Kutumikira Limodzi ndi Gulu la Yehova Mokhulupirika
“Kwa munthu wokhulupirika, inunso mudzakhala wokhulupirika.”—2 SAMUELI 22:26, NW.
1, 2. Kodi nzitsanzo zina zotani za kukhulupirika zomwe ife tonse timaona mumpingo?
USIKU wina, mkulu akukonzekera nkhani yoti akakambe kumsonkhano wachikristu. Iye angakonde kusiya kuti apume; komabe, alimbikira, akumafunafuna zitsanzo za m’Malemba ndi mafanizo omwe adzafika nkhosa pamtima ndi kuzilimbikitsa. Tsiku la msonkhano uja ndi lero usiku, makolo aŵiri otopa a mumpingo umodzimodziwo angakonde kungokhala panyumba madzulo; komabe, moleza mtima akukonzekeretsa ana awo napita kumsonkhano. Msonkhano watha tsopano, ndipo Akristu angapo akukambitsirana za nkhani ya mkulu uja. Mlongo wina akufuna kutchula kuti mbale mmodzimodziyo anamkhumudwitsa; komabe, alankhula mokondwa za mfundo ina imene mbaleyo anatchula. Kodi mukuuona mzimu umene zochitika zonsezi zikusonyeza?
2 Mzimu umenewo ndiwo kukhulupirika. Mkuluyo amagwira ntchito mokhulupirika kuti atumikire nkhosa za Mulungu; makolowo amapezeka pamisonkhano mokhulupirika; mlongoyo amachirikiza akulu mokhulupirika. (Ahebri 10:24, 25; 13:17; 1 Petro 5:2) Inde, pambali zonse za moyo, timaona kuti anthu a Mulungu ali otsimikiza kutumikira limodzi ndi gulu la Yehova mokhulupirika.
3. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kukhalabe okhulupirika ku gulu la Yehova la padziko lapansi?
3 Pamene Yehova ayang’ana dziko loipali, amaona anthu okhulupirika ochepa kwambiri. (Mika 7:2, NW) Ayenera kuti amakondwera chotani pamene aona kukhulupirika kwa anthu ake! Inde, kukhulupirika kwanu kumamkondweretsa. Komabe, kumakwiyitsa Satana, mpandu woyamba, ndipo kumamtsimikiza kuti ngwabodza. (Miyambo 27:11; Yohane 8:44) Dziŵani kuti Satana adzayesa kufooketsa kukhulupirika kwanu kwa Yehova ndi gulu Lake la padziko lapansi. Tiyeni tipende njira zina zomwe Satana amachitira zimenezo. Tikatero tidzaona bwino mmene tingakhalire okhulupirika mpaka mapeto.—2 Akorinto 2:11.
Kuyang’ana pa Zolakwa za Ena Kungawononge Kukhulupirika
4. (a) Kodi nchifukwa ninji kukayikira amene ali ndi ulamuliro nkwapafupi? (b) Kodi Kora anakhala bwanji wosakhulupirika ku gulu la Yehova?
4 Pamene mbale ali ndi udindo, zophophonya zake zingaonekere kwambiri. Nkwapafupi chotani nanga kuona ‘kachitsotso kali m’diso la mbale wathu, koma nkulephera kuona mtanda uli m’diso lathu’! (Mateyu 7:1-5) Komano, kumangoganizira zophophonya kungayambitse kusakhulupirika. Tinene mwachitsanzo, talingalirani za kusiyana kwa Kora ndi Davide. Kora anali ndi udindo waukulu, ndipo mwina anali wokhulupirika zaka zambiri, koma anaona ngati udindo wake wachepa. Anaipidwa ndi ulamuliro umene Mose ndi Aroni, achibale ake, anali nawo. Ngakhale kuti Mose anali wofatsa kwambiri pa anthu onse, Kora mwachionekere anayamba kumamkayikira. Angakhale ataona zophophonya za Mose. Komabe, zophophonya zimenezo sizinatanthauze kuti kusakhulupirika kwa Kora ku gulu la Yehova kunali bwino. Anawonongedwa kumchotsa pakati pa mpingowo.—Numeri 12:3; 16:11, 31-33.
5. Kodi nchifukwa ninji Davide akanaganizira zopandukira Sauli?
5 Davide analinso mtumiki wa Mfumu Sauli. Ngakhale kuti kale Sauli anali mfumu yabwino, iye anali ataipa. Davide anafunikira chikhulupiriro, chipiriro, ngakhale kuchenjera ndithu kuti apulumuke kuukira kwa Sauli wansanje. Komabe, pamene mpata unapezeka wakuti Davide abwezere, iye anati ‘Yehova amletsa’ kuchita chinthu chosakhulupirika kwa wodzozedwa wa Yehova.—1 Samueli 26:11.
6. Ngakhale ngati taona zofooka ndi zophophonya mwa akulu, kodi sitiyenera kuchitanji?
6 Pamene ena amene akutitsogolera achita zinthu mosaganiza bwino, kulankhula mwaukali, kapena aoneka ngati akukondera, kodi tidzayamba kumadandaula, mwina kuyambitsa mzimu wosuliza mumpingo? Kodi tidzasiya kupita kumisonkhano yachikristu kusonyeza kusakondwa kwathu? Ayi! Monga Davide, sitidzalola zophophonya za wina kutitayitsa kukhulupirika kwathu kwa Yehova ndi gulu lake!—Salmo 119:165.
7. Kodi ndi machitachita ati ena oipa omwe anali kuchitika pakachisi m’Yerusalemu, ndipo Yesu anamva motani ataona zimenezo?
7 Munthu amene anapereka chitsanzo chabwino koposa cha kukhulupirika ndi Yesu Kristu, amene ulosi unafotokoza kuti anali “wokondedwa [“wokhulupirika,” NW]” wa Yehova. (Salmo 16:10) Popeza kachisi m’Yerusalemu amamgwiritsira ntchito moipa pantchito isali yake, zingakhale zitawavuta anthu kusonyeza kukhulupirika. Yesu anadziŵa kuti ntchito ya mkulu wa ansembe ndi nsembe zomwe zinaphiphiritsa utumiki wake ndi imfa yake ya nsembe, ndipo anadziŵanso kuti anthu anafunikadi kuphunzirapo kanthu pa zinthuzo. Choncho anayeneradi kukwiya pamene anaona kuti kachisi wakhala “phanga la achifwamba.” Pokhala ndi ulamuliro wa Mulungu, anamuyeretsa kachisiyo kaŵiri.a—Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:15-17.
8. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani kukhulupirika pa makonzedwe a kachisi? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kulambira Yehova limodzi ndi gulu lake loyera?
8 Ngakhale zinali choncho, Yesu mokhulupirika anachirikiza makonzedwe a pakachisi. Kuyambira ubwana wake, anapita kumapwando pakachisi ndipo nthaŵi zambiri anaphunzitsa ali konko. Analipira ndi msonkho wa pakachisi womwe—ngakhale kuti sanafunikiradi kutero. (Mateyu 17:24-27) Yesu anathokoza mkazi wamasiye wosauka uja chifukwa choponyamo “moyo wake wonse” mosungiramo ndalama pakachisi. Posakhalitsa zitatha zimenezo, Yehova anamkaniratu kachisi uja. Koma zisanachitike zimenezo, Yesu anali wokhulupirikabe pakachisiyo. (Marko 12:41-44; Mateyu 23:38) Gulu la Mulungu la padziko lapansi lero limaposa kutali dongosolo lachiyuda ndi kachisi wake. Inde, silili langwiro ayi; ndiye chifukwa chake nthaŵi zina pamakhala masinthidwe. Komanso silodzala kuipa ayi, ndipo Yehova Mulungu sadzalichotsa nkuikapo lina. Tisalole zolakwa zilizonse zomwe timaona mwa ilo kutikhumudwitsa kapena kutisonkhezera kukhala ndi mzimu wosuliza, wodandaula. M’malo mwake, titsanziretu kukhulupirika kwa Yesu Kristu.—1 Petro 2:21.
Zolakwa Zathu
9, 10. (a) Kodi dongosolo la zinthu la Satana limapezerapo mwaŵi motani pa zolakwa zathu pofuna kutikopa kuti tikhale osakhulupirika? (b) Kodi amene wachita tchimo lalikulu ayenera kutani?
9 Satana amayesanso kutisonkhezera kusakhulupirika mwa kugwiritsira ntchito zolakwa zathu. Dongosolo lake la zinthu limapezerapo mwaŵi pa zofooka zathu, kutiyesa kuchita choipa pamaso pa Yehova. Nzachisoni kuti chaka chilichonse zikwizikwi amagonja pa chisembwere. Ena amawonjezera kusakhulupirika kwawoko mwa kukhala ndi moyo wapaŵiri, akumapitiriza kuchita zoipa koma nkumachita ngati alidi Akristu okhulupirika. Ponena za nkhani yokhudzana ndi mfundoyi mumpambo wakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” m’magazini ya Galamukani!, mtsikana wina analemba kuti: “Nkhanizo zinali kunena za ine.” Mwakabisira, iye anapalana chibwenzi ndi achinyamata osakonda Yehova. Zotsatirapo zake? Akulemba motere: “Moyo wanga unawonongeka, ndipo ndinachita chisembwere ndiyeno nkudzudzulidwa. Unansi wanga ndi Yehova unawonongeka, ndipo makolo anga ndi akulu analeka kundikhulupirira.”b
10 Mtsikana ameneyu anamthandiza akulu ndipo anayambanso kutumikira Yehova mokhulupirika. Komabe, nzachisoni kuti ambiri zinthu zimawaipira kwambiri, ndipo ena sabwerera konse m’khola. Mmene kulili kwabwino nanga kukhalabe okhulupirika ndi kukaniza ziyeso m’dziko loipali! Labadirani machenjezo a m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! onena za nkhani ngati mayanjano akudziko ndi zosangulutsa zoipa. Musachitetu chilichonse chosonyeza kusakhulupirika panthaŵi iliyonse. Koma ngati mwachita, musabise. (Salmo 26:4) M’malo mwake, pemphani thandizo. Nchimene makolo achikristu ndi akulu akhalirapo.—Yakobo 5:14.
11. Kodi nchifukwa ninji kungakhale kulakwa kuganiza kuti ndife oipa kosakonzeka, ndipo nchitsanzo chiti cha m’Baibulo chomwe chingatithandize kuwongola kaganizidwe kathu?
11 Zolakwa zathu zingatiikenso pangozi mwanjira ina. Ena amene amakhala osakhulupirika amaleka kuyesayesa kumkondweretsa Yehova. Kumbukirani kuti Davide anachita machimo aakulu kwambiri. Komabe, zaka zambiri pambuyo pa imfa ya Davide, Yehova anamkumbukira iye monga mtumiki wokhulupirika. (Ahebri 11:32; 12:1) Chifukwa? Chifukwa sanaleke kuyesayesa kukondweretsa Yehova. Miyambo 24:16 imati: “Wolungama amagwa kasanu ndi kaŵiri, nanyamukanso.” Inde, ngati tachitanso machimo aang’ono—inde mobwerezabwereza—chifukwa cha chofooka chomwe tikulimbana nacho, tingakhalebe olungama pamaso pa Yehova ngati tipitiriza ‘kunyamukanso’—kutanthauza, kulapa moona mtima ndi kuyambanso utumiki wokhulupirika.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:7.
Chenjerani ndi Mitundu Yobisika ya Kusakhulupirika!
12. Kodi kaganizidwe kawo Afarisi koumitsa zinthu ndi koumirira malamulo kanawatsogolera bwanji ku kusakhulupirika?
12 Kusakhulupirika kulinso ndi mitundu yake yobisika. Nthaŵi zina kungaoneke ngati kukhulupirika! Mwachitsanzo, Afarisi a m’tsiku la Yesu angakhale atadziyesa okhulupirika kwambiri.c Koma iwo sanathe kuona kusiyana kwa munthu wokhulupirika ndi woumirira malamulo a anthu, pakuti iwo ankakonda kuumitsa zinthu poweruza ndipo anali opanda chifundo. (Yerekezerani ndi Mlaliki 7:16.) Pamenepa iwo kwenikweni sanasonyeze kukhulupirika kwa anthu omwe anayenera kutumikira, pamzimu wa Chilamulo chimene amati anali kuphunzitsa, ndi kwa Yehova mwiniyo. Komabe, Yesu anasonyeza kukhulupirika pamzimu wa Chilamulo, umene unali chikondi. Ndiye chifukwa chake iye anawalimbikitsa anthu, mongadi ananenera maulosi onena za Mesiya.—Yesaya 42:3; 50:4; 61:1, 2.
13. (a) Kodi makolo achikristu angakhale bwanji osakhulupirika? (b) Nchifukwa ninji makolo ayenera kupeŵa nkhanza kwambiri, kusuliza kapena kupeza zifukwa polanga ana awo?
13 Akristu amene ali ndi ulamuliro pang’ono amapindula kwambiri ndi chitsanzo cha Yesu pankhaniyi. Mwachitsanzo, makolo okhulupirika amadziŵa kuti ayenera kulanga ana awo. (Miyambo 13:24) Koma amatsimikiza kuti sakuputa ana awo ndi chilango chankhanza choperekedwa mwaukali kapena kuwasuliza masiku onse. Ana amene amaganiza kuti sangathe kukondweretsa makolo awo kapena oganiza kuti kulambira kwa makolo ndiko kumawachititsa kuwapeza zifukwa ndi kuwasuliza angakhumudwe ndipo, chifukwa cha zimenezo, angatalikirane ndi chikhulupiriro choona.—Akolose 3:21.
14. Kodi ndi motani mmene abusa achikristu angakhalire okhulupirika kwa nkhosa zomwe amatumikira?
14 Momwemonso, akulu achikristu ndi oyang’anira oyendayenda amasamalira mavuto ndi ngozi zomwe nkhosa zimakumana nazo. Monga abusa okhulupirika, amapereka uphungu ngati ukufunika, akumatsimikiza kuti ali ndi maumboni onse choyamba ndipo mosamala amazika zomwe akunena pa Baibulo ndi zofalitsa za Sosaite. (Salmo 119:105; Miyambo 18:13) Amadziŵanso kuti nkhosa zimawadalira kuti azilimbikitse mwauzimu ndi kuzidyetsa. Choncho amayesetsa kutsanzira Yesu Kristu, Mbusa Wabwino. Mokhulupirika amatumikira nkhosa mlungu ndi mlungu pamisonkhano yachikristu—osati kuzilefula koma, m’malo mwake, kuzimangirira ndi kulimbitsa chikhulupiriro chawo.—Mateyu 20:28; Aefeso 4:11, 12; Ahebri 13:20, 21.
15. Kodi ena m’zaka za zana loyamba anasonyeza motani kuti kukhulupirika kwawo kunali polakwika?
15 Mtundu wina wobisika wa kusakhulupirika ndiwo kukhulupirika kolakwika. Malinga ndi Baibulo, kukhulupirika kwenikweni sikumatilola kuika kukhulupirika kwathu kwa wina aliyense patsogolo pa kukhulupirika kwathu kwa Yehova Mulungu. Ayuda ambiri m’zaka za zana loyamba anaumirira Chilamulo cha Mose ndi dongosolo la zinthu lachiyuda. Komabe nthaŵi ya Yehova inali itakwana yosamutsa dalitso lake kulichotsa pa mtundu wopandukawo kuliika pa mtundu wa Israyeli wauzimu. Oŵerengeka okha ndiwo anali okhulupirika kwa Yehova ndipo analandira masinthidwe aakuluwo. Ngakhale pakati pa Akristu oona, Ayuda ena Osunga Mwambo analimbikira kunena kuti abwerere kutsata “miyambo yofooka ndi yaumphaŵi” ya Chilamulo cha Mose, chimene chinakwaniritsidwa mwa Kristu.—Agalatiya 4:9; 5:6-12; Afilipi 3:2, 3.
16. Kodi atumiki okhulupirika a Yehova amatani pakakhala masinthidwe?
16 Kusiyana ndi amenewo, anthu a Yehova masiku ano asonyeza kukhulupirika kwawo panthaŵi imene zinthu zasintha. Pamene kuunika kwa choonadi chovumbulidwa kumka nikumaŵaliraŵalira, pamakhala masinthidwe. (Miyambo 4:18) Posachedwapa, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watithandiza kuwongolera kamvedwe kathu pa liwu lakuti “mbadwo” lopezeka pa Mateyu 24:34 ndi za nthaŵi yoweruza “nkhosa” ndi “mbuzi” zotchulidwa pa Mateyu 25:31-46, ndiponso ponena za ntchito zina za utumiki wa m’boma. (Mateyu 24:45) Mosakayikira ampatuko ena akanakondwa ngati ambiri mwa Mboni za Yehova akanaumirira kamvedwe kakale pa nkhani zonga zimenezo ndi kukana kupita patsogolo. Komatu zoterozo sizinachitike ayi. Chifukwa? Anthu a Yehova ngokhulupirika.
17. Kodi okondedwa athu nthaŵi zina angayese motani kukhulupirika kwathu?
17 Komabe, nkhani yosonyeza kukhulupirika kolakwika ingatikhudze ife eni. Pamene bwenzi lathu la pamtima kapena ngakhale wapabanja lathu wachita chinthu chimene chimaswa mapulinsipulo a Baibulo, tingaone ngati kuti kukhulupirika kwathu kwagaŵikana. Mwachibadwa, timakhala okhulupirika kwa apabanja lathu. Komatu tisaike konse kukhulupirika kwathu kwa iwo patsogolo pa kukhulupirika kwathu kwa Yehova! (Yerekezerani ndi 1 Samueli 23:16-18.) Olakwa sitingawathandize kubisa tchimo lawo lalikulu kapena kuthandizana nawo kutsutsa akulu amene akuyesa ‘kuwabweza mu mzimu wa chifatso.’ (Agalatiya 6:1) Kuteroko kungakhale kusakhulupirika kwa Yehova, gulu lake, ndi kwa wokondedwayo. Ndipotu, kuchinjiriza wochimwa kuti asalandire chilango chomwe akufunika ndiko kutsekereza chikondi cha Yehova kuti chisamfike. (Ahebri 12:5-7) Kumbukiraninso kuti “kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika.” (Miyambo 27:6) Uphungu wachikondi wosapita m’mbali wozikidwa pa Mawu a Mulungu ungalase mtima wa wokondedwa wathu wochimwa, koma ungadzapulumutse moyo wake mtsogolo!
Kukhulupirika Kumapirira Chizunzo
18, 19. (a) Kodi Ahabu anafunanji kwa Naboti, nanga nchifukwa ninji Nabotiyo anakana? (b) Kodi zimene zinachitikira Naboti chifukwa cha kukhulupirika kwake zinayeneradi kumchitikira? Fotokozani.
18 Satana nthaŵi zina amaukira mwachindunji kukhulupirika kwathu. Talingalirani za Naboti. Pamene Mfumu Ahabu inamuumiriza kuti aigulitse munda wake wa mpesa, iye anati: “Pali Yehova, ndi pang’ono ponse ayi, kuti ndikupatseni choloŵa cha makolo anga.” (1 Mafumu 21:3) Naboti sanali wouma mutu ayi; anali wokhulupirika. Chilamulo cha Mose chinalamula kuti Mwisrayeli aliyense asagulitse dziko chigulitsire. (Levitiko 25:23-28) Mosakayikira Naboti anadziŵa kuti mfumu yankhalwe imeneyo ingamuphe, pakuti Ahabu anali atalola kale mkazi wake, Yezebeli, kupha aneneri ambiri a Yehova! Koma Naboti analimbabe.—1 Mafumu 18:4.
19 Nthaŵi zina kukhulupirika kumakhala ndi zotsatirapo zake. Yezebeli, mothandizidwa ndi “anthu oipa,” anamsemera mlandu Naboti umene sanachite. Choncho iyeyo ndi ana ake anaphedwa. (1 Mafumu 21:7-16; 2 Mafumu 9:26) Kodi zimenezo zikutanthauza kuti kukhulupirika kwa Naboti kunali kolakwika? Ayi! Naboti ali mmodzi wa amuna ndi akazi ambiri okhulupirika amene ali “amoyo” m’chikumbukiro cha Yehova tsopano, ndi omwenso ali m’tulo ta phe m’manda mpaka nthaŵi ya chiukiriro.—Luka 20:38; Machitidwe 24:15.
20. Kodi chiyembekezo chingatithandize motani kukhalabe okhulupirika?
20 Lonjezo limodzimodzilo limawalimbikitsa okhulupirika a Yehova lerolino. Tikudziŵa kuti kukhulupirika kwathu kungatitayitse zinthu zazikulu ndithu m’dziko lino. Yesu Kristu anataya moyo wake chifukwa cha kukhulupirika kwake, ndipo anauza otsatira ake kuti nawonso zidzawakhalira chimodzimodzi. (Yohane 15:20) Monga momwe chiyembekezo chake chamtsogolo chinamlimbitsira, nafenso chathu chimatilimbitsa. (Ahebri 12:2) Choncho tingakhalebe okhulupirika kaya pakhale mazunzo otani.
21. Kodi Yehova amawatsimikiza za chiyani okhulupirika ake?
21 Zoona, ndi oŵerengeka chabe mwa ife amene kukhulupirika kwathu kumayesedwa mwachindunji choncho. Koma mwina anthu a Mulungu angadzakumane ndi zizunzo zambiri mapeto asanadze. Kodi tingatsimikize motani kuti tidzakhalabe okhulupirika? Mwa kukhalabe okhulupirika tsopano. Yehova watipatsa ntchito yaikulu—kulalikira ndi kuphunzitsa ena za Ufumu wake. Tiyeni tiichite ntchito yofunikayi mokhulupirika. (1 Akorinto 15:58) Tikapanda kulola zolakwa zaumunthu kuwononga kukhulupirika kwathu ku gulu la Yehova ndipo ngati tipeŵa mitundu yobisika ya kusakhulupirika monga kukhulupirika kolakwika, ndiye kuti tidzakhala okonzeka bwino ngati kukhulupirika kwathu kungayesedwe kwambiri. Kaya zikhale bwanji, tidziŵe nthaŵi zonse kuti Yehova mosalephera amakhala wokhulupirika kwa atumiki ake okhulupirika. (2 Samueli 22:26, NW) Inde, amasunga okhulupirika ake!—Salmo 97:10, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Yesu analimba mtima poukira eni malonda aphindu amenewo. Malinga ndi wolemba mbiri wina, panali kobiri lakale lachiyuda limene linafunika polipira msonkho wa pakachisi. Chotero alendo ambiri omwe anafika pakachisi anayenera kusintha ndalama zawo kuti alipire msonkho. Osinthitsa ndalama anali ndi ufulu wokhazikitsa mtengo wachikhalire wosinthira ndalama, motero iwo anapindula ndalama zambiri.
b Onani Galamukani! ya December 22, 1993, Chingelezi; January 8, 1994; ndi February 8, 1994.
c Kagulu kawo kanachokera kwa Ahasidi, gulu limene linakhalako zaka mazana ambiri kalelo kutsekereza chisonkhezero cha Agiriki. Ahasidi anatenga dzina lawo ku liwu lachihebri lakuti chasi·dhimʹ, kapena kuti “okhulupirika.” Mwina iwo ankaganiza kuti malemba omwe amatchula “okhulupirika” a Yehova anali kunena makamaka za iwo. (Salmo 50:5, NW) Iwowo, ndi Afarisi omwe anawatsatira, anadziika okha kutetezera zilembo za Chilamulo ndipo kukangalika kwawo kunali konkitsa.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi tingapeŵe motani kukhala osakhulupirika chifukwa cha zolakwa za ena?
◻ Kodi ndi motani mmene zolakwa zathu zingatiloŵetsere m’kusakhulupirika?
◻ Kodi tingalikanize motani lingaliro loika kukhulupirika kwathu polakwika?
◻ Kodi chidzatithandiza nchiyani kukhala okhulupirika ngakhale panthaŵi ya chizunzo?
[Bokosi patsamba 9]
Kutumikira pa Beteli Mokhulupirika
“Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.” Nzimene analemba mtumwi Paulo zimenezo. (1 Akorinto 14:40) Paulo anadziŵa kuti ngati mpingo uti uyende bwino, padzafunikira ‘chilongosoko,’ kulinganiza. Momwemonso lero, akulu amagamula za nkhani zina zofuna kuchitapo kanthu, monga kugaŵira abale malo osiyanasiyana a phunziro la buku, kulinganiza kukumana kwa utumiki wakumunda, ndi kupenda mmene gawo akulifolera. Makonzedwe onga amenewo nthaŵi zina amayesa kukhulupirika kwa munthu. Sali malamulo ouziridwa ndi Mulungu, ndipo si munthu aliyense amene angakonde zimenezo.
Kodi inu nthaŵi zina zimakuvutani kukhala wokhulupirika pamakonzedwe ena otsatirika omwe mpingo wachikristu umakonza? Ngati mumatero, mwina chitsanzo cha Beteli chingakuthandizeni. Dzinalo Beteli, liwu lachihebri lotanthauza “Nyumba ya Mulungu,” ndilo dzina lake la nthambi zonse 104 za Watch Tower Society, kuphatikizapo malikulu ake ku United States.d Antchito odzifunira omwe amakhala ndi kugwira ntchito pa Beteli amafuna kuti malo ameneŵa asonyeze ulemu ndi kuopa Yehova. Zimenezo zimafuna kuti munthu aliyense akhale wokhulupirika.
Alendo ocheza ku Beteli kaŵirikaŵiri amalankhula za dongosolo ndi ukhondo womwe amaona. Antchito ngadongosolo ndi achimwemwe; kalankhulidwe kawo ndi makhalidwe ndipo ngakhale kaonekedwe kawo kamasonyeza kuti ali ndi zikumbumtima zachikristu zokhwima ndiponso zophunzitsidwa Baibulo. Apabanja la Beteli onse amatsatira malamulo a Mawu a Mulungu mokhulupirika.
Ndiponso, Bungwe Lolamulira limawapatsa kabuku kakuti Dwelling Together in Unity, kamene mokoma mtima kamafotokoza makonzedwe otsatirika ofunika kuti banja lalikulu ngati limenelo ligwire ntchito bwino mogwirizana. (Salmo 133:1) Mwachitsanzo, kamafotokoza za zipinda, zakudya, ukhondo, kavalidwe ndi kapesedwe, ndi nkhani zina zokhudzana ndi zimenezo. Apabanja la Beteli amachirikiza ndi kutsatira makonzedwe amenewo mokhulupirika, ngakhale ngati zimene amakonda zingasiyane ndi zimenezo. Iwo samaona monga ngati kuti kabukuko kali mpambo wa malamulo ouma, koma monga mpambo wa zitsogozo zothandiza zimene zinakonzedwa kulimbikitsa umodzi ndi chimvano. Oyang’anira amachirikiza malangizo ozikidwa pa Baibulo ameneŵa mokhulupirika, ndipo amawagwiritsira ntchito bwino kumangirira ndi kulimbikitsa banja la Beteli kuchita utumiki wawo wopatulika wa pa Beteli.
[Mawu a M’munsi]
d Mafakitale, maofesi, ndi nyumba zokhalamo zimenezo sindizo kachisi wamkulu wauzimu wa Mulungu kapena nyumba. Kachisi wauzimu wa Mulungu ndiye makonzedwe ake a kulambira koyera. (Mika 4:1) Choncho, sali nyumba yeniyeni padziko lapansi.
[Bokosi patsamba 10]
Munthu Wokhulupirika ndi Munthu Woumirira Malamulo
Kale mu 1916 Encyclopædia of Religion and Ethics inatchula kuti “kusiyana kumeneku kwa munthu wokhulupirika ndi munthu woumirira malamulo kumakhalapo nthaŵi zonse ndiponso kulikonse.” Inafotokoza kuti: “Pali munthu woumirira malamulo yemwe amachita zimene amuuza, saswa malamulo alionse; amakhulupirira mawu olembedwa. Palinso munthu wokhulupirika yemwe amachitanso zimenezi koma . . . ngwodalirika pazambiri, amene maganizo ake onse amawaika pantchito yake, amene amaumba mzimu wake malinga ndi mzimu wa zimene akufuna kuchita.” Pambuyo pake, buku limodzimodzilo linati: “Kukhulupirika sikungotsata malamulo chabe. . . . Munthu wokhulupirika amasiyana ndi munthu wotsata malamulo pakuti iye amachita zinthu ndi mtima wonse ndi maganizo ake onse . . . Samachimwa dala mwa kuchita cholakwa, mwa kusachita choyenera, kapena chifukwa cha umbuli.”