Akapolo a Anthu Kapena Atumiki a Mulungu?
“MBONI ZA YEHOVA ndi anthu ochititsadi chidwi.” Limatero buku lachijeremani lakuti Seher, Grübler, Enthusiasten (Olota, Osinkhasinkha, Achangu). Ngakhale kuti bukuli silikugwirizana ndi Mboni pamfundo zina, ilo likuvomereza kuti: “Kwenikweni, iwo amakhala moyo wopanda milandu, ndiponso ali ndi khalidwe labwino. Pantchito, iwo ndi akhama ndiponso osamala, ali nzika zabata ndiponso amakhoma misonkho moona mtima. Iwo amapeŵa kufunafuna chuma mopambanitsa. . . . Khalidwe lawo pamisonkhano nloyamikirika. Kudzipereka kwawo kwangolingana ndi kudzipereka kwa gulu lina lililonse lachipembedzo; ponena za utumiki iwo amapambana zipembedzo zonse. Koma chimene chimawachititsa kukhala oposa tchalitchi chachikristu china chilichonse ndi gulu lachikristu lina lililonse m’tsiku lathu ndicho kutsimikiza mtima kwadzaoneni kumene amakhala nako polengeza ziphunzitso zawo m’mikhalidwe yonse ndiponso moyang’anizana ndi ngozi zonse.”a
Ngakhale kuti ena akuyamikira motero, anthu ena akuyesa kufotokoza Mboni za Yehova m’njira yosiyanako. M’maiko ambiri kuzungulira dziko lapansi, a Mboni akhala akuchita utumiki wawo wachipembedzo kwa zaka zambirimbiri popanda kusokonezedwa. Anthu mamiliyoni ambiri amawadziŵa, amawalemekeza ndipo amavomereza kuti ali ndi ufulu wotsatira chipembedzo chawo. Tsopano kodi nchifukwa chiyani anthu ena akukayikira a Mboni za Yehova?
Mwinamwake chifukwa china chochititsa kukayikira kumeneku nchakuti posachedwapa magulu ena angapo achipembedzo azunza ana, mamembala ake ambiri adzipha, ndiponso achita ziukiro zaupandu. Nzoona kuti khalidwe loipa limeneli lili kulikonse, osati chabe pakati pa anthu achipembedzo. Komabe, ponena za chipembedzo, anthu ambiri akhala okayikira, ndipo ena akhala ankhanza.
Ngozi ya Kutsatira Anthu
“Kagulu ka mpatuko” kamasuliridwa kukhala “kagulu kotsatira chiphunzitso chapadera kapena mtsogoleri winawake.” Mofananamo, a mu “kagulu kamalaulo” amakhala “odzipereka kotheratu kwa munthu, ku lingaliro linalake, kapena ku chinthu chinachake.” Kwenikweni, mamembala a gulu lililonse lachipembedzo amene amatsatira atsogoleri aumunthu ndi malingaliro awo ali pangozi yokhala akapolo a anthu. Anthu otsatira kwambiri mtsogoleri winawake angaike pangozi malingaliro awo ndi mkhalidwe wawo wauzimu. Ngoziyo ingakule ngati munthuyo anakulira mumpatuko.
Kwenikweni, amene amanena zimenezi amakhala atatayika ngati amakhulupirira zolimba kuti ndi mmene a Mboni za Yehova akhalira. Iwo anganene kuti a Mboni ali m’gulu lachipembedzo limene limaika paukapolo mamembala ake, kuwalamulira mopondereza, kuwadyerera ufulu wawo, ndi kuwachititsa kukhala osiyana ndi anthu ena onse.
A Mboni za Yehova amadziŵa kuti zonena zimenezi nzosatsimikizirika. Nchifukwa chake akukupemphani kuti mudzifufuzire nokha. Mutafufuza zonse bwinobwino, pezani mayankho anuanu. Kodi a Mboni ali atumiki a Mulungu, monga momwe iwo eni amanenera, kapena kwenikweni ndi akapolo a anthu? Kodi nyonga yawo amaitenga kuti? Nkhani ziŵiri pamasamba 12-23 zidzapereka mayankho okhutiritsa pamafunso ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
a Kope loyamba la mu 1950 linalibe mawu apamwambawa. Choncho kuonekera kwake m’kope lokonzedwanso la mu 1982 kukusonyeza kuti anthu akuyamba kumvetsa ponena za Mboni za Yehova.