Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w10 12/1 tsamba 30-31
  • Chinsinsi Chimene Ufunika Kuuzako Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chinsinsi Chimene Ufunika Kuuzako Ena
  • Nsanja ya Olonda—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Chinsinsi Chimene Tonsefe Timafuna Titachidziwa
    Phunzitsani Ana Anu
  • Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Chinsinsi Chopatulika Chivumbuluka
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2010
w10 12/1 tsamba 30-31

Phunzitsani Ana Anu

Chinsinsi Chimene Ufunika Kuuzako Ena

KODI munthu wina anayamba wakuuzako nkhani yachinsinsi?​—a Ineyo ndikufuna ndikuuze chinsinsi chinachake. Baibulo limanena kuti chinsinsi chimenechi ndi “chinsinsi chopatulika chimene chakhala chobisika kuyambira nthawi zakale.” (Aroma 16:25) Poyamba, Mulungu yekha ndiye ankadziwa “chinsinsi chopatulika” chimenechi. Tiye tione zimene Mulungu anachita n’cholinga chakuti anthu ambiri adziwe chinsinsi chimenechi.

Choyamba, kodi ukudziwa zimene mawu akuti ‘kupatulika’ amatanthauza?​— Mawu amenewa amatanthauza chinthu choyera, chosadetsedwa kapena chapadera kwambiri. Choncho chinsinsi chimenechi ndi chopatulika chifukwa ndi chochokera kwa Mulungu, amenenso ndi woyera. Kodi ukuganiza kuti ndani ankafuna kudziwa chinsinsi chimenechi?​— Angelo ankafuna atachidziwa chinsinsi chimenechi. Baibulo limati: “M’zinthu zimenezi angelo akulakalaka kusuzumiramo,” kapena kuti kudziwa. Inde, iwo ankafuna kumvetsa chinsinsi choyera chimenechi.​—1 Petulo 1:12.

Yesu atabwera padziko lapansi ananena za chinsinsi chopatulika chimenechi ndipo anayamba kufotokozera anthu tanthauzo lake. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira chinsinsi chopatulika cha ufumu wa Mulungu.” (Maliko 4:11) Kodi waona kuti chinsinsi chopatulika ndi chokhudza chiyani?​— Ndi chokhudza Ufumu wa Mulungu umene Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempha Mulungu kuti ubwere.​—Mateyu 6:9, 10.

Tsopano tiye tikambirane kuti Ufumu wa Mulungu unakhala bwanji chinsinsi “kuyambira nthawi zakale,” kufikira pamene Yesu anabwera padziko lapansi kudzafotokoza tanthauzo lake. Adamu ndi Hava ataphwanya lamulo la Mulungu anathamangitsidwa m’munda wa Edeni. Patapita nthawi, atumiki a Mulungu anaphunzira kuti cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi chidzakwaniritsidwabe. (Genesis 1:26-28; 2:8, 9; Yesaya 45:18) Iwo analemba zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike padziko lapansi Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira.​—Salimo 37:11, 29; Yesaya 11:6-9; 25:8;33:24; 65:21-24.

Tiye tikambirane za Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. Kodi ukudziwa kuti Mulungu anasankha ndani kuti akhale Wolamulira?​— Anasankha Mwana wake Yesu Khristu yemwe ndi “Kalonga Wamtendere.” Baibulo limati: “Paphewa pake padzakhala ulamuliro.” (Yesaya 9:6, 7) Iweyo ndi ine tiyenera ‘kudziwa molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.’ (Akolose 2:2) Tiyenera kudziwa kuti Mulungu anatenga moyo wa mngelo amene anayambirira kumulenga (yemwe ndi Mwana wake wauzimu) n’kuuika m’mimba mwa Mariya. Mwana ameneyo yemwe anali mngelo wamphamvu kwambiri ndi amene Mulungu anamutumiza padziko lapansi kuti adzakhale nsembe n’cholinga chakuti ife tipeze moyo wosatha.​—Mateyu 20:28; Yohane 3:16; 17:3.

Tsopano tadziwa kuti Mulungu anasankha Yesu kukhala Wolamulira Ufumu Wake. Koma palinso zinthu zina zimene tiyenera kudziwa. Mbali ina ya chinsinsi chopatulika chimenechi ndi yakuti palinso amuna ndi akazi amene adzakhale ndi Yesu kumwamba. Anthu amenewa adzalamulira ndi Yesu.​—Aefeso 1:8-12.

Tsopano tiye tione mayina a ena mwa anthu amene adzalamulira ndi Yesu kumwamba. Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti akupita kumwamba kukawakonzera malo. (Yohane 14:2, 3) Tiye tiwerenge malemba otsatirawa kuti tidziwe mayina a ena mwa amuna ndi akazi amene adzalamulire ndi Yesu mu Ufumu wa Atate wake.​—Mateyu 10:2-4; Maliko 15:39-41; Yohane 19:25.

Kwa zaka zambiri sizinkadziwika kuti ndi anthu angati amene adzalamulire kumwamba limodzi ndi Yesu mu Ufumu wake. Koma panopa timadziwa kuti ndi anthu angati. Nanga iweyo, kodi umadziwa kuti alipo angati?​— Baibulo limanena kuti alipo 144,000. Chimenechinso ndi chinsinsi chopatulika.​—Chivumbulutso 14:1, 4.

Kodi sukuvomereza kuti “chinsinsi chopatulika cha ufumu wa Mulungu” ndi chinsinsi chosangalatsa kwambiri, chimene aliyense ayenera kuchidziwa? Ngati ukuvomereza zingakhale bwino kuti tiziphunzira zambiri zokhudza chinsinsi chimenechi n’cholinga chakuti tizifotokozera anthu ambiri kuti nawonso adziwe.

a Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzere muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.

MAFUNSO:

  • Kodi chinsinsi chimene takambirana m’nkhani ino chimatchedwa chinsinsi chotani ndipo n’chifukwa chiyani?

  • Kodi chinsinsi chimenechi ndi chonena za chiyani ndipo ndani anayamba kuphunzitsa anthu za chinsinsi chimenechi?

  • Tchula zina mwa zinthu zokhudza chinsinsi chimenechi zimene waphunzira.

  • Kodi ungamufotokozere bwanji mnzako mfundo zokhudza chinsinsi chopatulika?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena