Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 2/15 tsamba 3-4
  • Nkukhaliranji Woyamikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkukhaliranji Woyamikira?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Peŵani Kusayamikira
  • “Khalani Akuyamika”
  • Kulitsani Mzimu Woyamikira
    Nsanja ya Olonda—1998
  • “Muziyamika pa Chilichonse”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Mudzachita Zinthu Zosonyeza Kuyamikira Yehova pa Nyengo ya Chikumbutso Ikubwerayi?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kuyamikira
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 2/15 tsamba 3-4

Nkukhaliranji Woyamikira?

OPALESHONI ya fupa lakumsana inachititsa Harley kusintha ntchito yake yaumisiri wa zamakina kukhala kalaliki wamuofesi. Atafunsidwa mmene amaonera kusintha kumeneku, Harley anati: “Nthaŵi zina ndimafunadi kugwira ntchito ya zamakina. Koma, kunena zoona, ndikusangalala kwambiri ndi ntchito imene ndikugwira tsopano kuposa ntchito yanga yakale.”

Pofotokoza chifukwa chimene analili wokhutira, Harley anasimba kuti: “Nchifukwa cha makhalidwe a anthu amene ndikugwira nawo ntchito. Mosiyana ndi anthu a kumene ndinali kugwira ntchito poyamba, amene akundiyang’anira ntchito tsopano ndiponso antchito anzanga amayamikira ntchito yanga, ndipo samazengereza kutchula zimenezo. Kumeneku nkusiyana kwakukulu kwambiri.” Harley tsopano ndi wantchito wachimwemwe chifukwa chakuti amadzimva kuti ndi wopindulitsa ndipo ena amamfuna.

Mawu oyamikira, ngati ngoyenerera, amasangalatsadi mtima. Koma kusayamikira, kungakhale kozizira monga momwe Shakespeare ananenera kuti: “Taomba, taomba, mphepo yachisanuwe, iwe wosakoma mtima monga kusayamikira kwa munthu.” Mwachisoni, ambiri akumana ndi kusakoma mtima kumeneku.

Peŵani Kusayamikira

M’dziko lamakonoli mawu oyamikira ochokera pansi pa mtima ayamba kusoŵa. Mwachitsanzo, wolemba wina anafunsa funso lakuti: “Ngati mkwatibwi anapeza nthaŵi yolemba makeyala pa makhadi 200 oitanira anthu kuukwati, kodi nchifukwa ninji sangapeze nthaŵi yolemba makalata oyamikira kwa anthu 163 amene anabweretsa mphatso?” Kaŵirikaŵiri ambiri samanena ngakhale liwu losavutalo lakuti “zikomo.” Kuyamikira kukupitirizabe kuloŵedwa m’malo ndi mzimu wa “ine choyamba.” Mkhalidwe umenewu ndiwo chimodzi mwa zizindikiro za masiku otsiriza. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Uyenera kudziŵa kuti m’masiku otsiriza nthaŵi zizadzala ndi ngozi. Anthu adzakhala odzikonda okha kwadzaoneni . . . Iwo adzakhala osayamika mpang’ono pomwe.”​—2 Timoteo 3:1, 2, Phillips.

Nthaŵi zina, kusyasyalika kumaloŵa m’malo mwa kuyamikira. Mawu oyamikira amachokera mumtima popanda kufuna kupindulapo kanthu. Komabe, kusyasyalika, kumene nthaŵi zambiri kumakhala kwaukathyali ndiponso kokokomeza, kungachokere pacholinga chobisika cha kufuna kukwezedwa kapena kupezerapo zinthu zina zaumwini. (Yuda 16) Kuwonjezera pa kunyenga munthu amene akuuzidwa zimenezo, kusyasyalika kotero kumakhala chipatso cha kunyada ndi kudzitukumula. Choncho, ndani angafune kusyasyalikidwa mwaukathyali? Koma kuyamikira kwenikweni kumatsitsimuladi moyo.

Munthu wosonyeza kuyamikira amapindula ndi kuchita zimenezo. Chikondi chimene amakhala nacho chifukwa chokhala woyamikira kuchokera pansi pa mtima chimamthandizira kukhala ndi chimwemwe ndi mtendere. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:13, 15.) Ndiponso popeza kuti ndi mkhalidwe wabwino, kuyamikira kumamtetezera kuti asakhale ndi malingaliro oipa monga mkwiyo, nsanje, ndi kuipidwa.

“Khalani Akuyamika”

Baibulo limatilimbikitsa kukulitsa mzimu woyamikira. Paulo analemba kuti: “M’zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Kristu Yesu.” (1 Atesalonika 5:18) Ndiponso Paulo analangiza Akolose kuti: “Mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yanu, . . . ndipo khalani akuyamika.” (Akolose 3:15) Masalmo ambiri ali ndi mawu oyamikira, zimene zikusonyeza kuti kuyamikira kochokera mumtima ndi mkhalidwe wabwino waumulungu. (Salmo 27:4; 75:1) Ndithudi, Yehova Mulungu amakondwera pamene tisonyeza kuyamikira pazinthu za tsiku ndi tsiku.

Koma kodi ndi zinthu zotani m’dziko lino losayamika zimene zimachititsa kuti kukulitsa mzimu woyamikira kukhale kovuta kwa ife? Kodi tingausonyeze motani mzimu woyamikira pamoyo watsiku ndi tsiku? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena