Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 1/15 tsamba 10-15
  • Chinsinsi Chopatulika Chivumbuluka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chinsinsi Chopatulika Chivumbuluka
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumasula Chinsinsicho
  • Mbali Zisanu ndi Imodzi
  • “Anawonekera M’thupi”
  • Mbali Zina
  • Kuphunzira Chinsinsi Chopatulika cha Kudzipereka Kwaumulungu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chinsinsi Chimene Ufunika Kuuzako Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu”
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Tsatirani Chitsanzo cha Yesu cha Kudzipereka Kwaumulungu
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 1/15 tsamba 10-15

Chinsinsi Chopatulika Chivumbuluka

“Chinsinsi Chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu nchachikuludi.”​—1 TIMOTEO 3:16, “NW.”

1. Kodi ndi chinsinsi chotani chimene chalongosoledwa pa 1 Timoteo 3:16?

KODI zinsinsi zimakukondweretsani? Kodi mumasangalala kufufuza m’zinsinsi? Ambiri a ife timatero! Chotero, gwirizanani nafe, pamene tikufufuza chimodzi cha zinsinsi zokulira kuposa zonse​—chinsinsi chomwe chakhala chotsekeredwa m’Mawu a Mulungu kwa zaka zikwizikwi. Chinsinsi chopatulika chimenechi mofunikira chimayambukira miyoyo yathu, ponse paŵiri nthaŵi ino ndi mtsogolo. Chiri ‘chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu,’ cholongosoledwa kaamba ka ife pa 1 Timoteo 3:16. (NW) Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kwa Yehova, “Wakuvumbulutsa zinsinsi,” pakutidziŵitsa ife mwachisomo chinsinsi chokulira chimenechi ndi kumasulira kwake!​—Danieli 2:28, 29.

2. (a) Kodi ndi liti pamene Yehova analankhula choyamba za chinsinsi chopatulika, ndipo kodi nchiyani chimene analonjeza panthaŵiyo? (b) Kodi ndi mafunso otani amene afunikira mayankho?

2 Yehova choyamba analankhula za chinsinsi chopatulika pambuyo pakunyengedwa kwa Hava ndi Njoka, ndipo Adamu atatsatira mkaziyo m’kupandukako. Mulungu pamenepo analonjeza kuti “mbewu,” kapena mbadwa, ikatswanya mutu wa Njokayo. (Genesis 3:15) Kodi ndani yemwe ali Mbewu imeneyi? Kodi ndimotani mmene akagonjetsera Njokayo? Kodi iye akalemekeza kuwona kwa Mulungu ndi chifuno Chake kulinga ku dziko lapansi lino?

3. Kodi maulosi aumulungu amapereka mfungulo zotani ponena za kuzindikiritsidwa ndi ntchito za Mbewuyo?

3 M’kupita kwa nthaŵi, maulosi aumulungu anavumbula mfungulo zonena za kuzindikiritsidwa ndi zochita za mtsogolo za Mbewuyo. Iye akakhala mbadwa ya Abrahamu, akaloŵa ufumu wa Davide, ndipo akatchedwa Kalonga wa Mtendere. ‘Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.’ (Yesaya 9:6, 7; Genesis 22:15-18; Salmo 89:35-37) Koma monga mmene Aroma 16:25 ikunenera, chinsinsi chopatulika chimenecho “chinabisika mwa nthaŵi zonse zosayamba.”

Kumasula Chinsinsicho

4. Kodi ndimotani mmene chinsinsi chopatulika chinayambira kuvumbuluka mu 29 C.E.?

4 Potsirizira pake, pambuyo pa zaka zikwi zinayi, kuwunikira kunawonekera! Mwanjira yotani? Mu 29 C.E., Yohane anabatiza Yesu wa ku Nazarete mu Mtsinje wa Yordano, ndipo kuchokera kumwamba liwu la Mulungu linalengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa, yemwe ndavomereza.” (Mateyu 3:17, NW) Aha, pano potsirizira panapezeka Mbewu yolonjezedwayo! Chinsinsi chopatulika chinali chitayamba kumasulidwa m’mbali zake zonse zaulemerero, kuphatikizapo nkhani ya kudzipereka kwaumulungu.

5. Kodi “kudzipereka kwaumulungu” nchiyani, ndipo kodi ndimotani mmene kumayambukira awo okuchita?

5 Kodi nchiyani chimene tikumvetsetsa mwa mawu akuti “kudzipereka kwaumulungu”? M’malemba Achikristu Achigriki, (NW) mawuwo amapezeka kokha nthaŵi 20, oposa theka la amenewa ali m’makalata aŵiri a Paulo kwa Timoteo. Bukhu la Insight on the Scriptures limamasulira “kudzipereka kwaumulungu” kukhala “ulemu, kulambira, ndi utumiki kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro ku ulamuliro wake wa chilengedwe chaponseponse.” Ulemu umachokera mumtima womwe umayandikira kwa Mulungu, m’kuwopa ukulu wake, umuyaya wake, ndi kuchulukira kwa zolengedwa zake zazikulu, limodzinso ndi kuyamikira kaamba ka mphatso zauzimu ndi zakuthupi zomwe iye amapereka pa anthu oyamikira. Zowonadi, aliyense wa ife amene amachita kudzipereka kwaumulungu anganene, monga mmene anachitira wamasalmo pa Salmo 104:1 kuti: “Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu; muvala ulemu ndi chifumu.”

6. (a) Kodi ndimotani mmene alambiri a Yehova amasiyanira ndi okhala m’malo aulemu a Dziko la Chikristu? (b) Kodi nchiyani chimene Paulo ananena pa Aroma 11:33, 34, ndipo kodi ndi mafunso otani amene akudzutsidwa?

6 Kudzipereka kwathu kwa Mulungu kuyenera kuwonekera, ndipo kumatero kupyolera m’machitidwe. Pa mfundo imeneyi, alambiri a Mulungu wowona, Yehova, ali osiyana mokulira ndi okhala m’malo aulemu a m’matchalitchi omazimiririka a Dziko Lachikristu. Kwa anthu ambiri pa dziko lapansi, chipembedzo​—ngati iwo adakali ndi chipembedzo​—chiri chovala, chophimba chimene amavala kuwapangitsa kuwoneka oyera pamene akukhala ndi moyo womwe umagwirizana ndi dziko loipitsidwa lowazungulira. Iwo samadziŵa nkomwe amene Mulungu ali. Motsimikizirika, anthu oterowo afunikira kulabadira mawu a Paulo pa Machitidwe 17:23, pamene iye ananena kwa Atene omwe analemekeza “Mulungu wosadziŵika” akuti: “Chimene muchipembedza osachidziŵa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.” Ponena za Mulungu wamkulu ameneyo, Paulo akufuula pa Aroma 11:33, 34 kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti anadziŵitsa ndani mtima wake wa [Yehova, NW]! Kapena anakhala mphungu wake ndani?” Pamenepa, kodi ndimotani mmene timadziŵira njira za Mulungu? Chiri kupyolera m’kuphunzira ‘chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu.’ Koma kodi ndimotani mmene timachitira chimenecho?

7. Kodi nchifukwa ninji chinganenedwe kuti “chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kumeneku movomerezeka nchachikuludi”?

7 Pa 1 Timoteo mutu 3, mtumwi Paulo choyamba akundandalitsa zofunikira kwa atumiki okhala ndi mathayo m’nyumba ya Mulungu, yolongosoledwa m’vesi 15 kukhala “mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi m’chirikizo wa chowonadi.” Kenaka Paulo akuwonjezera, mu vesi 16 (NW) kuti: “Chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu nchachikuludi.” Chachikuludi chifukwa chakuti Yehova anatumiza ku dziko lapansi Mwana wake wobadwa yekha kudzamasula chinsinsi chimenechi, kusonyeza chimene kudzipereka kwaumulungu m’chenicheni kuli ndi mmene kuliri kofunika, maziko, m’kulambira kowona. Chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kumeneku chikuwunikiridwa m’njira ya moyo ya Yesu pano pa dziko lapansi. Onse okonda Yehova ayenera kumanga chikhulupiriro ndi miyoyo yawo pa Kristu, yemwe anapereka chitsanzo cha kudzipereka kwaumulungu. Pamenepa, kodi ndimotani mmene Yesu anamveketsera chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu?

Mbali Zisanu ndi Imodzi

8. (a) Kodi ndi ziti zimene ziri mbali zisanu ndi imodzi za chinsinsi chopatulika zimene Paulo akulongosola pa 1 Timoteo 3:16? (b) Kodi ndani yemwe ali “Iye” amene anawonekera?

8 Mwa kuwuziridwa kwaumulungu, Paulo akuyankha funso limenelo. Pano pa 1 Timoteo 3:16, iye akulongosola mbali zisanu ndi imodzi za chinsinsi chopatulika chimenechi, akumanena kuti: “Iye [1] amene anawonekera m’thupi, [2] anayesedwa wolungama mumzimu, [3] anapenyeka ndi angelo, [4] analalikidwa mwa amitundu, [5] anakhulupiridwa m’dziko lapansi, [6] analandiridwa mu ulemerero.” Ndani “Iye” ameneyu yemwe anawonekera? Motsimikizirika, “Iye” ali Mbewu yolonjezedwa, Yesu, yemwe anabwera kudzachita chifuniro cha Mulungu. Iye ali maziko a chinsinsi chopatulika, kuchipangitsa icho kukhala chachikulu mowonadi.

9. Kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene chiripo chosonyeza kuti 1 Timoteo 3:16 siiyenera kuŵerenga kuti: “Mulungu anawonekera m’thupi”?

9 Okhulupirira Utatu amayesera kuphimba kumveketsedwa kwa chinsinsi chopatulikacho mwa kunena kuti “Iye” wa pa 1 Timoteo 3:16 ali Mulungu iyemwini. Iwo amazika nsonga imeneyi pa Baibulo la King James, limene limaŵerenga kuti,“Mulungu anawonekera m’thupi.” Komabe, kodi nchiyani chomwe mamanusikripiti ambiri odalirika Achigriki amanena? Mosasintha, iwo amagwiritsira ntchito m’neni “Iye” m’malo mwa “Mulungu.” Osuliza malemba atsopano amavomereza kuti kuikapo “Mulungu” pa lemba limeneli kuli kuphophonya kwa alembi. Chotero, matembenuzidwe amakono kwenikweni, onga ngati American Standard Version, The New English Bible, ndi New World Translation, amaŵerenga molondola kuti: ‘Iye [kapena, Iye amene] anawonekera m’thupi.’ Ayi, sanali Mulungu iyemwini yemwe anawonekera “m’thupi.” M’malomwake, anali Mwana wake wokondedwa ndi cholengedwe choyamba, za amene mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndipo Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.”​—Yohane 1:14.

“Anawonekera M’thupi”

10. (a) Kodi ndimotani mmene mbali yoyambirira ya chinsinsi chopatulika inawonekera pa ubatizo wa Yesu? (b) Kodi nchifukwa ninji Yesu anakhala “Adamu wotsiriza”?

10 Pa ubatizo wa Yesu mbali yoyambirira ya chinsinsi chopatulika inakhala yowonekera: Yesu “anawonekera m’thupi” monga Mwana wodzozedwa wa Mulungu. Yehova Mulungu anali adasamutsa moyo wa Mwana wake kuchokera kumwamba kupita m’mimba mwa Mariya kotero kuti Yesu akabadwe m’thupi monga munthu wangwiro. Chotero, monga mmene 1 Akorinto 15:45-47 ikusonyezera, Yesu anakhala Adamu wachiŵiri, kapena “wotsiriza,” moyo wangwiro waumunthu wolingana ndendende ndi Adamu woyambirira. Kaamba ka chifuno chotani? Timoteo woyamba 2:5, 6 akulozera kwa “Adamu wotsiriza” kukhala “munthu, Kristu Yesu, amene anadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse.” Pa maziko alamulo amenewa a nsembe yaumunthu yangwiro, Yesu akukhala nkhoswe ya pangano latsopano kulinga kwa a 144,000 aumunthu omwe akukhala oloŵa nyumba ndi iye mu Ufumu wake.​—Chibvumbulutso 14:1-3.

11. Kodi ndi kwandani kumene mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu akufutukukira?

11 Kodi ena nawonso akapindula kuchokera ku imfa yansembe ya Yesu? Motsimikizira inde! Yohane woyamba 2:2 amalongosola kuti Yesu Kristu “ndiye chiwombolo cha machimo athu [uko ndiko kuti, machimo a Akristu odzozedwa onga Yohane]; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” Chotero mapindu a dipo la Yesu amafutukuka kupyola pa Akristu odzozedwa a 144,000 kupita ku dziko lonse la mtundu wa anthu. “Khamu lalikulu” omwe tsopano ali amoyo ndi zikwi za mamiliyoni omwe adzawukitsidwa m’dziko lapansi la Paradaiso adzalandira moyo wosatha pa maziko a chikhulupiriro chawo mu nsembe ya dipo ya Yesu. Monga momwe zaloseredwera kale pa Chibvumbulutso 7:9, 10, khamu lalikulu lachapa zovala zawo naziyeretsa mwa kusonyeza chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Mwanawankhosa, Yesu Kristu. Iwo akupezedwa olungama kulinga ku ubwenzi ndi Mulungu. Ndi chisangalalo, iwo amaphunzira mbali zosiyanasiyana za chinsinsi chopatulika ndi kusonyeza kudzipereka kwaumulungu m’chigwirizano ndi chitsanzo cha Yesu!

Mbali Zina

12. Kodi ndimotani mmene Yesu “analengezedwa wolungama mumzimu”?

12 Bwanji, tsopano, ponena za mbali yachiŵiri pa 1 Timoteo 3:16? Yesu “anayesedwa wolungama mumzimu.” Koma motani? Mwa kuwukitsa kwa Yehova Mwana wake wosunga umphumphu kuchokera kwa akufa kukhala moyo wauzimu. Izi zinachititsa Mulungu kulengeza kuti Yesu anali ponse paŵiri wolungama ndi woyenerera ntchito zokwezeka mowonjezereka. Monga mmene Aroma 1:4 ikuchiikira icho, Yesu “[analengezedwa kukhala, NW] Mwana wa Mulungu monga mwa mzimu wa chiyero ndi kuwuka kwa akufa.” Kutsimikizira ichi, Petro akutiuza ife m’kalata yake yoyamba, mutu 3, vesi 18 kuti: “Kristunso [adafa kamodzi kwatha, NW], chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mu mzimu.” Kodi chitsanzo cha Yesu cha kudzipereka kwaumulungu chikukutsogozani inu kwa Mulungu?

13. Kodi Yesu wowukitsidwayo anawonekera kwa angero ati, ndipo kodi ndi mtundu wotani wa uthenga umene iye anaulalikira kwa iwo?

13 Kupitiriza ndi 1 Timoteo 3:16, Paulo chotsatira akulozera ku mbali yachitatu ya chinsinsi chopatulika, akumanena kuti Yesu “anapenyeka ndi angelo.” Kodi ndani omwe angakhale angelo amenewa? Ponena za Yesu, tsopano “wopangidwa wamoyo mu mzimu,” Petro akulemba pa 1 Petro 3:19, 20 kuti: “M’menenso anapita, nalalikira mizimu inali m’ndende, imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa.” Mogwirizana ndi Yuda 6, mizimu imeneyo inali “angelonso amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pawopawo” kumwamba. Iwo anavala matupi aumunthu ndi cholinga chofuna kusangalala ndi unansi wa kugonana kopanda lamulo ndi akazi. Pamene Chigumula chinakakamiza angelowo kubwerera ku malo a mizimu, iwo anaponyedwa m’Maenje Amdima, mkhalidwe wa m’malo otsika kotheratu. (2 Petro 2:4) Yesu wowukitsidwayo analalikira kwa iwo. Koma kodi umenewo unali uthenga wa chipulumutso? Ndithudi ayi! M’malomwake, Yesu anatsutsa kuipa kwawo kukhala kusemphana kwenikweni kwa kudzipereka kwaumulungu. Aliyense wa anthu a Mulungu omwe akuseŵera ndi chisembwere cha kugonana lerolino ayenera kutenga chenjezo kuchokera ku chiweruzo cholengezedwa pa angelo amenewo!

14. Kodi zinali motani kuti Yesu anayamba “kulalikidwa mwa amitundu”?

14 Mbali yachinayi ya 1 Timoteo 3:16 ndiyakuti Yesu “analalikidwa mwa amitundu.” Kodi ndimotani mmene ichi chakwaniritsidwira? Atakhala pang’ono kugwidwa, Yesu anawuza atumwi kuti: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, wokhulupirira ine, ntchito zimene ndichita ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita ine kwa Atate.” (Yohane 14:12) Mwamsanga pambuyo pake, pa Pentekoste wa 33 C.E., Yesu anatsanulira mzimu woyera pa ophunzira ake, ndipo mbiri yozizwitsa yakuti “Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa” inayamba kulalikidwa kwa Ayuda. Pambuyo pake, Asamariya nawonso analandira mawu a Mulungu ndi kuyamba kulandira mzimu woyera. (Machitidwe 2:32; 8:14-17) Kenaka, mu 36 C.E., Petro analalikira kwa Korneliyo ndi Akunja ena osonkhana m’nyumba yake. Chotero, mbiri yabwino yonena za Yesu inayamba “kulalikidwa pakati pa amitundu,” uko ndiko kuti, pakati pa osakhala Ayuda, amenenso anadzozedwa ndi mzimu woyera.

15. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Akristu a mzaka za zana loyamba anali adaphunzira bwino lomwe chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu?

15 Monga momwe zasimbidwira pa Machitidwe 12:24, “mawu a [Yehova, NW] anakula nachulukitsa.” Machitidwe 17:6 imasimba kuti kumpoto kwa Grisi otsutsa anafuula, monga momwe amachitira kumeneko kufikira lerolino: “Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso.” Mkati mwa zaka 30, Paulo anakhoza kulemba kuchokera ku Roma kuti mbiri yabwino inali “italalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akolose 1:23) Akristu a nthaŵi imeneyo anali ataphunzira bwino lomwe chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu. Ndi mwachangu chotani nanga mmene iwo anali kuchigwiritsira ntchito! Ndipo lolani kuti nafenso tichiphunzire mofananamo ndi kuchigwiritsira ntchito m’tsiku lomalizira lino la kulalikira Ufumu!

16. Kodi nchiyani chimene chinali mbali yachisanu ya chinsinsi chopatulika, ndipo kodi ndi ntchito yotani imene inaipangitsa iyo kuwonekera?

16 M’kuyankha ku kulalikira kwa zaka za zana loyamba kumeneko, mbali yachisanu ya chinsinsi chopatulika cha 1 Timoteo 3:16 inakhala yowonekera kwenikweni. Yesu tsopano “anakhulupiridwa m’dziko lapansi.” Ichi chinatulukapo chifukwa cha kudzipereka kwaumulungu konga kwa Kristu kwa amishonale achangu, kuphatikizapo Paulo ndi Timoteo. Iwo anatenga mbiri yabwino kuloŵa nayo mu Asia Minor ndi Europe, mwinamwake kufika kutali ku Spain, ndi Kum’mawa kwa Africa kupyolera pakamwa pa m’Aitopia wobatizidwa, pamene Petro anatumikira mu Babulo.

17. Kodi nchifukwa ninji Yesu akukhulupiridwa m’dziko lonse lamakono?

17 Bwanji ponena za tsiku lathu? Chiyambire 1919 otsalira odzozedwa akhala akusonyeza kudzipereka kwaumulungu kopereka chitsanzo. Odzozedwa amenewa amanga zolimba pa maziko a chikhulupiriro chokhazikitsidwa ndi Yesu. Makamaka chiyambire 1935, iwo apitirizabe kusonkhanitsa khamu lalikulu, omwe amasangalala m’chiyembekezo cha kupyola “chisautso chachikulu” ndi kusangalala ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi. (Chibvumbulutso 7:9, 14) Chotero, mbiri yabwino yoloza pa Yesu ikukhulupiridwa kupyola m’dziko lonse lamakono. M’kudzipereka kwaumulungu, Mboni za Yehova zoposa 3,700,000 zikulalikira tsopano ndi kupambana kuzungulira chiwunda chonse!

18. Kodi ndimotani mmene Yesu “analandiridwa mu ulemerero”?

18 Pasalabe mbali imodzi ya chinsinsi chopatulika chimenecho, ya chisanu ndi chimodzi: Yesu “analandiridwa mu ulemerero.” M’kati mwa masiku 40 pambuyo pa kukhalitsidwa wamoyo mu mzimu, Yesu anasandulika m’matupi aumunthu, akumawonekera kwa ophunzira ake ndi kuwawuza iwo “zinthu zonena za Ufumu wa Mulungu.” Kenaka anakwera kumwamba. (Machitidwe 1:3, 6-9) Chotero pemphero lake, lolembedwa pa Yohane 17:1-5, linayankhidwa: “Atate, . . . lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni inu . . . Ndalemekeza inu pa dziko lapansi . . . Ndipo tsopano, Atate inu, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.”

19. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chinalonjera kubwerera kwa Yesu kumwamba?

19 Ndi kusangalala kwakukulu kotani nanga komwe kunalonjera kubwerera kwa Yesu kumwamba! Kuchiyambiyambi, pamene Yehova anakhazikitsa dziko lapansi, “ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Kuposadi pamenepo makamu a angelo amenewa angakhale anasangalala kwenikweni kulandiranso pakati pawo Ngwazi yokhulupirika ya ulamuliro wa Yehova!

20. Kodi nchifukwa ninji Yesu watenga dzina lolemekezeka chotero, ndipo kodi nchiyani chimene anachita pamene anali padziko lapansi?

20 Pa Ahebri 1:3, 4, Paulo akunena za Yesu wolakika kuti: “Ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mawu a mphamvu yake, mmene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m’Mwamba, atakhala wakuposa angelo, monga momwe adaloŵa dzina lakuposa iwo.” Kristu analandira dzina limenelo chifukwa cha chilakiko chake pa chisalungamo. Mwana wa Mulungu ameneyu ndithudi anawalitsa maziko a kudzipereka kwaumulungu pano pa dziko lapansi. Iye anakhazikitsanzo chitsanzo kaamba ka ena onse omwe adzafikira moyo wosatha. Ndi kukwezedwa kwa Yesu ku dzanja lamanja la Mulungu kumwamba, chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kumeneku chinavumbulidwa m’mbali zake zonse.

Kodi Mukayankha Motani?

◻ Kodi “kudzipereka kwaumulungu” nchiyani?

◻ Kodi ndimotani mmene Yesu “anawonekera m’thupi” ndipo pambuyo pake “kulengezedwa wolungama mumzimu”?

◻ Kodi ndi kwa angero ati amene Yesu anawonekerako, ndipo ndi uthenga wotani?

◻ Kodi ndimotani mmene Kristu “analalikidwa mwa amitundu” ndi “kukhulupiridwa m’dziko”?

◻ Kodi ndi liti pamene Yesu “analandiridwa mu ulemerero,” ndipo panali pambuyo pochita chiyani kulinga ku kudzipereka kwaumulungu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena