Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 18
  • Kuthaŵira ku Gulu la Teokrase la Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthaŵira ku Gulu la Teokrase la Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Choonadi cha Baibulo Chikupitiriza Kulalikidwa mu Ireland
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Madagascar
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Ntchito Yongodzipereka Yokhala ndi Mapindu Okhalitsa
    Galamukani!—2001
  • Zilumba za Faeroe Zinalumikizana Mochititsa Chidwi
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 18

Olengeza Ufumu Akusimba

Kuthaŵira ku Gulu la Teokrase la Yehova

KALEKALE mneneri Yesaya ananena kuti: “Lemekezani inu Yehova . . . , m’zisumbu za m’nyanja.” (Yesaya 24:15) Mboni za Yehova zimaona zisumbu za m’nyanja monga mbali ya ‘dziko lonse lapansi’ imene Yesu ananena kuti ‘Uthenga Wabwino uyenera kulalikidwako.’​—Mateyu 24:14; Marko 13:10.

Zisumbu za Marquesas zili pamtunda wa makilomita 1,400 kumpoto cha kummaŵa kwa Tahiti. Ndi mbali ya zisumbu za kutali mu South Pacific zotchedwa French Polynesia. Zomera zimakula bwino pa zisumbu zimenezi chifukwa ndi kwa nthaka ya chonde ndi kofunda ndiponso kwamnyontho. Komabe, zisumbu za Marquesas zikubeleka zipatso za mtundu wina. Lingalirani za banja lina lomwe linalabadira uthenga wa Ufumu pa chisumbu cha Hiva Oa.

Jean ndi mkazi wake, Nadine, anali osakondwa kumakhala m’malo otchedwa kuti otukuka ku Western Europe. Motero anaganiza zosiya moyo wokhala motangwanika wa kumeneko nasamuka ndi mwana wawo kupita ku zisumbu za Marquesas. Nyumba yawo yatsopano, ya nsungwi, inamangidwa m’chigwa kwaokhaokha. Kuti apeze munthu wokhala pafupi ndi iwo, amayenera kuyenda kukwera mapiri kwa maola aŵiri. Mudzi wapafupi wokhala ndi chipatala, sukulu ndi sitolo unali pamtunda wokwanira kuyenda maola atatu pa galimoto.

Jean ndi Nadine sanali okondweretsedwa ndi chipembedzo. Komabe, nthaŵi zina amakambitsirana za chiyambi cha moyo. Kaŵirikaŵiri nkhani imene imabuka inali ya ziphunzitso zovuta kumvetsa za chisinthiko. Komabe palibe chimodzi cha ziphunzitso zimenezi chinawagwira mtima.

Atakhala kwaokhaokha kwa zaka zisanu ndi ziŵiri, anadabwa kuti Mboni za Yehova ziŵiri zinadzawachezera. Mbonizo zinamva za kumene Jean ndi Nadine anali kukhala pamudzi woyandikana nawo. Mwachizoloŵezi, makambitsirano anafika poyamba kukamba za chiphunzitso cha chisinthiko. Mbonizo zinali zitatenga buku la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, chinthu chomwe chinakondweretsa banjalo. Jean ndi Nadine anasangalala kupeza buku lomwe linalongosola bwino mosamalitsa mmene moyo unabwerera padziko.

Nthaŵi pang’ono pambuyo pake, phunziro la Baibulo lanayambidwa. Pafupifupi zaka zitatu, Jean ndi Nadine anasonyeza kupita patsogolo. Anakhulupirira kuti posachedwa dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Pamene banja lawo linakula kufika pokhala ndi ana atatu, kuyenda maola anayi kupita ku misonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu kunakhala ntchito yovuta. Komabe izi sizinawalepheretse kumasonkhana nawo. Kenaka Jean ndi Nadine anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mu ubatizo wa m’madzi. Anachita izi pamsonkhano womwe unachitikira m’mudzi waukuluwo ndipo chiŵerengero cha osonkhana chinali anthu 38!

Ncholinga chofuna kuthandiza kagulu kochepako ka olengeza Ufumu, banjalo linaganiza zochoka kwaokhaokhako. Anasamukira pamudzi wokhala ndi anthu pafupifupi chikwi chimodzi, kumene tsopano Jean akutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo wa Mboni za Yehova wakumaloko. Banja ili lomwe poyamba linapita ku zisumbu kuthaŵa chitukuko, limaona monga mwaŵi kuti linapeza malo othaŵirako a chisungiko chenicheni, Gulu la Teokrase la Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena