Olengeza Ufumu Akusimba
Kuchirimika Kusukulu Kufupidwa
BAIBULO limaneneratu kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Mawu akuti “ana ako onse” angagwirenso ntchito mokulira pa gulu lonse la atumiki a Mulungu padziko lapansi, kuphatikizapo achichepere kwambiri. Lero, makolo achikristu amatsimikizira kuti ana awo akuphunzitsidwa ndi Yehova panyumba ndiponso pamisonkhano yachikristu.
Komabe, pamene ali kusukulu, Akristu achichepere amayang’anizana ndi zitokoso zovuta. Kaŵirikaŵiri amaona kukhala kofunika kuchirimika mwamphamvu pazimene aphunzira m’Baibulo. Pamene atero, zotulukapo zake zimakhala zopindulitsa kwa ophunzirawo ndi aphunzitsi omwe, monga mmene chikusonyezera chokumana nacho cha ku Micronesia chotsatirachi.
Pa chisumbu chaching’ono cha Tol kumadzulo kwa Pacific m’zisumbu za Chuuk, aphunzitsi pasukulu ya kumaloko anauza ana kukonzekera ndi kutengamo mbali m’phwando la Halloween la pasukulupo. Ana a Mboni anadziŵa kuti phwandolo likaphatikizapo zokometsera ndi zovala zoyerekezera mizukwa, abathwa, ndi afiti—zonse zokhudza miyambo ya zamizimu. Ana ameneŵa sakanatengamo mbali ndi chikumbumtima choyera.a
Mwa maphunziro awo ozikidwa pa Baibulo kunyumba ndi mumpingo wachikristu, ophunzirawo anadziŵa kuti machitachita oterowo ali osakondweretsa kwa Mulungu, ngakhale pamene achitidwa mongodzisangulutsa chabe. Kuti awathandize kufotokoza bwino kaimidwe kawo, anawo anaitana Barak, mmodzi wa amishonale a Mboni pachisumbucho, kuti adzalankhule ndi aphunzitsi awo.
Atamva mafotokozedwewo, aphunzitsiwo analinganiza msonkhano wachiŵiri, kuti Barak adzalankhule kwa aphunzitsi onse apasukulupo. Pamsonkhanowu, Barak anapereka maumboni osonyeza mkhalidwe weniweni wa Halloween. Anapeza chidziŵitso chake m’zofalitsa zingapo za Watch Tower ndi mabuku ena. Aphunzitsi ndi oyang’anira sukulu anadabwa pamene anamva za chiyambi, mbiri, ndi mbali yachipembedzo ya phwandolo. Anaganiza za kukhala ndi msonkhano wa aphunzitsi kuti amvane mmene angathetsere nkhani imeneyi.
Pambuyo pa masiku oŵerengeka, chigamulo chosayembekezeredwa chinalengezedwa. Makonzedwe onse a Halloween anaimitsidwa. Sukuluyo sinachitenso phwando chaka chimenecho. Nchotulukapo chabwinotu nanga chimene chinakhalapo pa kutsimikiza kwa Mboni zachichepere zimenezi kuchita chimene chili choyenera kusukulu! Achichepere safunikira konse kuwopa kapena kuchita manyazi kuchirikiza mwamphamvu choonadi cha Baibulo.
Padziko lonse, Mboni za Yehova zimaphunzitsa ana awo kulimbikira sukulu. Mboni zachichepere zimaphunzitsidwanso kutsatira malamulo a Baibulo ndi kumauza ophunzira anzawo za ziyembekezo zawo ndi zikhulupiriro pamene apeza mwaŵi. Ngakhale pamene zotulukapo sizili zabwino kapena sizili zanthaŵi yomweyo monga mmene zinakhalira m’chochitika chino, achichepere angakhale ndi chidaliro ndi chikhutiro chimene chimadza mwa kuchita chimene chili choyenera. Ndipo chofunika koposerapo, angatsimikizire kuti Atate wawo wakumwamba ngwokondwa ndipo adzawadalitsa chifukwa cha kumvera kwawo mokhulupirika.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zambiri za Halloween ndi chiyambi chake cha zamizimu, onani kope la Galamukani! wachingelezi wa November 22, 1993, wofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.