Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwfq nkhani 31
  • Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu la Mpatuko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu la Mpatuko?
  • Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi mawu akuti mpatuko amatanthauza chiyani?
  • Timagulu Totsatira Anthu—Kodi Ito Nchiyani?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Mboni za Yehova Ndikagulu Kotsatira Munthu?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Unamwali—Chifukwa Ninji?
    Galamukani!—1996
  • Chinsinsi m’Dzina la Ambuye
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
ijwfq nkhani 31
One of Jehovah’s Witnesses teaching a literacy class to a group of people.

Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu la Mpatuko?

Ayi, a Mboni za Yehova si gulu la mpatuko. M’malomwake, ndife Akhristu ndipo timayesetsa kutsanzira chitsanzo cha Yesu Khristu komanso kuchita zimene iye anatiphunzitsa.

Kodi mawu akuti mpatuko amatanthauza chiyani?

Anthu amatanthauzira mawu akuti “mpatuko” mosiyanasiyana. Komabe, m’nkhaniyi tiona zinthu ziwiri zimene anthu ambiri amaganiza akamva mawuwa. Tionanso kusiyana kwa zinthu zimenezi ndi mmene ifeyo tilili.

  • Ena amaganiza kuti a mpatuko ndi gulu logalukira ku chipembedzo china n’kuyambitsa chawo. A Mboni za Yehova sanayambitse chipembedzo chatsopano. M’malomwake, timalambira mofanana ndi mmene Akhristu oyambirira ankachitira, ndipo zimene ankachita komanso zimene ankaphunzitsa zinalembedwa m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16, 17) Timakhulupirira kuti anthu ayenera kutsatira zimene Malemba Opatulika amanena pa nkhani yokhudza kulambira.

  • Anthu ena akamva za mpatuko amaganiza za gulu loopsa lachipembedzo lokhala ndi munthu wolitsogolera. A Mboni za Yehova alibe munthu amene amamuona kuti ndi mtsogoleri wawo. M’malomwake, timatsatira zimene Yesu anauza ophunzira ake pamene ananena kuti: “Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”​—Mateyu 23:10.

A Mboni za Yehova si gulu loopsa la mpatuko. Iwo amachita zinthu zimene zimathandiza anthu a m’chipembedzo chawo komanso anthu a m’dera limene akukhala. Mwachitsanzo, ntchito yathu yolalikira yathandiza anthu ambiri kusiya makhalidwe oipa, monga kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Kuwonjezera pamenepa, padziko lonse lapansi timathandiza anthu ambirimbiri kuphunzira kuwerenga ndi kulemba. Komanso timathandiza pakagwa masoka a chilengedwe. Timagwira ntchito mwakhama pothandiza ena, ndipo izi n’zimene Yesu analamula otsatira ake kuti azichita.​—Mateyu 5:13-16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena