‘Kuyenda mwa Chikhulupiriro Osati mwa Chionekedwe’
“Tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.”—2 AKORINTO 5:7.
1. Kodi ‘kuyenda mwa chikhulupiriro’ kumatanthauzanji?
NTHAŴI zonse tikamapemphera mogwirizana ndi zitsogozo zolembedwa m’Mawu a Mulungu, timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro ndithu. Pamene tiyamba kuchitira umboni kwa ena ponena za Ufumu wa Mulungu, izinso zimasonyeza chikhulupiriro. Ndiponso pamene tipatulira moyo wathu kwa Yehova, tikupereka umboni wakuti cholinga chathu ndicho ‘kuyenda mwa chikhulupiriro,’ ndiko kuti, kutsata moyo wotsogozedwa ndi chikhulupiriro.—2 Akorinto 5:7; Akolose 1:9, 10.
2. Kodi nchifukwa ninji kuchita nawo ntchito za mumpingo sikuli umboni wokwanira wakuti munthu ali ndi chikhulupiriro?
2 Kuti tikhaledi ndi moyo umenewo, tifunikira kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Ahebri 11:1, 6) Anthu ambiri amakopeka ndi Mboni za Yehova chifukwa cha makhalidwe awo abwino kwambiri ndi chikondi chimene chili pakati pa Mbonizo. Chimenecho ndi chiyambi chabwino, koma sizitanthauza kuti anthu oterowo ali ndi chikhulupiriro. Ena angakhale ndi mnzawo wa muukwati kapenanso kholo lawo limene lili ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo angathe kumachita ntchito zina zimene wokondedwayo amachita. Kukhala ndi chisonkhezero chotero m’banja la munthu ndi dalitsodi, komatu zimenezi sizingafanane ndi chikondi chaumwini chimene munthu amayenera kusonyeza kwa Mulungu ndiponso chikhulupiriro chimene iye amayenera kukhala nacho.—Luka 10:27, 28.
3. (a) Kuti ifeyo tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, kodi tiyenera kukhala ndi chikhutiro chathuchathu chotani ponena za Baibulo? (b) Nchifukwa ninji anthu ena amakhutiritsidwa mwamsanga kusiyana ndi ena ponena za kuuziridwa kwa Baibulo?
3 Amene amayendadi mwa chikhulupiriro ali okhutira kuti Baibulo ndilodi Mawu a Mulungu. Pali umboni wokwanira wakuti Malemba Opatulika alidi ‘ouziridwa ndi Mulungu.’a (2 Timoteo 3:16) Kodi ndi umboni wochuluka motani umene munthu amafunikira kuupenda asanakhutiritsidwe? Zimenezo zingadalire pa chidziŵitso cha munthuyo. Zimene zimakhutiritsa kwambiri munthu wina zingakhale zopanda tanthauzo kwa wina. Nthaŵi zina, ngakhale pamene munthu apatsidwa umboni wokwanira wokhutiritsa, iye angapitirizebe kukana zimene kwenikweni umboniwo ukutanthauza. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha zikhumbo za mumtima mwake. (Yeremiya 17:9) Choncho, ngakhale munthu atasonyeza chidwi pa chifuno cha Mulungu, mtima wake ungakhumbe chiyanjo cha dziko. Sangafune kusiya moyo wake umene umaombana ndi malamulo a m’Baibulo. Komabe, ngati munthu alidi ndi njala ya choonadi, ngati ali woona mtima, ndipo ngati ali wodzichepetsa, m’kupita kwa nthaŵi iye adzazindikira kuti Baibulo ndilodi Mawu a Mulungu.
4. Kodi munthu payekha amafunikira kuchitanji kuti akhale ndi chikhulupiriro?
4 Nthaŵi zambiri patangopita miyezi yoŵerengeka, anthu amene akuthandizidwa kuphunzira Baibulo amavomereza kuti iwo apeza umboni wokwanira wakuti lilidi Mawu a Mulungu. Ngati zimenezi ziwasonkhezera kukonzekeretsa mitima yawo kuti iphunzitsidwe ndi Yehova, ndiye kuti malingaliro awo ochokera pansi pa mtima, zikhumbo zawo, ndiponso zochita zawo zidzayamba kusonkhezeredwa pang’onopang’ono ndi zimene akuphunzira. (Salmo 143:10) Aroma 10:10 amati ‘mtima’ ndiwo umapangitsa munthu kukhala ndi chikhulupiriro. Chikhulupiriro chimenecho chimasonyeza mmenedi munthuyo amalingalirira, ndipo zimenezi zimasonyezedwa m’moyo wake wa tsiku ndi tsiku.
Nowa Anasonkhezeredwa ndi Chikhulupiriro Cholimba
5, 6. Kodi nchiyani chimene chinali maziko a chikhulupiriro cha Nowa?
5 Nowa anali munthu amene anali ndi chikhulupiriro cholimba. (Ahebri 11:7) Kodi nchiyani chimene chinali maziko a chikhulupiriro chake? Nowa anali ndi mawu a Mulungu, osati olembedwa, koma olankhulidwa kwa iye. Genesis 6:13 amati: ‘Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo.’ Yehova anauza Nowa kuti amange chingalawa ndipo anamuuzanso mamangidwe ake mwatsatanetsatane. Ndipo Mulungu anawonjezera kuti: “Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiwononge zamoyo zonse, mmene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m’dziko lapansi zidzafa.”—Genesis 6:14-17.
6 Kodi mvula inali itagwapo kale zisanachitike zimenezi? Baibulo silifotokoza. Genesis 2:5 amati: ‘Yehova Mulungu sanavumbitse mvula.’ Koma umu ndi mmene Mose, amene anakhalapo zaka mazana ambiri zimenezi zitachitika, anafotokozera osati za m’tsiku la Nowa koma zakale kwambiri zimenezo zisanachitike nkomwe. Monga momwe zasonyezedwera pa Genesis 7:4, Yehova ananena za mvula pamene anali kulankhula kwa Nowa, ndipo mwachionekere Nowa anamvetsetsa zimene iye anatanthauza. Komatu ngakhale zinali choncho, chikhulupiriro cha Nowa sichinadalire pa zimene iye anaona. Mtumwi Paulo analemba kuti Nowa ‘anachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke.’ Mulungu anauza Nowa kuti Iye anali kudzadzetsa padziko lapansi “chigumula cha madzi,” kapena kuti “nyanja yakumwamba,” monga momwe mawu amtsinde a mu New World Translation akufotokozera pa Genesis 6:17. Kuyambira pachiyambi mpaka nthaŵiyo, zinthu zotero zinali zisanachitikepo. Koma chilengedwe chonse chimene Nowa anatha kuchiona chinali umboni wokwanira wakuti Mulungu angadzetsedi chigumula chowonongacho. Posonkhezeredwa ndi chikhulupiriro, Nowa anamanga chingalawa.
7. (a) Kodi Nowa sanafunikire chiyani asanachite zimene Mulungu anamlamulira? (b) Kodi timapindula motani tikamalingalira za chikhulupiriro cha Nowa, ndipo kodi chikhulupiriro chathu chingakhale dalitso kwa ena motani?
7 Mulungu sanafotokozere Nowa za tsiku limene Chigumulacho chinali kudzayamba. Koma Nowa sanachione chimenecho ngati chodzikhululukira kuti achite zinthu mozengereza m’moyo wake, mwa kuika pambuyo ntchito yomanga chingalawa ndi kulalikira. Panthaŵi yake, Mulungu anauza Nowa za nthaŵi yoloŵa m’chingalawamo. Panthaŵi imeneyi, “Anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:22) Nowa anayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa chionekedwe. Tili oyamikira chotani nanga kuti iye anatero! Chifukwa cha chikhulupiriro chake, ife tili ndi moyo lero. Ifenso, chikhulupiriro chimene tili nacho chingakhale chothandizanso kwambiri mtsogolo mwathu osati kwa ife tokha komanso kwa ana athu ndiponso kwa anansi athu.
Chikhulupiriro cha Abrahamu
8, 9. (a) Kodi nchiyani chimene chinali maziko a chikhulupiriro cha Abrahamu? (b) Kodi Yehova “anaonekera” motani kwa Abrahamu?
8 Talingalirani za chitsanzo china—chija cha Abrahamu. (Ahebri 11:8-10) Kodi nchiyani chimene chinali maziko a chikhulupiriro cha Abrahamu? Malo amene iye anakuliramo ku Uri wa kwa Alkadayo anali odzala ndi kulambira mafano ndiponso anthu ake anali okondetsa chuma. Koma zinthu zina ndizo zimene zinasintha moyo wa Abrahamu. Mosakayika konse iye anayanjanapo ndi Semu, mwana wa Nowa, amene anakhala naye pamodzi kwa zaka 150. Abrahamu anakhutira kuti Yehova ndiyedi “Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 14:22.
9 Panali chinthu china chake chimene chinasonkhezera kwambiri Abrahamu. Yehova “anaonekera kwa . . . Abrahamu, pokhala iye m’Mesopotamiya, asanayambe kukhala m’Harana; nati kwa iye, Tuluka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.” (Machitidwe 7:2, 3) Kodi Yehova “anaonekera” motani kwa Abrahamu? Abrahamu sanaone Mulungu mwachindunji. (Eksodo 33:20) Komabe, zingatheke kuti Yehova anaonekera kwa Abrahamu m’maloto, mu ulemerero waukulu koposa, kapenanso mwa mthenga waungelo, kapena nthumwi. (Yerekezerani ndi Genesis 18:1-3; 28:10-15; Levitiko 9:4, 6, 23, 24.) Kaya Yehova anaonekera kwa Abrahamu motani, munthu wokhulupirika ameneyo anali ndi chidaliro chakuti Mulungu anali kumpatsa mwaŵi wa mtengo wapatali. Abrahamu anachitapo kanthu mwa chikhulupiriro.
10. Kodi Yehova analimbitsa motani chikhulupiriro cha Abrahamu?
10 Chikhulupiriro cha Abrahamu sichinadalire pa kukhala ndi malongosoledwe atsatanetsatane a dziko limene Mulungu anamuuza kukakhalako. Sichinadalire pa kudziŵa kwake nthaŵi imene dzikolo linali kudzapatsidwa kwa iye. Iye anali ndi chikhulupiriro chifukwa chakuti anadziŵa kuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse. (Eksodo 6:3) Yehova anauza Abrahamu kuti iye anali kudzakhala ndi mwana, koma nthaŵi zina Abrahamu anali kukayikira kuti zimenezo zingatheke bwanji. Iye anali wokalamba. (Genesis 15:3, 4) Yehova analimbitsa chikhulupiriro cha Abrahamu mwa kumuuza kuti ayang’ane kumwamba naŵerenge nyenyezi zonse ngati angathe kutero. “Zoterezo zidzakhala mbewu zako,” anatero Mulungu. Abrahamu anasonkhezeredwa kwambiri. Zinali zachidziŵikire kuti Mlengi wa zakumwamba zodabwitsazo anali wokhoza kukwaniritsa zimene analonjeza. Abrahamu “anakhulupirira Yehova.” (Genesis 15:5, 6) Abrahamu sanakhulupirire chabe chifukwa chakuti anasangalala ndi zimene anauzidwazo ayi; iye anali ndi chikhulupiriro cholimba.
11. (a) Pamene anali pafupi kukwanitsa zaka 100 zakubadwa, kodi Abrahamu analabadira motani lonjezo la Mulungu lakuti Sara wokalambayo adzakhala ndi mwana? (b) Kodi Abrahamu anali ndi chikhulupiriro chotani pa chiyeso cha kupita ndi mwana wake ku Phiri la Moriya kukampereka nsembe?
11 Pamene Abrahamu anali pafupi kukwanitsa zaka 100 zakubadwa ndiponso pamene mkazi wake, Sara, anali pafupi kukwanitsa zaka 90 zakubadwa, Yehova anafotokozanso kuti Abrahamu adzakhala ndi mwana wamwamuna ndipo anati Sara ndiye adzakhale amake. Abrahamu analingalira mozama za mkhalidwe wawo. “Ndipo poyang’anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mumtima kuti, chimene iye analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.” (Aroma 4:19-21) Abrahamu anadziŵa kuti lonjezo la Mulungu silikanalephera. Patapita nthaŵi, chifukwa cha chikhulupiriro chake, Abrahamu anamvera pamene Mulungu anamuuza kuti atenge mwana wake Isake napite naye ku dziko la Moriya nakampereke nsembe. (Genesis 22:1-12) Abrahamu anali ndi chidaliro chokwanira chakuti Mulungu amene anapangitsa kuti mwana ameneyo abadwe mozizwitsa analinso wokhoza kumuukitsa kuti akwaniritse malonjezo owonjezereka amene anawapereka mogwirizana ndi mwanayo.—Ahebri 11:17-19.
12. Kodi Abrahamu anayenda mwa chikhulupiriro kwa nthaŵi yaitali motani, ndipo kodi ndi mphotho yotani imene iyeyo akuyembekezera pamodzi ndi a m’banja lake amene anasonyeza chikhulupiriro cholimba?
12 Abrahamu anasonyeza kuti anali kutsogozedwa ndi chikhulupiriro, osati pazochitika zoŵerengeka zokha, koma pa moyo wake wonse. Abrahamu akali ndi moyo, Mulungu sanampatse mbali iliyonse ya Dziko Lolonjezedwa monga choloŵa chake. (Machitidwe 7:5) Komabe, Abrahamu sanafooke ndi kubwerera ku Uri wa kwa Alkadayo. Kwa zaka 100, kufikira imfa yake, iye anakhala m’mahema m’dziko limene Mulungu anamuuza kukakhala. (Genesis 25:7) Ponena za iye ndi mkazi wake Sara, mwana wawo Isake, ndiponso mdzukulu wawo Yakobo, Ahebri 11:16 akuti: “Mulungu sachita manyazi nawo poitanidwa Mulungu wawo; pakuti adawakonzera mudzi.” Ndithudi, Yehova anawakonzera malo m’dziko lapansi la Ufumu wake Waumesiya.
13. Kodi ndani pakati pa atumiki a Yehova lerolino amene akusonyeza umboni wakuti ali ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu?
13 Pakati pa atumiki a Mulungu lerolino palinso anthu amene ali ngati Abrahamu. Iwo ayenda mwa chikhulupiriro kwa zaka zambiri. Mwa mphamvu imene Mulungu amapereka, iwo agonjetsa zopinga zokhala ngati mapiri. (Mateyu 17:20) Kusadziŵa kwawo nthaŵi imene Mulungu adzawapatsa choloŵa chimene walonjeza sikukupangitsa chikhulupiriro chawo kukhala chogwedezeka. Iwo amadziŵa kuti mawu a Yehova salephera, ndipo amaona kuti kukhala mmodzi wa Mboni zake ndi mwaŵi wa mtengo wapatali koposa. Kodi ndi mmenenso inu mumaonera?
Chikhulupiriro Chimene Chinasonkhezera Mose
14. Kodi chikhulupiriro cha Mose chinayamba motani?
14 Mose ali chitsanzo china cha chikhulupiriro. Kodi chikhulupiriro chake chinayambika motani? Chinayambika akali wamng’ono. Ngakhale kuti mwana wamkazi wa Farao anapeza Mose m’bokosi la gumbwa mu Mtsinje wa Nile namtenga monga mwana wake, amake enieni a Mose achihebri, Yokobedi, anamyamwitsa mwanayo ndipo anamlera m’zaka zake zoyambirira. Mwachionekere, Yokobedi anamphunzitsa bwino, kumdziŵitsa za chikondi cha Yehova ndi kumuuza za malonjezo Ake kwa Abrahamu. Patapita nthaŵi, monga wa m’banja la Farao, Mose “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto.” (Machitidwe 7:20-22; Eksodo 2:1-10; 6:20; Ahebri 11:23) Komabe, ngakhale kuti Mose anayanjidwa ndi Aigupto, mtima wake unali kulingalira za anthu a Mulungu amene anali mu ukapolo.
15. Kodi kudziika kwake m’gulu la anthu a Yehova kunatanthauzanji kwa Mose?
15 Pamene anali ndi zaka 40 zakubadwa, Mose anakantha Mwaigupto pofuna kupulumutsa Mwisrayeli amene anali kuzunzidwa. Zimenezi zinasonyeza mmene Mose anali kuonera anthu a Mulungu. Zoonadi, “ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao.” M’malo moumirirabe “kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi” monga wa m’banja lachifumu la Aigupto, iye anasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro nasankha kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu.—Ahebri 11:24, 25; Machitidwe 7:23-25.
16. (a) Kodi ndi ntchito yotani imene Yehova anapatsa Mose, nanga Mulungu anamthandiza motani? (b) Pochita ntchito yakeyo, kodi Mose anasonyeza chikhulupiriro motani?
16 Mose anali wofunitsitsa kuchitapo kanthu kuti apulumutse anthu ake, koma nthaŵi ya Mulungu yoti iwo alanditsidwe inali isanafikebe. Mose anathaŵa ku Igupto. Patapita zaka pafupifupi 40 mpamene Yehova kudzera mwa mngelo anatuma Mose kuti abwerere ku Igupto kukatulutsa Aisrayeli m’dzikolo. (Eksodo 3:2-10) Kodi Mose anatani? Iye sanakayikire zoti Yehova angalanditse Israyeli, koma anaona kuti sakanatha kuchita ntchito imene Mulungu anampatsayo. Mwachikondi, Yehova analimbikitsa Mose. (Eksodo 3:11–4:17) Chikhulupiriro cha Mose chinalimbitsidwa. Anabwerera ku Igupto nachenjeza Farao maso ndi maso ndiponso mobwerezabwereza za miliri imene inali kuyembekezera kukantha Igupto chifukwa chakuti wolamulirayo anakaniza Aisrayeli kukalambira Yehova. Mose analibe mphamvu zakezake zoti angadzetse miliriyo. Iye anayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa chionekedwe. Anakhulupirira Yehova ndi mawu ake. Farao anaopseza Mose. Koma Mose analimbikirabe. “Ndi chikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Mose anali wopanda ungwiro. Anali ndi zophophonya zake. (Numeri 20:7-12) Komabe, atatumidwa ndi Mulungu, moyo wake wonse unatsogozedwa ndi chikhulupiriro.
17. Kodi nchiyani chimene chinali chotsatirapo cha kuyenda mwa chikhulupiriro kwa Nowa, Abrahamu, ndi Mose, ngakhale kuti iwo anafa asanaone dziko latsopano la Mulungu?
17 Chikhulupiriro chanu chikhaletu chofanana ndi chija cha Nowa, Abrahamu, ndi Mose. Nzoona kuti iwo sanaone dziko latsopano la Mulungu m’tsiku lawo. (Ahebri 11:39) Imeneyo sinali nthaŵi yoikika ya Mulungu; panali mbali zina za chifuno chake zimene zinayenera kukwaniritsidwa. Komabe, kukhulupirira kwawo mawu a Mulungu sikunagwedezeke, ndipo maina awo analembedwa m’buku la Mulungu la moyo.
18. Nchifukwa ninji kuyenda mwa chikhulupiriro kuli kofunika kwa amene anaitanidwira ku moyo wakumwamba?
18 “Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa,” analemba motero mtumwi Paulo. Ndiko kuti, Mulungu anakonzera kanthu koposa awo amene, monga Paulo, anaitanidwira ku moyo wakumwamba pamodzi ndi Kristu. (Ahebri 11:40) Awa ndiwo amene kwenikweni Paulo anali kunena pamene analemba mawu opezeka pa 2 Akorinto 5:7 akuti: “Tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.” Pamene zimenezo zinalembedwa, palibe ndi mmodzi yemwe wa iwo amene anali atalandira mphotho yawo ya kumwamba. Iwo sanaione ndi maso awo aumunthu, koma anali ndi chikhulupiriro cholimba cha mphothoyo. Kristu anali ataukitsidwa kwa akufa, zipatso zoyamba za amene adzadalitsidwa mwa kupatsidwa moyo wakumwamba. Ndipo mboni zoposa 500 zinamuona asanakwere kumwamba. (1 Akorinto 15:3-8) Iwo anali ndi chifukwa chabwino kwambiri cha kutsogozedwa ndi chikhulupiriro chimenecho m’moyo wawo wonse. Ifenso tili ndi zifukwa zabwino kwambiri zoyendera mwa chikhulupiriro.
19. Monga momwe zasonyezedwera pa Ahebri 1:1, 2, kodi Mulungu walankhula kwa ife mwa yani?
19 Lerolino, Yehova sakulankhula kwa anthu ake mwa mngelo, monga momwe anachitira kwa Mose pachitsamba choyaka moto. Mulungu walankhula mwa Mwana wake. (Ahebri 1:1, 2) Zimene Mulungu analankhula mwa iye, anazilemba m’Baibulo, limene latembenuzidwa m’zinenero za anthu padziko lonse.
20. Kodi zinthu zili bwino motani kwa ife kusiyana ndi mmene zinalili kwa Nowa, Abrahamu, ndi Mose?
20 Tili ndi Mawu ake ambiri kuposa amene Nowa, Abrahamu, ndi Mose anali nawo. Tili ndi Mawu onse a Mulungu—amene ambiri mwa iwo anakwaniritsidwa kale. Polingalira zonse zimene Baibulo limanena zokhudza amuna ndi akazi amene anakhaladi mboni zokhulupirika za Yehova polaka ziyeso zosiyanasiyana, Ahebri 12:1 akutilangiza kuti: “Ifenso . . . titaye cholemetsa chili chonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” Chikhulupiriro chathu sitiyenera kuchiona mopepuka. ‘Tchimo limene limangotizinga’ ndilo kupanda chikhulupiriro. Tifunikira kumenyera zolimba kuti tipitirizebe ‘kuyenda mwa chikhulupiriro.’
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukutipo Bwanji?
◻ Kodi ‘kuyenda mwa chikhulupiriro’ kumaphatikizapo chiyani?
◻ Kodi tingapindule motani ponena za mmene Nowa anasonyezera chikhulupiriro?
◻ Kodi kulingalira za mmene Abrahamu anasonyezera chikhulupiriro kumatithandiza motani?
◻ Nchifukwa ninji Baibulo limatchula Mose kuti ndiye chitsanzo cha chikhulupiriro?
[Chithunzi patsamba 10]
Abrahamu anayenda mwa chikhulupiriro
[Chithunzi patsamba 10]
Mose ndi Aroni anasonyeza chikhulupiriro pamaso pa Farao