Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 7/1 tsamba 27-30
  • Kodi Ndinu Bwenzi la Mulungu?—Chimene Mapemphero Anu Amavumbula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndinu Bwenzi la Mulungu?—Chimene Mapemphero Anu Amavumbula
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupeza Nthaŵi Yoti Nkupemphera
  • Kuwongolera Mapemphero Athu
  • Kutonthozedwa ndi Kumvedwa m’Nthaŵi za Mavuto
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Mapemphero Anu Ali a Tanthauzo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 7/1 tsamba 27-30

Kodi Ndinu Bwenzi la Mulungu?​—Chimene Mapemphero Anu Amavumbula

KODI munamvapo mwamwaŵi anthu aŵiri akukambitsirana? Mosakayika sizinakutengereni nthaŵi kuti muzindikire mtundu wa ubwenzi wawo​—kuti ndi ogwirizana kwambiri kapena angokumana, ongodziŵana kapena okondana kwambiri, mabwenzi okhulupirirana. Mofananamo, mapemphero athu angavumbule unansi wathu ndi Mulungu.

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Ndithudi, amatipempha kuti timdziŵe. Tikhoza kukhala ngakhale mabwenzi ake. (Salmo 34:8; Yakobo 2:23) Tikhoza kukhala paubwenzi wa ponda apa mpondepo ndi iye! (Salmo 25:14) Kunena zoona, unansi wathu ndi Mulungu ndi chinthu cha mtengo wapatali koposa chomwe anthu opanda ungwirofe tingakhale nacho. Ndipo Yehova amaona ubwenzi wathu monga wamtengo wapatali. Tingatsimikizire izi chifukwa maziko a ubwenzi wathuwo ndi kukhala kwathu ndi chikhulupiriro mwa Mwana wake wobadwa yekha, yemwe anapereka moyo wake m’malo mwa ife.​—Akolose 1:19, 20.

Motero mapemphero athu ayenera kusonyeza chikondi chachikulu ndi kuyamikira kwathu Yehova. Ngakhale zili tero, kodi munayamba mwaonapo kuti mapemphero anu, ngakhale ndi aulemu, sakhalabe ochokera pansi pa mtima? Izi sizachilendo. Nchiyani chomwe chingathandize kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino? Kukulitsa ubwenzi wanu ndi Yehova Mulungu.

Kupeza Nthaŵi Yoti Nkupemphera

Choyamba, zimatenga nthaŵi kuti mukulitse ubwenzi. Tsiku lililonse mukhoza kumalonjera kapena ngakhale kumakambitsirana ndi anthu ambiri​—anansi, anzanu akuntchito, oyendetsa mabasi, ndi ogulitsa m’sitolo. Komabe, izi sizitanthauza kuti mulidi nawo paubwenzi. Ubwenzi umakula pamene muyamba kukambitsirana kwambiri ndi wina, mukumasiya kukamba nkhani wamba nkuyamba kukamba za pansi pa mtima.

Mofananamo, pemphero limatithandiza kuyandikira kwa Yehova. Koma muyenera kutherapo nthaŵi yokwanira; pamafunika zambiri zoposa kunena mwachidule kuti zikomo pa nthaŵi ya chakudya. Pamene mulankhula kwambiri ndi Yehova mpamene mumatha kulongosola bwino zakukhosi, zolinga zanu, ndi zochita zanu. Njira zothetsera mavuto aakulu zimayamba kuoneka pamene mzimu wa Mulungu ukukumbutsani mapulinsipulo a m’Mawu ake. (Salmo 143:10; Yohane 14:26) Komanso, pamene mupemphera, Yehova amaoneka kuti alikodi, ndipo mumazindikira kwambiri za chikondi chake ndi chisamaliro chake pa inu.

Izi makamaka zimatero mutaona kuti mwayankhidwa pemphero lanu. Yehova “angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife”! (Aefeso 3:20) Izi sizikutanthauza kuti Mulungu adzakuchitirani zozizwitsa. M’malo mwake, angakupatseni malangizo ofunika kapena kukutsogolerani kupyolera mwa Mawu ake olembedwa, zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika, kapena mwa mawu a abale ndi alongo. Mwinanso angakupatseni mphamvu zomwe mungafunikire kuti mupirire kapena kugonjetsa chiyeso. (Mateyu 24:45; 2 Timoteo 4:17) Tikakumana ndi zotere timasangalala chifukwa cha Bwenzi lathu lakumwamba!

Choncho munthu ayenera kupeza nthaŵi yopemphera. Zoonadi, nthaŵi imasoŵa masiku ovuta ano. Koma ngati mumalingaliradi za munthu wina, nthaŵi zonse mumapeza nthaŵi yoti mukacheze naye. Onani momwe wamasalmo ananenera za iye mwini: “Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo: ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?” (Salmo 42:1, 2) Kodi inunso muli ndi chilakolako chotere cholankhula ndi Mulungu? Ndiyetu pezani nthaŵi yochitira zimenezo!​—Yerekezerani ndi Aefeso 5:16.

Mwachitsanzo, mungadzuke m’mamaŵa kuti mupeze mpata wabwino woti mupemphere. (Salmo 119:147) Kodi nthaŵi zina mumalephera kugona usiku? Ndiye kuti, monga wamasalmo, mungagwiritsire ntchito nthaŵi yosautsa imeneyi kufotokoza nkhaŵa zanu kwa Mulungu. (Salmo 63:6) Mwina mwachidule mukhoza kumangopereka mapemphero afupiafupi koma kaŵirikaŵiri usana. Wamasalmo anati kwa Mulungu: “Pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.”​—Salmo 86:3.

Kuwongolera Mapemphero Athu

Nthaŵi zina mudzaona kuti kuli bwino kuwonjezerako utali wa mapemphero anu. M’pemphero lalifupi, mwina mukhoza kumangonena nkhani zodziŵikiratu. Koma ngati munena mapemphero atalipo ndipo apansi pa mtima, mudzatha kunena malingaliro anu ndi mmene mukudzimvera. Yesu nthaŵi ina anachezera kupemphera. (Luka 6:12) Mosakayikira mudzaona kuti mapemphero anu adzakhala omveka ndiponso atanthauzo malinga ngati mupewa kupemphera mwandithendithe.

Izi sizikutanthauza kumangopondaponda pamene muli ndi zonena zochepa; komanso sizikutanthauza kumangobwerezabwereza mosalingalira bwino. Yesu anachenjeza kuti: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo. Chifukwa chake inu musafanane nawo: pakuti Atate wanu adziŵa zomwe muzisoŵa, inu musanayambe kupempha iye.”​—Mateyu 6:7, 8.

Ngati mulingaliriratu zimene mufuna kutchula pasadakhale, mudzatha kunena zomveka m’pemphero. Zoti nkunena zambiri​—kutchulapo zochepa chabe: chimwemwe chathu mu utumiki, kufooka ndi kulephera kwathu, kukhumudwa kwathu, mavuto athu azachuma, mavuto a kusukulu kapena kuntchito, kakhalidwe ka mabanja athu, ndi mkhalidwe wauzimu wa mpingo wathu.

Kodi nthaŵi zina popemphera mumayambanso kuganiza zina? Ndiye kuti muyenera kuyesetsa kumaika mtima kwambiri pa pemphero. Ndipotu, Yehova amafuna ‘kutchera khutu ku mapemphero athu.’ (Salmo 17:1) Kodi sikoyenera kuti ife tiziyesetsa kumvetsera mapemphero athu omwe? Inde, ‘samalirani zinthu za mzimu’ ndipo kanizani maganizo anu kuganiza zina.​—Aroma 8:5.

Mafikidwe athu pamaso pa Yehova nawonso ali nkanthu. Ngakhale amafuna kuti tizimuona monga mnzathu, tisaiŵale kuti tikulankhulana ndi Mfumu ya chilengedwe chonse. Ŵerengani ndipo lingalirani za chithunzi chochititsa mantha choperekedwa mu Chivumbulutso machaputala 4 ndi 5. Pamenepo Yohane anaona m’masomphenya ulemerero wa Amene timamfikira m’pempheroyo. Ndi mwaŵi wotani nanga kuti tingathe kufikira ndi kulankhulana ndi “Iye wakukhala pa mpando wachifumu”! Sitiyenera kulankhula mopanda ulemu kapena kugwiritsira ntchito mawu oluluza. M’malo mwake tiyenera kuyesetsa kuti ‘mawu a m’kamwa mwathu ndi maganizo a m’mtima mwathu avomerezeke pamaso pa Yehova.’​—Salmo 19:14.

Komabe, zindikirani kuti sitisangalatsa Yehova mwa kulankhula mwaluso ndi modzikweza. Amasangalala ndi kulankhula kwathu kwaulemu ndi kochokera pansi pa mtima, mosasamala kanthu kuti sitinazilankhule mwaluso.​—Salmo 62:8.

Kutonthozedwa ndi Kumvedwa m’Nthaŵi za Mavuto

Pamene tikufuna chithandizo ndi chitonthozo, nthaŵi zambiri timapita kwa bwenzi kuti litithandize ndi kutimvera chifundo. Koma, palibe bwenzi losavuta kulifikira mwamsanga kuposa Yehova. Iye ndi “thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Salmo 46:1) Monga “Mulungu wa chitonthozo chonse,” amamvetsetsa bwino zimene tikukumana nazo kuposa munthu wina aliyense. (2 Akorinto 1:3, 4; Salmo 5:1; 31:7) Iye amamvetsetsa ndipo amachitira chifundo amene ali m’mavuto. (Yesaya 63:9; Luka 1:77, 78) Tikazindikira kuti Yehova ndi bwenzi lomvetsetsa zinthu, tidzamasuka kulankhula naye mochokera mumtima ndiponso mwamphamvu. Timasonkhezereka kunena mantha athu ndi nkhaŵa zathu za pansi pa mtima. Motero timayamba kuona mwachindunji mmene ‘zotonthoza [za Yehova] zimakondweretsera moyo wathu.’​—Salmo 94:18, 19.

Nthaŵi zina tingadzione kukhala opereŵera kumfikira Mulungu chifukwa cha zolakwa zathu. Koma bwanji ngati mnzanu wokondedwa wakulakwirani ndipo akupempha kuti mumkhululukire? Kodi simungasonkhezereke kumtonthoza ndi kumlimbikitsa? Tsopano nchifukwa ninji mungakayikire kuti Yehova sangachitenso motero? Iye amawakhululukira mwaufulu anzake omwe amalakwa chifukwa cha kupanda kwawo ungwiro. (Salmo 86:5; 103:3, 8-11) Podziŵa izi, sitiopa kuulula machimo athu mwaufulu kwa iye; ndife otsimikiza za chikondi ndi chifundo chake. (Salmo 51:17) Ngati tayamba kuchita tondovi chifukwa cha zolakwa zathu, tingatonthozedwe ndi mawu a pa 1 Yohane 3:19, 20: “Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, m’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”

Komabe, sitiyenera kusangalala ndi chisamaliro ndi chikondi cha Mulungu pamene tili m’mavuto chabe. Yehova ali ndi chidwi ndi chilichonse chimene chingakhudze mkhalidwe wathu wauzimu ndi maganizo. Inde, sitiyenera kuganiza kuti malingaliro ndi nkhaŵa zathu nzazing’ono zosati nkutchulidwa m’pemphero. (Afilipi 4:6) Mukakhala ndi bwenzi lanu, kodi mumangokambitsirana nkhani zikuluzikulu zokha za m’moyo wanu? Kodi simukambitsirananso tinkhani tina ndi tina? Mofananamo, muyenera kumasuka kukamba chilichonse ndi Yehova chokhudza moyo, podziŵa kuti “Iye asamalira inu.”​—1 Petro 5:7.

Monga mudziŵa, ubwenzi sungakhalitse ngati mumangokamba zanu zokha. Momwemonso, m’mapemphero athu tisamangotchula za ife tokha. Tiyeneranso kutchula chikondi chathu ndi kukhudzidwa mtima kwathu ndi Yehova ndi zokonda zake. (Mateyu 6:9, 10) Pemphero si mpata woti tizingopemphera chabe chithandizo kwa Mulungu komanso ndi nthaŵi yoti tizimthokoza ndi kumtamanda. (Salmo 34:1; 95:2) Phunziro laumwini lidzatithandiza ‘kudziŵa’ zimenezi, popeza limatithandiza kukhala wozoloŵeranapo ndi Yehova ndi njira zake. (Yohane 17:3) Kuŵerenga buku la Masalmo ndi kuona mmene atumiki ena okhulupirika amalankhulirana ndi Yehova mudzakuona kukhala kothandiza.

Ubwenzi ndi Yehova ndi chinthu cha mtengo wapatalidi. Chonde tiyeni tisonyeze kuti tikuyamikira mwa kupanga mapemphero athu kukhala aubwenzi kwambiri, ochokera pansi pa mtima, ndi aumwini. Tikatero tidzakhala ndi chimwemwe monga chomwe chinanenedwa ndi wamasalmo, yemwe anati: “Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa.”​—Salmo 65:4.

[Zithunzi patsamba 28]

Tikhoza kupemphera kwa Mulungu nthaŵi iliyonse malinga ngati mpata upezeka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena