Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/1 tsamba 3
  • Kodi Nchifukwa Ninji Palibenso Kukhulupirika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Palibenso Kukhulupirika?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusinthasintha kwa Muyezo wa Kukhulupirika
  • Kodi Mudzasungabe Umphumphu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Umphumphu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kukhulupirika m’Dziko Lopanda Ungwiro
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/1 tsamba 3

Kodi Nchifukwa Ninji Palibenso Kukhulupirika?

KUPOSA pang’ono zaka zana limodzi zapitazo, Barney Barnato, wogulitsa madiamondi, anabwerera ku England kuchokera ku South Africa. Atafika anatsutsa nkhani yotuluka m’nyuzipepala yonena za iye. Choncho anakapatsa mkonzi wa nyuzipepalayo mapepala ena olemba ndi manja kuti afalitsenso nkhaniyo, “kungoti tiwongolere mfundo zina,” anatero atapereka ndi cheke cha ndalama zambiri.

Mkonziyo, J. K. Jerome, anataya mapepalawo mu mtanga wotayamo mapepala nambwezera cheke chakecho. Zimenezo zinamdabwitsa Barnato, koma msangamsanga anaŵirikiza ndalamazo. Mkonziyo anakanabe. “Kodi mukufuna zingati?” anafunsa. Pokumbukira chochitikacho, Jerome akuti: “Ndinamuuza kuti zimenezi nzosatheka​—osati muno m’London.” Kukhulupirika kwake pantchito yake yaukonzi sikunali kochita nako malonda.

“Kukhulupirika” akumasulira kuti ndiko “khalidwe lolungama; kuona mtima.” Munthu wokhulupirika ngwodalirika. Koma lero, kusanena choona​—kusakhulupirika​—kumakhudza anthu onse.

Ofalitsa nkhani ku Britain atchukitsa liwu lakuti “katangale” potchula kutayika kwa kukhulupirika pamakhalidwe. Monga momwe inanenera nyuzipepala yakuti The Independent, katangale amachitikira “mwambiri kuyambira pa chibwenzi ndi chinyengo cha m’boma mpaka ziphuphu pamaoda aakulu opita kunja.” Palibe mbali iliyonse m’moyo imene yatsala.

Kusinthasintha kwa Muyezo wa Kukhulupirika

Kunena zoona, kukhulupirika sikumalira ungwiro, koma kumasonyeza mkhalidwe wabwino mwa munthu. M’dziko lathuli lolimbikitsa kulemera mofulumira, anthu angaone kukhulupirika kukhala chopinga, osati khalidwe labwino. Mwachitsanzo, kunyenga pamayeso ndi ziŵiya zamachenjera kukuwonjezeka pakati pa ophunzira, ndipo nkovuta kwabasi kudziŵa ngati munthu ali ndi ziŵiya zimenezi. Profesa wina wachibritishi wa payunivesite akunena kuti oposa theka la ophunzira onse m’Britain anachita chinyengo, ndipo si m’Britain mokha ayi.

Tisaiŵalenso za mmene ena amavutikiramo pamene osakhulupirikawo anama ndi kuchita chinyengo. Titenge chitsanzo cha zimene zinachitika mu 1984 m’tauni ya Bhopal ku India, pamene mpweya wapaizoni unapha anthu oposa 2,500, amuna, akazi ndi ana omwe ndi kuvulaza ena zikwi mazana ambiri. Nyuzipepala ya Sunday Times inati: “Katangale akulepheretsa ntchito zothandiza okhudzidwa ndi ngoziyi. . . . Kupeza enieni ofunikira thandizo kwakhala kovuta chifukwa cha zikwi zambiri za madandaulo abodza, zikalata zopeka ndi maumboni onama.” Chifukwa cha zimenezo, pambuyo pa zaka khumi, $3,500,000 yokha pa ndalama za chithandizo zokwanira $470,000,000 ndiyo inagaŵidwa kwa ofunikira thandizowo.

Nanga chipembedzo bwanji? Kodi chikuchita bwanji pankhani ya kukhulupirika? Nzachisoni chifukwa kaŵirikaŵiri muyezo wake ungofanana ndi wa dziko. Titenge chitsanzo cha Eamon Casey, bishopu wa Roma Katolika, amene anaulula kuti ndiye tate wake wa mwana wam’chigololo, mnyamata tsopano. Nkhani ya Casey “sinali yachilendo konse,” inatero nyuzipepala ya Guardian ya m’Britain. Nyuzipepala ya Times inanenanso chimodzimodzi: “Choonadi ponena za mtonzo wa Bishopu Casey si chakuti tchimo lakelo nlachilendo, koma kuti kuswa lumbiro la umbeta sikwachilendo ndipo nkofala.” Povomereza mfundo imeneyi, nyuzipepala ya The Glasgow Herald, ku Scotland, inanena kuti 2 peresenti yokha ya akuluakulu a Roma Katolika mu United States ndiwo sanachitepo chisembwere cha mwamuna ndi mkazi ndi cha amuna okhaokha. Kaya chiŵerengerochi ncholondola kapena ayi, chimasonyezabe mbiri ya khalidwe la ansembe achikatolika.

Poona zitsanzo zonsezi, kodi nkotheka kuti munthu akhale wokhulupirika pamakhalidwe? Kodi nkofunikiradi? Kodi kumafunanji, ndipo mphoto yake nchiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena