Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 8/1 tsamba 7
  • Anapeza “Ngale Yamtengo Wapatali”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anapeza “Ngale Yamtengo Wapatali”
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kudya Mtedza wa Betel Kuli ndi Mavuto Otani?
    Galamukani!—2012
  • Anapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”
    Baibulo Limasintha Anthu
  • ‘Kupeza Ngale Imodzi ya Mtengo Wapatali’
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kufunafuna ‘Ngale ya Mtengo Wapatali’ Lerolino
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 8/1 tsamba 7

Olengeza Ufumu Akusimba

Anapeza “Ngale Yamtengo Wapatali”

“UFUMU wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo mmene anaipeza ngale imodzi yamtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” Mwa mawu ameneŵa, Yesu anafanizira kufunika kwa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 13:45, 46) Aja amene amazindikira kufunika kwa Ufumuwo kaŵirikaŵiri amadzimana kwambiri zinthu zaumwini kuti aupeze. Chokumana nacho chotsatirachi cha ku Pingtung County, Taiwan, chikusonyeza zimenezo.

Mu 1991, Bambo ndi Mayi Lin anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pamene mkulu wachipembedzo cha kwawoko anadziŵa zimenezo, anayesa kuwakopera kutchalitchi chake. Popeza a Lin ndi akazi awo anali ndi bizinesi yogulitsa mwazi wa nkhumba ndi wa abakha pamsika wa kwawoko, anaganiza kumfunsa mkulu wachipembedzoyo za nkhaniyo. “Chilichonse chimene Mulungu anapanga chingakhale chakudya cha munthu,” anayankha choncho. Koma Mbonizo, zinawalimbikitsa kumva zimene Mawu a Mulungu anganene. Anaphunzira kuti Yehova Mulungu amaona mwazi kukhala wopatulika, pakuti “moyo wa nyama ndiwo mwazi wake.” (Levitiko 17:10, 11, The New English Bible) Chotero Akristu oona ayenera ‘kusala . . . mwazi.’ (Machitidwe 15:20) Atapenda zimene Malemba amanena pankhaniyi, a Lin ndi akazi awo anasankha kuleka kugulitsa mwazi, ngakhale kuti anali kupeza nawo ndalama zochuluka. Komabe, pasanapite nthaŵi, anakumana ndi chiyeso china chachikulu.

Asanaphunzire choonadi, a Lin ndi akazi awo anabzala mitengo 1,300 ya betel nut pakhomo pawo. Ngakhale kuti pakanapita zaka zisanu mitengoyo isanawapindulitse, koma itangoti yabala, a Lin ndi akazi awo akanayembekeza kupezapo $77,000 pachaka. Pamene nthaŵi ya kututa koyamba inayandikira, a Lin ndi akazi awo anali ndi nkhani yaikulu yofuna kugamula. Anadziŵa kupyolera m’phunziro lawo la Baibulo kuti Akristu ayenera kudziyeretsa “kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu” mwa kupeŵa kugwiritsira ntchito, kapena kuchirikiza, zizoloŵezi zodetsa zonga kusuta fodya, anamgoneka, ndi kutafuna betel nut. (2 Akorinto 7:1) Kodi akanatani?

Bambo Lin analeka kuphunzira Baibulo chifukwa chikumbumtima chawo chinayamba kuwavuta. Panthaŵi imodzimodziyo, Mayi Lin anagulitsa ma betel nut awo omwe anatchera m’mitengo yawo ina yakale ndipo anapindula nawo ndalama zoposa $3,000. Zimenezo zinangowasonyeza chabe kuti ataisamala mitengo yawoyo posachedwapa adzapezanso ndalama zambiri. Komabe, chikumbumtima cha Bambo Lin chinali kungowavutabe.

Analimbana nayo nkhaniyo mpaka tsiku lina anapempha Mboni za kwawoko kuti ziwadulire mitengo ya betel imeneyo. Mbonizo zinawafotokozera kuti ndiwo anayenera kusankha chochita; chotero, anayenera ‘kusenza katundu wawo wa iwo eni’ ndi kudula mitengoyo okha. (Agalatiya 6:4, 5) Anawalimbikitsa kukumbukira lonjezo lili pa 1 Akorinto 10:13, lakuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” Mbonizo zinawauzanso kuti: “Ngati ifeyo takudulirani mitengo yanu, mungadzadandaule ndi kutiimba mlandu.” Patangopita kanthaŵi pang’ono, Mayi Lin podzuka mmaŵa anamva phokoso lamacheka. Anali amuna awo ndi ana akumadula mitengo ya betel ija!

Bambo Lin anaona kuti Yehova amalonjeza zoona. Anapeza ntchito imene inawasiya ali ndi chikumbumtima chabwino, imene inawathandiza kukhala wotamanda Yehova. Anabatizidwa pamsonkhano wadera wa Mboni za Yehova mu April 1996.

Inde, Bambo Lin ‘anagulitsa zonse anali nazo’ ndi kugula “ngale yamtengo wapatali.” Tsopano ali ndi mwaŵi wosayerekezereka wakukhala paunansi ndi Yehova Mulungu ndi kugwira nawo ntchito ya Ufumu Wake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena