Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Achichepere Ena Amangosangalala Mmene Amafunira?
“Timangofuna kusangalala, koma nzovuta kwambiri,” anadandaula motero Jason wazaka 15.
NKWACHIBADWA kufuna kusangalala—makamaka pamene uli wachichepere! Kwa achichepere ambiri, kusangalala nkofunika monga momwe kudya ndi kugona kulili. Atasonkhezeredwa ndi ausinkhu wawo ndi oulutsa nkhani, achichepere amalondola zosangulutsa zambiri zosiyanasiyana. Malinga ndi kufufuza kwina, kuchezera mabwenzi, kuonerera TV, kupita ku mafilimu, kuchita mapwando, ndi kuvina ndizo zinali zoyambirira pa mndandanda wa zinthu zokondedwa kwambiri zotayirako nthaŵi zamadzulo pakati pa achichepere. Kuŵerenga, kuchita maseŵero, ndi kumvetsera nyimbo zinalinso zokondedwa.
Pokhala pali zosangalatsa zambiri chotero, mwinamwake achikulire sangamvetse chifukwa chimene achichepere ena, monga Jason, amaona kuti samasangalala kwambiri. Koma zimenezo ndizo zimenedi achichepere ena achikristu anena! Casey wachichepere, mmodzi wa Mboni za Yehova, anati: “Umaona anzako onse kusukulu akumachita mapwando ndi kumachita zinthu zosiyanasiyana, ndipo umamvadi kukhala ukutsalira.” Koma kodi mkhalidwewo ngwoipadi?
Kodi Baibulo silimalola kukhala ndi nthaŵi ya kusangalala? Kutalitali. Baibulo limatcha Yehova kukhala “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Chotero siziyenera kukudabwitsani kuti Mfumu Solomo inati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake . . . ; mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:1, 4) Panopo liwu lenileni lachihebri lakuti “kuseka” ndi mawu ena ofanana nalo angatanthauzenso “kuchita phwando,” “kuseŵera,” “kuchita maseŵero,” ‘kusangalatsa,’ ndi “kukhala ndi nthaŵi ya kusangalala.”—2 Samueli 6:21; Yobu 41:5; Oweruza 16:25; Eksodo 32:6; Genesis 26:8, NW.
Kumbuyoku m’nthaŵi za Baibulo, anthu a Mulungu ankasangalala ndi zinthu zabwino zosiyanasiyana, zonga kuliza ziŵiya zoimbira, kuimba, kuvina, kucheza, ndi kuchita maseŵero. Analinso ndi nthaŵi zapadera za mapwando, ndi mayanjano osangalatsa. (Yeremiya 7:34; 16:9; 2 Samueli 13:23-28; 25:30 Luka 15:25) Ehe, Yesu Kristu iye mwini anapita ku phwando laukwati!—Yohane 2:1-10.
Chotero kusangalala kwabwino sikoletsedwa pakati pa Akristu achichepere lerolino. Inde, Baibulo limati: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako.” Komabe, Solomo akuchenjeza pambuyo pake kuti: “Koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.” (Mlaliki 11:9) Inde, kwa Mulungu muli ndi thayo pa zosankha zimene mumapanga. Chotero ponena za kusanguluka muyenera ‘kupenya bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru.’ (Aefeso 5:15, 16) Chifukwa chake? Achichepere ambiri amapanga zosankha zoipa pankhaniyi.
Pamene Kusangalala Kukhala Kosalamulirika
Talingalirani za zimene zinachitika kumbuyoku m’nthaŵi za Baibulo. Aisrayeli ena anatayirira khalidwe ponena za kusanguluka, akumachita mapwando osalamulirika usiku wonse! Mneneri Yesaya anati: “Tsoka kwa iwo amene adzuka mmamaŵa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m’mapwando awo.” Sindiye kuti kukumana pamodzi ndi kusangalala ndi zakudya, nyimbo, ndi kuvina kunali kolakwika. Koma Yesaya akuti ponena za ochita mapwando aphokoso ameneŵa: “Sapenyetsa ntchito ya Yehova.”—Yesaya 5:11, 12.
Achichepere ambiri lerolino amachita chimodzimodzi—samalingalira Mulungu pamene akusanguluka. Ena amanyalanyaza miyezo yaumulungu modzigangira, akumagonana popanda ukwati, kuwononga zinthu mwadala, kugwiritsira ntchito anamgoneka, ndi makhalidwe ena osadziletsa nati ndiko “kusangalala.” Komabe, m’zochitika zina, achicheperewo samafuna kukhala oipa. Koma amalephera kuchita zinthu mwachikatikati ndi kupeŵa zomkitsa. (Miyambo 23:20; 1 Timoteo 3:11) Chotero pamene akumana pamodzi kuti asangalale, zinthu kaŵirikaŵiri zimakhala zosalamulirika.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:6-8.
Posachedwapa, Galamukani! anafunsa achichepere ena kuti “Kodi nchiyani chimene chimachitika pamapwando akudziko lerolino?” Mtsikana wina anayankha kuti: “Anamgoneka ndi kumwetsa. Zimachitikadi.” Andrew wachichepere anati ponena za achichepere ena a pasukulu yake amene amapita kumapwando: “Iwo amangodzitama pa kuchuluka kwa moŵa umene anamwa.” Jason anafikadi pa kunena kuti: “Pafupifupi phwando lililonse lakudziko limakhala ndi zochitika zoipa.” Popeza kuti “mapwando aphokoso,” kapena “mapwando osalamulirika,” amatsutsidwa m’Baibulo, kaŵirikaŵiri achichepere owopa Mulungu amapeŵa macheza amene amakhala ndi zinthu zimenezi.—Agalatiya 5:21; Byington.
Pangakhale ngozi ngakhale pa zosangulutsa zimene zingaonekere kukhala zosavulaza. Mwachitsanzo, ambiri a mafilimu otchuka a masiku ano amasonyeza za umaliseche, kugonana kwapoyera, ndi chiwawa choipitsitsa. Kaŵirikaŵiri nyimbo zotchuka zimakhala ndi mawu auchiwerewere. Pa makonsati a rock nthaŵi zambiri pamakhala kugwiritsira ntchito anamgoneka, phokoso losalamulirika, ndi chiwawa.a
Pamene Makolo Akana
Kodi chenicheni chachikulu nchiyani? Ngati ndinu Mkristu, simungachite zonse zimene ausinkhu wanu amasangalala kuchita. Ndi iko komwe, Yesu ananena kuti otsatira ake ‘sadzakhala a dziko lapansi,’ ndipo zimenezo zimatanthauza kukhala osiyana ndi anthu ena. (Yohane 15:19) Ngati makolo anu amawopa Mulungu, zimenezi amazidziŵa bwino lomwe. Chotero nthaŵi zina, pofunitsitsa kukutetezerani, makolo anu sangayamikire zinthu zina kapena angaziletseretu molimba—zinthu zimene achichepere ena amaloledwa kuchita. Zimenezi zimavuta kuzivomereza nthaŵi zina. “Anthu amafuna kusangalala!” ananenetsa motero mtsikana wina. “Makolo athu ankasangalala pamene anali aang’ono, koma nthaŵi zina zimaoneka ngati kuti akufuna kutitsekereza ku zonse.”
Kutsatira uphungu wa makolo anu pankhani zimenezi kungakhale kovuta, ngakhale pamene kwenikweni mukuvomerezana ndi lingaliro lawo. Wachichepere wina wokonda maseŵero amene tidzatcha kuti Jared akukumbukira kuti: “Ndinali kufuna kuti ndiziseŵera basketball m’timu ya sukulu. Anthu ambiri anali kundisonkhezera kuti ndiziseŵera, ndipo zinachita ngati zandivutitsa. Komano ndinalankhula ndi makolo anga.” Makolo a Jared anatchula za ngozi za “mayanjano oipa” namkumbutsa za mmene maseŵero ake adzakhalira odya nthaŵi. (1 Akorinto 15:33) “Zinathera pompo,” Jared akutero mwachisoni. Iye analabadira uphungu wa makolo ake, koma sanamve bwinobe kuti sanayambe kuseŵera mpirawo.
‘Ndikutsalira!’
Mulimonse mmene mkhalidwe wanu ulili, inunso nthaŵi zina simungakondwe pamene mumva anzanu a pasukulu akumadzitama pa kusangalala kwawo. ‘Kodi nchifukwa ninji achichepere ena amangosangalala mmene amafunira?’ mungafunse motero. Inde, kodi mungagonjetse motani malingaliro akuti mukumanidwa?
Kungakhale kothandiza ngati mwaŵerenga Salmo 73 ndi kusinkhasinkha pachokumana nacho cha wolemba Baibulo wina wotchedwa Asafu. M’mavesi 2 ndi 3, akuvomereza motero: “Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira.” Inde, pamene kuli kwakuti Asafu anali ndi moyo wokhala ndi ziletso, ena ankadzitamandira kuti ankachita zilizonse zimene ankafuna—mwachionekere popanda zotulukapo zoipa. Zichita ngati kuti anali ndi zinthu zambiri ndipo anali kupeza zowonjezereka nthaŵi zonse. (Vesi 12) Chotero Asafu analefulidwa kwambiri kwakuti anadandaula kuti: “Chotero, kodi ndinadzisunga woyera ndi wosachita tchimo kwachabe?”—Salmo 73:13, Today’s English Version.
Mwamwaŵi, Asafu anazindikira asanachite chilichonse mothamangira. Anapita ku “zoyera za Mulungu,” ndipo pamalo abwino amenewo, analingalira za nkhaniyo mwamphamvu. Posapita nthaŵi Asafu anafika pa chigamulo chabwino kwambiri cha nkhani yonena za ofunafuna chisangalalo osapembedzawo kuti: “Indedi muwaika poterera: muwagwetsa kuti muwawononge.”—Salmo 73:17, 18.
Zimenezi zinganenedwenso pa ambiri a ausinkhu anu ofunafuna zosangulutsa. Iwo angalingalire kuti akusangalala tsopano. Koma zokondweretsa za uchimo nzosakhalitsa! (Ahebri 11:25) Chifukwa chakuti samatsatira miyezo ya Baibulo, iwo akuima “poterera” ndipo nthaŵi zonse ali pangozi ya kugwa moipitsitsa—mwadzidzidzi ndipo popanda chenjezo. Mawu a Mulungu amati: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Mosakayikira mwamvapo za achichepere ausinkhu wanu amene amwalira kale mwadzidzidzi, atenga matenda opatsirana mwa kugonana, atenga mimba zosafunidwa, kapena kuponyedwa m’ndende chifukwa cha “chisangalalo” changozi. Motero, kodi kusaloŵa m’zinthu zimenezo sikopindulitsa kwa inu?—Yesaya 48:17.
Solomo akupereka uphungu wabwino pamene akuti: “Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse; pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.” (Miyambo 23:17, 18) Inde, palibe nthaŵi ‘yosangalatsa’ imene tingailole motaya chiyembekezo cha munthu mwini cha kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.
Pakali pano, kodi mungakhutiritse motani chikhumbo chanu chachibadwa cha kusangalala nthaŵi zina? Kodi pali njira zachisungiko ndi zabwino zochitira motero? Bwanji ngati mulibe ndalama zokwanira ndi zinthu zina? Galamukani! anafunsa achichepere kuzungulira dziko kaamba ka njira zina ndi malingaliro. Zimenezi zidzafotokozedwa m’nkhani yamtsogolo ya mpambo uno.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndiyenera Kupita ku Makonsati a Rock?” m’kope la January 8, 1995.
[Chithunzi patsamba 28]
Kodi muyenera kumva kukhala mukutsalira chifukwa chakuti simungaloŵe m’zimene dziko limatcha ‘chisangalalo?’