Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 12/8 tsamba 4-7
  • Kodi Ndani Amene Amakhala m’Malo a Mizimu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Amene Amakhala m’Malo a Mizimu?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse
  • Angelo, Atumiki Amphamvu a Mulungu
  • Satana ndi Ziŵanda, Adani a Mulungu ndi Munthu
  • Kodi Makolo Ali Kuti?
  • Kubwerera Kunthaka
  • Ali Kudziko la Mizimu Ndani?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
  • Kodi Makolo Athu Ali Kuti?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
  • Kodi Anthu Akafa Amapita Kudziko la Mizimu?
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Masomphenya a Zinthu Zakumwamba
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 12/8 tsamba 4-7

Kodi Ndani Amene Amakhala m’Malo a Mizimu?

DZIKO lakhala ngati “supamaliketi” ya zikhulupiriro zachipembedzo ndi ziphunzitso. Mu Afirika mokha muli magulu azipembedzo zikwi zambiri, chilichonse chokhala ndi malingaliro akeake ponena za amene amamka kumalo a mizimu. Koma kuti tikhale ndi chithunzi chabwino ndiponso choona, tifunikira kupenda Baibulo. Limadziŵikitsa mizimu—yabwino ndi yoipa yomwe—imene imakhala kumalo a mizimu. Limasonyezanso amene tingampempheko thandizo ndi chitetezero ndi kuzilandira.

Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse

Chipembedzo cha makolo mu Afirika chimaphunzitsa kuti Mulungu wamphamvuyonse ndiye amene amatsogolera makolo ndi milingu ina. Buku lakuti African Mythology likuti: “Palibe chikayikiro chilichonse chakuti pafupifupi mafuko onse a mu Afirika, ngati saali onse amene, amakhulupirira mwa Munthu wina Wapamwamba, mlengi wa zinthu zonse.” Buku lakuti African Religion in African Scholarship likunena kuti: “Popeza kuti Mulungu ndiye wolamulira chilengedwe chonse, zinthu zina zonse ndi mphamvu zonse zakhalako chifukwa cha Iye. Ulamuliro wonse ndi mphamvu uli mwa Iye.”

Baibulo limavomereza kuti pali Uyo amene ali ulamuliro wapamwamba m’malo a mizimu. Limamfotokoza kukhala ‘Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi wowopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.’—Deuteronomo 10:17.

Mu Afirika monse muli maina wamba ndi maina aulemu zikwi zambiri operekedwa kwa uyo amene amamlingalira kukhala wapamwamba. Komabe, kodi Mawu a Mulungu amati bwanji ponena za dzina la Mulungu? Wamasalmo analemba kuti: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Dzina lopatulika limeneli limapezeka m’Baibulo nthaŵi zoposa 7,000, ngakhale kuti otembenuza Baibulo ena alichotsamo ndi kuikamo maina aulemu onga akuti “Mulungu” kapena “Ambuye.”

Chifukwa chakuti Yehova ndi wamphamvuyonse, angathe kutithandiza. Amadzilongosola iye mwini kukhala “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.”—Eksodo 34:6, 7; 1 Samueli 2:6, 7.

Angelo, Atumiki Amphamvu a Mulungu

Kalekale Yehova asanalenge anthu kapenanso ngakhale dziko lenilenilo, analenga anthu auzimu kumwamba. Baibulo limanena kuti panthaŵiyo pamene Mulungu ‘anaika maziko a dziko lapansi . . . , ana onse [aungelo] a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.’ (Yobu 38:4-17) Pali angelo miyandamiyanda. Danieli mtumiki wa Yehova analemba za masomphenya a zinthu zakumwamba mmene anaona “zikwizikwi anamtumikira [Mulungu], ndi unyinji wosaŵerengeka unaima pamaso pake.”—Danieli 7:10.

Munthu woyamba wauzimu amene Yehova analenga anali uyo amene anadzadziŵika monga Yesu Kristu. (Yohane 17:5; Akolose 1:15) Asanakhale munthu padziko lapansi, Yesu anakhala ndi moyo kumwamba monga cholengedwa chauzimu champhamvu. Pambuyo pa imfa yake monga munthu, Yesu anaukitsidwira kumwamba, kumene anapitiriza kukhala ndi moyo monga cholengedwa chauzimu champhamvu.—Machitidwe 2:32, 33.

Yesu ali ndi mphamvu yaikulu kumwamba. Pa Yuda 9, Yesu, wodziŵikanso kuti Mikayeli, amatchedwa “mkulu wa angelo,” kutanthauza kuti iye ndiye wamkulu, kapena mngelo wotsogolera. (1 Atesalonika 4:16) Alinso ndi ulamuliro padziko lapansi. Yehova wampatsa “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire.” (Danieli 7:13, 14) Ngakhale kuti ali ndi ulamuliro waukulu, Yesu ali wogonjera kwa Atate wake, Yehova.—1 Akorinto 11:3.

Pamene kuli kwakuti angelo okhulupirika amatumikira Yehova, iwo amatumikiranso atumiki a Mulungu padziko lapansi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kodi siili yonse mizimu [angelo] yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzaloŵa chipulumutso?” (Ahebri 1:14) Iwo makamaka amafuna kuti anthu aphunzire choonadi chonena za Yehova. Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu; ndi kunena ndi mawu aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero.”—Chivumbulutso 14:6, 7.

Satana ndi Ziŵanda, Adani a Mulungu ndi Munthu

Mwachisoni, si angelo onse amene akhala okhulupirika kwa Mulungu. Ena anampandukira, akumakhala adani a Mulungu ndi anthu. Wopanduka wamkulu ndiye Satana Mdyerekezi.

Pamene kuli kwakuti ambiri lerolino amati Satana kulibe, palibe aliyense amene amakana za kukhalako kwa kuipa. Kukhulupirira kuti kuipa kuliko pamene sukhulupirira kuti kuli ndi wokuchititsa kumabweretsa “vuto losazembeka,” likutero buku lakuti The Death of Satan. “Tikuzindikira kuti pali chinthu chimene mwambo wathu sumatipatsa konse mawu ochifotokozera.”

Mosiyana ndi zimenezo, Baibulo lili ndi mawu ndipo limalongosola bwinobwino choonadi chonena za magwero a kuipa. Limalongosola kuti zolengedwa zonse zaungelo zimene Yehova analenga zinali zolungama ndi zabwino; iye sanalenge angelo alionse oipa. (Deuteronomo 32:4; Salmo 5:4) Komabe, angelowo, mofanana ndi anthu, anapatsidwa mphamvu ya kusankha chabwino kapena choipa. Mmodzi wa ana auzimu ameneŵa angwiro anakhala ndi chikhumbo chadyera cha kulanda kulambira kumene moyenerera kuli kwa Yehova. Motero iye anadzipezera dzina lakuti Satana, limene limatanthauza “Wotsutsa.” (Yerekezerani ndi Yakobo 1:14, 15.) Satana saali watsenga wamba, monga momwe zipembedzo zina za mu Afirika zimaphunzitsira; ndiponso saali “mlonda” amene amatetezera aja amene amapereka nsembe kwa iye nthaŵi zonse. Baibulo limamsonyeza kukhala woipitsitsa ndi wolusa.

Angelo ena anagwirizana ndi Satana popandukira Mulungu. Ziŵanda za angelo zimenezi zilinso adani a anthu padziko lapansi. Nazonso nzanjiru ndiponso nzoipa. Kale, zinachititsa anthu ena kusalankhula ndi khungu. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Ena, kuphatikizapo ana, zinawasautsa ndi nthenda ndi misala. (Mateyu 17:15, 18; Marko 5:2-5) Mwachionekere, palibe munthu wanzeru amene angafune kuchita kanthu kalikonse ndi Satana kapena ndi ziŵanda zimenezo.

Kodi Makolo Ali Kuti?

Anthu miyandamiyanda a mu Afirika ndi mbali zina amakhulupirira kuti imfa sili mapeto a moyo koma kuti yangokhala njira yosamukirira kwina, kupita ku moyo kumalo a mizimu, malo a milungu ndi makolo omwe. Katswiri wina John Mbiti, wodziŵa kwambiri za zipembedzo za mu Afirika, akulemba za kukhulupirira mwa makolo, amene akuwatcha kuti “akufa amoyo”: “Imeneyi ndi ‘mizimu’ imene anthu a mu Afirika amaisamala kwambiri . . . Imadziŵa ndipo ili ndi chidwi pa zimene zimachitika m’banja [padziko lapansi]. . . . Ndiyo osamalira nkhani za banja, miyambo, makhalidwe ndi ntchito. Kuchita molakwa pa nkhani zimenezi ndiko kulakwiranso makolo amene, pokhala m’malo amenewo, amachita monga apolisi osaoneka a mabanja ndi mafuko. Chotero, chifukwa chakuti akali ‘anthu’, akufa amoyowo ndiwo gulu lopambana koposa la ankhoswe pakati pa anthu ndi Mulungu: amadziŵa zimene anthu amafuna, iwo anali pano ‘posachedwapa’ pamodzi ndi anthu, ndipo pa nthaŵi imodzimodziyo ali ndi njira zokwanira zolankhulana ndi Mulungu.”

Komabe, kodi Baibulo limanenanji za mkhalidwe wa akufa? Limasonyeza kuti kulibe “akufa amoyo.” Anthu amakhala amoyo kapena akufa—osati zonse. Mawu a Mulungu amaphunzitsa kuti akufa sangamve, sangaone, sangalankhule, kapena kuganiza. Akufa sangathe kuyang’anira amoyo. Baibulo limati: “Akufa sadziŵa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; . . . mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 6, 10) “[Munthu] abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:4.

Kubwerera Kunthaka

Ngati mukuona zimenezi kukhala zovuta kuvomereza, lingalirani zimene zinachitika kwa munthu woyamba, Adamu. Yehova anaumba Adamu “ndi dothi lapansi.” (Genesis 2:7) Pamene Adamu sanamvere lamulo la Yehova, chilango chake chinali imfa. Mulungu anati kwa iye: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—Genesis 3:19.

Yehova asanalenge Adamu kuchokera kufumbi, Adamu kunalibe. Chotero pamene ‘anabwerera kunthaka,’ iyeyo kachiŵirinso anakhala wopanda moyo, monga fumbi. Sanawolokere ku malo a mizimu ya makolo. Sanapite kumwamba kapena ku helo. Pamene anafa, amenewo ndiwo anali mapeto ake.

Kodi chinthu chimodzimodzicho chimachitika kwa anthu ena pa imfa? Inde, chimachitika. Baibulo limati: “Onse [anthu ndi nyama zomwe] apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.” (Mlaliki 3:20) Baibulo limalonjeza kuti Mulungu adzaukitsa anthu akufa kukhala amoyo m’dziko la paradaiso, komano nthaŵiyo ikali mtsogolo. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Pakali pano, ife sitiyenera kuwopa akufa kapena kupereka nsembe kwa iwo, popeza kuti iwowo sangatithandize kapena kutivulaza.

Satana ndi ziŵanda zake amafuna kusokeretsa anthu ponena za mkhalidwe wa makolo awo akufa, chotero amachirikiza bodza lakuti anthu amapitiriza kukhala ndi moyo pambuyo pa imfa. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndiyo kupyolera mu nkhani zonama. (1 Timoteo 4:1) Amagwiritsiranso ntchito masomphenya, maloto, ndi obwebweta kunyengera anthu kuti ayambe kuganiza kuti alankhula ndi akufa. Koma saali akufawo amene amalankhula nawo. M’malo mwake, ziŵanda nzimene zimayerekezera kukhala anthu amene afa. Nchifukwa chake Yehova amatsutsa mwamphamvu aja amene amafunsira kwa akufa, mwachindunji kapena m’njira zina, monga kupenduza.—Deuteronomo 18:10-12.

[Chithunzi patsamba 6]

Mwa masomphenya, maloto, ndi obwebweta, ziŵanda zimanyenga ndi kuwopseza anthu

[Zithunzi patsamba 7]

Kuti zisokeretse anthu, ziŵanda zimayerekezera kukhala aja amene afa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena