Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 2/15 tsamba 5-7
  • Kodi Mboni za Yehova Ndikagulu Kotsatira Munthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mboni za Yehova Ndikagulu Kotsatira Munthu?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Umboni Umasonyeza
  • Chipembedzo Chodziŵika Bwino
  • ‘Nzotanganitsidwa Kuthandiza Anthu’
  • Kumamatira Mosamalitsa ku Baibulo
  • Kodi Mtsogoleri Wawo Ndani?
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu la Mpatuko?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Timagulu Totsatira Anthu—Kodi Ito Nchiyani?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Akristu ndi Chitaganya cha Anthu Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 2/15 tsamba 5-7

Kodi Mboni za Yehova Ndikagulu Kotsatira Munthu?

YESU KRISTU ananenezedwa kukhala wakumwaimwa, wamadyaidya, wakuswa Sabata, mboni yonama, wochitira mwano Mulungu, ndi mthenga wa Satana. Ananenezedwanso kukhala woukira.​—Mateyu 9:34; 11:19; 12:24; 26:65; Yohane 8:13; 9:16; 19:12.

Imfa ndi chiukiriro cha Yesu zitachitika, ophunzira ake nawonso anali chandamale cha zinenezo zowopsa. Kagulu kena ka Akristu a m’zaka za zana loyamba kanakokeredwa kwa olamulira a mzinda ndi anthu omafuula kuti: ‘Anthu awa asanduliza dziko lokhalamo anthu.’ (Machitidwe 17:6) Panthaŵi ina mtumwi Paulo ndi tsamwali wake Sila anatengeredwa kwa olamulira ndi kuimbidwa mlandu wa kusokoneza kwambiri zinthu mumzinda wa Filipi.​—Machitidwe 16:20.

Pambuyo pake Paulo ananenezedwa kukhala munthu wonga “ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu” ndi wa kuyesa “kuipsa kachisi.” (Machitidwe 24:5, 6) Amuna otsogolera Achiyuda ku Roma anafotokoza molondola mkhalidwe wa otsatira a Yesu pamene anavomereza kuti: “Pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.”​—Machitidwe 28:22.

Mwachionekere, kagulu katsopano kameneka kokhazikitsidwa ndi Yesu Kristu kanalingaliridwa ndi ena kukhala kagulu kachipembedzo kokhala ndi malingaliro ndi machitachita osintha zinthu amene anawombana ndi zimene zinali zovomerezedwa m’masiku amenewo kukhala khalidwe labwino m’chitaganya. Mosakayikira, ambiri lerolino akanaona Akristu kukhala kagulu kowononga kotsatira munthu. Kaŵirikaŵiri oimba mlandu anali ziŵalo zachitaganya zotchuka ndi zolemekezedwa, ndipo zimenezi zikuwonekera kukhala zitawonjezera mphamvu ya zinenezo zimenezo. Ambiri anakhulupirira zinenezo zoperekedwa pa Yesu ndi ophunzira ake. Komabe, monga momwe mwinamwake mumadziŵira, chilichonse cha zinenezo zimenezi chinali chonama! Chenicheni chakuti anthu amanena zinthu zimenezi sichinapangitse zinthuzo kukhala zowona.

Bwanji nanga lerolino? Kodi kukakhala kolondola kutchula Mboni za Yehova kukhala gulu la chipembedzo lokhala ndi malingaliro a kusintha zinthu ndi machitachita amene amawombana ndi zimene zili zovomerezedwa kukhala khalidwe labwino m’chitaganya? Kodi Mboni za Yehova ndikagulu kotsatira munthu?

Zimene Umboni Umasonyeza

Mkulu wina waboma wa mzinda wa St. Petersburg, ku Russia, anafotokoza kuti: “Mboni za Yehova zinafotokozedwa kwa ife kukhala mpatuko wina wochita zinthu mobisa mumdima ndi kumapha ana ndi kudzipha.” Komabe, anthu a m’Russia posachedwapa afikira pakudziŵa mkhalidwe weniweni wa Mboni. Pambuyo pa kugwira ntchito ndi Mboni za Yehova yokhudza msonkhano wa mitundu yonse, mkulu waboma mmodzimodziyo anati: “Tsopano ndikuona anthu abwino, omwetulira, abwinodi kwambiri kuposa anthu ambiri amene ndimadziŵa. Iwo ngamtendere ndi abata, ndipo amakondana kwambiri.” Anawonjezera kuti: “Sindikumvetsetsa chifukwa chake anthu amawanamizira motero.”

Mboni za Yehova sizimachititsa misonkhano ya madzoma, ndiponso kulambira kwawo sikumachitidwa mwachinsinsi. Wolemba buku wina amene sali Mboni Julia Mitchell Corbett akunena kuti: “Pamene asonkhana, kaŵirikaŵiri koposa kamodzi pamlungu, m’Nyumba Zaufumu (malo awo osonkhanira samatchedwa matchalitchi), nthaŵi yawo yambiri imatheredwa m’phunziro la Baibulo ndi makambitsirano.” Malo awo osonkhanira amakhala ndi chikwangwani cholembedwa bwino. Misonkhanoyo njotsegukira munthu aliyense, ndipo anthu amaitanidwa kukafikapo. Alendo osaitanidwa alionse amalandiridwa kwambiri.

“Mboni zili ndi mbiri yabwino ya kukhala zowona mtima, zaulemu, ndi zachangu pantchito,” akuwonjezera motero Corbett m’buku lake lakuti Religion in America. Ambiri amene sali Mboni amavomereza mosavuta kuti palibe chinthu chilichonse chosadziŵika kapena chachilendo ponena za Mboni za Yehova. Khalidwe lawo silimawombana ndi zimene zimavomerezedwa kukhala khalidwe labwino m’chitaganya. The New Encyclopædia Britannica ikunena molondola kuti Mboni “zimaumirira pa lamulo lapamwamba la makhalidwe m’mayendedwe a munthu mwini.”

Mkulu wa nkhani ndi ntchito zapadera za siteshoni ya wailesi yakanema mu United States analembera Mboni za Yehova poyankha lipoti lolakwika lonena za Mboni paprogramu ya nkhani za pa TV yotchedwa 60 Minutes. Iye anati: “Ngati anthu ambiri akanakhala monga achipembedzo chanu, dzikoli silikanakhala monga momwe lilirimu. Ine ndine mmodzi wa oulutsa nkhani amene amadziŵa kuti gulu lanu nlozikidwa pachikondi ndi pachikhulupiriro cholimba mwa Mlengi. Ndikufuna kuti mudziŵe kuti sianthu onse Oulutsa Nkhani amene ali ndi malingaliro olakwika.”

Chipembedzo Chodziŵika Bwino

Kodi kunena kuti Mboni za Yehova ndikagulu kachipembedzo kakang’ono kotengeka maganizo nkoyenera? M’lingaliro lina, Mboni za Yehova zili ndi chiŵerengero chochepa poyerekezera ndi zipembedzo zina. Komabe, kumbukirani zimene Yesu ananena: “Chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”​—Mateyu 7:13, 14.

Mulimonse mmene zingakhalire, Mboni sizili kagulu kakang’ono kotsatira munthu kotengeka maganizo mpang’ono pomwe. M’ngululu ya 1993, anthu mamiliyoni 11 anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu cha Mboni. Koma chofunika koposa chiŵerengero chawo ndicho khalidwe lawo labwino, limene lawachititsa kuyamikiridwa padziko lonse. Mosakayikira zimenezi ndizo zachitika m’maiko amene awaloleza mwalamulo kukhala chipembedzo chenicheni.

Kwapadera ndiko kugamulidwa kwa mlandu kochitidwa ndi European Commission of Human Rights. Bungweli linalengeza kuti Mboni ziyenera kupatsidwa ufulu wa kulingalira, chikumbumtima, ndi chipembedzo ndi kuti zili ndi kuyenera kwa kulankhula za chikhulupiriro chawo ndi kuchiphunzitsa kwa ena. Zimenezi sizikanatheka ngati Mboni za Yehova zinadziŵika kukhala zogwiritsira ntchito chinyengo ndi njira zosemphana ndi makhalidwe abwino kupezera ziŵalo zake kapena ngati zinagwiritsira ntchito njira zamachenjera kulamulira maganizo a otsatira awo.

Unyinji wa anthu kuzungulira padziko lonse umadziŵa bwino Mboni za Yehova. Ponena za mamiliyoni amene sali Mboni amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni kapena amene aphunzira nazo panthaŵi ina, tikuwafunsa kuti, Kodi panali kuyesayesa kulikonse kwa kusukuluza maganizo anu? Kodi Mbonizo zinagwiritsira ntchito njira zolamulira maganizo anu? Mosakayikira inu mosabisa mawu mukayankha kuti “Ayi.” Mwachionekere, ngati njira zimenezi zikanagwiritsiridwa ntchito, pakanakhala chiŵerengero chachikulu koposa cha mikhole yake yotsutsa ndemanga iliyonse yoyanja Mboni za Yehova.

‘Nzotanganitsidwa Kuthandiza Anthu’

Ziŵalo za kagulu kotsatira munthu zimatalikirana ndi mabanja, mabwenzi, ndipo ngakhale ndi anthu onse. Kodi zimenezo zili choncho ndi Mboni za Yehova? “Sindili wa Mboni za Yehova,” analemba motero mwamuna wina wofalitsa nkhani ku Czech Republic. Komabe iye anawonjezera kuti: “Nkwachionekere kuti izo [Mboni za Yehova] zili ndi nyonga yaikulu kwambiri ya makhalidwe abwino. . . . Zimalemekeza maboma olamulira koma zimakhulupirira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo umene ukhoza kuthetsa mavuto onse a mtundu wa anthu. Komatu dziŵani​—izo sizotengeka maganizo. Izo zili anthu otanganitsidwa kuthandiza anthu.”

Ndipo sizimakhala zokhazokha, zikumadzipatula kwa achibale ndi ena. Mboni za Yehova zimazindikira kuti ndithayo lawo Lamalemba kukonda ndi kusamalira mabanja awo. Zimakhala ndi kugwira ntchito ndi anthu a mafuko onse ndi zipembedzo. Pamene tsoka likantha, zimafulumira kupereka katundu wachithandizo ndi chithangato china chabwino.

Chofunika kwambiri nchakuti, zili ndi programu ya maphunziro imene ili yosayerekezeredwa ndi ina iliyonse. Kodi ndizipembedzo zingati zimene zili ndi dongosolo lolinganizika lofikira munthu aliyense m’chitaganya chawo? Mboni za Yehova zimachita zimenezi m’maiko oposa 200 ndi m’zinenero zoposa 200! Mwachionekere, Mboni za Yehova ‘nzotanganitsidwa kuthandiza anthu.’

Kumamatira Mosamalitsa ku Baibulo

Zowonadi, ziphunzitso za Mboni za Yehova nzosiyana ndi zija zophunzitsidwa ndi matchalitchiwo. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Yehova ndiye Mulungu wamphamvuyonse ndi kuti Yesu ndiye Mwana wake, osati mbali ya mulungu wautatu. Chikhulupiriro chawo nchogwirizana zolimba ndi chiphunzitso chakuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungadzetse chitonthozo kwa anthu ovutika. Zimachenjeza anthu ponena za chiwonongeko chimene chayandikira cha dongosolo lino loipa la zinthu. Zimalalikira za lonjezo la Mulungu la paradaiso wa padziko lapansi wa anthu omvera. Sizimalambira mtanda. Sizimakondwerera Krisimasi. Zimakhulupirira kuti moyo umafa ndi kuti kulibe moto wa helo. Sizimadya mwazi, ndipo sizimavomereza kuthiridwa mwazi. Siziloŵa m’ndale zadziko ndi kukhala ndi phande m’nkhondo. Kodi munayamba mwadzifunsapo chifukwa chake ziphunzitso za Mboni za Yehova zili zosiyana kwambiri chotero?

Nyuzipepala ina ya ku Massachusetts, yotchedwa Daily Hampshire Gazette, ikufotokoza kuti “mamasuliridwe [a Mboni za Yehova] osamalitsa a Baibulo amaletsa machitachita amene ambiri amawalingalira kukhala oyenera . . . , akuchita zonsezo kuyesayesa kutsatira chitsanzo cha Akristu a m’zaka za zana loyamba ndi mawu a Baibulo.” The Encyclopedia of Religion imavomereza kuti “zonse zimene amakhulupirira nzozikidwa pa Baibulo. Iwo ‘amatsimikizira umboni ndi lemba’ (ndiko kuti, amapereka lemba la Baibulo lochirikiza) pamawu aliwonse a chiphunzitso, akumavomereza mosakayikira ulamuliro wa Baibulo, umene umatsutsa mwambo kotheratu.” Buku lakuti Religion in America limati: “Gululo silinagwedezeke konse pakugogomezera kwake phunziro la Baibulo, ndipo ziphunzitso zake zimachirikizidwa ndi dongosolo lolinganizidwa mosamalitsa la zisonyezero za malemba.”

Kodi Mtsogoleri Wawo Ndani?

Chilidi chifukwa cha kumamatira ku ziphunzitso za Baibulo kumeneku kuti kupembedzedwa ndi kulambiridwa kwa atsogoleri aumunthu kochitidwa ndi timagulu totsatira anthu lerolino sikumapezeka pakati pa Mboni za Yehova. Izo zimakana lingaliro la kusiyanitsa kagulu ka atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba olambira. The Encyclopedia of Religion ikunena molunjika za Mboni za Yehova kuti: “Kagulu ka atsogoleri achipembedzo ndi maina aulemu apadera nzoletsedwa.”

Amatsatira Yesu Kristu monga Mtsogoleri wawo ndiponso monga Mutu wa mpingo Wachikristu. Anali Yesu amene anati: “Musatchedwa Rabi; pakuti mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa kumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.”​—Mateyu 23:8-12.

Nkwachionekere kuti Mboni za Yehova sizili konse kagulu kotsatira munthu monga momwe Yesu sanaliri wamadyaidya ndi wakumwaimwa. Zowonadi, sialiyense amene anasonkhezeredwa ndi malipoti onama onena za Yesu ndi ophunzira ake amene anagwera mumsampha wa kumneneza. Ena angakhale atangouzidwa molakwa. Ngati muli ndi zikayikiro ponena za Mboni za Yehova ndi zikhulupiriro zawo, bwanji osadziŵana nawo bwinopo? Awo onse amene akufunafuna chowonadi ali olandiridwa kwambiri pa Nyumba zawo Zaufumu.

Nanunso mungapindule ndi kufufuza kwawo kosamalitsa chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo ndi kuphunzira mmene mungalambirire Mulungu mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.”​—Yohane 4:23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena