Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/1 tsamba 4-7
  • Kukhulupirika m’Dziko Lopanda Ungwiro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhulupirika m’Dziko Lopanda Ungwiro
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutaya Kukhulupirika Koyamba
  • Maziko a Kukhulupirika
  • Kukhulupirika Kuyesedwa
  • Kukhulupirika kwa Yobu
  • Kukhulupirika ndi Utumiki Wachikristu
  • Kukhulupirika​—Mphoto Zake
  • Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Mudzasungabe Umphumphu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Umphumphu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Yendani mu Umphumphu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/1 tsamba 4-7

Kukhulupirika m’Dziko Lopanda Ungwiro

“CHABWINO chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.” Kodi nzimene zimachitika kwa inunso? Dziŵani kuti mtumwi Paulo anali ndi vuto limodzimodzi; komabe anali Mkristu wokhulupirika kwambiri. Kodi zimenezi sizikuwombana? M’kalata yake kwa Akristu a ku Roma, Paulo analongosola vutolo: “Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe mkati mwanga ndiwo.” Kodi akunena za tchimo liti, ndipo analigonjetsa motani kuti akhale wokhulupirika?​—Aroma 7:19, 20.

Kuchiyambi kwa kalata yake, Paulo analemba kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” “Munthu mmodzi” ameneyo ndiye Adamu. (Aroma 5:12, 14) Uchimo wa Adamu​—munthu woyamba​—ndiwo unadzetsa kupanda ungwiro kobadwa nako kwa anthu ndi kuchititsa kuti kukhulupirika kukhale kovuta kwambiri.

Lingaliro la Paulo pa “tchimo loyamba,” monga momwe ankalitchera kale, ambiri samalivomereza lero chifukwa nkhani ya m’Baibulo ya chilengedwe aikana ophunzitsa zaumulungu navomereza ziphunzitso za chisinthiko. Ndemanga yamakono inati ponena za Aroma 5:12-14: “Akatswiri akankhira pambali ndime yonseyo.” Komabe, zaka zana limodzi zapitazo, ndemanga za pa Baibulo nthaŵi zonse zinanena kuti “pamene Adamu anachimwa . . . anaipitsa mbadwa zake zonse ndi tchimolo ndi zotsatirapo zake.”a

Kutaya Kukhulupirika Koyamba

Mmene ambiri lero amakanira za kukhalako kwa Adamu, munthu woyamba, amakananso za kukhalako kwa Satana, Mdyerekeziyo, namati ndi nthanthi chabe.b Koma Yesu Kristu wamkulu koposa anthu onse, amatiuza kuti ameneyo “sanaima m’choonadi,” kapena kuti, anali wosakhulupirika. (Yohane 8:44) Ndipo anali Satana yemwe anasonkhezera Adamu ndi mkazi wake, Hava, kupandukira Yehova kuti ataye kukhulupirika kwawo poyesedwa.​—Genesis 3:1-19.

Pakuti tonse tinachokera kwa Adamu, tonse tili ndi chibadwa cha uchimo. Munthu wanzeru Solomo anati: “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Komabe, munthu aliyense atha kukhala wokhulupirika. Kodi zitheka bwanji? Chifukwa kukhala wokhulupirika sikulira kukhala wangwiro.

Maziko a Kukhulupirika

Mfumu Davide wa Israyeli anachita zolakwa zambiri, kuphatikizapo chigololo chake ndi Bateseba cholembedwa bwino lomwe. (2 Samueli 11:1-27) Zolakwa zambiri za Davide zinasonyeza kuti sanali wangwiro konse. Komabe, kodi Yehova anayang’ananji mwa iye? Polankhula ndi mwana wa Davide, Solomo, Yehova anati: ‘Uyende pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama.’ (1 Mafumu 9:4) Ngakhale kuti anachita zolakwa zambiri, Yehova anaona kukhulupirika mwa Davide. Chifukwa ninji?

Davide anapereka chifukwa chake pamene anauza Solomo kuti: “Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Davide ankalakwa, koma anali wodzichepetsa, ndipo anafuna kuchita cholungama. Nthaŵi zonse analabadira chidzudzulo ndi chilangizo​—ndi kuchipempha komwe, ankapempha. “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga,” anatero popempha. (Salmo 26:2) Ndipo Davide anayeretsedwadi. Mwachitsanzo, zotsatira tchimo lake ndi Bateseba zinamtsata mpaka imfa yake. Komabe, Davide sanayese konse kulungamitsa cholakwa chake. (2 Samueli 12:1-12) Chachikulu kwambiri nchakuti sanapatuke pa kulambira koona. Pachifukwa chimenechi, ndi chifukwa cha chisoni chake chenicheni ndi kulapa kwake Davide, Yehova analola kumkhululukira machimo ake namuyesa munthu wokhulupirika.​—Onani Salmo 51.

Kukhulupirika Kuyesedwa

Yesu anayesedwa ndi Satana Mdyerekezi poyesa kumtayitsa kukhulupirika kwake. Iye anakhalabe wokhulupirika pokumana ndi mavuto, kusiyana ndi Adamu wangwiro, amene anangoyesedwa pakumvera kwake lamulo la Mulungu. Ndiponso, Yesu anadziŵanso kuti kupulumuka kwa banja la anthu onse kunadalira pa kukhulupirika kwake.​—Ahebri 5:8, 9.

Satana, pofunitsitsa kuswa kukhulupirika kwa Yesu, anafika kwa iye pamene Yesuyo anali wofooka kwabasi​—atakhala masiku 40 akusinkhasinkha ndi kusala kudya m’chipululu. Anamuyesa Yesu katatu konse​—kuti asandutse miyala mkate; kuti alumphe kuchokera pamwamba pa chimbudzi cha kachisi, naati angelo akampulumutsa kuti chikhale chozizwitsa chosonyeza umboni wa Umesiya wake; ndi kuti alandire ulamuliro wa maufumu onse a padziko lapansi ‘atangomgwadira’ Satana kamodzi kokha kumlambira. Koma Yesu anatsutsa chiyeso chilichonse, nasunga kukhulupirika kwake kwa Yehova.​—Mateyu 4:1-11; Luka 4:1-13.

Kukhulupirika kwa Yobu

Kulimbika kwa Yobu, kusataya kukhulupirika kwake poyesedwa, nkodziŵika bwino lomwe. Komabe, Yobu sanadziŵe chifukwa chake tsoka lidamgwera. Sanadziŵenso kuti Satana anali atamneneza mabodza, akumati Yobu anatumikira Mulungu pazifukwa za dyera ndi kuti Yobu akanataya kukhulupirira kwake kuti apulumutse khungu lake. Mulungu analola kuti Yobu akumane ndi chiyeso cha zoŵaŵazo pofuna kusonyeza kuti Satana anali wabodza.​—Yobu 1:6-12; 2:1-8.

Anzake onyenga atatu anafika. Iwo mwamachenjera ananena zopotoza muyezo wa Mulungu ndi zifuno zake. Ngakhale mkazi wake wa Yobu analepheranso kuona nkhani yeniyeni, nalephera kulimbikitsa mwamuna wake panthaŵi ya nsautso yake. (Yobu 2:9-13) Koma Yobu anachirimikabe. “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga. Ndiumirira chilungamo changa, osachileka; chikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.”​—Yobu 27:5, 6.

Chitsanzo chogwira mtima cha Yobu, limodzi ndi kukhulupirika kwa amuna ndi akazi ambiri olembedwa m’Baibulo, zimatsimikizira kuti Satana ali wabodza.

Kukhulupirika ndi Utumiki Wachikristu

Kodi Yehova amafuna kuti tikhale okhulupirika kotero kuti akhutiritse mtima wake chabe? Iyayi. Kukhulupirika kuli ndi phindu lenileni kwa anthufe. Yesu potilangiza kuti “uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse,” anafuna kuti tipindule nazo. Kunena zoona, “ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba,” ndipo kuti mwamuna, mkazi, kapena mwana alisunge ayenera kukhala wokhulupirika. (Mateyu 22:36-38) Kodi kumaloŵetsamonji, ndipo mphoto yake njotani?

Munthu wokhulupirika amakhala wodalirika. Osati kwa munthu mnzake chabe, komanso kwa Mulungu makamaka. Kuongoka mtima kwake kumaonekera m’zochita zake; amakhala wopanda chinyengo. Sali waukathyali kapena wakatangale. Mtumwi Paulo ananena motere: “Takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.”​—2 Akorinto 4:2.

Onani kuti Paulo akutchula za maganizo ochirikiza utumiki wachikristu. Kodi mtumiki wachikristu angatumikire motani ena ngati manja ake ali osayera, ngati sali munthu wokhulupirika? Mkulu wa bungwe la chipembedzo la ku Ireland yemwe posachedwapa anatula pansi udindo wake akusonyeza bwino mfundo imeneyo. Anavomereza kuti “analola wansembe woipsa ana kupitiriza kugwira ntchito ndi ana mkhalidwe wakewo utadziŵika kale kwa nthaŵi yaitali,” malinga ndi nyuzipepala ya The Independent. Nkhaniyo inati kuipsa anako anakuchita kwa zaka zoposa 24. Wansembeyo anammanga zaka zinayi, koma tangolingalirani nsautso ya mtima yomwe inali ndi ana omwe anaipsawo pazaka zonsezo chifukwa chakuti womyang’anira wake sanali wokhulupirika pakhalidwe nalephera kuchitapo kanthu!

Kukhulupirika​—Mphoto Zake

Mtumwi Yohane anali munthu wopanda mantha. Kaamba ka changu chake ndi cha mbale wake Yakobo, Yesu anawatcha “Ana a Bingu.” (Marko 3:17) Pokhala munthu wokhulupirika kwambiri, Yohane, limodzi ndi Petro, anafotokoza kwa olamulira achiyuda kuti ‘sakanatha kuleka kulankhula’ zimene iye anaona ndi kumva pamene anali ndi Yesu. Yohane analinso mmodzi wa atumwi omwe anati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 4:19, 20; 5:27-32.

Kukuoneka kuti pamene Yohane anali m’zaka zaukalamba za m’ma 90, anaikidwa m’ndende pachisumbu cha Patmo “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Pausinkhu wakewo, angakhale ataganiza kuti utumiki wake unafika kumapeto. Koma ndiye yekha anali wokhulupirika woyenerera ntchito yolemba masomphenya osangalatsawo a Chivumbulutso. Yohane anachita ntchitoyo mokhulupirikadi. Umenewo unalidi mwaŵi waukulu kwa iye! Ndipo panalinso zina zinalinkudza. Pambuyo pake, pafupi ndi Efeso, analemba Uthenga wake Wabwino ndi makalata atatu. Mwaŵi waukulu woterowo unali chimake cha utumiki wake wokhulupirika wa zaka 70!

Kukhala munthu wokhulupirika m’njira zonse kumakhutiritsa mtima kwambiri. Kukhala wokhulupirika kwa Mulungu kumadzetsa mphoto zosatha. Lerolino, “khamu lalikulu” la olambira oona likukonzekera kuloŵa m’dziko latsopano la mtendere ndi chimvano, ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Chivumbulutso 7:9) Tiyenera kukhalabe okhulupirika pankhani zazikulu za khalidwe ndi kulambira, mosasamala kanthu za mayesero a dongosolo la zinthuli ndi mavuto ambiri amene Satana angadzetse pa ife. Dziŵani kuti ndi mphamvu yomwe Yehova amapereka, mukhoza kupambana!​—Afilipi 4:13.

Ponena za nthaŵi ino ndi yamtsogolo, wamasalmo Davide akutipatsa chitsimikizo ichi tonsefe m’pemphero lake lothokoza Yehova: “Mundigwirizize m’ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu ku nthaŵi yamuyaya. Wodalitsika Yehova, . . . Amen, ndi Amen.”​—Salmo 41:12, 13.

[Mawu a M’munsi]

a Ndemanga ya mu The New Testament of Our Lord and Saviour Jesus Christ, according to the Authorised Version, with a brief commentary by various authors.

b Dzinalo Satana limatanthauza “Wotsutsa.” “Mdyerekezi” limatanthauza “Woneneza.”

[Chithunzi patsamba 4]

Ngakhale kuti Davide analakwa, anasonyeza kuti anali wokhulupirika

[Chithunzi patsamba 5]

Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino cha kukhulupirika

[Zithunzi patsamba 7]

Kukhala wokhulupirika kumakhutiritsa mtima kwambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena