Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 5/8 tsamba 20-23
  • Kulera Ana a Ena—Chifukwa Ninji ndipo Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulera Ana a Ena—Chifukwa Ninji ndipo Motani?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulera Kapena Kusalera Mwana wa Ena?
  • Ngati Mwasankha Kulera Mwana wa Ena . . .
  • Wafuko Lina?
  • Wochokera ku Dziko Lina?
  • Kodi Muyenera—Kulera Ana a Ena?
    Galamukani!—1996
  • Kulera Ana a Ena—Kodi Ndiyenera Kukuona Motani?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumakwaniritsa Zinthu Zotani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Ndinakhaliranji Mwana wa Makolo Amene Sanandibereke?
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 5/8 tsamba 20-23

Kulera Ana a Ena—Chifukwa Ninji ndipo Motani?

KODI nchifukwa ninji chiŵerengero cha ana olera ku Britain chatsika kwambiri m’zaka 20 zapitazi? Zifukwa ziŵiri zaperekedwa—kukhalapo kwa kutaya mimba mwalamulo ndiponso kuchuluka kwa anthu ovomereza kuti amayi angasunge mwana wawo popanda mwamuna. Kukhala banja la kholo limodzi tsopano kukuonedwa ngati chitokoso chimene chingagonjetsedwe mwachipambano m’chitaganya chamakono.

Komabe, zaka zoposa 100 zapitazo, zinthu sizinali motere. Pamene Polly, amayi wa Edgar Wallace, wolemba manovelo achiwawa wachingelezi, anakhala ndi mimba ya mwana wa owalemba ntchito, iwo anachoka panyumbapo ndi kukabereka mwachinsinsi. Edgar anali ndi masiku asanu ndi anayi okha pamene namwino analinganiza kuti mkazi wa George Freeman, wamtengatenga pamsika wansomba wa Billingsgate ku London, akamsamlire. Banja la a Freeman linali kale ndi ana awo khumi, ndipo Edgar anakula ndi dzina lakuti Dick Freeman. Nthaŵi zonse Polly ankapereka malipiro othandiza kusamalira mwana wake, ndipo atate wake sanadziŵe konse za kukhalapo kwa mwana wawo wamwamuna.

Lerolino pamene makanda sakufunidwa, kaŵirikaŵiri mabungwe a boma amadzitengera thayo limenelo. Amatenga ana ambiri kuti awasamalire chifukwa amafunikira kutetezeredwa ku nkhanza kapena chifukwa chakuti ali ndi matenda ena a m’thupi kapena m’maganizo. Amene makolo awo anamwalira m’nkhondo ndi ana obadwa chifukwa cha kugwiriridwa chigololo akuwonjezerabe chiŵerengero cha ana ofunitsitsa chikondi ndi chitetezo cha makolo—m’mawu ena, kuleredwa.

Kulera Kapena Kusalera Mwana wa Ena?

Nthaŵi zonse kulera mwana wa ena sikwapafupi, ndipo sikwanzeru konse kupanga chosankha chamwamsanga pamene mukukulingalirapo. Ngati mwatayikidwa khanda, kungakhale bwino koposa kuyembekezera kufikira pamene kupwetekedwa mtima kapena chisoni chitha musanapange chosankha chomaliza ponena za kulera mwana wa ena. Zimenezi zilinso motero kwa okwatirana amene auzidwa kuti ngouma.

Mwana aliyense amatengera mkhalidwe wosiyana wa majini kwa makolo ake. Kaŵirikaŵiri makolo amadabwa ndi zikhoterero zachibadwa za ana awo, koma nkovuta kudziŵa nzeru ndi mtima wa khanda ngati makolo ake samadziŵika.

Kodi mumaona maphunziro kukhala chinthu chofunika koposa? Ngati zili choncho, kodi mudzamva bwanji ngati mwana wanu wolera sakwaniritsa ziyembekezo zanu? Kodi mwana wakufa mutu kapena wopunduka mudzamuona monga chitokoso chimene mungalimbane nacho?

Antchito ophunzitsidwa akumabungwe oyang’anira pa ana olera kapena antchito yothandiza anthu ovutika adzakufunsani mafunso otero musanadzipereke. Nkhaŵa yawo yaikulu imakhala chisungiko ndi chimwemwe cha mwanayo.

Ngati Mwasankha Kulera Mwana wa Ena . . .

Dziko lililonse lili ndi malamulo ake a kulera ana a ena amene afunika kuwaphunzira. Ku Britain kuli mabungwe ambirimbiri oona pa za kulera ana a ena, ndipo kaŵirikaŵiri amagwirizana ndi olamulira a boma akumaloko. Mabungwe onse ali ndi malamulo awoawo.

Makamaka mapwando a kulera ana ndiwo ofala ku Britain, kumene angapo ofuna kulera ana a ena amayanjana ndi ana amene akufuna owalera, popanda kuvutika mtima kwambiri kumene kungakhalepo pa kukambitsirana ndi mwana mmodzi. Mkhalidwe womasuka umene umakhalapo umachititsa ofuna kulera mwana kukana mosavuta kutenga mwana wakutiwakuti ndipo si kwenikweni kuti ana angaone kukhala ogwiritsidwa mwala, popeza samasumika chisamaliro pa mwana mmodzi yekha.

Nthaŵi zambiri pamakhala msinkhu woikika umene ofuna kulera ana a ena ayenera kukhala nawo, pafupifupi zaka 35 kapena 40—ngakhale kuti zimenezi kaŵirikaŵiri zimagwira ntchito pa kulera makanda, osati kwenikweni ana aakulupo. Mabungwe oyang’anira pa kulera ana amanena kuti malire a msinkhu amakhalapo poyerekezera utali wa moyo umene ofuna kukhala makolo olerawo adzakhala nawo. Komabe, iwo amadziŵa kuti chidziŵitso chabwino kwambiri chimadza ndi msinkhu.

M’zaka zapitazo kulera ana kunali kulinganizidwa ndi okhala mu ukwati okha. Lerolino, osakhala mu ukwati angapemphe kulera ana akutiakuti ndi kuloledwa. Ndiponso, ulova ndi kupunduka kwa ofuna kulera ana sizili kwenikweni zifukwa zowakanira. Funso lalikulu ndilo lakuti, Kodi nchiyani chimene makonzedwewo adzapatsa mwana?

Ngakhale pamene makonzedwe a kulera mwana atha m’kupita kwanthaŵi, makolowo angamawayang’anire nthaŵi zonse kuti atsimikizire kuti zinthu zikuyenda bwino.

Wafuko Lina?

Zaka makumi atatu zapitazo ana achikuda ku Britain ankavuta kuwapezera mabanja achikuda oti awalere, ndipo chifukwa cha chimenecho, ambiri anapita kwa makolo achiyera. Kuyambira 1989 lakhala lamulo la dziko la Britain kupezera ana makolo owalera afuko limodzimodzi. Amakhulupirira kuti mwa njira imeneyi mwana amadziŵa fuko lake ndi mwambo mwamsanga. Komabe, zimenezi zachititsa mikhalidwe ina yodabwitsa.

Posachedwapa The Sunday Times inanena kuti makolo ena achiyera “atchedwanso ‘achikuda’” kuwatheketsa kulera mwana wachikuda. Sikwachilendo kwa makolo achiyera kusunga mwana wachikuda, zimene zikutanthauza kuti amamsamalira kwakanthaŵi. Koma ngati pambuyo pake sanawalole kulera mwanayo kwachikhalire, chotulukapo chake chimakhala kusweka mtima kwa mwana ndi makolo omwe.

Okwatirana a ku Scotland, amene kwa zaka zisanu ndi chimodzi anasunga ana aŵiri achimwenye, posachedwa anayang’anizana ndi vuto lalikulu la kulera ana a fuko lina. Bwalo la milandu linawalola kulera anawo pamaziko akuti makolowo “adzayesetsa kutsimikizira kuti anawo adzawaphunzitsa za [fuko] lawo ndi kuwalera akumadziŵa za fuko limene anachokerako ndi miyambo yawo,” ikutero The Times. Pambali imeneyi makolo owalerawo anali atayamba kale kuchita zimenezo. Anawo ankaphunzitsidwa Chipunjabi ndipo nthaŵi zina ankawaveka zovala zakwawo.

Ambiri angavomerezane ndi mawu a mkazi wolankhulira antchito othandiza anthu ovutika wa ku Britain amene ananena kuti kulera ana a mafuko ena kuyenera kuloledwa kwambiri. “Tikukhala m’chitaganya cha mafuko osiyanasiyana,” iye anatero, “ndipo kusunga ndi kulera ana kuyenera kusonyeza zimenezo.”

Wochokera ku Dziko Lina?

Kulera ana ochokera ku maiko ena ndiko ‘malonda omakula,’ malinga ndi nyuzipepala ya The Independent. Ngakhale kuti malipoti akusonyeza kuti ena a malonda ameneŵa ndi aukatangale, Eastern Europe ndiye wopereka malondawo wamkulu wa Britain.

Mwachitsanzo, makanda ena obadwa chifukwa cha kugwiriridwa chigololo pa kusweka kwa amene kale anali Yugoslavia asiyidwa. Ena, zikumveka motero, akanatayidwa asanabadwe bwenzi panalibe “owapezera malonda ogulitsa makanda” amene ankalonjeza kulera mwanayo ngati anabadwa panthaŵi yake. Komabe, maboma a maiko Akummadzulo akudera nkhaŵa za ndalama zolipiridwa pogula ana olera ameneŵa.

Chodetsa nkhaŵa chachikulu chikukhudza zimene ena ananena kuti madokotala amalemba zipepala zabodza panthaŵi ya kubadwa. Nyuzipepala ya The European inanena za nkhani yakuti anakubala ena ku Ukraine anauzidwa kuti makanda awo anabadwa akufa. Kunanenedwanso kuti makanda ameneŵa anagulitsidwa pambuyo pake. Anakubala ena angakhale atauzidwa kuti ana awo anali akufa mitu. Povutika mtima chotero, anakubala osadziŵa chochita amanyengeka ndi kulola ana awo kuti akaleredwe ndi ena. Komabe ana ena apititsidwa ku maiko ena asanafike konse kumalo osungira ana opanda makolo kumene anatumizidwako.

Mkwiyo ukuonekera m’maiko omatukuka. Iwo akunena kuti maiko achuma Akummadzulo ayenera kumathandizabe mabanja a kumaiko enawo kusamalira mbadwa zawo kwawoko m’malo mozitenga kuti zikaleredwe kudziko lina.

Maiko Akummadzulo ayeneranso kudziŵa bwino mwambo wakale lomwe wa mabanja apachibale, cholimbitsa chitaganya cha anthu ambiri m’maiko. Kaŵirikaŵiri mwana sadzasoŵa chisamaliro pamene akukhala pakati pa mtundu wake, ngakhale ngati makolo ake amwalira. Kusiyapo a m’banja apafupi kwambiri, monga agogo, banja lalikulu lapachibale lokhala ndi adzakhali ndi amalume lidzaona mwanayo monga wawo, ndipo pempho lililonse lokamlera la anthu ena angaliganizire molakwa ndi kuliona monga msokonezo wosaloleka.a

Kulinganiza kulera mwana wa ena sikwapafupi, ndipo ngakhale pamene zonse zatha, kugwiritsa ntchito nkofunika kuti makonzedwewo akhale achipambano. Koma monga mmene tidzaonera, palinso zinthu zochititsa chimwemwe chachikulu.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mukufuna kuŵerenga tsatanetsatane wa kubwereketsa ana kwa a m’banja ena, onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1988, masamba 28—30, yofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Bokosi patsamba 21]

Kodi Mwana Wanga Adzandifunafuna?

MAKOLO anga analekana pamene ndinali ndi zaka 11. Ndinali kulakalaka chikondi. Pamene ndinali kukoleji, ndinayamba kukondana ndi mnyamata wina; inali njira yopezera chikondi. Ndiyeno moipidwa ndinaona kuti ndinali ndi mimba. Zinali zogwiritsa mwala. Ineyo ndi wophunzira mnzanga tinalidi osakhwima. Sindinagwiritsirepo ntchito anamgoneka, moŵa, kapena fodya, koma bwenzi langa lachimuna linali lowonongeka kwambiri chifukwa cha LSD amene anali atagwiritsirapo ntchito.

Ndinauzidwa kutaya mimbayo, koma atate anandiuza kusatero. Sindinafune kukhala ndi mimba, komanso sindinafune kupha. Pamene mwana wanga wamwamuna anabadwa mu 1978, ndinasankha kusalembetsa dzina la atate wake pa chipepala cha kubadwa kwake kutsimikizira kuti atate wake asakhale ndi chonena pa iye. Kwenikweni, khandalo litangobadwa ndinavomereza kuti likaleredwe ndi ena; motero analitenga nthaŵi yomweyo ndi kukalisunga kwakanthaŵi. Sindinalione nkomwe. Koma tsono ndinasintha maganizo anga. Ndinatenga khanda langa kumene ankalisungirako ndi kuyesetsa kulisamalira ineyo. Koma sindinathe, ndipo ndinatsala pang’ono kupsinjika mtima.

Mwana wanga anali ndi miyezi isanu ndi umodzi pamene pempho lakuti akaleredwe ndi ena linavomerezedwa ndipo ndinampereka. Ndikukumbukira kuti ndinamva ngati kuti wina wangondipyoza kumene ndi mpeni. Ndinasiya kukhudzika mtima. Ndi kokha pamene ndakhala ndili kulandira uphungu waakatswiri pa zaka ziŵiri zapitazi pamene ndakhala wokhoza kukhala ndi maunansi atanthauzo. Sindinathe kulira—mwana wanga anali wamoyo. Komanso sindinathe kulingalira za iye—ndinadzikaniza kutero. Zinalidi zoipa.

Chopweteka kwambiri ndicho kumva anthu akunena kuti: “Ngati upereka mwana wako kuti akaleredwe ndi ena, ndiye kuti mwana wako sumamkonda.” Koma sizinali choncho kwa ine! Ndinali kumkonda mwana wanga nchifukwa chake ndinampereka! Mpaka nditampereka ndinapitirizabe kudzifunsa kuti: ‘Nanga munthu angatani? Kodi ndiyenera kutani?’ Panalibe mochitira. Ndinadziŵa kuti sindikanatha ndi kuti mwana wanga akanavutika ndikanayesa kumsunga ineyo.

Ku England, anthu tsopano amavomereza mabanja a kholo limodzi—koma osati pamene ndinabereka. Ndingoti ndikanamsamalira bwino mwana wanga. Ndiyesa uphungu umene ndalandira posachedwapa ukanandithandiza, koma zinapita kale. Kodi mwana wanga akali moyo? Kodi iye wakula kukhala mnyamata wotani? Atafika zaka 18, ana olera mwalamulo amakhala ndi ufulu wa kufunafuna makolo awo. Nthaŵi zambiri ndimadzifunsa ngati mwana wanga adzandifunafuna.—Yoperekedwa.

[Bokosi patsamba 21]

Kwa Ife Zinagwira Ntchito

NDI anyamata athuathu aŵiri, tinali banja lachingelezi lokhutira ndi logwirizana. Lingaliro la kukhala ndi mwana wamkazi—ndipo wa fuko lina—sitinakhalepo nalo. Ndiyeno tinayamba kulingalira za Cathy. Cathy anabadwira ku London, England. Iye anakula monga Mroma Katolika, koma pamene anali mwana wamng’ono, anapitapo ku misonkhano ingapo ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ndi amayi wake. Komabe, atakhala ndi zaka 10 anaperekedwa ku nyumba yolererako ana.

Ngakhale kuti zinthu kumeneko zinali zomvutirapo, anakwanitsabe payekha kumapezeka pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu, kumene tinaonana naye. Cathy anali mtsikana wolingalira. Pamene ineyo ndi mkazi wanga tinapita kukamchezera kunyumba yolererako ana, tinazindikira kuti khoma lapafupi ndi kama wake linali ndi zithunzithunzi za nyama ndi malo akumidzi, mosiyana ndi zithunzithunzi za oimba otchuka zimene atsikana ena anamamatiza.

Nthaŵi ina pambuyo pake Cathy anakaonana ndi bungwe lina lofufuza, limene linamfunsa ngati anafuna kuchoka panyumbapo ndi kukakhala ndi banja lina m’malo mwake. “Kokha ndi banja la Mboni za Yehova!” anayankha motero. Pamene Cathy anatiuza za zimenezi ndi zimene anali atanena, zinatichititsa kulingalirapo kwambiri. Tinali ndi chipinda chapadera. Kodi tikanakhoza kutenga thayo lamtundu umenewu? Monga banja, tinakambitsirana nkhaniyo ndi kuipempherera. Panali pambuyo pake pokha pamene tinaona kuti njira imeneyi—kufunsa mwanayo malingaliro ake—inali chinthu chatsopano kwa antchito yothandiza anthu ovutika, kuyesa kumene panthaŵiyo anali kukumaliza.

Antchito yothandiza anthu ovutika anafufuza za ife kwa apolisi ndi dokotala wathu napeza ziyeneretso zathu. Posapita nthaŵi tinachitirana pangano. Anatiuza kuti tingakhale ndi Cathy monga kuyesa chabe ndi kuti tingambwezere ngati sitinamkonde! Zimenezi zinatiwopsa, ndipo tinanenetsa kuti sitidzachita zimenezo. Cathy anali ndi zaka 13 pamene tinamtenga mwalamulo.

Unansi wapadera wa chikondi pakati pathu tonsefe unapitirizabe kukhala wolimba. Cathy tsopano akutumikira monga mpainiya (mlaliki wanthaŵi yonse) mumpingo wachifalansa wa Mboni za Yehova kumpoto kwa London. Chaka chimene anachoka panyumba kukachita upainiya, anatilembera kalata yogwira mtima yakuti: “Pali mwambi wakuti ‘sungasankhe banja lako.’ Komabe, ndikukuyamikani kuchokera pansi pa mtima wanga kaamba ka kundisankha.”

Tili okondwa kwambiri kuti Cathy anagwirizana ndi banja lathu! Kumpanga kukhala wa m’banja lathu kunalemeretsa moyo wathu. Kwa ife zinagwira ntchito!—Yoperekedwa.

[Chithunzi]

Cathy ndi makolo ake omlera ndi alongo ake opeza

[Chithunzi patsamba 22]

Ana ambiri amafunitsitsa chikondi ndi chitetezo cha makolo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena