Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 12/8 tsamba 3-4
  • Kulankhulana ndi Akumalo a Mizimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhulana ndi Akumalo a Mizimu
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Makomo a Dziko la Mizimu
  • Kodi Ndani Amene Amakhala m’Malo a Mizimu?
    Galamukani!—1996
  • Mfumu Ifotokoza za Mtsogolo Mwake
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mafunso Okhudza Mmene Zilili Kumwamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Makolo Athu Ali Kuti?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 12/8 tsamba 3-4

Kulankhulana ndi Akumalo a Mizimu

PAKATI pa tauni ina ya ku West Africa panali nyumba yokongola, yopakidwa utoto woyera ndi wobiriŵira. Alembi aŵiri anali kugwira ntchito ndi mataipi m’chipinda chake cholandirira alendo. Anthu angapo anali atakhala m’mipando, akumayembekezera kuonana ndi babaláwo, wopenduza.

Kuseri kwa desiki la mu ofesi imene inali pafupi, babaláwo mwiniyo anakhala pafupi ndi makina a fax. Wokulupala, watsitsi loyamba kumera imvi, anavala mkanjo woyera wautali—wokwera mtengo, wokhala ndi zokometsera. “Atate wanga anali wopenduza,” iye anatero. “Ndinabadwira m’mwambo umenewo. Ndinakulira mmenemo. Pamene ndinafika zaka zisanu, pamene atate anali kupita kukapenduza, ndinali kutsagana nawo. Ndinali kuona mmene anali kuchitira, ndipo ndinkawatsanzira kufikira kunakhala mbali yanga yofunika.”

Babaláwo ameneyo analoza pabolodi lina lalikulu lathabwa losonyeza zipangizo zopenduzira zimene anthu a mtundu wake anagwiritsira ntchito m’mibadwo yambiri. Pokhala uli wozikidwa pa kuponya mbewu 16 za mngole, mchitidwewu uli wowanda ku West Africa konse ndi kwina. “Anthu amadza kwa ine ndi mavuto osiyanasiyana” iye anatero. “Kuvutana ndi akazi, kusabala, ulova, misala, thanzi, ndi zina zotero. Pempho limaperekedwa kwa makolo kapena ku mizimu [milungu], malinga ndi zotulukapo za kupenduza. Mulimonse mmene zingakhalire, nsembe ya mtundu winawake iyenera kuperekedwa.”

Mapembedzedwe a makolo, kuphatikizapo kupenduza, ngolimba kwambiri m’derali, ngakhalenso matchalitchi a Dziko Lachikristu. Pafupi ndi maofesi a babaláwo pali nyumba zopakidwa njereza zokhala ndi zikwangwani kumaso kwake zakuti: King Solomon II Church, Cherubim and Seraphim, Celestial Church of Christ, Christ Apostolic Church, Christ Trumpeters Church. Matchalitchi ameneŵa amagwirizana ndi mapembedzedwe a makolowo ndi kuwalandira nthaŵi zina. Babaláwo ameneyo anati: “Ndinali kulankhula ndi bishopu wina posachedwapa. Iye anafika kuno. Titakambitsirana nkhani zina kwa mphindi ngati 30, anati anafuna kuti ife tipange makonzedwe akuti Akristu ndi otsatira miyambo ya makolo akumane kuti akambitsirane ndi kupatsana malingaliro ndi kuthetsa kusamvana.”

Makomo a Dziko la Mizimu

Kusamvana kumeneko kaŵirikaŵiri kuli konena za amene kwenikweni amakhala kumalo a mizimu. Mu Afirika yense kummwera kwa Sahara, ambiri amakhulupirira kuti pali magulu aŵiri a anthu amene amakhala m’dziko la mizimu. Gulu loyamba lili la milungu, imene sinayambe yakhalapo anthu a dziko lapansi. Gulu lachiŵiri ndi la makolo, kapena mizimu ya akufa, amene ali ndi thayo la kuonetsetsa kuti mabanja awo padziko lapansi ali moyo ndiponso olemera. Amakhulupirira kuti magulu aŵiri onsewo a milungu ndi makolo ali ndi mphamvu za kuthandiza kapena kuvulaza awo amene ali padziko lapansi. Chotero, magulu aŵiri onsewo ayenera kulemekezedwa ndi kupembedzedwa.

Zikhulupiriro zofananazo zimapezeka kumbali zambiri za dziko. Akumagwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana, anthu kulikonse amafikira magulu a mizimu, akumafunafuna chidziŵitso chonena za mtsogolo ndi thandizo ndi chitsogozo m’mavuto a moyo a tsiku ndi tsiku. Kodi kupeza thandizo kumalo a mizimu nkothekadi? Yesu Kristu, amene anakhala kumeneko, anasonyeza kuti nkotheka. Iye anati: “Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.” (Mateyu 7:7) Koma kuti tilandire thandizo limenelo, tiyenera kupempha kwa munthu woyenera, kufunafuna m’njira yoyenera, ndi kugogoda pakhomo loyenera. Ngati tigogoda pakhomo losayenera, lingatsegulidwe ndi munthu amene adzatichitira zoipa, osati zabwino.

Chotero, kuli kofunika kwambiri kudziŵa za amene amakhala m’malo a mizimu ndi amene samakhalamo. Tifunikiranso kudziŵa za kusiyana kwa awo amene angatithandize ndi aja amene angativulaze. Potsirizira pake, tifunikira kudziŵa zimene tiyenera kuchita kuti tilandire thandizo kwa amene ali okonzekera kulipereka. Nkhani zotsatira zidzafotokoza mfundo zimenezi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chithunzithunzi pamasamba 3-4: The Star, Johannesburg, S.A.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena