Kodi Muyenera—Kulera Ana a Ena?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRITAIN
“KULERA ana a ena ndiko kuthandiza ana, osati kuthandiza okwatirana opanda ana kuti akhale ndi mwana,” akutero wantchito yothandiza anthu ovutika wa ku Britain. Ngakhale zili choncho, kodi mwana anganenenji pa kutengedwa kwake kuti ena akamlere?
Kodi mukulingalira zolera mwana wa ena? Ndiye kuti mukuyang’anizana ndi chosankha chokhudza mtima ndi chosasinthika. Kodi mwanayo adzazoloŵera bwino motani m’banja lanu?
Ngati ndinu mwana woleredwa ndi ena, kodi makolo anu okubalani mumawadziŵa? Ngati sitero, kodi mukuganizira kuti pakanakhala kusiyana kotani mukanawadziŵa?
Kodi ndinu amayi amene mukulingalira zopereka mwana wanu kuti akaleredwe ndi ena? Kodi kuleredwa kwa mwana ndi ena ndiko njira yokha yochitira ndipo yopindulitsadi mwana wanu?
Mu 1995, ana oposa 50,000 anatengedwa kukaleredwa ndi ena ku United States, ndipo pafupifupi 8,000 a iwo anali obadwira kunja kwa dzikolo. Anthu owonjezereka akulera ana a ena ochokera ku maiko akunja. Malinga ndi magazini a Time, m’zaka 25 zapitazi mabanja ku United States atenga ana pafupifupi 140,000 obadwira kunja kukawalera. Ziŵerengero zonga zimenezo za ku Ulaya ndizo Sweden 32,000, Holland 18,000, Germany 15,000, ndi Denmark 11,000.
Kodi mukulingalira kuchita chimodzi cha zimenezi? Kulera mwana wa ena kumatanthauza kuti moyo wanu—osati moyo wa mwana wokha—sudzakhalanso chimodzimodzi. Moyenerera makolo olera amayembekezera kukhala ndi chikondwerero chachikulu, komanso ayenera kukonzekera kaamba ka mavuto ndi kugwiritsidwa mwala kochuluka. Momwemonso, kupwetekedwa mtima kumene amayi amakhala nako popereka mwana wawo kuti akaleredwe sikungathe konse.
Mkhalidwe uliwonse umakhala ndi chitokoso cha kumanga kapena kumanganso moyo wa mwana wamng’ono ndi chikondi. Nkhani zotsatira zidzatchula zina za zikondwerero—ndi zitokoso—za kulera mwana wa ena.