Lingaliro la Baibulo
Kodi Muyenera Kuwopa Akufa?
YAMBITSANI nkhani ya akufa, ndipo anthu ambiri amapeŵa kukambitsirana za iyo mowonjezereka. Komabe, ena samangokhala osamasuka pa nkhaniyo; amagwidwa ndi mantha. Chotero sikwachilendo kupeza miyambo yogwirizana ndi kuwopa akufa m’mafuko padziko lonse. Mwachitsanzo, tiyeni tione miyambo yopezeka ku maiko a ku Afirika a kumunsi kwa Sahara.
Mkazi wina mumzinda wina wa ku West Africa akukumbukira bwino kwambiri zimene zinachitika pamene wam’banja lake anamwalira. Iye akusimba kuti: “Wachibale ankakonza mbale ya chakudya nthaŵi zonse kaamba ka wakufa ndi kuiika m’chipinda chake chogona bwinobwino. Pamene sanalipo, ndinali kupita kukadya chakudyacho. Pamene wachibaleyo anabwerera, ankakondwa kwambiri! Iye ankakhulupirira kuti wakufayo walandira zakudya zabwinozo. Zimenezi zinachitika kwa nthaŵi yakutiyakuti mpaka pamene ndinadwala. Chikhumbo changa cha kudya chinatha ndipo sindinakhoze kudya chakudya chilichonse. Zimenezi zinandichititsa mantha! Ambiri a achibale anga ankanena kuti kudwala kwanga kunachititsidwa ndi wachibale wathu wakufayo. Ayenera kukhala atakwiyitsidwa ndi winawake m’banjamo, iwo analingalira motero.”
Mumzinda umodzimodziwo, ngati banja lakhala ndi mapasa ndipo mmodzi amwalira, palibe amene ayenera kulankhula za wakufayo m’nyumbamo. Ngati wina afunsa za winayo amene anafa, mwamwambo banjalo limayankha kuti: “Wapita kukagula m’chere.” Amakhulupirira mwamphamvu kuti moyo wa winayo amene ali ndi moyo udzatengedwa ngati alankhula choonadi.
Ndiyeno, tapangani chithunzi ichi m’maganizo: Mwamuna amene anali ndi akazi atatu wamwalira. Tsiku la pambuyo pa maliro, zovala zoyera zapadera zipangidwira akaziwo. Panthaŵi imodzimodziyo, malo apadera opangidwa ndi mitengo ndi udzu amangidwa pafupi ndi nyumbayo, kumene akaziwa adzasambira ndi kuvala zovala zoyerazo. Palibe amene ayenera kuloŵa kumalowo kusiyapo iwo ndi mkazi amene waikidwa kuti awathandize. Atatuluka m’malo osambira apadera ameneŵa, nkhope za akaziwo zaphimbidwa ndi nsalu. Akaziwo avalanso sebe, chingwe chamkhosi cha “chitetezero.” Kusamba kwamwambo kumeneku kukuchitidwa Lachisanu ndi Lolemba lililonse kwa masiku 100. Mkati mwa nthaŵi imeneyi iwo sangatenge chinthu chilichonse mwachindunji kuchokera kwa mwamuna aliyense. Ngati mwamuna akufuna kuwapatsa chinachake, ayenera choyamba kuchiika pansi kapena pathebulo. Ndiyeno mkaziyo adzachitenga. Palibe amene akuloledwa kukhala kapena kugona pa kama wa akazi ameneŵa. Nthaŵi zonse pamene achoka panyumba, onse ayenera kutenga ndodo yapadera. Akulingalira kuti kukhala ndi ndodo imeneyi kudzaletsa mwamuna wawo wakufayo kuwaukira. Ngati malangizowa satsatiridwa, akulingalira kuti mwamuna wawo wakufayo angakwiyitsidwe ndi kuwavulaza.
Zochitika zotero nzofala ku mbali imeneyo ya dziko. Komabe, mitundu imeneyi ya miyambo si ya mu Afirika mokha.
Mantha a Akufa Ngapadziko Lonse
Insaikolopediya ina, Encarta, imanena zotsatirazi ponena za mmene anthu amaonera makolo awo akufa: “Achibale akufa . . . amakhulupiriridwa kuti akhala zolengedwa zamphamvu zauzimu kapena, nthaŵi zina, kuti akhala milungu. [Lingaliro limeneli] nlozikidwa pa chikhulupiriro chakuti makolo akufa ndi ziŵalo zokangalika zachitaganya, ofunitsitsabe kudziŵa nkhani za achibale awo amoyo. Zimenezi zaonedwa kwambiri m’zitaganya za ku West Africa . . . , ku Polynesia ndi Melanesia (Adobu ndi Amanusi), pakati pa anthu osiyanasiyana ku Indo-Europe (a Skandinaviya akale ndi Ajeremani), ndipo makamaka ku China ndi Japan. Ambiri amakhulupirira kuti makolo akufa ali ndi ulamuliro waukulu, okhala ndi mphamvu zapadera zimene amalamulira nazo zochitika kapena kulamulira ubwino wa achibale awo amoyo. Chitetezo cha banja ndicho chimodzi cha nkhaŵa zawo zazikulu. Amaonedwa monga nkhoswe pakati pa mulungu wamkulu kapena milungu, ndi anthu, ndipo angalankhule ndi amoyo mwa maloto ndi mwa kugwidwa ndi mzimu wawo. Amawopedwa ndi kupatsidwanso ulemu. Ngati anyalanyazidwa, makolo akufawo angabweretse matenda ndi masoka ena. Kuwatonthoza, kupembedza, pemphero, ndi nsembe ndizo njira zosiyanasiyana zimene amoyo angalankhulire ndi makolo awo akufa.”
Ndithudi, chuma cha banja chikhoza kutha chifukwa cha kuwopa akufa. Kaŵirikaŵiri, mapwando ambambande ofuna zakudya ndi zakumwa, nyama zamoyo zopereka nsembe, ndi zovala zamtengo wapatali zimafunidwa ndi awo amene amakhulupiriradi kuti akufa ayenera kuwopedwa.
Koma kodi achibale kapena makolo akufa alidi mumkhalidwe umene umafunikira kuwopedwa ndi kupatsidwa ulemu? Kodi nchiyani chimene Mawu a Mulungu, Baibulo, amanena?
Kodi Akufa Angakuvulazeni?
Mungakondwe kudziŵa kuti Baibulo limanenapo pa zikhulupiriro zimenezo. M’buku la Deuteronomo, machitachita okhudza kuwopa akufa amatchulidwa. Ilo limati:
‘Asapezeke mwa inu munthu . . . wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.’—Deuteronomo 18:10-12.
Onani kuti Yehova Mulungu anatsutsa miyambo imeneyi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti njozikidwa pa bodza. Bodza lalikulu ponena za akufa ndilo lakuti sou simafa. Mwachitsanzo, magazini akuti The Straight Path ananena zotsatirazi ponena za zimene zimachitikira akufa: “Imfa kwenikweni ndiyo kutuluka kwa sou. . . . Manda ndiwo mosungira thupi lokha, osati sou.”
Baibulo silivomereza. Dziŵerengereni nokha Ezekiel 18:4: “Taonani, sou zonse ndi zanga; monga sou ya atate, momwemonso sou ya mwana ndizo zanga: sou yochimwayo, ndiyo idzafa.” (King James Version) Ndiponso, mkhalidwe wa akufa unamveketsedwa bwino m’Mawu a Mulungu pa Mlaliki 9:5 kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” Zimenezi zimafotokoza chifukwa chake chakudya chosiyidwira wakufa sichimadyedwa pokhapokhapo chitadyedwa ndi wina wamoyo.
Komabe, Baibulo silimangotisiya opanda chiyembekezo ponena za awo amene ali m’manda. Angakhalenso ndi moyo! Baibulo limanena za ‘chiukiriro.’ (Yohane 5:28, 29; 11:25; Machitidwe 24:15) Chimenechi chidzachitika panthaŵi yoikidwa ya Mulungu. Pakali pano, akufa sakudziŵa kalikonse m’manda, ‘akugona,’ kufikira nthaŵi ya Mulungu yakuti ‘auke.’—Yohane 11:11-14; Salmo 13:3.
Anthu ambiri amawopa zinthu zosadziŵika. Chidziŵitso cholongosoka chingamasule munthu pa mantha opanda maziko. Baibulo limatipatsa choonadi ponena za mkhalidwe wa awo amene ali m’manda. Kunena mwachidule, simuyenera kuwopa akufa!—Yohane 8:32.