Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Tetragramatoni (zilembo zinayi zachihebri zoimira dzina la Mulungu) imapezeka m’malembo achihebri a Mateyu ojambulidwa ndi sing’anga wachiyuda wa m’zaka za zana la 14, Shem-Tob ben Isaac Ibn Shaprut?
Ayi, siimapezeka. Komabe, malembo ameneŵa a Mateyu amagwiritsira ntchito hash·Shem’ (lolembedwa lonse kapena chidule chake) nthaŵi 19, malinga ndi zimene Nsanja ya Olonda ya August 15, 1996, inanenera patsamba 13.
Liwu lachihebrilo hash·Shem’ limatanthauza “Dzinalo,” limene mosakayikira limanena za dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, m’malembo a Shem-Tob, chidule cha hash·Shem’ chikupezeka pa Mateyu 3:3, vesi limene Mateyu anagwiramo mawu a Yesaya 40:3. Nkoyenera kunena kuti pamene Mateyu anagwira vesi la m’Malemba Achihebri limene lili ndi Tetragramatoni, anaikamo dzina la Mulungu mu Uthenga wake Wabwino. Chotero ngakhale kuti malembo achihebri a Shem-Tob alibe Tetragramatoni, kugwiritsira ntchito kwake “Dzinalo,” monga pa Mateyu 3:3, kumasonyeza kuti kugwiritsira ntchito “Yehova” m’Malemba Achigiriki Achikristu kuli koyenera.
Shem-Tob anajambula malembo achihebri a Mateyu m’buku lake lotsutsa lakuti ʼEʹven boʹchan. Nanga kodi malembo achihebri amenewo anachokera kuti? Profesa George Howard, amene wafufuza nkhani imeneyi kwambiri, akuti “deti lake la Mateyu wachihebri wa Shem-Tob limasonyeza kuti ali wa m’zaka mazana anayi oyambirira a nyengo yachikristu.”a Ena sagwirizana nazo zimenezi.
Howard akuti: “Mateyu wachihebri wophatikizidwa m’malembo ameneŵa ali ndi mbali zambiri zosiyana kwambiri ndi Mateyu wachigiriki wovomerezedwa.” Mwachitsanzo, malinga ndi malembo a Shem-Tob, Yesu ponena za Yohane anati: “Indetu ndinena kwa inu, mwa onse obadwa mwa akazi sanauka munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi.” Koma amasiya mawu a Yesu otsatira akuti: “Koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.” (Mateyu 11:11) Mofanananso, mawu achihebri omwe akupezekabe m’Malemba Achihebri akusiyana kwambiri ndi mmene mawu a lemba limodzimodzilo alembedwera m’Baibulo la Greek Septuagint. Pamene kuli kwakuti tikuvomereza kusiyana kumeneko, malembo akalewo atheka kuwafufuza mwa kuwayerekezera.
Monga tatchulira kale, malembo a Mateyu wa Shem-Tob ali ndi “Dzinalo” pamalo amene pali zifukwa zabwino zokhulupirira kuti Mateyu anagwiritsiradi ntchito Tetragramatoni. Ndiye chifukwa chake, kuyambira 1950, malembo a Shem-Tob agwiritsiridwa ntchito monga maziko a dzina la Mulungu m’Malemba Achigiriki Achikristu, ndipo mawu ake amagwidwabe mu The New World Translation of the Holy Scriptures—With References.b
[Mawu a M’munsi]
a Onaninso New Testament Studies, Voliyumu 43, Nambala 1, January 1997, masamba 58-71.
b Yofalitsidwa mu 1984 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.