Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/1 tsamba 3-4
  • Kodi Ufulu wa Chipembedzo Umatanthauzanji kwa Inu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ufulu wa Chipembedzo Umatanthauzanji kwa Inu?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Bwanji Nanga za Ufulu wa Chipembedzo?
  • Mtundu Wina wa Ufulu wa Chipembedzo
  • Musaphonye Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu!”
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/1 tsamba 3-4

Kodi Ufulu wa Chipembedzo Umatanthauzanji kwa Inu?

Ngakhale kuti ufulu wa chipembedzo umaonedwa kukhala woyenera kwambiri ku United States, m’ma 1940 magulu achiwawa anaukira Mboni za Yehova m’dziko lonselo

MAMILIYONI ambiri achimenyera nkhondo. Ena ngakhale kuchifera. Anthu amachiyesadi chuma chawo china chamtengo wapatali koposa. Kodi chimenecho nchiyani? Ufulu! The World Book Encyclopedia imamasulira kuti ufulu ndiwo “kukhoza kupanga zosankha ndi kuzichita.” Imapitiriza kuti: “Malinga ndi malamulo, anthu amakhala aufulu ngati chitaganya sichiwaikira malire opondereza, osafunikira, kapena opanda pake. Chitaganya chiyeneranso kutetezera zoyenera zawo​—ndiko kuti, ufulu wawo woyambirira, mphamvu, ndi mwaŵi.”

Lingaliro limenelo likumveka ngati lapafupi. Komabe, kukuoneka kuti nkosatheka mpang’ono pomwe m’moyo watsiku ndi tsiku kuti anthu agwirizane ponena za penipeni pamene malire a ufulu ayenera kuikidwa. Mwachitsanzo, ena amakhulupirira kuti boma liyenera kukhazika malamulo otetezera ufulu wa nzika zake. Koma ena amatsutsa ndi kunena kuti malamulo ameneŵa ndiwo nsingazo zimene nzika ziyenera kumasukako! Ndithudi, ufulu umatanthauza zinthu zosiyana kwa anthu osiyana.

Bwanji Nanga za Ufulu wa Chipembedzo?

Mwinamwake ufulu umene amachitirapo mikangano kwambiri ndiwo ufulu wa chipembedzo, umene aumasulira kuti ndiwo “kuyenera kwa kukhulupirira ndi kutsata chipembedzo chimene munthu wadzisankhira.” Malinga ndi United Nations Universal Declaration of Human Rights, “aliyense ayenera kukhala ndi ufulu wa malingaliro, chikumbumtima ndi chipembedzo.” Zimenezi zimaphatikizapo kuyenera kwa munthu “kusintha chipembedzo kapena chikhulupiriro chake,” limodzinso ndi ufulu wa “kusonyeza chipembedzo kapena chikhulupiriro chake pophunzitsa, pochitsata, polambira ndi posunga mwambo wake.”​—Chigawo 18.

Ndithudi, tingayembekezere kuti mtundu uliwonse umene umasamaliradi nzika zake udzapereka ufulu umenewu. Mwachisoni, si nthaŵi zonse pamene izi zimachitika. “Chipembedzo chimakhudza mtima wa anthu ambiri,” ikutero The World Book Encyclopedia. “Maboma ena amagwirizana kwambiri ndi chipembedzo chimodzi naona anthu a zikhulupiriro zina ngati osokoneza ulamuliro wa ndale. Boma lingaonenso chipembedzo ngati changozi pandale chifukwa zipembedzo zingaike kukhulupirika kwawo kwa Mulungu pamwamba pa kumvera boma.”

Pazifukwa zimenezi maboma ena amaika malire pa zachipembedzo. Angapo amaletseratu zachipembedzo. Ena, ngakhale kuti amati akuchirikiza ufulu wa chipembedzo, amalamulira mwamphamvu zochitika zonse zachipembedzo.

Mwachitsanzo, talingalirani za mkhalidwe umene unali ku Mexico zaka zambiri. Ngakhale kuti Konsichushoni inapereka ufulu wa chipembedzo, inalamula kuti: “Matchalitchi olambiriramo anthu onse ali katundu wa Mtundu uno, woimiridwa ndi Boma la Federal, limene lidzagamula amene angapitirizebe kugwiritsiridwa ntchito motero.” Mu 1991 Konsichushoniyo anaikonza kuti athetse chiletso chimenechi. Komabe, chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti ufulu wa chipembedzo umaonedwa mosiyana m’maiko osiyanasiyana.

Mtundu Wina wa Ufulu wa Chipembedzo

Kodi kudziko limene mumakhala kuli ufulu wa chipembedzo? Ngati zili choncho, kodi mumati uwo nchiyani? Kodi mungalambire Mulungu m’njira imene mwasankha, kapena kodi mumakakamizidwa kukhala membala wa tchalitchi cha Boma? Kodi mumaloledwa kuŵerenga kapena kufalitsa mabuku achipembedzo, kapena kodi boma limaletsa zinthu zosindikiza zimenezo? Kodi mungalankhule ndi ena za chikhulupiriro chanu, kapena kodi amaona zimenezi monga kudodometsa zoyenera zawo za chipembedzo?

Mayankho a mafunso ameneŵa akudalira ndi kumene mumakhala. Komabe, nkokondweretsa kuti pali mtundu wina wa ufulu wa chipembedzo umene sumadalira pa malo mpang’ono pomwe. Akali ku Yerusalemu m’chaka cha 32 C.E., Yesu anati kwa otsatira ake: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:31, 32.

Kodi Yesu anatanthauzanji ndi mawuwo? Omvetsera ake achiyuda ankafunitsitsa kumasuka ku ulamuliro wachiroma. Koma Yesu sanali kulankhula za kumasuka ku chitsenderezo chandale. M’malo mwake, anali kulonjeza ophunzira ake chinachake chabwino kwambiri, monga momwe tidzaonera m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena