Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula ndi makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ndiye bwanji osadziyesa kuona ngati mutha kukumbukira mafunso otsatirawa?
◻ Kodi Armagedo idzakhala yotani? (Chivumbulutso 16:14, 16)
Sidzakhala chiwonongeko cha nyukiliya kapena tsoka lina lochititsidwa ndi anthu. Ayi, iyo ndi nkhondo ya Mulungu yothetsa nkhondo zonse za munthu, kuwononga onse ochirikiza nkhondo zimenezi, ndi kudzetsa mtendere weniweni kwa aja amene amakonda mtendere. Siidzazengereza. (Habakuku 2:3)—4/15, tsamba 17.
◻ Kodi ndi ukwati wotani umene umalemekeza Yehova?
Ukwati umene pachuluka zauzimu m’malo mwa njira za dziko umalemekezadi Yehova. Akristu adzakondwa nacho chochitikacho ngati apeŵa miyambo ya dziko ndi zikhulupiriro zake, kuchita zinthu monkitsa; ngati salola ukwati kusokoneza zochita zanthaŵi zonse zateokrase; ndipo ngati asonyeza chifatso m’malo mwa matamandidwe a moyo.—4/15, tsamba 26.
◻ Kodi munthu wokhulupirika amadziŵika bwanji?
Munthu wokhulupirika amakhala wodalirika, osati kwa munthu mnzake chabe, komanso kwa Mulungu makamaka. Kuongoka mtima kwa munthu wotero kumaonekera m’zochita zake. Amakhala wopanda chinyengo. Sali waukathyali kapena wakatangale. (2 Akorinto 4:2)—5/1, tsamba 6.
◻ Kodi nchifukwa ninji Yeremiya anati: “Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono”? (Maliro 3:27)
Kuphunzira kulimbana ndi mavuto ukali wamng’ono kumathandiza kuti udzathe kulimbana ndi mavuto aakulu utakula. (2 Timoteo 3:12) Mapindu a kukhulupirika amaposa mpumulo uliwonse wosakhalitsa womwe kugonja kungabweretse.—5/1, tsamba 32.
◻ Kodi kuonekera kwa Mose ndi Eliya m’masomphenya a kusandulika kwa Yesu kunaphiphiritsa chiyani?
Pakusandulikako, Mose ndi Eliya anaimira abale odzozedwa a Yesu. ‘Kuonekera muulemerero’ kwawoko, limodzi ndi Yesu kunasonyeza kuti Akristu odzozedwa okhulupirika ‘adzalandira ulemerero pamodzi’ ndi Yesu m’makonzedwe a Ufumu wakumwamba. (Luka 9:30, 31; Aroma 8:17; 2 Atesalonika 1:10)—5/15, tsamba 12, 14.
◻ Kodi “chinsinsi chopatulika” cha Mulungu nchiyani? (1 Akorinto 2:7, NW)
“Chinsinsi chopatulika” cha Mulungu chimanena za Yesu Kristu. (Aefeso 1:9, 10, NW) Komabe, sikungodziŵa chabe kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa. Chimaphatikizapo boma lakumwamba, Ufumu Waumesiya wa Mulungu, ndipo chimaphatikizapo udindo umene Yesu apatsidwa kuti achite pachifuno cha Mulungu.—6/1, tsamba 13.
◻ Kodi Mkristu ayenera kuuona motani ukalamba ndi matenda?
M’malo moona ziyeso kuti zikuchepetsa utumiki wake kwa Yehova, ayenera kuziona monga mwaŵi wokulitsira chidaliro chake pa iye. Ayeneranso kukumbukira kuti kufunika kwa Mkristu sikumapimidwa ndi unyinji wa ntchito zake, komanso ndi chikhulupiriro chake ndi ukulu wa chikondi chake. (Marko 12:41-44)—6/1, tsamba 26.
◻ Kodi Yehova anasonyeza motani nzeru yake yaikulu mwa kugwiritsira ntchito anthu kulemba Baibulo m’malo mwa angelo?
Ngati uthenga wa Baibulo ukanapandiratu umunthu, tikanavutika kuumvetsa. Ndiponso, Baibulo limamveka bwino, lili ndi mafotokozedwe amitundumitundu, ndipo limakopa chifukwa linalembedwa ndi anthu.—6/15, tsamba 8.
◻ Kodi chinsinsi cha chimwemwe cha banja nchiyani?
Chinsinsi chake chili m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi m’kugwiritsira ntchito mapulinsipulo ake, monga kudziletsa, kuzindikira umutu, kulankhulana kwabwino, ndi chikondi.—6/15, masamba 23, 24.
◻ Kodi kuchiritsa kwa Yesu kunasiyana bwanji ndi kumene ambiri amachita omwe amati ali ndi mphamvu yochiritsa lerolino?
Anthuwo sanali kutengeka mtima ndipo ngakhale Yesu sanali kuchita kunyanyuka ayi. Ndiponso, Yesu sanalepherepo kuchiritsa wodwala nkumanamizira kuti iwo sanalipire ndalama zokwanira kapena kuti analibe chikhulupiriro.—7/1, tsamba 5.
◻ Kodi Yehova wawathandiza motani anthu ake kukhala ndi malo m’chifuno chake chaumulungu okhudza dzina lake ndi Ufumu?
Choyamba, Yehova wapatsa anthu ake choonadi. Chachiŵiri, anawapatsa mzimu wake woyera. Ndipo chachitatu, tili ndi ubale wathu wa padziko lonse ndi makonzedwe a Yehova olambira monga gulu.—7/1, masamba 19, 20.
◻ Kodi khalidwe labwino nchiyani?
Khalidwe labwino ndilo ukoma, ubwino, machitidwe ndi malingaliro olondola. Si mkhalidwe wosachita kanthu, koma wa zochita zambiri ndi wothandiza. Khalidwe labwino sindilo kungopeŵa uchimo basi; limatanthauza kulondola chabwino. (1 Timoteo 6:11)—7/15, tsamba 14.
◻ Kodi choloŵa chopindulitsa kwambiri chomwe makolo angasiyire ana awo nchiyani?
Choloŵa chopindulitsa kwambiri ndicho chitsanzo chawo cha kusonyeza chikondi kwa ena. Ana, makamaka, afunika kuona ndi kumva makolo awo akulankhula za chikondi chenicheni pa Mulungu mwa zonse zomwe amachita.—7/15, tsamba 21.
◻ Kodi zofunika zina nzotani kuti phunziro la banja likhale logwira mtima?
Phunziro la banja liyenera kuchitika nthaŵi zonse. Muyenera ‘kuwombola nthaŵi’ ya phunzirolo. (Aefeso 5:15-17, NW) Chititsani kuti nyengo yophunzira ikhale yosangalatsa mwa kupangitsa Baibulo kukhala lamoyo. Kuti ana akondwe nalo, ayenera kuona kuti akutengamo mbali.—8/1, masamba 26, 28.