Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 3/1 tsamba 29
  • “Mmodzi Chabe mwa Anthu Ambiri Amene Munakhudza Mtima”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mmodzi Chabe mwa Anthu Ambiri Amene Munakhudza Mtima”
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Loya Amene Anafufuza Zimene Mboni za Yehova Zimaphunzitsa
    Galamukani!—2010
  • Kulera Mabanja Padziko Lonse Kusonyeza Ukholo Mwachikondi, Chilango, Chitsanzo, ndi Makhalidwe Auzimu
    Galamukani!—1991
  • Mulungu Amayankha Mapemphero
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 3/1 tsamba 29

“Mmodzi Chabe mwa Anthu Ambiri Amene Munakhudza Mtima”

KALE mu January 1996, Carol anali ndi fundo kuubongo. Anali wazaka za m’ma 60 ndipo nthaŵi zonse anali mkazi wachimwemwe, wojintcha ndi wolimbikitsa aliyense. Koma tsopano madokotala anali kumenyera nkhondo kuchotsa chotupa chakuphacho. Adakavutika choncho, Carol analandira kalata yotsatirayi:

“Wokondedwa Carol:

“Pepani kuti thanzi lanu silili bwino. Tili ndi mwaŵi kukhala ndi chiyembekezo chenicheni chimene Baibulo limatithandiza kudziŵa ndi kukonda. Chiyembekezo chimenechi nchakuti Ufumu wa Yehova udzalamulira padziko lapansi kuti tidzakhale m’paradaiso, nthaŵi yomwe tonsefe tikuyembekezera.

“Ndikufuna kuti mudziŵe kuti ntchito yanu yolalikira yapulumutsa anthu ambiri ku imfa yosatha. Ine ndine mmodzi wa anthu amenewo. Sindidziŵa ngati mukukumbukira nthaŵi yoyamba imene tinakumana. Panthaŵiyo ndinali ndi zaka 20. Ndinali ndi tsitsi lalitali, ndinkagulitsa anamgoneka, ndipo ndinkayenda ndi zigaŵenga. Tonsefe tinali ndi mfuti ndipo tinalibe chikondi chenicheni koma kudzikonda tokha basi.

“Munagogoda pachitseko changa muli ndi Mboni ina ndi kundigaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndinayesa kukupatsani dola imodzi nkukuuzani kuti sindinali kuwafuna magaziniwo. Munandiuza kuti simunali kupemphapempha ndalama. Munandiuza kuti munali kuchita ntchito yothandiza anthu kuŵerenga Baibulo. Sindidziŵa ngati ndinawatenga magaziniwo kapena kuwaŵerenga. Komabe, munabzala mbewu ya choonadi m’moyo wanga.

“Zaka zingapo pambuyo pake, Mboni ina, Gary, anafika panyumba ya amayi anga inenso ndilipo. Ndinamuuza kuti munandichezerapo zaka zingapo zapitazo. Gary anandiphunzitsa Baibulo kwa nthaŵi yaitali kufikira nditabatizidwa mu 1984. Tsopano ndikuphunzitsa ana anga choonadi cha Ufumu wa Mulungu.

“Ndikukhulupirira kuti ndangokhala mmodzi chabe mwa anthu ambiri amene munakhudza mtima m’zaka zanu za utumiki wokhulupirika. Komabe, mwa kukoma mtima kumeneku, mwathandiza ine ndi banja langa kudziŵa Mulungu Wamkulu, Yehova, ndi Mwana wake, Kristu Yesu. Ndikuyembekezera tsiku limene ndidzakuonani m’dongosolo latsopano la zinthu pamene Yehova adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso pathu, ndipo imfa siidzakhalakonso.​—Chivumbulutso 21:4.

“Koma ine ndi banja langa, tili okondwa kuti tinakudziŵani, nitikhala mbali ya ntchito yanu yolalikira. Zikomo kwambiri.

“Chikondi chaubale,

Peter”

Atadwala miyezi isanu ndi umodzi, Carol anamwalira mu March 1996, atabzala mbewu zambiri za choonadi m’zaka 35 ali mlaliki wachangu. Anazindikira kuti munthu sangadziŵe kuti ndi liti pamene mbewu ingabale chipatso, ngakhale zaka zingapo pambuyo pake.​—Mateyu 13:23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena