Mfumu Ifotokoza za Mtsogolo Mwake
MFUMU ina ya ku West Africa inali mtsogoleri wokondedwa kwambiri ndi wolemekezedwa kwambiri m’dziko lake. Pa tsiku lake lakubadwa la 78, mabwenzi ake, banja, ndi anthu ena oifunira mafuno abwino anasonkhana kudzakondwera nayo pamodzi. Polankhula, mfumuyo inasankha mutu wankhani wachilendo pa chochitika chimenecho. Iyo inafotokoza za malingaliro ake onena za moyo wa pambuyo pa imfa.
Iyo inati pambuyo pa imfa “pali dziko latsopano lopanda chinyengo, nsanje ndi umbombo.” Analifotokoza kukhala dziko “lachinsinsi,” lokhalamo olungama okha, amene amalankhulana ndi Mulungu.
Zikhulupiriro zotero nzofala pakati pa anthu mu Afirika monse. Malinga ndi kunena kwa chipembedzo china chamwambo cha mu Afirika, imfa siili mapeto a moyo koma yangokhala kusamuka chabe, kusamuka kwa moyo kuloŵa mu dziko la mizimu. Kumanenedwa kuti pa imfa munthu amachoka m’dziko looneka kumka ku losaoneka. Monga mzimu, pamenepo munthuyo amaloŵa m’dera lokhalamo makolo ake akufa.
Anthu ambiri a ku West Africa amakhulupirira kuti makolo awo akufa, kapena mizimu ya makolo awo akufa, imayang’anira mabanja awo pa dziko lapansi. Buku lakuti West African Traditional Religion limati: “Palibe kusiyana kwakukulu pakati pa ukumu wa ziŵalo za mafuko zimene zikali moyo pa dziko lapansi pano, ndi uja wa amene ali m’dziko linalo. Pamene anali pa dziko lapansi, [makolowo] anali akulu a mabanja awo. Koma tsopano popeza kuti sititha kuwaona, iwo akali akulu m’dziko la mizimu. Samaleka kuchita ntchito yosamalira mabanja awo.”
Chifukwa chake, mfumu yokalamba yotchulidwa pachiyambiyo inayembekezera kukagwirizana ndi makolo ake akufa ndi kugwira nawo ntchito m’dziko la mizimu. Iyo inati: “Ndimakhulupirira mwamphamvu moyo wina pambuyo pa imfa ndi kuthekera kwa kupitiriza kwanga kutumikira—ngakhale pambuyo pa imfa.”
Komabe, chifukwa cha zina zimene mfumuyo inanena, nyuzipepala ya Sunday Times inanena kuti mfumuyo inaonekera “kukhala yosakhulupirira kwenikweni” moyo umene uliko munthu atafa. Anauza khamu limene linasonkhana kuti anamva za buku lina limene linafotokoza za moyo umene ulipo pambuyo pa imfa. Mfumuyo inali kufunafuna bukulo kwa zaka zisanu. Iyo inafunitsitsa kuliŵerenga kwakuti inalonjeza mphoto ya $1,500 (U.S.) kwa aliyense amene akampezera kope.
Mfumuyo sikanakhala ndi vutolo ngati ikanaŵerenga buku limene lili losavuta kupeza. Ilo ndilo buku lopezedwa mosavuta lotulutsidwa osati ndi munthu koma ndi Mlengi wa anthu onse. (1 Atesalonika 2:13) Buku limenelo ndilo Baibulo. Kodi limati bwanji ponena za moyo wa pambuyo pa imfa?