Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/15 tsamba 9-14
  • Kodi Chachikulu Kopambana m’Moyo Wanu Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chachikulu Kopambana m’Moyo Wanu Nchiyani?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo pa Chimene Chili Chachikulu Kopambana
  • Yehova Amamva ndi Kuyankha Mapemphero Athu
  • Kulimbana ndi Zoyesayesa za Adani
  • Kudziŵa Njira Yoyendamo
  • Mfumu Ilankhula
    Nsanja ya Olonda—1987
  • “Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Yehova ‘Anapulumutsa’ Anthu Ake M’nthawi za M’baibulo
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/15 tsamba 9-14

Kodi Chachikulu Kopambana m’Moyo Wanu Nchiyani?

“Mundidziŵitse njira ndiyendemo.”​—SALMO 143:8.

1. Kodi Mfumu Solomo ananenanji za zochita za munthu ndi zipambano zake?

MWINAMWAKE inunso mukudziŵa kuti moyo ngwodzala ndi zochita ndi nkhaŵa zambiri. Polingalira za icho, mukhoza kutchula zina za zimenezo kukhala zofunika. Zochita zina ndi nkhaŵa zina sizili zofunika kwenikweni mwinanso nkukhala zopanda pake. Kuzindikira kwanu zimenezi kumatanthauza kuti mukugwirizana ndi mmodzi wa amuna anzeru koposa chikhalire, Mfumu Solomo. Atasinkhasinkha mosamalitsa zochitika za m’moyo, ananena kuti: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 2:4-9, 11; 12:13) Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika kwa ife?

2. Kodi ndi funso lofunika lotani limene anthu owopa Mulungu ayenera kudzifunsa, likumabutsanso mafunso ena otani okhudzana nalo?

2 Ngati mukufuna ‘kuwopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,’ dzifunseni nokha funso lofunika lakuti: ‘Kodi chofunika kopambana m’moyo wanga nchiyani?’ Zoona, mwinamwake simumaganizira za funso limenelo tsiku lililonse, koma bwanji osaganiza za ilo tsopano? Kwenikweni, ilo limabutsa mafunso ena okhudzana nalo, monga akuti, ‘Kodi mwina ine ndikupereka maganizo mopambanitsa pa ntchito yanga kapena luso langa kapena zinthu zakuthupi? Kodi ndimasamala za nyumba yanga, banja langa, ndi okondedwa anga?’ Wachichepere angafunse kuti, ‘Kodi ndimapereka chisamaliro chachikulu motani ndi nthaŵi pa maphunziro? Kwenikweni, kodi chochita chapamtima, maseŵero, kapena zosangulutsa zina ndizo zazikulu m’moyo wanga?’ Ndipo mosasamala kanthu za msinkhu kapena mkhalidwe wathu, tiyenera kufunsa kuti, ‘Kodi kutumikira Mulungu kuli ndi malo otani m’moyo wanga?’ Mwachionekere, mukuvomereza kuti nkofunika kuika zinthu zofunika patsogolo. Koma kodi ndi motani ndipo nkuti kumene tingapeze thandizo lakuti tiziike m’malo ake?

3. Kodi kuika zinthu zofunika patsogolo kumaphatikizaponji kwa Akristu?

3 Liwu lakuti “Chachikulu Kopambana” kwenikweni limatanthauza chinthu chimene chimakhala chofunika kuposa china chilichonse kapena chofuna kusamaliridwa choyamba. Kaya ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova kapena muli pakati pa mamiliyoni a ophunzira Mawu a Mulungu oona mtima amene amayanjana nazo, talingalirani za choonadi ichi: “Kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.” (Mlaliki 3:1) Moyenerera, zimenezo zimaphatikizapo kusonyeza nkhaŵa yanu yachikondi kwa a m’banja lanu. (Akolose 3:18-21) Zimaphatikizapo kupereka zofunika za banja lanu moona mtima mwa kugwira ntchito yakuthupi. (2 Atesalonika 3:10-12; 1 Timoteo 5:8) Ndipo kuti musintheko zinthu, mwakamodzikamodzi mukhoza kupatula nthaŵi yochita zinthu zapamtima kapena kupuma. (Yerekezerani ndi Marko 6:31.) Komabe, mutaganizira mozama, kodi simukuona kuti palibe chilichonse cha zinthuzi chimene chili chachikulu kopambana m’moyo? Chilipo chinthu china chimene chili chofunika kwambiri.

4. Kodi Afilipi 1:9, 10 amakhudza motani za kuika kwathu zinthu zofunika patsogolo?

4 Mwinamwake mwazindikira kuti mapulinsipulo opereka chitsogozo chabwino a m’Baibulo ali chithandizo chofunika pa kuika zinthu zofunika patsogolo ndi kupanga zosankha zanzeru. Mwachitsanzo, pa Afilipi 1:9, 10, NW, Akristu akulimbikitsidwa kuti ‘asefukire, awonjezere m’chidziŵitso cholongosoka ndi kuzindikira konse.’ Ndi cholinga chotani? Mtumwi Paulo anawonjezera kuti: “Kuti mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri.” Kodi zimenezi sizili zanzeru? Mwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka, Mkristu wozindikira angadziŵe chimene chiyenera kukhala choyambirira​—chachikulu kopambana​—m’moyo.

Chitsanzo pa Chimene Chili Chachikulu Kopambana

5. Polongosola chitsanzo choperekedwa kwa Akristu, kodi Malemba amasonyeza motani chimene chinali chachikulu kopambana m’moyo wa Yesu?

5 Timapeza mbali ya mtengo wapatali ya chidziŵitso m’mawu a mtumwi Petro akuti: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Inde, kuti tipeze zotithandiza kudziŵa chimene chili chachikulu kopambana m’moyo, tiyenera kupenda zimene Yesu Kristu analingalira pa zimenezo. Salmo 40:8 linanena mwaulosi za iye kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali mkati mwa mtima mwanga.” Lingaliro limodzimodzilo analinenanso m’mawu aŵa: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.”​—Yohane 4:34; Ahebri 12:2.

6. Kodi ndi motani mmene tingapezere zimene Yesu anapeza pamene tiika chifuniro cha Mulungu patsogolo?

6 Onani mawu ofunikawo​—kuchita chifuniro cha Mulungu. Chitsanzo cha Yesu chimasonyeza chimene ophunzira ake ayenera kuchiyesa chinthu chachikulu kopambana m’moyo wawo, pakuti iye anati “yense, mmene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.” (Luka 6:40) Ndipo pamene Yesu anayenda m’njira imene Atate wake anafuna kuti ayendemo, anasonyeza kuti kuyesa chifuniro cha Mulungu kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo kuli ndi “chimwemwe chokwanira.” (Salmo 16:11; Machitidwe 2:28) Kodi mukuona kuti zimenezo zikutanthauzanji? Pamene otsatira a Yesu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo wawo, adzakhala ndi “chimwemwe chokwanira” ndi moyo weniweni. (1 Timoteo 6:19) Motero pali zifukwa zambiri zoyesera kuchita chifuniro cha Mulungu kukhala chinthu choyambirira m’moyo wathu.

7, 8. Kodi Yesu anakumana ndi mayesero otani, ndipo tingaphunzireponji pa zimenezi?

7 Yesu atangosonyeza kudzipereka kwake pa kuchita chifuniro cha Mulungu, Mdyerekezi anayesayesa kuti ampambutse. Motani? Mwa kumuyesa m’mbali zitatu. Nthaŵi iliyonse Yesu anayankha ndi mawu otsimikiza a m’Malemba. (Mateyu 4:1-10) Koma mayesero ena anali kumyembekezera​—chizunzo, kusekedwa, kuperekedwa ndi Yudase, kupatsidwa milandu yonama, ndiyeno imfa pamtengo wozunzirapo. Chikhalirechobe, palibe chilichonse cha mayesero ameneŵa chimene chinagwedeza Mwana wa Mulungu wokhulupirikayo panjira yake. Pamene zinthu zinafika poipitsitsa, Yesu anapemphera kuti: “Si monga ndifuna Ine, koma Inu. . . . Kufuna kwanu kuchitidwe.” (Mateyu 26:39, 42) Kodi aliyense wa ife sayenera kukhudzidwa mozama ndi mbali imeneyi ya chitsanzo chimene anatisiyira, chikumatikhozetsa ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera’?​—Aroma 12:12.

8 Inde, pamene tiika zinthu zofunika patsogolo m’moyo wathu, timafunikira kwambiri chitsogozo chaumulungu, makamaka ngati tikuyang’anizana ndi adani a choonadi ndi otsutsa chifuniro cha Mulungu. Kumbukirani Mfumu yokhuluphirika Davide pamene anachonderera chitsogozo poyang’anizana ndi chitsutso cha adani. Tidzaona zimenezi pamene tipenda chigawo china cha m’Salmo 143. Izi ziyenera kutithandiza kuzindikira mmene tingalimbitsire unansi wathu ndi Yehova ndi kulimbitsidwa pa kuchita chifuniro cha Mulungu monga chinthu choyamba m’moyo wathu.

Yehova Amamva ndi Kuyankha Mapemphero Athu

9. (a) Ngakhale kuti Davide anali wochimwa, kodi mawu ake ndi machitidwe ake zimasonyezanji? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuleka kuchita chimene chili choyenera?

9 Ngakhale kuti anali munthu wochimwa wokhoza kufa, Davide anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzamva pempho lake. Iye anachonderera modzichepetsa nati: “Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupempha kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu. Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.” (Salmo 143:1, 2) Davide anali wozindikira za kupanda ungwiro kwake, koma mtima wake unali wamphumphu kwa Mulungu. Chifukwa chake, anali ndi chidaliro chakuti adzalandira yankho m’njira yolungama. Kodi zimenezi sizikutilimbikitsa? Ngakhale kuti timapereŵera pa chilungamo cha Mulungu, tingakhale ndi chidaliro chakuti iye amatimva ngati mitima yathu ili yamphumphu kwa iye. (Mlaliki 7:20; 1 Yohane 5:14) Polimbikira chilimbikire m’pemphero, cholinga chathu chiyenera kukhala ‘kugonjetsa chabwino ndi choipa’ m’masiku ano oipa.​—Aroma 12:20, 21; Yakobo 4:7.

10. Kodi nchifukwa ninji Davide anakumana ndi nthaŵi zodetsa nkhaŵa?

10 Davide anali ndi adani ake, monga momwe ife takhalira nawo. Kaya monga wothaŵathaŵa kwa Sauli, wokakamizika kubisala m’malo obisika ayekha, kapena monga mfumu yovutitsidwa ndi adani, zimenezi zinali nthaŵi zodetsa nkhaŵa kwa Davide. Iye anafotokoza mmene zimenezi zinamkhudzira: “Mdani alondola moyo wanga; . . . Andikhalitsa mumdima . . . Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhaŵa mkati mwanga.” (Salmo 143:3, 4) Kodi munakhalapo ndi chifukwa chomvera mwa njira imeneyo?

11. Kodi ndi nthaŵi zodetsa nkhaŵa zotani zimene atumiki a Mulungu amakono akumana nazo?

11 Chitsenderezo cha adani, mayesero ochititsidwa ndi kusoŵeratu ndalama, matenda aakulu, kapena mavuto ena odetsa nkhaŵa achititsa ena a anthu a Mulungu kumva monga mzimu wawo wakomoka. Nthaŵi zina mitima yawo yatenganso nkhaŵa. Zili monga kuti aliyense wa iwo afuula kuti: “Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, Mudzatipatsanso moyo, . . . ndipo munditembenukire kundisangalatsa.” (Salmo 71:20, 21) Kodi iwo athandizidwa motani?

Kulimbana ndi Zoyesayesa za Adani

12. Kodi Mfumu Davide analimbana motani ndi ngozi ndi mayesero?

12 Salmo 143:5 limasonyeza zimene Davide anachita pamene anazingidwa ndi ngozi ndi mayesero aakulu: “Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pa ndekha za ntchito ya manja anu.” Davide anakumbukira zochita za Mulungu kwa atumiki Ake ndi mmene iye mwiniyo analanditsidwira. Anasinkhasinkha pa zimene Yehova anali atachita kaamba ka dzina Lake lalikulu. Inde, Davide nthaŵi zonse anaganizira za ntchito za Mulungu.

13. Pamene tiyang’anizana ndi mayesero, kodi kusinkhasinkha kwathu pa zitsanzo zakale ndi zamakono za atumiki okhulupirika kudzatithandiza motani kupirira?

13 Kodi sitimakumbukira kaŵirikaŵiri zimene Mulungu wachitira anthu ake? Timaterodi! Zimenezi zimaphatikizapo mbiri yopangidwa ndi ‘mtambo waukulu wa mboni’ m’nthaŵi zakale Chikristu chisanakhale. (Ahebri 11:32-38; 12:1) Akristu odzozedwa a m’zaka za zana loyamba nawonso analimbikitsidwa ‘kukumbukirabe masiku akale’ ndi zimene anazipirira. (Ahebri 10:32-34) Bwanji ponena za zokumana nazo za atumiki a Mulungu a m’nthaŵi zamakono, monga zija zotchulidwa m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom?a Nkhani zolembedwa mmenemo ndi m’zofalitsa zina zimatikumbutsa mmene Yehova anathandizira anthu ake kupirira ziletso, ndende, magulu achiwawa, ndi misasa yachibalo ndi ya ntchito zaukapolo. Pakhalanso mayesero m’maiko osakazidwa ndi nkhondo, monga Burundi, Liberia, Rwanda, ndi Yugoslavia wakale. Pamene chitsutso chinabuka, atumiki a Mulungu anapirira chifukwa cha kusunga unansi wolimba ndi Yehova. Dzanja lake linachirikiza aja omwe anayesa kuchita chifuniro chake kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo wawo.

14. (a) Kodi ndi chitsanzo chimodzi chotani pamene Mulungu anapulumutsa munthu mumkhalidwe umene ungafanane ndi wathu? (b) Kodi mukuphunziranji pachitsanzo chimenecho?

14 Komabe, munganene kuti simunakumanepo ndi nkhanza zoipa zotero, ndipo mungaganize kuti zikuoneka kuti sizidzakuchitikirani. Komabe, chichirikizo cha Mulungu kwa anthu ake, sichinakhale kokha m’mikhalidwe imene ena angaione kukhala yachilendo kwambiri. Iye wachirikiza “anthu wamba” ambiri m’mikhalidwe “yozoloŵereka.” Nachi chimodzi chokha mwa zitsanzo zambirimbiri: Nsanja ya Olonda ya December 1, 1996 ili ndi nkhani yosimbidwa ndi Penelope Makris. Nchitsanzo chopambana chotani nanga cha umphumphu wachikristu! Kodi mungakumbukire zimene anapirira kwa anansi ake, mmene analimbanira ndi matenda aakulu, ndi kulimbikira kwake kuti akhalebe mu utumiki wake wa nthaŵi zonse? Bwanji nanga za chokumana nacho chake chofupa ku Mytilene? Mfundo yake pano ndi yakuti, Kodi mumaona zitsanzo zoterozo kukhala zothandiza tonsefe kuika patsogolo zinthu zofunika, kuika kuchita chifuniro cha Mulungu patsogolo m’moyo wathu?

15. Kodi ndi ziti zina mwa zochita za Yehova zimene tiyenera kumasinkhasinkhapo?

15 Kusinkhasinkha pa zochita za Yehova kumatilimbitsa, mofanana ndi Davide. Polinganiza chifuno chake, Yehova anapanga makonzedwe a chipulumutso kupyolera mwa imfa ya Mwana wake, chiukiriro chake, ndi kulemekezedwa kwake. (1 Timoteo 3:16) Iye wakhazikitsa Ufumu wake wakumwamba, wayeretsa kumwamba mwa kuchotsako Satana ndi ziŵanda zake, ndipo wabwezeretsa kulambira koona pano padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-12) Iye wamanga paradaiso wauzimu ndipo wadalitsa anthu ake ndi chiwonjezeko. (Yesaya 35:1-10; 60:22) Anthu ake tsopano akupereka umboni womaliza chisanaulike chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Inde, tili nazo zochuluka zoti tisinkhesinkhe.

16. Kodi tikulimbikitsidwa kumaganizira za chiyani, ndipo zimenezi zidzatipatsa chitsimikizo cha chiyani?

16 Kumaganizira ntchito za manja a Mulungu m’malo mwa kutanganitsidwa ndi zochita za anthu kumatipatsa chitsimikizo chakuti mphamvu ya Yehova ili yosakanika. Komabe, ntchito zimenezo sizimangophatikizapo zolengedwa zodabwitsa zakuthambo ndi za padziko lapansi. (Yobu 37:14; Salmo 19:1; 104:24) Ntchito zake zodabwitsa zimaphatikizapo kulanditsa anthu ake kwa adani otsendereza, monga momwe zinasonyezedwera m’zokumana nazo za anthu ake osankhidwa akale.​—Eksodo 14:31; 15:6.

Kudziŵa Njira Yoyendamo

17. Kodi Yehova anali weniweni motani kwa Davide, ndipo zimenezi zingatilimbikitse motani?

17 Davide anapempherera chithandizo kuti chinyontho cha moyo wake chisaume mwa iye: “Nditambalitsira manja anga kwa Inu: moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula. Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nawo akutsikira kudzenje.” (Salmo 143:6, 7) Davide wochimwayo, anadziŵa kuti Mulungu anadziŵa za mkhalidwe wake. (Salmo 31:7) Nthaŵi zina ifenso tingalingalire kuti mkhalidwe wathu wauzimu watsika kwambiri. Koma mkhalidwewo suli wopanda chiyembekezo. Yehova, amene amamva mapemphero athu, angatichiritse mofulumira mwa kutipatsanso nyonga kupyolera mwa akulu achikondi, nkhani za mu Nsanja ya Olonda, kapena nkhani za pamsonkhano zimene zimaoneka monga kuti azikonzera ife.​—Yesaya 32:1, 2.

18, 19. (a) Kodi pempho lathu kwa Yehova lochokera pansi pamtima liyenera kukhala lotani? (b) Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?

18 Chidaliro chathu mwa Yehova chimatisonkhezera kumchonderera kuti: “Mundimvetse chifundo chanu mamaŵa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziŵitse njira ndiyendemo.” (Salmo 143:8) Kodi iye anamgwiritsa mwala Mlongo Makris, amene anali kwa yekha pachisumbu cha Greece? Chotero kodi adzakugwiritsani mwala pamene kuchita chifuniro chake kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo wanu? Mdyerekezi ndi atumiki ake angakonde kudodometsa kapena kuletseratu ntchito yathu yolengeza Ufumu wa Mulungu. Kaya tikutumikira m’maiko mmene kulambira koona kumaloledwa kapena ngati tikutumikira kumene kulambira koona kuli koletsedwa, mapemphero athu ogwirizana amagwirizananso ndi pemphero la Davide lakuti: “Mundilanditse kwa adani anga, Yehova; ndibisala mwa Inu.” (Salmo 143:9) Chisungiko chathu pa tsoka lauzimu timachipeza mwa kukhala m’malo obisika a Wam’mwambamwamba.​—Salmo 91:1.

19 Kutsimikiza mtima kwathu ponena za chimene chili chachikulu kopambana kwaima pamaziko olimba. (Aroma 12:1, 2) Pamenepo, kanizani zoyesayesa za dziko zofuna kukakamiza pa inu zimene anthu amaziona kukhala zofunika. Pitirizani kulola mbali iliyonse ya moyo wanu kusonyeza chimene mukuchidziŵa kukhala chachikulu kopambana m’moyo wanu​—kuchita chifuniro cha Mulungu.​—Mateyu 6:10; 7:21.

20. (a) Kodi taphunziranji za Davide pa Salmo 143:1-9? (b) Kodi Akristu lerolino amasonyeza motani mzimu wa Davide?

20 Mavesi asanu ndi anayi oyambirira a Salmo 143 amagogomezera unansi wathithithi wa Davide ndi Yehova. Pamene anazingidwa ndi adani, anachonderera chitsogozo cha Mulungu momasuka. Anatsanulira mtima wake, akumapempha thandizo lomsonyeza njira yoyenera kuyendamo. Zilinso chimodzimodzi lerolino kwa otsalira odzozedwa ndi mzimu apadziko lapansi limodzi ndi atsamwali awo. Iwo amaona unansi wawo ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali pamene amachonderera chitsogozo chake. Amaika patsogolo kuchita chifuniro cha Mulungu, mosasamala kanthu za zitsenderezo za Mdyerekezi ndi za dziko.

21. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa ife kupereka chitsanzo chabwino kuti tiphunzitse ena chimene chiyenera kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo wawo?

21 Mamiliyoni omwe akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova afunikira kudziŵa kuti kuchita chifuniro cha Mulungu ndiko chinthu chachikulu kopambana. Tingawathandize kumvetsetsa zimenezi pokambitsirana nawo mutu 13 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, umene umagogomezera mapulinsipulo oloŵetsedwa m’kukhala omvera Mawu.b Ndithudi, iwo ayenera kuona mwa ife chitsanzo cha zimene timawaphunzitsa. Posapita nthaŵi yaitali kwambiri, iwonso adzadziŵa njira imene ayenera kuyendamo. Pamene mamiliyoni ameneŵa azindikira chimene chiyenera kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo wawo, ambiri adzasonkhezereka kuchitapo kanthu kuti adzipatulire ndi kubatizidwa. Pambuyo pake, mpingo ungawathandize kupitirizabe kuyenda m’njira ya moyo.

22. Kodi ndi mafunso otani omwe adzayankhidwa m’nkhani yotsatira?

22 Ambiri amavomereza mosavuta kuti chifuniro cha Mulungu ndicho chiyenera kukhala chinthu chachikulu kopambana m’moyo wawo. Nangano ndi motani mmene Yehova amaphunzitsira atumiki ake mopita patsogolo kuchita chifuniro chake? Kodi zimenezi zimawapatsa mapindu otani? Mafunsoŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira, pokambitsirananso vesi lofunika kwambiri la Salmo 143:10.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa mu 1993 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Lofalitsidwa mu 1995 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Mwa kugwiritsira ntchito Afilipi 1:9, 10, kodi ndi motani mmene tingaikire zinthu zofunika patsogolo?

◻ Kodi Yesu anasonyeza motani chimene chinali chinthu chachikulu kopambana m’moyo wake?

◻ Kodi tingaphunzirenji pa machitidwe a Davide pamene anayang’anizana ndi chiyeso?

◻ Kodi Salmo 143:1-9 likutithandiza m’njira yotani lerolino?

◻ Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chachikulu kopambana m’moyo wathu?

[Chithunzi patsamba 10]

Machitidwe a Davide anasonyeza chidaliro chake pa Yehova

[Mawu a Chithunzi]

Chopangidwanso kuchokera pa Illustrirte Pracht - Bibel/​Heilige Schrift des Alten und Neuen Testaments, nach der deutschen Uebersetzung D. Martin Luther’s

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena