Ripoti la Olengeza Ufumu
Mfumu Ilankhula
CHIRI cholimbikitsa kudziŵa kuti padakali anthu ena m’malo apamwamba m’dziko iri amene amakonda kuwona mtima ndi chilungamo ndi amene amalankhula kusungilira mikhalidwe yotereyi. Chitsanzo chiri mfumu ya ku dziko la mu Africa kumene ntchito ya Mboni za Yehova iri pansi pa chiletso. Lolani ripotilo litiuze ife:
“Posachedwapa magulu achipembedzo osiyanasiyana anapanga msonkhano wa kusakanizana kwa zipembedzo mu mzinda wathu, ndipo ichi chinaphatikizamo Akatolika, Apresbyterian, Apentecostal, ndi ena otero. Mfumu yaikulu inaitanidwa kupereka nkhani pa msonkhanowo cha kuzigawo zomalizira. Ku kudabwitsidwa kwa onse osonkhanawo, iye anauza iwo, pakati pa zinthu zina, kutsanzira kuwona mtima ndi makhalidwe apamwamba a Mboni za Yehova, kuwonjezera kuti ngati iwo anali ngati Mboni za Yehova, pakanakhala mtendere mu mtunduwo.
“Tsiku lotsatira ziwalo zotsogolera za matchalitchi oimiridwa pa msonkhanowo zinabwera ku nyumba ya chifumu ya Mfumuyo ndi kudandaula mopsya mtima kutsutsana ndi mbali ya nkhani yake yomwe inalemekeza Mboni ndi kumufunsa iye ngati sanali kudziŵa kuti Mboni zinaletsedwa m’dzikolo. Mfumuyo inayankha movomereza koma inauza iwo kuti iye sanapeze cholakwika ndi Mboni za Yehova. Iye anapitiriza kunena kuti: ‘Kwa zaka zanga monga Mfumu Yaikulu, palibe nkamodzi komwe pamene mmodzi wa Mboni za Yehova anabweretsedwa ku bwalo langa la milandu kaamba ka choipa chachikulu. Kumbali ina, ngati chinangwa chabedwa kuchokera m’munda, kaŵirikaŵiri chimatembenukira kuti ali m’Katolika amene ali mbala. Ngati ndi m’mpama wabedwa, amakhala Presbyterian amene ali ndi thayo. Ziwalo za tchalitchi chanu zawononga dziko langa ndi kuchotsa mimba, ndipo palibe ngakhale mmodzi wa Mboni za Yehova amene anabweretsedwa pa bwalo langa la milandu kaamba ka zolakwa zoterozo. Kodi malamulo a Mulungu samaletsa zoipa zoterozo, kapena kodi matchalitchi sakumangiriridwanso ndi malamulo a Mulungu?’ Atsogoleri achipembedzo analibe yankho.
“Pambuyo pake, Mfumu Yaikuluyo inaitana oimira a Mboni za Yehova ndi kuwachenjeza kupitirizabe kudzisamalira iwo eni kotero kuti palibe chitonzo chimene chikubweretsedwa pa dzina la Mulungu wawo ndi pa dzina lake iyemwini monga Mfumu Yaikulu yomwe inalankhula kaamba ka Mboni za Yehova.”
Ripotilo lanena kuti tsopano anthu ambiri achatsopano akutenga kaimidwe kawo kaamba ka chowonadi. Mboni imodzi inanena kuti posachedwapa yakhala yokhoza kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi mafumu atatu a m’deralo, mmodzi wa iwo kukhala Mfumu Yaikuluyo, ndipo atatu a iwo akupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova!
Yehova Mulungu amazindikira awo amene amakonda chowonadi ndi chilungamo ndi kulankhula m’malo mwa atumiki Ake.—Mateyu 10:42.