Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 11/15 tsamba 3-4
  • Kodi Akufa Angathe Kutiona?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akufa Angathe Kutiona?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Makolo Athu Ali Kuti?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
  • Kodi Akufa Ali Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Muyenera Kuwopa Akufa?
    Galamukani!—1996
  • Mfumu Ifotokoza za Mtsogolo Mwake
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 11/15 tsamba 3-4

Kodi Akufa Angathe Kutiona?

MKAZI wapha mwamuna wake. Patapita zaka zisanu ndi ziŵiri iye akuchita mantha ndi loto limene akukhulupirira kuti ndilo chizindikiro cha mkwiyo wa mwamuna wake wakufayo. Kuti akondweretse “mzimu” wa mwamunayo, akutuma mwana wake wamkazi kukathira nsembe ya moŵa pamanda ake.

Mwana wamkaziyo sakudziŵa zimene ati anene kwa mzimu wa atate wake, chifukwa chakuti nsembeyo yachokera kwa amake omwe anawapha. Mlongo wake akupenyerera ali pamalo obisika. Iye akufika pamenepo, ndipo limodzi ndi mlongo wakeyo akupemphera kwa atate wawo kuti awathandize kulipsira imfa yawo.

Chochitika chimenechi chikuchokera mu seŵero Lachigiriki lotchedwa The Libation Bearers, lolembedwa zaka zoposa 2,400 zapitazo. M’mbali zina za dziko, makamaka mu Afirika, nsembe zotero zoperekedwa pamanda zimaperekedwa ngakhale lerolino.

Mwachitsanzo, talingalirani za chochitika cha Ibe, yemwe amakhala ku Nigeria. Atafedwa ana atatu, akufikira sing’anga, yemwe akuuza Ibe kuti pali chochititsa imfazo​—atate ake a Ibe akufawo ali okwiya chifukwa chakuti maliro awo sanaikidwe mwa mwambo woyenera.

Potsatira chilangizo choperekedwa ndi sing’angayo, Ibe akupereka nsembe ya mbuzi, natsanulira nsembe ya kachasu ndi vinyo pamanda a atate wake. Apembedzera kwa mzimu wa atate wake, akumapempha chikhululukiro, akutsimikiziritsa chikondi chake, ndi kupempha dalitso.

Ibe sakukayikira konse kuti atate wake akhoza kumuona ndi kumumva. Iye sakukhulupirira kuti atate wake ali opanda moyo koma kuti pa imfa iwo “anawoloka” kuchokera kudziko looneka kumka kudziko losaoneka. Ibe akukhulupirira kuti atate wake achoka kudziko la nyama ndi mwazi ndi kuloŵa ku dziko la mizimu, malo a makolo akufa.

Ibe akulingalira motere: ‘Ngakhale kuti Atate salinso m’dziko lino, akundikumbukirabe ndipo amafuna kudziŵa za moyo wanga. Ndipo popeza kuti tsopano iwo ali mzimu ndipo ali ndi mphamvu zokulirapo, ali mumkhalidwe wabwino kwambiri wa kundithandiza kuposa mmene analiri pamene anali munthu padziko lapansi. Ndiponso, iwo akhoza kundilankhulira mwachindunji kwa Mulungu, popeza kuti Mulungu ndi mzimu nayenso. Atate angakhale okwiya pakali pano, koma ngati ndiwasonyeza ulemu woyenera, adzandikhululukira ndi kundidalitsa.’

Mu Afirika chikhulupiriro chakuti akufa amaona anthu padziko ndi kusonkhezera miyoyo yawo nchofala pakati pa ochita chipembedzo chamwambo. Chimaonekeranso pakati pa odzinenera kukhala Akristu. Mwachitsanzo, mkazi atakwatitsidwa m’tchalitchi, sichachilendo kuti iye apite kumudzi kwa makolo ake kukalandira dalitso lamwambo. Kumeneko amapembedzera makolo akufa, ndipo nsembe ya moŵa imatsanuliridwa kwa iwo. Anthu ochuluka amakhulupirira kuti kulephera kuchita zimenezi kumadzetsa tsoka paukwatiwo.

Amalingalira kuti makolo akufawo, kapena mizimu ya makolo, imatetezera miyoyo ya mabanja awo padziko ndi kuwalemeretsa. Malinga ndi lingaliro limeneli, mizimuyo imaonedwa kukhala athandizi amphamvu, okhoza kutheketsa zotuta zochuluka, kuchititsa umoyo wabwino, ndi kutetezera anthu ku tsoka. Iyo imachonderera m’malo mwa anthu. Komabe, itanyalanyazidwa kapena kukwiyitsidwa, imadzetsa tsoka​—matenda, umphaŵi, ngakhale imfa yeniyeniyo. Chifukwa chake, kupyolera mwa nsembe ndi dzoma, anthu amayesayesa kusunga unansi wabwino ndi akufa.

Kodi inu mumakhulupirira kuti akufa amachita mbali m’miyoyo ya amoyo? Kodi munayamba mwaimirirapo pamanda a wokondedwa wanu ndi kuyamba kulankhula mawu angapo, kuti mwina angakumveni? Eya, kaya akufawo amationa ndi kutimva kapena ayi zimadalira pa chimene chimachitika pa imfa. Tiyeni tipende zimene Baibulo limanena pa nkhani yofunika kwambiri imeneyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena