Unamwali—Chifukwa Ninji?
“CHIPHUNZITSO cha unamwali”—ndimo mmene Randall Balmer, mmodzi wa maprofesa achipembedzo pa Barnard College/Columbia University, akutchera mkhalidwe womwe ukuoneka kukhala ukukula pakati pa achichepere wa kukankhira mtsogolo kugonana kufikira atakhala achikulire.
Mosadabwitsa, chilimbikitso chochuluka cha kupeŵa kugonana chikuchokera m’magulu azipembedzo. “Koma chisonkhezero cha chiphunzitso cha unamwali nchochokera m’dziko, osati m’chipembedzo,” akusonyeza motero Dr. Balmer. “Chisonkhezero chenicheni chokhalira namwali ndicho mantha—osati kuwopa chilango cha Mulungu, koma kuwopa nthenda yakupha.” Motero, iye akusiyanitsa “chiphunzitso cha Namwali Mariya,” chimene chinasonyeza kusagonanako kukhala chonulirapo chachipembedzo, ndi “chiphunzitso cha unamwali” chamakono, chimene chimasonyeza kusagonanako makamaka monga nkhani ya zaumoyo.
“Ndi chitsanzo chochititsa chisoni ponena za mkhalidwe wa chipembedzo m’ma 1990 kuti kuwopa nthenda nkumene kukulamulira makhalidwe,” akupitiriza motero Dr. Balmer. “Atsogoleri achipembedzo, amene ali osafuna mpang’ono pomwe kukwiyitsa anthu, avomereza mkhalidwe wosalimba, kapena kungolekerera zinthu. Motero asiyira asayansi ndi akuluakulu azaumoyo wa anthu kulangiza achichepere za mmene angachitire ndi moyo wawo m’zakugonana.”
Komabe, zimenezi sizili choncho kwa Akristu enieni. Lingalirani za Chad, wachichepere amene akuleredwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Mtsikana wina anafikira Chad nayamba kucheza naye. Komano posapita nthaŵi kunali kwachionekere kuti zolinga zake sizinali za kungocheza chabe. “Ndiyeno lingaliro linandifikira,” akutero Chad. “Sindikanatha kugwiritsa mwala Yehova. Pokhala ndi lingaliro la kufuna kukondweretsa Yehova nthaŵi zonse, ndinamuuza kuti ndikuchoka.”
Mofanana ndi Chad, achichepere ambiri pakati pa Mboni za Yehova akusunga makhalidwe abwino osati kokha chifukwa chakuti akhale athanzi labwino koma makamaka kuti akondweretse Mlengi wawo, Yehova Mulungu. Makhalidwe awo samalamuliridwa ndi kuwopa nthenda. M’malo mwake, achichepere amenewo amatsatira uphungu wa Mlaliki 12:1 wakuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.”