Kodi Uchimo Mumauona Motani?
“MWA inu mulibe uchimo iyayi, simumasoŵa kanthu inu iyayi, ndinu nkhokwe ya mphamvuzonse.” Wafilosofi wotchuka wachihindu Vivekananda, ananena mawu ameneŵa pamene anali kufotokoza nkhani ina m’buku loyera lachihindu, lotchedwa Bhagavad Gita. Potchula mawu a m’Vedanta, iye akuti: “Kunena kuti ndiwe wopanda nzeru, kuti ndiwe wochimwa nkulakwa kwambiri.”a
Komabe, kodi nzoona kuti munthu alibe uchimo? Ndiye ngati zili choncho, nchiyani chimene munthu amabadwa nacho? “Maonekedwe a thupi ndiwo okha omwe timapeza mwa choloŵa,” akutero Nikhilananda, Mhindu wanzeru. Mikhalidwe ina timakhala nayo mwa “zochita [zathu] za pamoyo wakale.” Malinga ndi Vivekananda, “mumakonza nokha mtsogolo mwanu.” Chihindu sichimaphunzitsa chilichonse ponena za uchimo wobadwa nawo.
Azoroastriani, Ashinto, Akonfyushani, ndi Abuda sadziŵanso kuti pali uchimo wobadwa nawo. Ngakhale m’zipembedzo zachiyuda ndi zachikristu, zimene zimaphunzitsa mwa mwambo chiphunzitso cha uchimo wobadwa nawo, maganizo a anthu ponena za uchimo akusintha. Anthu ambiri lerolino samaganiza kuti ali ochimwa.
“Nzeru yamakono simalimbikitsa kutsutsa khalidwe loipa; kwenikweni, simalimbikitsa munthu kudzitsutsa yekha,” akutero katswiri wa zaumulungu Cornelius Plantinga, Jr. Zipembedzo za Dziko Lachikristu zilinso ndi mlandu wopeputsa uchimo. “Ngati mukufuna kumva za uchimo musapite kutchalitchi,” anatero mkulu wachipembedzo pa Yunivesite ya Duke. Ndipo malinga ndi Plantinga, matchalitchi ena amalankhula za uchimo monga nkhani wamba basi.
Ndithudi, lerolino masoka a anthu ngambiri. Chiwawa, upandu, nkhondo, mafuko kumalimbana, kumwa anamgoneka, kusaona mtima, kutsendereza, ndi chiwawa kwa ana nzofala. Tingoti zaka za zana la 20 zino zatchedwa kuti zaka za nkhanza yosaneneka imene anthu sanaonepo. Ndiye onjezanipo kupweteka ndi kuvutika chifukwa cha matenda, ukalamba ndi imfa. Kodi ndani amene samakhumba kumasuka pa mavuto aakulu omwe ali padziko lapansi lerolino?
Kodi nanga uchimo mumauona motani? Kodi uchimo timabadwa nawo? Kodi tsiku lina tidzamasuka pazopweteka ndi mavuto? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
a Filosofi ya Vedanta ikupezeka mu Upanishads, imene ili kumapeto kwa malemba achihindu otchedwa Vedas.