Ntchito Zachikristu Pakati pa Chipwirikiti
ZONSE zinayamba mwadzidzidzi tsiku lina mu April 1994. Ngozi ya ndege inapha mapulezidenti a Burundi ndi Rwanda. M’maola ochepa, chiwawa chochititsa mantha chinakuta Rwanda. M’miyezi yoposa pang’ono pa itatu chabe, anthu oposa 500,000 a ku Rwanda—amuna, akazi, ndi ana—anafa. Anthu ena amasonya ku zochitikazo monga “kupululutsa anthu.”
Theka la anthu 7,500,000 okhala ku Rwanda anakakamizika kuthaŵa. Izi zinaphatikizapo anthu 2,400,000 omwe anathaŵira m’maiko oyandikana nawo. Unali ulendo wa gulu la othaŵa kwawo waukulu ndi wa mwadzidzidzi kwambiri m’mbiri ya makono. Misasa ya othaŵa kwawo inakonzedwa mofulumira mu dziko la Zaire (tsopano Democratic Republic of Congo), Tanzania, ndi Burundi. Ina mwa misasa imeneyi—yaikulu kwambiri padziko lonse—inali ndi anthu 200,000.
Pakati pa othaŵa kwawowo panali Mboni za Yehova zochuluka, anthu okonda mtendere amene amagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’miyoyo yawo. M’dziko lililonse limene amapezekamo, amasunga uchete kwambiri ndipo amagwiritsira ntchito pulinsipulo lopezeka m’mawu awa a Yesaya 2:4: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Mboni za Yehova zikudziŵika paliponse monga gulu lachipembedzo limene silinatenge nawo mbali m’kupululutsa anthu mu Rwanda.
Yesu Kristu anati otsatira ake “sakhala a dziko lapansi.” Komabe, chifukwa chakuti iwo ali “m’dziko lapansi,” chipwirikiti cha mitundu sangachipewe nthaŵi zonse. (Yohane 17:11, 14) Panthaŵi ya kupululutsa anthu ku Rwanda, Mboni pafupifupi 400 zinataya miyoyo yawo. Pafupifupi Mboni ndi anthu okondweretsedwa ndi uthenga wa Ufumu 2,000 anakhala othaŵa kwawo.
Kodi kusakhala a dziko lapansi kumatanthauza kuti Mboni za Yehova sizichitapo kanthu pamene masoka akantha? Kutalitali! Mawu a Mulungu amati: “Mbale kapena mlongo akakhala wausiŵa, nichikamsoŵa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nawo, mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosoŵa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.” (Yakobo 2:15-17) Chikondi cha pa mnansi chimasonkhezeranso Mboni kuthandiza anthu amene sali a chipembedzo chawo.—Mateyu 22:37-40.
Ngakhale kuti Mboni za Yehova padziko lonse zinali zofunitsitsa kuthandiza okhulupirira anzawo omwe anali mumkhalidwe wovuta ku Rwanda, ntchito yoyang’anira za chithandizo inagaŵiridwa kwa Mboni za ku Western Europe. Mkati mwa chilimwe cha 1994, gulu la a ntchito odzifunira a Mboni a ku Ulaya anakathandiza abale ndi alongo awo achikristu ku Afirika. Misasa yolinganizidwa bwino ndi zipatala za m’misasa zinapangidwa kaamba ka othaŵa kwawo a ku Rwanda. Zovala, mabulangeti, chakudya, ndi mabuku ofotokoza Baibulo ochuluka anatumizidwa kwa ameneŵa pandege kapena pogwiritsa ntchito njira zina. Anthu ovutika oposa 7,000—pafupifupi kuŵirikiza katatu chiŵerengero cha Mboni za Yehova panthaŵiyo ku Rwanda—anapindula ndi ntchito za chithandizo zimenezo. Pofika December chaka chimenecho, zikwi za othaŵa kwawo, kuphatikizapo Mboni za Yehova zochuluka, anabwerera ndi kukakhalanso ku Rwanda.
Nkhondo ku Congo
Mu 1996, nkhondo inabuka m’chigawo chakummawa kwa dziko la Democratic Republic of Congo. Dera limeneli limachita malire ndi Rwanda ndi Burundi. Kunonso kunali kugwirira akazi ndi kupha. Zipolopolo zikuuluka ndipo midzi ikuyaka moto, anthu anathaŵitsa miyoyo yawo. Mboni za Yehova zinali kumalo achipwirikiticho, ndipo pafupifupi 50 anafa. Ena anaphedwa ndi zipolopolo zoponyedwa mwachisawawa. Ena anaphedwa chifukwa anali a mtundu wakutiwakuti kapena anayesedwa kuti ndi adani. Mudzi wina mmene munkakhala Mboni 150 unawonongedwa ndi moto. M’midzi ina nyumba zochuluka ndi Nyumba zina za Ufumu zinatenthedwa. Zitatayikidwa nyumba ndi katundu, Mboni zinathaŵira kumadera ena ndipo zinathandizidwa ndi alambiri anzawo kumeneko.
Njala imatsatira nkhondo, popeza kuti mbewu zimawonongedwa, nkhokwe za chakudya amazifunkha, ndipo njira zopezera chakudya zimatsekedwa. Chakudya chomwe chimapezeka chimakhala chodula. Mu Kisangani, kumayambiriro a May 1997, kilogalamu imodzi ya mbatata inali kugulidwa ndi madola atatu, zosatheka kwa anthu ambiri. Anthu ochuluka anali kungodya kamodzi patsiku. Inde, chakudya chikachepa matenda amabwera mosavuta. Matenda a njala amachepetsa mphamvu ya thupi yolimbana ndi malungo ndi matenda a m’mimba. Ana makamaka amadwala ndi kufa.
Kufufuza Zofunika
Kachiŵirinso Mboni za Yehova ku Ulaya zinachitapo kanthu. Pofika mu April 1997 gulu la Mboni lopereka chithandizo limene linaphatikizapo madokotala aŵiri linali litafika ndi mankhwala ndi ndalama. Ku Goma Mboni za kumaloko zinali zitapanga kale makomiti a chithandizo oti afufuze za mkhalidwewo kotero kuti chithandizo chamwamsanga chiperekedwe. Gululo linayendera mzindawo ndi madera ozungulira. Mithenga inatumidwa kukatenga malipoti a kumalo akutali. Chidziŵitso cha mmene zinthu zinalili ku Kisangani, amene ali pamtunda wa makilomita 1,000 kumadzulo kwa Goma, chinapezedwanso. Abale akumaloko anathandizira kuyang’anira ntchito za chithandizo ku Goma, kumene kumakhala Mboni 700.
Mmodzi wa akulu achikristu ku Goma anati: “Tinakhudzidwa mtima kwambiri kuona abale athu amene anabwera kudzatithandiza kuchokera kutali. Tinathandizana tokhatokha iwo asanabwere. Abale anathaŵa kumidzi ndi kubwera ku Goma. Ena anali atatayikidwa nyumba ndipo anasiya minda yawo. Tinawalandira m’nyumba zathu ndipo tinagawana zovala ndi chakudya chochepa chimene tinali nacho. Zimene tikanatha kuchita mwa ife tokha zinali zochepa. Ena a ife anali kudwala matenda a njala.
“Komabe, abale a ku Ulaya anabweretsa ndalama zimene zinatithandiza kugula chakudya, chimene chinali chosoŵa ndi chodula kwambiri. Chakudyacho chinabwera panthaŵi yoyenerera popeza kuti ambiri analibe chakudya m’nyumba zawo. Tinagaŵira chakudya kwa Mboni ndi omwe sanali Mboni. Ngati thandizolo silikanafika panthaŵi imeneyo, ambiri anakafa, makamaka ana. Yehova anapulumutsa anthu ake. Anthu omwe sali Mboni anachita chidwi kwambiri. Ambiri anakambapo pa mgwirizano ndi chikondi chathu. Ena anavomereza kuti chipembedzo chathu ndicho chipembedzo choona.”
Ngakhale kuti chakudya chinali kugulidwa kumalo komweko ndipo mankhwala anali kuperekedwa, zambiri zinali kufunika. Zovala, mabulangeti, ndiponso chakudya ndi mankhwala ochuluka zinali kufunika. Chithandizo chinalinso kufunika kuti nyumba zomwe zinali zitawonongeka zimangidwenso.
Anthu Apereka Moolowa Manja
Abale ku Ulaya analinso ofunitsitsa kuthandiza. Ofesi ya Mboni za Yehova ku Louviers, France, inadziŵitsa mipingo ya ku Rhône Valley, Normandy, ndi ya kudera la Paris za kufunika kwa thandizolo. Pulinsipulo lina la m’Malemba linagwira ntchito kunoko: “Iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta. Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.”—2 Akorinto 9:6,7.
Mwachimwemwe anthu zikwizikwi anagwiritsira ntchito mpatawo kuti apereke. Mabokosi ndi matumba a zovala, nsapato, ndi katundu wina zinasonkhanitsidwira m’Nyumba za Ufumu ndipo kenaka zinatumizidwa ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku France. Kumeneko antchito odzifunira 400 anali okonzekera gawo lotsatira la ntchito ya “Thandizani Zaire.” Pamene katundu wachithandizoyu anafika, antchito odzifunirawa anasankha, anapinda, ndi kulongedza zovala m’mabokosi omwe anali kuwunjikidwa m’magulu a mabokosi 30. Ana anali ataganizira abale ndi alongo awo ang’onoang’ono mu Afirika ndipo anatumiza zoseŵeretsa—timagalimoto tonyezimira, nguli, zidole, ndi tizimbalangondo ta zidole. Izi zinalongedzedwa pamodzi ndi katundu wofunika pa moyo. Zonse zomwe zinatumizidwa ku Congo zinalongedzedwa mu zotengeramo zikuluzikulu zisanu ndi zinayi zautali wa mamita 12.
Kodi ndi chithandizo chochuluka motani chimene chaperekedwa ku Central Africa ndi thandizo la Mboni zikwi za ku Belgium, France, ndi Switzerland? Pofika June 1997 zonse zinali makilogalamu 500 a mankhwala, matani 10 a mabisiketi okhala ndi proteni wochuluka, matani 20 a zakudya zina, matani 90 a zovala, mapeyala a nsapato 18,500, ndi mabulangeti 1,000. Mabuku ofotokoza Baibulo anatumizidwanso. Zonsezi zinayamikiridwa kwambiri, zinatonthoza othaŵa kwawowo ndi kuwathandiza kupirira mayesero awo. Mtengo wa katundu wonsewo unali pafupifupi $1,000,000 U.S. Zopereka zotero zinali umboni wa ubale ndi chikondi pakati pa awo amene amatumikira Yehova.
Kugaŵira Zinthuzo ku Congo
Pamene katundu anayamba kufika ku Congo, abale aŵiri ndi mlongo mmodzi anabwera kuchokera ku France kudzagwira ntchito ndi makomiti a chithandizo a kumaloko. Ponena za chiyamikiro chomwe Mboni za ku Congo zinasonyeza, Joseline anati: “Tinalandira makalata ambiri a chiyamikiro. Mlongo wina wosauka anandipatsa chokometsera chamwala wa malachite wonga mkuwa. Ena anatipatsa zithunzi zawo. Pamene tinali kuchoka, alongo anandipsompsona, kundikupatira, ndi kulira. Ndinaliranso. Ambiri ankanena kuti, ‘Yehova ndi wabwino. Yehova amatiganizira.’ Choncho anazindikira kuti Mulungu ndiye amene ayenera kulandira chiyamikiro kaamba ka kupatsaku. Pamene tinali kugaŵira chakudya, abale ndi alongo anatamanda Yehova ndi nyimbo za Ufumu. Zinali zokhudza mtima.”
Dokotala wotchedwa Loic anali membala wa gululo. Anthu ochuluka anadzazana m’Nyumba ya Ufumu ndipo mopirira anayembekezera kuti nthaŵi yawo yoonana ndi dokotalayo ikwane. Pofuna kuchitaponso kanthu, mlongo wina wa ku Congo anaphika ndi kupereka mandasi 40 kwa amene anali kuyembekezera kuonana ndi dokotalayo. Popeza kuti onse analipo 80, aliyense analandira theka la ndasi.
Chithandizo kwa Osakhala Mboni
Chithandizochi sichinaperekedwe kokha kwa Mboni za Yehova. Enanso analandira monga mmene zinalili mu 1994. Zimenezi ndi zogwirizana ndi Agalatiya 6:10 amene amati: ‘Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pabanja la chikhulupiriro.’
Mboni zinagaŵira mankhwala ndi zovala ku masukulu a pulaimale angapo ndi malo osungirapo ana amasiye ku Goma. Pali ana 85 pa malo osungirapo ana amasiyewo. Paulendo woyamba wokafufuza mmene mkhalidwe unalili, gulu lachithandizoli linafika pamalo osungirapo ana amasiyewa ndi kulonjeza kuti adzawapatsa mabokosi 50 a mabisiketi okhala ndi proteni wochuluka, mabokosi a zovala, mabulangeti 100, mankhwala, ndi zoseŵeretsa. Anawo anaima mu mizere pabwalo ndi kuwaimbira nyimbo alendowo. Ndiyeno anali ndi pempho lapadera—kodi angadzawapatse mpira woti azidzaseŵera?
Gulu la chithandizolo linakwaniritsa lonjezo lawo milungu ingapo pambuyo pake. Atachita chidwi ndi kuolowa manja ndi zimenenso anaŵerenga m’buku lofotokoza Baibulo limene anapatsidwa, mkulu wa pamalopo anati akufuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Kodi anawo anapatsidwa mpira? “Ayi,” anayankha Claude, mtsogoleri wa gulu la chithandizo la ku France. “Tinawapatsa mipira iŵiri.”
Misasa ya Othaŵa Kwawo
Chithandizo sichinaperekedwe kokha mu Congo. Zikwi za anthu othaŵa nkhondo zinathaŵira m’dziko lina lapafupi kumene misasa itatu inapangidwa mofulumira. Mboni zidakafikanso kumeneko kuti zikaone chimene chingachitidwe. Pamene lipotili linali kulembedwa, m’misasamo munali anthu othaŵa kwawo 211,000, ochuluka a iwo ochokera ku Congo. Pafupifupi 800 anali Mboni ndi ana awo ndi anthu okondweretsedwa ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Kupereŵera kwa chakudya linali vuto limene anapezana nalo mofulumira m’misasamo. Pamsasa wina panali chakudya chokwanira masiku atatu okha, kuphatikizapo nyemba zogonera zaka zitatu.
Komabe, Mboni zinali ndi mzimu wabwino. Ngakhale kuti anali ndi mabuku ofotokoza Baibulo ochepa, anali kukhala ndi misonkhano poyera mokhazikika kuti adzilimbikitse mwauzimu. Analinso otanganitsidwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa ena m’misasamo.—Mateyu 24:14; Ahebri 10:24, 25.
Gulu lofufuza la Mbonilo linaphatikizapo dokotala. Ngakhale kuti akuluakulu a boma anawapatsa masiku ochepa chabe kuti akhale pamsasa uliwonse, gululo linapereka chithandizo cha mankhwala. Anali kusiyira akulu achikristu mankhwala ndi ndalama. Motero, abale anakhalabe ndi moyo. Gululo linayembekezeranso kuti posakhalitsa Mboni zinali m’misasazo zikabwerera kwawo.
Bwanji nanga za mtsogolo? Yesu Kristu ananeneratu kuti tsiku lathu likakhala la zipwirikiti, nthaŵi ya nkhondo ndi kupereŵera kwa zakudya. (Mateyu 24:7) Mboni za Yehova zimadziŵa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa kuvutika kumene kulipo lerolino padziko lapansi. Mu ulamuliro wake, mudzi wathu dziko lapansi udzakhala paradaiso wa mtendere, wokhala ndi zinthu zochuluka, ndi chimwemwe chosatha kwa anthu omvera. (Salmo 72:1, 3, 16) Padakali pano, Mboni zidzalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa kumwambawo ndipo zidzapitirizanso kuthandiza olambira anzawo ndi ena m’nthaŵi za mavuto.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Kuyambira mu 1994, Mboni za Yehova za ku Ulaya kokha zinatumiza chakudya, zovala, mankhwala, ndi zinthu zina zachithandizo zoposa matani 190 ku dera la nyanja zikuluzikulu za kummaŵa ndi pakati pa Afirika zotchedwa Great Lakes
[Bokosi patsamba 6]
Chikondi Chachikristu Chigwiritsiridwa Ntchito
Pakati pa awo amene anatengamo mbali mofunitsitsa mu ntchito ya “Thandizani Zaire” ku France, panali Ruth Danner. Pamene anali wamng’ono, anaikidwa m’misasa ya chibalo ya Nazi chifukwa cha chikhulupiriro chake chachikristu. Iye anati: “Tinali okondwa kwambiri kuti tiwachitireko kanthu kena abale ndi alongo athu a ku Afirika! Koma panali china chake chimene chinandipangitsa kukhala wokondwa kwambiri. Pamene tinabwerera kunyumba kuchokera ku Germany mu 1945, tinalibiretu kanthu kalikonse. Ngakhale zovala zomwe tinavala zinali zobwereka. Komabe posakhalitsa, tinalandira chithandizo cha kuthupi kuchokera kwa abale athu auzimu a ku America. Choncho chithandizo ichi chinandipatsa mwaŵi wobwezera chifundo chomwe tinasonyezedwa zaka zambiri zapitazo. Ndi mwaŵi waukulu chotani nanga kukhala mbali ya banja lalikulu la abale amene amagwiritsira ntchito chikondi chachikristu!”—Yohane 13:34, 35.
[Chithunzi patsamba 7]
Posachedwapa—dziko lapansi lokhala ndi zochuluka kaamba ka onse