Mutu 8
Kodi Muyenera Kuopa Akufa?
SI ALI yense amaona akufa kukhala ofunikira chithandizo. Chimene’nso chiri chofala kwambiri ndicho chikhulupiriro chakuti amoyo ndiwo amene amafunikira chithandizo—kuwatetezera kwa akufa. Usiku, kumanda kawiri-kawiri kumapewedwa. Modabwitsa, ngakhale achibale ndi mabwenzi amene anakondedwa pamene anali moyo, pambuyo pa imfa angafikire kuonedwa kukhala ochititsa mantha ndi oopsya.
Pakati pa Amwenye okhala m’mapiri a Central Chiapas, Mexico, tsabola amafukizidwa pa tsiku la kuika maliro. Kumene’ku kumachitidwa moyembekezera kuti utsi wosakondweretsa udzachititsa moyo wa munthu wakufa’yo kutuluka m’nyumba’yo.
M’mbali zina za Yuropu, anthu amatsegula mwamsanga makomo ndi mazenera onse mwamsanga pamene ifa ichitika. Zimene’zi zimachitidwa ndi lingaliro la “kumasula” moyo. Kotero kuti malodza asakhale ali pa yense, chiwalo cha banja’lo chimaika manja a munthu wakufa’yo pa mtima pake ndipo chimatseka maso a munthu’yo ndi makobiri.
Pamene Mbuda wa ku Mongolia afera m’hema, mtembo wake sumatulutsiridwa pa khomo la masiku onse. Khomo lina kungabooledwe pa hema’yo ndipo, pamene mtembo’wo watulutsidwa, khomo limene’li limatsekedwa. Kapena chophimbira chaudzu chingaikidwe pa khomo la nthawi zonse’lo. Mtembo’wo utatulutsidwamo, chophimbira chaudzu’cho chimatenthedwa. Chifuno cha kachitidwe kotero’ko ndicho kuletsa mzimu wa munthu wakufa’yo kubwerera m’nyumba’yo ndi kubvulaza amoyo.
M’mbali zambiri za Afirika, pamene matenda agwa m’banja, pamene mwana amwalira, pamene bizinesi sikuyenda bwino kapena tsoka la mtundu uli wonse lichitika, mwamuna mwamsanga adzapita kukafunsa sing’anga. Kawiri-kawiri wamaula’yo amamuuza kuti chiwalo chakufa cha banja’lo chakwiyitsidwa. Ula umafunsidwa ndipo nsembe zimachulidwa. Sing’anga’yo amalipiritsa zimene’zi ndalama zochuluka ndipo’nso amatenga nyama ya chiweto chiri chonse chimene chaperekedwa nsembe.
Kodi anthu ayenera kuopa akufa motero, ngakhale kufika pa kuononga ndalama zambiri kuti adzitetezere?
Baibulo ponena za akufa limati: “Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kali konse kachitidwa pansi panso.” (Mlaliki 9:6) Chotero palibe chibvulazo chimene chingadze kwa inu kuchokera kwa akufa. Ndipo palibe ali yense amene angatsutse mau a Baibulo amene’wa.
Zoona, anthu anganene kuti zooneka zina zimachitizidwa ndi mizimu ya akufa. Iwo anganene kuti iwo anapeza mpumulo ku matenda, mabvuto a kusowa ndalama ndi zina zofanana nazo pambuyo pa kutonthozedwa kwa mizimu ya akufa. Koma kodi sipangakhale magwero ena a bvuto lotero’lo ndi mpumulo wachionekere ku bvuto?
Kodi si kodabwitsa kuti anthu ali osazindikira kukhala atakhumudwitsa wachibale wakufa kufikira kufunsa kwao sing’anga kapena wina wake wokhala ndi malo antchito ofanana’wo? Ndipo, kodi n’chifukwa ninji kuyenera kukhala kwakuti “mzimu” wa atate, amai, mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi wakufa ukaononga chimwemwe ndi thanzi la awo amene, kale, anali kukondedwa kwambiri? Kodi n’chiani chimene chikachititsa “mzimu” wa munthu wakufa kukhala wolipsyira pamene umene’wo sunali mkhalidwe wa munthu’yo pamene anali ndi moyo? Popeza kuti zimene zimanenedwe kukhala zochititsidwa ndi akufa kawiri-kawiri zimakhala zosemphana kwambiri ndi umunthu wa munthu’yo pamene anali wamoyo, kodi zimene’zi sizipereka chichirikizo champhamvu ku lingaliro lakuti “mizimu” ya akufa sikulowetsedwamo? Ndithudi chikapereka. Baibulo liri’di lolondola pamene limanena kuti akufa ‘alibe gawo liri lonse m’chiri chonse chimene chiyenera kuchitidwa kunja kuno.’
Lingalirani’nso chiyambukiro chobvulaza chimene kuopa akufa kumakhala nacho pa amoyo. Ambiri alowetsedwa mu ukapolo kwa asing’anga kapena atsogoleri ena achipembedzo amene amanena kuti mwai ndi masoka a mwamuna kapena mkazi zimalamuliridwa kwakululu-kulu ndi “mizimu” ya akufa. Anthu amene’wa adzikhazikitsa monga anthu amene angathe kukonza zinthu ndi akufa okhumudwitsidwa’wo. Pokhulupirira mau ao, anthu ambiri aononga ndalama zochuluka pa madzoma oonongetsa ndalama kwambiri, ndalama zimene iwo akanazigwiritsira ntchiro m’njira ina kaamba ka zinthu zofunika za moyo. Ngakhale kuli kwakuti ena amanena kuti iwo ndithudi athandizidwa mwa madzoma otero’wo, kodi chokumana nacho chao chapanga mwa iwo chisangalalo cheni-cheni m’kukhala atakhala ndi mwai wa kuchita kanthu kena kuthetsa kusagwirizana ndi wakufa wokondedwa’yo? M’malo mwake, kodi iwo samachita mofanana kwambiri ndi munthu amene walandidwa kanthu kena?
Pamenepo, talingalirani’nso, njira zachinyengo zimene zimagwiritsiridwa ntchito kawiri-kawiri—kufukiza tsabola, kutulutsira wakufa’yo pa khomo lina la chihema ndi zina zotero—kuletsa “mizimu” wa wakufa’yo kusabwera’nso ndi kubvutitsa amoyo. Kodi mungafune kunyengedwa motere m’kati mwa nthawi ya moyo wanu? Kodi n’koyenera kwa munthu kuyesa kunyenga anthu akufa amene iye sakanafuna kuwanyenga pamene anali moyo?
Kachitidwe keni-keni’ko ka kutembenukira ku chinyengo kangathe’nso kukhala ndi chiyambukiro choipa pa munthu. Pamene munthu angobvomereza kunyenga akufa amene iye amawaona kukhala akupitirizabe kukhala ndi moyo wozindikira, kodi iye sadzafooketsa chikumbu mtima chake mpaka kufika pa kuyesa kunyenga amoyo pamene kumene’ko kuonekera kukhala kopindulitsa.
Uyo amene amadzidziwikitsa m’Baibulo kukhala Mulungu woona sakadabvomereza machita-chita amene akhalako chifukwa cha kuopa akufa kwa anthu. Kulekeranji kutero? Chifukwa chakuti machita-chita amene’wo, kuphatikiza pa kukhala ozikidwa pa lingaliro lonyenga, ali osagwirizana kotheratu ndi umunthu Wake, njira ndi machitidwe. “Mulungu sindiye munthu, kuti aname.” (Numeri 23:19) Iye samabvomereza chinyengo chochitidwa kaamba ka phindu ladyera. Baibulo limanena kuti: “Munthu . . wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.”—Salmo 5:6.
Popeza kuti Baibulo limabvumbula kuti akufa ali osadziwa kanthu, kodi n’chifukwa ninji muyenera kuwaopa? (Salmo 146:4) Iwo sangakuthandizeni kapena kukubvulazani. Inu tsopano mukudziwa kuchokera m’Baibulo kuti “moyo” umafa ndi kuti “mzimu” sumakhala ndi moyo wozindikira popanda thupi. Zooneka ziri zonse zimene zichititsa kuopa akufa chifukwa cha chimene’cho ziyenera kukhala zochokera ku magwero ena. Popeza kuti m’zochitika zina anthu amanena kukhala atapeza kuongokera kwina m’zobvuta zao chifukwa cha kuchita machitidwe a kutonthoza akufa, magwero amene’wa akayenera kukhala uyo amene ali wofunitsitsa kudzetsa mpumulo wakanthawi, koma kaamba ka cholinga cholakwa. Kodi n’chiani chimene chiri cholinga chake? Kuchititsa anthu kukhalabe mu ukapolo ndi kuchititsidwa kusaona njira ya ku moyo wopanda mantha ndi chinthenthe.
N’kofunika kudziwa magwero amene’wa.
[Chithunzi patsamba 71]
Kuopa akufa kumasonkhezera ambiri kufunsa asing’anga