Olengeza Ufumu Akusimba
Kuleka Kutumidwa ndi Ziŵanda
ANTHU akhala akukhulupirira mizimu kwa nthaŵi yaitali. Koma nzotheka kuleka! Ndi zimene zinachitikira anthu ambiri mumzinda wakale wa Efeso. Malinga nkunena kwa Baibulo, “ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha . . . Chotero mawu a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.”—Machitidwe 19:19, 20.
Lerolinonso mpingo wachikristu ukukula. Monga momwe zinalili ku Efeso, pakati pa awo amene akukhulupirira, pali ena amene kale amakhulupirira ziŵanda. Chochitika chotsatirachi cha ku Zimbabwe chikusonyeza zimenezi.
Gogo Mthupha anali wotchuka pa using’anga wamizimu. Anthu amachokera kutali monga ku Zambia, Botswana, ndi ku South Africa kuti adzachiritsidwe ndi mankhwala azitsamba. Gogo Mthupha amaphunzitsanso ena kukhala a n’anga, kapena kuti asing’anga. Ndipo nthaŵi zina amalodza anthu!
Tsiku lina pa Sande Mboni za Yehova zomwe zimalalikira khomo ndi khomo zinafika pa nyumba yake. Anasangalala kwambiri kukambitsirana nazo za lonjezo la Baibulo la dziko lolungama, dziko lopanda zoipa zonse. Analandira buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndi kuvomera phunziro la Baibulo lapanyumba.a Atangochita maphunziro atatu chabe, anayamba kubwera kumisonkhano.
Paphunziro lake la Baibulo, Gogo Mthupha anaphunzira kuti mphamvu zake zapaderazo zimachokera kwa zolengedwa zauzimu zomwe zinapandukira uchifumu wa Yehova. (2 Petro 2:4; Yuda 6) Anaphunziranso kuti ziŵanda zimenezi zikufunadi kupangitsa aliyense yemwe zingathe, kupandukira Yehova ndi kulambira koona. Poti amapeza zofunika pamoyo wake modalira kufunsira zolengedwa zauzimu zimenezi, tsopano akanatani?
Gogo Mthupha anafotokoza kuti akufuna kutaya zithumwa ndi nyanga zonse. Zimenezi zinali zinthu monga chisoti chapadera ndi “nyanga za ng’ombe zolankhula,” zomwe amagwiritsira ntchito pochiritsa anthu monga n’anga. Gogo Mthupha amafuna kutaya zinthu zimenezi kuti azitumikira Mulungu wamoyo ndi woona yekha, Yehova.
Komabe, ena mwa abale ake anakana zimenezi chifukwa amawathandiza powapatsa ndalama. Anampempha kuti awapatse nyangazo, kuphatikizapo mphamvu zake zochitira matsenga, kuti iwowo apitirize kumapindula. Gogo Mthupha anakana.
Mothandizidwa ndi mpingo wa Mboni za Yehova wa kumaloko, anasonkhanitsa nyanga zake zokwanira masaka atatu akuluakulu ndipo zonsezo anazitentha. Pamene malaŵi a moto anakuta zithumwa ndi zinthu zake zolambirira ziŵanda, Gogo Mthupha anafuula kuti: “Taonani! Nyanga iyo, siingathe kudzipulumutsa.”
Patapita nthaŵi, Gogo Mthupha mwachimwemwe anasonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi. Koma nanga tsopano amapeza bwanji zosoŵa za moyo wake? Mwa kugulitsa ndiwo zamasamba. Inde, kupyolera mwa Mawu a Mulungu, munthu angathe kuleka kulambira ziŵanda. Gogo Mthupha akuti: “Sindinayambe ndakhalapo waufulu chotere”.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.