Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 10/1 tsamba 8
  • Choonadi cha Baibulo Chikupitiriza Kulalikidwa mu Ireland

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Choonadi cha Baibulo Chikupitiriza Kulalikidwa mu Ireland
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kulera Ana a Ena—Chifukwa Ninji ndipo Motani?
    Galamukani!—1996
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda—1996
w96 10/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

Choonadi cha Baibulo Chikupitiriza Kulalikidwa mu Ireland

M’ZAKA zaposachedwapa dziko lokongola la Ireland lakhala malo a chipwirikiti chachikulu. Panthaŵi imodzimodziyo, anthu achiairishi alabadira uthenga wa Baibulo wa chiyembekezo umene Mboni za Yehova zawabweretsera. Zokumana nazo zotsatirazi zochokera ku Ireland zikuchitira umboni zimenezi.

▪ Ku Dublin Mboni ya Yehova ina ndi mwana wake wamng’ono wamkazi anali kuchita nawo ntchito yolalikira kukhomo ndi khomo. Iwo anakumana ndi mkazi wina wotchedwa Cathy amene anali wotanganitsidwa kwambiri ndi ana ake ambiri. Mboniyo inampempha ngati angakonde kuti mwana wakeyo, amene anali kuphunzira kulalikira, akambitsirane za uthenga wachidule ndi mkaziyo. Cathy anavomera, ndipo kamsungwanako kanapereka ulaliki womveka ndiponso wolingaliridwa bwino. Cathy anachita chidwi ndi kuona mtima kwapoyera ndi ulemu wa mwanayo, ndipo analandira trakiti lofotokoza Baibulo.

Pambuyo pake Cathy anasinkhasinkha za kukonzekera ndi khalidwe labwino la mlendo wake wachichepereyo. “Ndinachita chidwi kuona kuti kamsungwanako kanatha kundiuza uthenga wokondweretsa popanda kudzionetsera,” anatero mkaziyo. “Ndinasankha kuti pamene Mboni za Yehova zidzafikanso, ndidzazimvetsera.”

Zikali choncho Cathy anasamukira ku tauni ina yaing’ono kummwera cha kumadzulo kwa Ireland kufupi ndi malire a maboma a Cork ndi Kerry. Nthaŵi ina pambuyo pake Mboni za Yehova zinafika pakhomo pake, ndipo anazipempha kuti ziloŵe. Anavomera phunziro la Baibulo lokhazikika ndipo tsopano amafika pamisonkhano ndi ana ake angapo. Cathy ngwothokoza chifukwa cha chikhumbo choona mtima cha kamsungwanako cha kumuuza uthenga wabwino.

▪ M’dera la Tullamore, Mboni zinakambitsirana za Baibulo ndi mkazi wina wotchedwa Jean kwa nyengo yoposa zaka zisanu ndi ziŵiri. Nthaŵi zina iyeyo anali kusonyeza chidwi ndipo ankalandira mabuku, komanso nthaŵi zina chidwi chake chinkazirala. Tsiku lina, pamene Mboni ina yotchedwa Frances ndi mnzake anafikira Jean, anampeza ali m’mkhalidwe wotsutsa kwambiri. “Zilizonse zimene tinanena,” ikusimba motero Mboniyo, “iyeyo anawonjezera kukwiya. Potsirizira pake, anatiuza kuti tidzimka motithamangitsa namenyetsa chitseko.”

Frances anasinkhasinkha ngati kumfikiranso kungachititsenso mkhalidwe umodzimodziwo. ‘Mwinamwake kumfikiranso nkosayeneranso ngati alibe chidwi chenicheni ndi uthenga,’ analingalira motero Frances. Komabe, anakambitsirana nkhaniyo ndi mwamuna wake, Thomas, ndipo iyeyo anali ndi chiyembekezo chachikulu. Nthaŵi yotsatira pamene anali m’deralo, anafikiranso Jean. Iyeyo anali waubwenzi ndipo analandira makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kucheza kwawo kwina kowonjezereka kunali kosangalatsa, ndipo Thomas ndi Frances anayamba kuchita phunziro la Baibulo lapanyumba lokhazikika ndi mkaziyo.

Kodi nchifukwa ninji anasintha? Jean akufotokoza kuti pa nthaŵi imene anachitira chipongwe Mbonizo, anali atangobala kumene mwana ndipo anali atangotuluka kumene m’chipatala. Chifukwa cha kuyamwitsa khanda lake latsopano ndi kudyetsa mwana wake wokulirapo, iye anali kugona ola limodzi lokha ndi theka usiku. “Sindinkafuna nkomwe kulankhula za chipembedzo,” Jean anatero.

Miyezi iŵiri isanathe Jean anali kufika pa misonkhano yonse ya mpingo, ndipo miyezi inayi isanathe anali kuchita nawo utumiki wakumunda. Miyezi khumi itakwana kuyambira pamene anayamba kuphunzira Baibulo, iyeyo anabatizidwa. Tsopano chochitika cha Jean iye mwini chimamthandiza mu utumiki. Akusimba kuti: “Ngati ndikumana ndi munthu wina amene ali wachipongwe kwambiri, ndimayesetsa kukhala wozindikira. Nthaŵi zonse ndimakhala wosamala zimenezi. Mwina mkhalidwe ungadzasinthe pamene ndidzabweranso; mwina munthuyo angakhale akupeza bwinopo ndi kukhala womasuka kwambiri.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena