Kodi Kuchiritsa Kozizwitsa Kudakachitikabe?
“KHULUPIRIRANI Yesu muchiritsidwe!” Mawu ngati amenewo anampangitsa Alexandre, wa tchalitchi cha Evangelical kuganiza kuti kumwa mankhwala utadwala kungasonyeze kupanda chikhulupiriro. Anakhutira kuti chikhulupiriro chake chokha chikanachita zomwe anali kufuna, kumchiritsa mozizwitsa. Benedita, Mkatolika wokangalika, anakhudzika mtima kwambiri pamene anamva za kuchiritsa kozizwitsa kumalo opatulika a Aparecida do Norte, ku São Paulo, Brazil. Akumagwiritsira ntchito mawu ena amatsenga omwe mdzakhali wake anamphunzitsa, Benedita anapemphera kwa Mayi Wathu wa Aparecida, Anthony, ndi “oyera mtima” ena kuti ampatse mphamvu yochiritsira odwala.
Ngakhale tsopano m’zaka zino za zana la 20, nzachionekere kuti anthu ambiri amakhulupirira kuchiritsa kozizwitsa—koma nchifukwa ninji? Mwina ena amagwiritsidwa mwala pamene madokotala amalephera kuthetsa matenda, zopweteka, ndi kuvutika kwa okondedwa awo, makamaka ana awo. Aja amene adwala kwa nthaŵi yaitali amaganiza kuti popeza mankhwala amakonoŵa akwera mtengo chonchi, ndi bwino kukafunafuna ochiritsa mwachikhulupiriro. Ena amaona pa TV matchalitchi osiyanasiyana ndi anthu ena akunena kuti akhoza kuchiritsa AIDS, kupsinjika maganizo, kansa, misala, BP, ndi matenda ena ambiri. Kaya amakhulupirira zonena zawozo kapena samakhulupirira, amapitabe kwa iwo monga kotsirizira kufunafunako chithandizo. Komanso ena amene amakhulupirira kuti imene ikuwadwalitsa ndi mizimu yoipa amaona kuti mankhwala achizungu alibe mphamvu yowachiritsa.
Komanso, pali aja amene amakana ndithu, ngakhale kutsutsa lingaliro lakuti “oyera mtima” akufa kapena ochiritsa amoyo angachiritse mozizwitsa. Malinga ndi magazini ya Jornal da Tarde, wasayansi ya mphamvu zathupi zotetezera matenda, Dráusio Varella, amaona kuti kukhulupirira zimenezo “kumagwiritsa mwala opusa ndi osoŵa chochita.” Akuwonjezera kuti: “Pofuna zozizwitsa, ambiri amaleka mankhwala amphamvu akuchipatala chifukwa cha onyenga ameneŵa.” Ndipo The New Encyclopædia Britannica ikulongosola kuti: “Kale amakhulupirira kuti munthu amachira popanda kugwiritsira ntchito mankhwala mwa kupita kumalo opatulika ndi kutsata mwambo wa chipembedzo, ndipo asayansi ya zamankhwala amati machiritso onsewo amatheka chifukwa chotsata njira yozoloŵereka yomgoneka tulo munthu pamalo abwino.” Komabe, pali ambiri amene amakhulupiriradi kuti anachira mwa chozizwitsa. Kwa iwowo, kuchirako kunalidi kwenikweni!
Amene alizoloŵera Baibulo amadziŵa kuti Yesu Kristu anachiritsapo odwala nthaŵi zambiri, akumachita zimenezo mwa “mphamvu ya Mulungu.” (Luka 9:42, 43, NW) Chotero angafunse kuti: ‘Kodi mphamvu ya Mulungu idakagwirabe ntchito ndi kumachiritsa mozizwitsa leronso?’ Ngati zili choncho, nanga nchifukwa ninji amene amayesa kuchiritsa amalephera kuchita zimene alonjeza? Kodi chingakhale chifukwa choti wodwalayo alibe chikhulupiriro kwenikweni kapena chifukwa choti zopereka zake sizokwanira? Kodi nkoyenera kuti Mkristu afunefune ochiritsa mozizwitsa pamene akudwala nthenda yopweteka kapena mwina yosachiritsika? Ndipo kodi kuchiritsa kozizwitsa kosalephereka kofanana ndi kumene Yesu anachitapo kale kudzachitikanso? Mayankho a mafunso ofunika ameneŵa muwapeza m’nkhani yotsatirayo.