Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 3/15 tsamba 18-23
  • Kukhala Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwachikristu mu Ufulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwachikristu mu Ufulu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mzimu wa Mulungu Umapangitsa Kuti Pasakhale Malamulo Ambiri
  • Kudziŵerengera Mlandu ku Bungwe Lolamulira?
  • Ophunzira ndi Asilikali
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi “Kapolo Wokhulupirika Ndi Wanzeru” Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 3/15 tsamba 18-23

Kukhala Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwachikristu mu Ufulu

“Pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.”​—2 AKORINTO 3:17.

1. Kodi Mboni za Yehova zili zodzipatulira kwa ndani, ndipo nchifukwa ninji amagwiritsira ntchito mabungwe alamulo?

MBONI ZA YEHOVA zimakhulupirira kuti chipembedzo chawo chidzakhalapo kosatha. Choncho iwo amayembekeza kuti adzatumikira Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi” kwamuyaya. (Yohane 4:23, 24) Monga anthu amene ali ndi ufulu wodzisankhira, Akristu ameneŵa anadzipatulira kotheratu kwa Yehova Mulungu ndipo ali otsimikiza mtima kukhala mogwirizana ndi kudzipatulira kumeneku. Kuti akwaniritse zimenezo, iwo amadalira Mawu a Mulungu ndi mzimu wake woyera. Pamene iwo atsatira ndi mtima wonse njira ya kudzipatulira kwawo kwachikristu mu ufulu wopatsidwa ndi Mulungu, Mboni zimapereka ulemu woyenerera kwa “maulamuliro aakulu” a maboma ndiponso amagwiritsira ntchito moyenerera malamulo a boma ndi makonzedwe ake. (Aroma 13:1; Yakobo 1:25) Mwachitsanzo, Mboni zimagwiritsira ntchito Watch Tower Society monga bungwe lalamulo​—limodzi mwa mabungwe ambiri m’maiko osiyanasiyana​—kuti iwathandize kukwaniritsa ntchito yawo yothandiza anthu anzawo, makamaka m’zinthu zauzimu. Koma Mboni zili zodzipatulira kwa Mulungu, osati ku bungwe lina lililonse lalamulo, ndipo kudzipatulira kwawo kwa Yehova kudzakhalapo kosatha.

2. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimayamikira kwambiri Watch Tower Society ndi mabungwe ena alamulo ofananawo?

2 Monga atumiki odzipatulira kwa Mulungu, Mboni za Yehova ziyenera kutsatira malangizo a Yesu a ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa.’ (Mateyu 28:19, 20) Ntchito imeneyi idzapitirizabe mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu, popeza kuti Yesu ananenanso kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:3, 14) Chaka chilichonse, mafakitale osindikiza a Watch Tower Society ndi mabungwe enanso ofananawo amapereka kwa Mboni za Yehova, mamiliyoni a mabaibulo, mabuku, mabrosha, ndi magazini kuti azigwiritsira ntchito pantchito yawo yolalikira ya padziko lonse. Choncho, mabungwe alamulo ameneŵa ngofunika kwambiri pothandiza atumiki a Mulungu kuti akhalebe mogwirizana ndi kudzipatulira kwawo kwa iye.

3. Kodi kale Mboni za Yehova zinali kugwiritsira ntchito mawu akuti “Sosaite” m’lingaliro lotani?

3 Wina anganene kuti mmene Mboni zimanenera za Watch Tower Society​—kapena kuti “Sosaite” monga momwe amaitchulira kaŵirikaŵiri​—zimasonyeza kuti amaiona ngati si bungwe lalamulo chabe. Kodi iwo saiona monga ulamuliro womaliza pankhani zokhudza kulambira? Buku lotchedwa Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom limafotokoza bwino lomwe mfundo imeneyi kuti: “Pamene Nsanja ya Olonda yachingelezi [June 1, 1938] inatchula za ‘Sosaite,’ zimenezi zinatanthauza bungwe la Akristu odzozedwa amene anapanga bungwe lalamulo limenelo ndi kuligwiritsira ntchito osati bungwe lalamulo wamba ayi.”a Choncho, mawu ameneŵa anaimira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Kaŵirikaŵiri Mboni zinali kugwiritsira ntchito mawu akuti “Sosaite” m’lingaliro limeneli. Ndithudi, mawu akuti bungwe lalamulo sagwiritsiridwa ntchito mofanana ndi mawu akuti “kapolo wakhulupirika ndi wanzeru.” Oyang’anira Watch Tower Society amachita kusankhidwa, pamene Mboni zimene zimapanga “kapolo wokhulupirika” zimachita kudzozedwa ndi mzimu wa Yehova.

4. (a) Kodi Mboni zambiri zimalankhula motani pofuna kupeŵa kumvana molakwa? (b) Nchifukwa ninji sitiyenera kudera nkhaŵa mopambanitsa ponena za katchulidwe ka zinthu?

4 Pofuna kupeŵa kumvana molakwa, Mboni za Yehova zimayesetsa kusamala pamene zilankhula. M’malo monena kuti, “Sosaite imaphunzitsa kuti,” Mboni zambiri zimakonda kugwiritsira ntchito mawu akuti, “Baibulo limati” kapena, “Ndimakhulupirira kuti Baibulo limaphunzitsa kuti.” Mwa njira imeneyi iwo amagogomezera chosankha chaumwini chimene Mboni iliyonse inadzipangira povomereza ziphunzitso za m’Baibulo ndiponso amapeŵa kupereka malingaliro onama akuti Mboni zimadalira kwambiri chitsogozo cha olamulira a gulu linalake la chipembedzo. Komabe, malingaliro okhudza katchulidwe ka zinthu sayenera kukhala nkhani yoyambitsa mikangano. Kunena zoona, katchulidwe ka zinthu kali kothandiza chifukwa chakuti kamapangitsa kuti pasakhale kumvana molakwa. Kuchita zinthu moyenerera kwachikristu nkofunika. Baibulo limatilangiza kuti ‘tisachite makani ndi mawu.’ (2 Timoteo 2:14, 15) Malemba amatchulanso pulinsipulo ili: “Inu ngati mwa lilime simupereka mawu omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa?”​—1 Akorinto 14:9.

Mzimu wa Mulungu Umapangitsa Kuti Pasakhale Malamulo Ambiri

5. Kodi mawu a pa 1 Akorinto 10:23 tingawamvetse motani?

5 “Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse,” anatero mtumwi Paulo. Iye anawonjezera kuti: “Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.” (1 Akorinto 10:23) Mwachionekere, Paulo sanatanthauze kuti kuli kololeka kuchita zinthu zimene Mawu a Mulungu amatsutsiratu. Poyerekezera ndi malamulo pafupifupi 600 opatsidwa kwa Aisrayeli akale, moyo wachikristu umalamuliridwa ndi malamulo achindunji ochepa kwambiri mosiyana ndi amenewo. Choncho, nkhani zambiri zimadalira pa chikumbumtima cha munthu aliyense payekha. Munthu amene anadzipatulira kwa Yehova amakhala ndi ufulu umene umadza mwa kutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu. Popeza kuti anatenga choonadi kukhala chakechake, Mkristu amatsatira chikumbumtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo ndipo amadalira chitsogozo cha Mulungu mwa mzimu woyera. Zimenezi zimathandiza Mkristu wodzipatulira kulingalira za zinthu ‘zomangirira’ ndiponso zimene zidzakhala ‘zopindulitsa’ kwa iyemwini ndi ena. Iye amazindikira kuti zosankha zimene apanga zidzakhudza unansi wake ndi Mulungu, popeza kuti anadzipatulira kwa iye.

6. Pamisonkhano yachikristu, kodi tingasonyeze motani kuti tapanga choonadi kukhala chathuchathu?

6 Mboni imasonyeza kuti inatenga choonadi kukhala chakechake mwa kuyankhapo pamisonkhano yachikristu. Choyamba, iye amangobwereza zimene zafotokozedwa m’chofalitsa chimene chikuphunziridwa. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, iye amapita patsogolo ndipo amatha kufotokoza ziphunzitso za m’Baibulo m’mawu akeake. Choncho, iye amapereka umboni wakuti akukulitsa luso lake la kuganiza osati kungobwereza zimene ena anena kale. Pamene afotokoza mfundo m’mawu akeake ndi kunena mawu olondola a choonadi kuchokera pansi pa mtima zidzampatsa chimwemwe ndiponso zidzasonyeza kuti ali wokhutiritsidwa mumtima mwake.​—Mlaliki 12:10; yerekezerani ndi Aroma 14:5b.

7. Kodi ndi zosankha ziti zimene atumiki a Yehova apanga mwaufulu?

7 Mboni za Yehova zimasonkhezeredwa ndi chikondi chawo cha pa Mulungu ndi munthu mnzawo. (Mateyu 22:36-40) Zoonadi, iwo ngolunzanitsidwa ndi chomangira cha chikondi chonga cha Kristu monga gulu la abale lapadziko lonse. (Akolose 3:14; 1 Petro 5:9) Komatu monga munthu wokhala ndi ufulu wa kudzisankhira, aliyense analingalira yekha zoti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, kusunga uchete pankhani zandale, kukana magazi, kupeŵa mitundu ina ya zosangulutsa, ndiponso kukhala mogwirizana ndi malamulo a m’Baibulo. Iwo sanakakamizidwe kupanga zosankha zimenezi. Zimenezi ndi zosankha zimene zili mbali ya njira ya moyo imene anthu oyembekeza kukhala Mboni amapanga asanapange nkomwe kudzipatulira kwachikristu.

Kudziŵerengera Mlandu ku Bungwe Lolamulira?

8. Kodi ndi funso liti limene liyenera kufotokozedwa bwino lomwe?

8 Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti Akristu oona satumikira Mulungu mokakamizidwa. Ilo limati: “Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Koma kodi tingagwirizanitse motani mfundo imeneyi ndi lingaliro la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi Bungwe lake Lolamulira?​—Mateyu 24:45-47.

9, 10. (a) Kodi pulinsipulo la umutu limagwira ntchito motani mumpingo wachikristu? (b) Kodi kutsatira pulinsipulo la umutu kunatheketsa chiyani mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba?

9 Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenera kukumbukira pulinsipulo la m’Malemba lonena za umutu. (1 Akorinto 11:3) Pa Aefeso 5:21-24, Kristu akutchulidwa kuti ndiye “mutu wa Eklesia [“mpingo,” NW],” umene mpingo “umvera.” Mboni za Yehova zimadziŵa kuti kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amapangidwa ndi abale auzimu a Yesu. (Ahebri 2:10-13) Gulu limeneli la kapolo wokhulupirika linaikidwa kuti lizipatsa anthu a Mulungu ‘chakudya [chauzimu] panthaŵi yake.’ M’nthaŵi ino yamapeto, Kristu anakhazika kapolo ameneyu kuti akhale “woyang’anira zinthu zake zonse.” Choncho, chifukwa cha udindo umenewu, kapoloyu ayenera kulemekezedwa ndi munthu aliyense wodzinenera kukhala Mkristu.

10 Cholinga cha umutu ndicho kusunga umodzi ndi kuonetsetsa kuti “zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.” (1 Akorinto 14:40) Pofuna kukwaniritsa zimenezi m’zaka za zana loyamba, Akristu odzozedwa angapo ochokera m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anasankhidwa kuti aziimira gulu lonselo. Monga momwe zochitika zotsatirapo zinasonyezera, uyang’aniro umene unachitika ndi bungwe lolamulira limeneli la m’zaka za zana loyamba unali wovomerezeka ndiponso unadalitsidwa ndi Yehova. Akristu a m’zaka za zana loyamba anagwirizana mosangalala ndi makonzedwe ameneŵa. Inde, iwo analandiradi ndi kuyamikira zotsatirapo zake zosangalatsa.​—Machitidwe 15:1-32.

11. Kodi Bungwe Lolamulira lamakono liyenera kuonedwa motani?

11 Makonzedwe ameneŵa ali ofunikabe mpaka lero. Tsopano, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lili ndi Akristu khumi odzozedwa, ndipo onsewo akhala Akristu kwa zaka zambirimbiri. Iwo amapereka chitsogozo chauzimu kwa Mboni za Yehova, monga momwe linachitira bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba. (Machitidwe 16:4) Mofanana ndi Akristu oyambirira, Mboni zimadalira mosangalala abale okhwima a m’Bungwe Lolamulira kuti zipeze chitsogozo chozikidwa pa Baibulo pankhani zokhudza kulambira. Ngakhale kuti mamembala a m’Bungwe Lolamulira ali akapolo a Yehova ndi Kristu, monga momwe alili Akristu anzawo, Baibulo limatilangiza kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.”​—Ahebri 13:17.

12. Kodi Mkristu aliyense payekha ayenera kuŵerengera mlandu wake kwa ndani?

12 Kodi udindo woyang’anira umene Malemba amapereka ku Bungwe Lolamulira umatanthauza kuti aliyense wa Mboni za Yehova ayenera kuŵerengera ntchito zake ku bungwelo? Zimenezo zingakhale zosagwirizana ndi mawu a Paulo kwa Akristu a ku Roma kuti: “Iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu . . . Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.”​—Aroma 14:10-12.

13. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimapereka lipoti la ntchito yawo yolalikira?

13 Komabe, kodi sizoona kuti Mboni iliyonse imayenera kupereka lipoti la ntchito yake yolalikira? Inde, koma cholinga chake chikufotokozedwa bwino lomwe m’buku lamalangizo la Mboni, limene limati: “Otsatira Yesu Kristu oyambirira anakondwera ndi malipoti a kupita patsogolo m’ntchito yolalikira. (Marko 6:30) Pamene ntchitoyo inakula, malipoti aziŵerengero anasonkhanitsidwa limodzi ndi nkhani za zokumana nazo zapadera za awo okhala ndi phande m’kulalikira mbiri yabwino. . . . (Machitidwe 2:5-11, 41, 47; 6:7; 1:15; 4:4, NW) . . . Kunali kolimbikitsa chotani nanga kwa antchito okhulupirika Achikristu amenewo kumva malipoti a zimene zinalinkuchitidwa! . . . Mofananamo, gulu lamakono la Yehova limayesayesa kusunga zolembedwa zolongosoka za ntchito yochitidwa mokwaniritsa Mateyu 24:14, NW.”

14, 15. (a) Kodi mawu a pa 2 Akorinto 1:24 amakhudza motani Bungwe Lolamulira? (b) Kodi zosankha zaumwini za Mkristu aliyense payekha ziyenera kuzikidwa pa chiyani, ndipo ayenera kuchita zimenezo pozindikira nkhani iti?

14 Bungwe Lolamulira lili chogaŵira chachikondi ndiponso chitsanzo cha chikhulupiriro chimene tingachitsanzire. (Afilipi 3:17; Ahebri 13:7) Mwa kumamatira kwawo Kristu ndi kutsatira chitsanzo chake, iwo angabwerezenso kunena mawu a Paulo akuti: “Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.” (2 Akorinto 1:24) Mwa kuyang’anitsitsa pazimene zikuchitika, Bungwe Lolamulira limasumika maganizo pa mapindu a kutsatira uphungu wa m’Baibulo, limapereka malingaliro a mmene malamulo ndi mapulinsipulo a m’Baibulo tingawagwiritsire ntchito, limachenjeza za zoopsa zobisika, ndiponso limapereka chilimbikitso chofunika kwa ‘othandizana nawo.’ Choncho, bungweli limachita udindo wake wachikristu, kuwathandiza kuti asungebe chimwemwe chawo, ndiponso kumangirira chikhulupiriro chawo kotero kuti akhalebe olimba.​—1 Akorinto 4:1, 2; Tito 1:7-9.

15 Ngati Mboni ina ipanga zosankha zake zozikidwa pa uphungu wa m’Baibulo woperekedwa ndi Bungwe Lolamulira, iye amatero mwa kufuna kwake chifukwa chakuti phunziro lake laumwini la Baibulo lampangitsa kukhulupirira kuti chosankha chakecho nchoyenerera. Mboni iliyonse imasonkhezeredwa kwambiri ndi Mawu a Mulungu kuti itsatire uphungu wofunika wa m’Malemba woperekedwa ndi Bungwe Lolamulira, akumazindikira bwino lomwe kuti zosankha zimene iye apanga zidzakhudza unansi wake ndi Mulungu, popeza kuti anadzipatulira kwa iye.​—1 Atesalonika 2:13.

Ophunzira ndi Asilikali

16. Ngakhale kuti zosankha zokhudzana ndi makhalidwe zili nkhani yaumwini, kodi nchifukwa ninji ena amachotsedwa?

16 Koma ngati munthu amayenera kupanga chosankha chaumwini chokhudzana ndi makhalidwe ena, nanga nchifukwa ninji ena a Mboni za Yehova amachotsedwa? Palibe munthu amene ali ndi udindo wonena kuti munthu wochita tchimo lakutilakuti ayenera kuchotsedwa. M’malo mwake, kuchotsa nkofunika mwa Malemba kokha pamene munthu wina wamumpingomo achita machimo aakulu mosalapa, monga amene analembedwa m’chaputala chachisanu cha Akorinto Woyamba. Choncho, pamene kuli kwakuti Mkristu amachotsedwa atachita chigololo, zimenezi zimachitika kokha pamene munthuyo sakuvomereza chithandizo chauzimu cha abusa achikondi. Mboni za Yehova si okhawo amene amatsatira khalidwe limeneli lachikristu. Buku lotchedwa The Encyclopedia of Religion likuti: “Gulu lililonse la anthu lili ndi ufulu wodzitetezera ku mamembala ake ochita zinthu zosayenera amene angaike pangozi ubwino wa gulu lonse. Pankhani ya chipembedzo ufulu wochita zimenezi wagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri pokhulupirira kuti mchitidwe [wochotsawo] ungakhudze unansi wa munthu ndi Mulungu.”

17, 18. Kodi nkhani ya kuchotsa ingachitiridwe chitsanzo motani ndi (a) dongosolo la sukulu? (b) gulu lankhondo?

17 Mboni za Yehova zili ophunzira Baibulo. (Yoswa 1:8; Salmo 1:2; Machitidwe 17:11) Programu ya maphunziro a Baibulo yoperekedwa ndi Bungwe Lolamulira ingayerekezeredwe ndi mpambo wa maphunziro amene amaperekedwa ndi bungwe la maphunziro. Ngakhale kuti bungwelo limadalira ziŵiya zophunzirira zochokera kwina, ilo limakhazikitsa mpambo wa maphunziro, kulinganiza njira yophunzitsira, ndiponso kupereka chitsogozo choyenerera. Ngati wina akana poyera kukhala mogwirizana ndi zofunika za pasukulupo, adzetsa mavuto kwa ophunzira anzake, kapena kuchita zinthu zochititsa manyazi sukuluyo, iye angachotsedwe. Akuluakulu a sukulu ali ndi ufulu wochita zinthu zopindulitsa ophunzira onse.

18 Kuwonjezera pa kukhala ophunzira, Mboni za Yehova ndi asilikali a Yesu Kristu, amene amalangizidwa ‘kumenya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.’ (1 Timoteo 6:12; 2 Timateo 2:3) Kaŵirikaŵiri, makhalidwe oipa a msilikali wachikristu amgampangitse kuti atsutsidwe ndi Mulungu. Monga munthu amene ali ndi ufulu wa kudzisankhira, msilikali wachikristu angachite zimene afuna, koma ayenera kuyang’anizana ndi zotsatirapo za zosankha zake. Paulo anati: “Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali. Koma ngatinso wina ayesana nawo m’makani a maseŵero, samveka korona ngati sanayesana monga adapangana.” (2 Timoteo 2:4, 5) Akristu okhwima, kuphatikizapo awo a m’Bungwe Lolamulira, amatsatira kotheratu Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu, kusunga ‘malamulo’ kotero kuti adzapate mphotho ya moyo wosatha.​—Yohane 17:3; Chivumbulutso 2:10.

19. Popeza kuti tsopano takambitsirana matanthauzo enieni a kudzipatulira kwachikristu, kodi tingakhale otsimikizira za chiyani?

19 Kodi mfundo zatchulidwazi sizikusonyeza bwino lomwe kuti Mboni za Yehova zili atumiki a Mulungu, osati akapolo a anthu? Monga Akristu odzipatulira okhala ndi ufulu umene Kristu anawasandutsira mfulu, iwo amalola mzimu wa Mulungu ndi Mawu ake kulamulira miyoyo yawo pamene atumikira mogwirizana ndi abale awo a mumpingo wa Mulungu. (Salmo 133:1) Maumboni ameneŵa ayeneranso kuchotseratu kukayikira kulikonse ponena za magwero a nyonga yawo. Iwo angaimbe mogwirizana ndi wamasalmo kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza: chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.”​—Salmo 28:7.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa mu 1993 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi Watch Tower Society ndi mabungwe ena alamulo ofananawo amathandiza Mboni za Yehova motani?

◻ Kodi Akristu amapindula motani ndi ntchito ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova?

◻ Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova amapereka lipoti la ntchito yawo yolalikira?

◻ Kodi kuchotsa Mkristu wodzipatulira kuli koyenera pamikhalidwe iti?

[Chithunzi patsamba 19]

Bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba linali ndi udindo woonetsetsa kuti chiphunzitso chikhale chogwirizana

[Chithunzi patsamba 23]

Kuzungulira dziko lonse, Mboni za Yehova zili ndi ufulu umene Kristu anawasandutsira mfulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena