Kumasulidwa ndi Choonadi
KU United States, anthu oposa miliyoni imodzi ali m’ndende. Mwa ameneŵa, pafupifupi zikwi zitatu aweruzidwa kuti anyongedwe. Dziikeni m’malo awo. Kodi mungamve bwanji? Kungoganizira kuti mukuyembekezera chimenecho nkoopsadi. Komabe, m’lingaliro lina, anthu onse ali mumkhalidwe wofananawo. Baibulo limati: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Inde, monga mbadwa za Adamu, tili “m’ndende” chifukwa cha mkhalidwe wauchimo. (Aroma 5:12) Tsiku lililonse timamva zotulukapo za kumangidwa kwathu, monga momwe anamvera mtumwi wachikristu Paulo amene analemba kuti: “Ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.”—Aroma 7:23.
Chifukwa cha mkhalidwe wathu wauchimo, aliyense wa ife waweruzidwa kuti anyongedwe, titero kunena kwake, chifukwa Baibulo limati: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Wamasalmo Mose anaufotokoza bwino mkhalidwe wathu kuti: “Zaka makumi asanu ndi aŵiri ndizo zokha zomwe tili nazo—zaka makumi asanu ndi atatu, ngati tili nayo mphamvu; koma zimangotibweretsera mavuto ndi chisoni; moyo umatha msanga, ndipo timakhala titapita.”—Salmo 90:10, Today’s English Version; yerekezerani ndi Yakobo 4:14.
Yesu ankaganizira za ukapolo wa anthu kuuchimo ndi imfa pamene anati kwa ophunzira ake: “Choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Ndi mawuwo, Yesu anali kupatsa otsatira ake chiyembekezo cha chinachake chachikulu kuposa kumasuka ku ulamuliro wachiroma—anali kuwapatsa chikhululukiro cha machimo ndi kuwamasula ku imfa! Kodi akanawapatsa motani zimenezi? “Ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu,” Yesu anawauza motero, “mudzakhala mfulu ndithu.” (Yohane 8:36) Inde, mwa kupereka moyo wake, ‘Mwanayo,’ Yesu, anakhala nsembe yachiombolo yoombolanso zimene Adamu anataya. (1 Yohane 4:10) Zimenezi zinatheketsa anthu onse omvera kuti amasulidwe kuukapolo wa uchimo ndi imfa. Mwana wa Mulungu wobadwa yekha anafa “kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Chotero choonadi chimene chingatimasule chikunena za Yesu Kristu. Awo amene amakhala otsatira mapazi ake ali ndi chiyembekezo cha kumasulidwa kuuchimo ndi imfa pamene Ufumu wa Mulungu udzatenga ulamuliro wonse wa zinthu padziko lapansi. Ngakhale tsopano, awo amene amalandira choonadi cha Mawu a Mulungu amakhala ndi ufulu weniweni. Motani?
Kumasuka pa Kuopa Akufa
Anthu miyandamiyanda lerolino amaopa akufa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zipembedzo zawo zawaphunzitsa kuti sou imachoka m’thupi paimfa ndi kupita kumalo ena a mizimu. Nchifukwa chake m’maiko ena ndi mwambo achibale a wakufayo kuchezera masiku angapo. Kaŵirikaŵiri pamakhalanso kuimba mofuula ndi kuomba ng’oma. Olira amakhulupirira kuti zimenezi zidzakondweretsa munthu wakufayo ndi kukaniza mzimu wake kuti usabwerere kudzavutitsa amoyo. Ziphunzitso zonyenga za Dziko Lachikristu ponena za akufa zangolimbitsa mwambo umenewu.
Komabe, Baibulo limavumbula choonadi cha mkhalidwe wa akufa. Limanena momveka kuti sou yanu ndiyo inuyo, osati mbali yanu inayake yosadziŵika bwino imene imapitiriza kukhala ndi moyo pambuyo pa imfa. (Genesis 2:7 NW; Ezekieli 18:4; NW) Ndiponso, akufa sakuzunzidwa ku helo wamoto, ndipo salinso kudziko lamizimu limene lingayambukire amoyo. “Akufa,” Baibulo limatero, “sadziŵa kanthu bi, . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:5, 10.
Choonadi cha Baibulo chimenechi chamasula anthu ambiri pakuopa anthu akufa. Iwo sakuperekanso nsembe zowonongetsa ndalama zambiri kuti apepeze makolo awo, ndipo sakuderanso nkhaŵa kuti okondedwa awo akuzunzidwa mwankhanza chifukwa cha zolakwa zawo. Iwo aphunzira kuti Baibulo likupereka chiyembekezo chabwino kwambiri cha omwalira, popeza limatiuza kuti panthaŵi yoikika ya Mulungu, kudzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15; Yohane 5:28, 29) Chotero, akufa tsopano akungopumula, monga kuti ali mtulo tabwino.—Yerekezerani ndi Yohane 11:11-14.
Choonadi cha mkhalidwe wa akufa ndi chiyembekezo cha chiukiriro chingatimasule pakutaya mtima kumene imfa imachititsa. Chiyembekezo chimenechi chinalimbitsa banja lina ku United States pamene mwana wawo wazaka zinayi anamwalira m’ngozi. “Tikusoŵa chinachake m’moyo wathu chimene sichidzapezeka mpaka titaonanso mwana wathu pakuuka kwa akufa,” akuvomereza motero amake. “Koma tikudziŵa kuti kupwetekedwa kwathu ndi kwakanthaŵi chabe, popeza Yehova akulonjeza kutipukuta misozi yonse ndi chisoni.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kumasuka pa Kuopa Zamtsogolo
Kodi kulinji mtsogolo? Kodi dziko lathu lidzanyeka m’chipiyoyo cha nyukiliya? Kodi kuwononga malo okhala a padziko lapansi kudzachititsa pulaneti lathu kukhala losayenera zamoyo? Kodi kuwonongeka kwa makhalidwe kudzachititsa kusayeruzika ndi chipwirikiti? Ameneŵa ndi mantha aakulu a anthu ambiri lerolino.
Komabe, Baibulo limatimasula pamantha oipa amenewo. Limatitsimikiza kuti “dziko lingokhalabe masiku onse.” (Mlaliki 1:4) Yehova sanalenge pulaneti lathu kuti anthu osasamala akangoliwononga. (Yesaya 45:18) M’malo mwake, Yehova analenga dziko lapansi kuti likhale mudzi wa paradaiso wa banja la anthu logwirizana. (Genesis 1:27, 28) Chifuno chake sichinasinthe. Baibulo limatiuza kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18) Pambuyo pake, “ofatsa adzalandira dziko lapansi,” limatero Baibulo, “nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:11.
Lonjezo limeneli nlodalirika, chifukwa Mulungu sanama. Yehova anati kupyolera mwa mneneri wake Yesaya: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:11; Tito 1:2) Choncho, mwachidaliro tingadikire kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu lolembedwa m’Baibulo pa 2 Petro 3:13 lakuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”
Kumasuka pa Kuopa Anthu
Baibulo limatipatsa zitsanzo zabwino kwambiri za amuna ndi akazi amene anasonyeza kudzipereka kwawo kwa Mulungu mopanda mantha. Ena a ameneŵa anali Gidiyoni, Baraki, Debora, Danieli, Estere, Yeremiya, Abigayeli, ndi Yaeli—kungotchulapo angapo okha. Amuna ndi akazi okhulupirika ameneŵa anasonyeza maganizo a wamasalmo yemwe analemba kuti: “Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa; munthu adzandichitanji?”—Salmo 56:11.
M’zaka za zana loyamba, mtumwi Petro ndi Yohane anasonyezanso kulimba mtima kofananako pamene akuluakulu a chipembedzo anawalamula kuleka kulalikira. “Pakuti,” iwo anayankha motero, “sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” Chifukwa cha kaimidwe kawo kolimba, Petro ndi Yohane anamangidwa pambuyo pake. Atamasulidwa mozizwitsa, iwo anayambanso ntchito yawo napitiriza ‘kulankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.’ Posachedwa Petro ndi atumwi ena anawapititsa kubwalo lachiyuda la Sanhedrin. “Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili,” anawauza motero mkulu wa ansembe, “ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu.” Petro ndi atumwi ena anayankha nati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 4:16, 17, 19, 20, 31; 5:18-20, 27-29.
Pantchito yawo yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, Mboni za Yehova lerolino zimayesetsa kutsanzira changu cha Akristu a m’zaka za zana loyamba. Ngakhale achichepere amene ali pakati pawo nthaŵi zambiri amadzisonyeza kuti alibe mantha mwa kulankhula ndi ena za chikhulupiriro chawo. Talingalirani zitsanzo zina.
Stacie, mtsikana, ngwamanyazi mwachibadwa. Choncho, kulankhula ndi ena za chikhulupiriro chake kunali kovuta poyamba. Kodi anatani kuti agonjetse manyazi ake? “Ndinaphunzira Baibulo ndi kutsimikiza kuti ndinamvetsa zimene ndinali kulankhula,” iye akutero. “Zinapeputsa zinthu, ndipo ndinakhala ndi chidaliro chachikulu.” Mbiri yabwino ya Stacie inalembedwa m’nyuzipepala ya kumaloko. Nkhaniyo, yolembedwa ndi mphunzitsi wa pasukulu pake, inati: “Chikhulupiriro [cha Stacie] chikuoneka kuti chinampatsa nyonga yolimbanirana ndi zovuta zambiri zimene achichepere ambiri amakumana nazo. . . . Amaona kuti utumiki kwa Mulungu uyenera kukhala chinthu choyamba m’maganizo mwake.”
Tommy anayamba kuphunzira za Baibulo kwa makolo ake pamene anali ndi zaka zisanu zokha. Ngakhale pamene anali mwana, anaima molimba kumbali ya kulambira koona. Pamene anzake achichepere a m’kalasi anali kujambula zithunzi za maholide, Tommy ankajambula zithunzi za Paradaiso wolonjezedwa wa Mulungu. Atafika paunyamata, Tommy anazindikira kuti ophunzira ambiri sanali kumvetsa zikhulupiriro za Mboni za Yehova. M’malo mokhala chete chifukwa cha mantha, anapempha mmodzi wa aphunzitsi ake kuti achititse kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho m’kalasi mwake kotero kuti ayankhe mafunso awo onse nthaŵi imodzi. Anampatsa ufuluwo, ndipo umboni wabwino unaperekedwa.
Pamene anali ndi zaka 17, Markietta anapeza mwaŵi wabwino kwambiri wolankhula ndi ena m’kalasi mwake za chikhulupiriro chake. “Anatiuza kuti tidzalankhule nkhani,” iye akutero. “Ndinasankha mutu wanga m’buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.a Ndinasankha mitu isanu m’bukumo ndi kuilemba pa bolodi. Ndinapempha kalasi kuindandalika malinga ndi imene anaona kuti njofunika koposa.” Ndiyeno panatsatira kukambitsirana ndi kalasi. “Ndinasonyeza kalasi bukulo,” akumaliza motero Markietta, “ndipo ophunzira angapo anati akufuna makope awo. Ngakhale mphunzitsi wanga anati akufuna kope lake.”
Choonadi Chingakumasuleni
Monga momwe taonera, choonadi chomwe chili m’Baibulo chili ndi mphamvu yomasula amisinkhu yonse amene amachiphunzira ndi kuloŵetsa uthenga wake mumtima mwawo. Chimawamasula pakuopa akufa, kuopa zamtsogolo, ndi kuopa anthu. Koposa zonse, dipo la Yesu lidzamasula anthu omvera kuuchimo ndi imfa. Kudzakhala kosangalatsa chotani nanga kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso, osakhalanso m’ndende chifukwa cha mkhalidwe wauchimo wacholoŵa!—Salmo 37:29.
Kodi mungakonde kuphunzira zambiri ponena za madalitso amene Mulungu walonjeza? Ngati mungakonde, kodi muyenera kuchitanji? Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Choncho ngati mukufuna kukhala ndi ufulu umene Yesu analonjeza ophunzira ake, muyenera kuphunzira za Yehova Mulungu ndi Mwana wake. Mufunikira kudziŵa chifuniro cha Mulungu ndiyeno kuchichita, chifukwa Baibulo limati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 7]
Mu Ufumu wa Mulungu, anthu adzamasulidwa kuuchimo ndi imfa pomalizira pake