patsamba 26]

Mtumwi Petro anaphunzira kuti Mulungu alibe tsankhu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena