Sanadzipangire Dzina
BAIBULO siliwatchula maina anthu omwe anamanga nsanja yotchuka ndi mbiri yoipa, nsanja ya Babele. Nkhaniyo imati: “Ndipo [iwo, NW] anati, Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.”—Genesis 11:4.
Kodi “iwo” anali ndani? Zimenezi zinachitika pafupifupi zaka 200 pambuyo pa Chigumula. Panthaŵiyo Nowa, yemwe anali ndi zaka pafupifupi 800, anali kukhala ndi zidzukulu zake zikwizikwi. Onse anali kulankhula chinenero chimodzi ndipo anali kukhala dera limodzi kumene iye ndi ana ake anakhazikikako pambuyo pa Chigumula. (Genesis 11:1) Panthaŵi ina yake, ena a anthu omawonjezerekawa analoŵera kummaŵa ndipo “anapeza chigwa m’dziko la Sinara.”—Genesis 11:2.
Kulephereratu
Ndi m’chigwachi mmene gululi linaganiza zopandukira Mulungu. Motani? Eya, Yehova Mulungu anasonyeza chifuno chake pamene analamula anthu aŵiri oyambawo kuti ‘abalane, achuluke, adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Pambuyo pa Chigumula, Nowa ndi ana ake anauzidwanso mawuwa. Mulungu anawalangiza kuti: “Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane padziko lapansi, nimuchuluke mmenemo.” (Genesis 9:7) Posemphana ndi chitsogozo cha Yehova, anthuwa anamanga mudzi ncholinga chakuti “[a]sabalalike padziko lonse lapansi.”
Anthuwa anayambanso kumanga nsanja ncholinga chakuti adzipangire “dzina.” Koma mosemphana ndi zimene anali kuyembekezera, iwo sanamalize kumanga nsanjayo. Baibulo limasimba kuti Yehova anasokoneza chinenero chawo kotero kuti sanamvane. “Ndipo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi,” imatero nkhani youziridwayo.—Genesis 11:7, 8.
Kulephereka kotheratu kwa ntchitoyi kukusonyezedwa nchakuti anthu omangawo sanadzipangire “dzina” konse, kapena kutchuka. Kwenikweni, maina awo sakudziŵika ndipo mulibe m’mbiri ya anthu. Koma bwanji za chidzukulu tubzi cha Nowa, Nimrode? Kodi iye sindiye anatsogolera kupandukira Mulungu kumeneku? Kodi dzina lake silotchuka?
Nimrode—Wopanduka Wachipongwe
Mosakayikira, Nimrode anali mtsogoleri wa opandukawo. Genesis chaputala 10 akumsonyeza kukhala “mpalu wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.” (Genesis 10:9, NW) Malemba amanenanso kuti “iye anayamba kukhala wamphamvu padziko lapansi.” (Genesis 10:8) Nimrode anali mwamuna wankhondo, munthu wachiwawa. Anadzilonga ufumu ndipo anali munthu woyamba kulamulira pambuyo pa Chigumula. Nimrode analinso mmisiri womanga nyumba. Baibulo limamtchula kuti anamangitsa mizinda isanu ndi itatu, kuphatikizapo Babele.—Genesis 10:10-12.
Motero Nimrode—wotsutsa Mulungu, mfumu ya Babele, ndi womanga mizinda—mosakayikira anamanga nawo nsanja ya Babele. Kodi iye sanadzipangire dzina? Ponena za dzinalo Nimrode, wophunzira wa Kummaŵa E. F. C. Rosenmüller analemba kuti: “Nimrode anapatsidwa dzinali kuchokera ku liwu lakuti [ma·radhʹ], ‘anapanduka,’ ‘analekana nawo namachita zina,’ mogwirizana ndi tanthauzo lachihebri.” Ndiyeno Rosenmüller akulongosola kuti “anthu a Kummaŵa anazoloŵera kutchula anthu awo otchuka ndi maina omwe awapatsa atamwalira, zimene nthaŵi zambiri zimachititsa kugwirizana kodabwitsa kwa maina ndi zinthu zomwe anthuwo anachita.”
Akatswiri ambiri a zamaphunziro amavomerezana kuti dzina lakuti Nimrode si dzina la paukhanda. M’malo mwake amati ndi dzina lomwe anapatsidwa panthaŵi ina pomgwirizanitsa ndi mkhalidwe wake waupandu pamene unadziŵika. Mwachitsanzo, C. F. Keil anati: “Dzinalo Nimrode kuchokera ku liwu lakuti [ma·radhʹ], ‘tidzaukira,’ limasonyeza kutsutsana ndi Mulungu mwachiwawa. Tanthauzo lake nlachindunji kotero kuti anthu omwe anali ndi moyo pamene iye anali moyo ndi okhawo anakampatsa dzinali, choncho linakhala dzina lake lenileni.” M’mawu amtsinde Keil anagwira mawu wolemba mbiri Jacob Perizonius kuti analemba kuti: “Ndingakhulupirire kuti munthuyu [Nimrode], monga mlenje woopsa ndipo wokhala ndi mabwenzi ake pafupi, pofuna kupandutsa anthu onse, nthaŵi zonse anali kunena mobwerezabwereza liwulo ‘nimrode, nimrode,’ ndiko kuti, ‘Tiyeni tipanduke! Tiyeni tipanduke!’ Motero pambuyo pake, anthu ena kuphatikizapo Mose iye mwini, anampatsa liwulo kukhala dzina lake lenileni.”
Mwachionekere, Nimrode sanadzipangire konse dzina. Dzina lake la paukhanda nlosadziŵika. Mulibe m’mbiri, monganso maina a anthu omwe anamtsatira. Analibe ngakhale mwana woti adzatenge dzina lake. M’malo molandira ulemu ndi kutchuka, iye wadziŵika ndi mbiri yoipa. Kunthaŵi zonse, dzinalo Nimrode lamdziŵikitsa kuti ndi wopanduka wachipongwe amene anatsutsana mopusa ndi Yehova Mulungu.