Moyo Wanga Monga Wakhate—Wachimwemwe ndi Wodalitsidwa Mwauzimu Yosimbidwa ndi Isaiah Adagbona
NDINAKULIRA KU AKURE, NIGERIA.
Banja langa linali kulima zilazi, nthochi, chinangwa, ndi cocoa. Atate wanga sanafune kuti ndikaphunzire kusukulu. Anandiuza kuti: “Iwe ndiwe mlimi. Palibe amene adzakuuza kuphunzira za chilazi.”
KOMABE, ndinali kufuna kuti ndiphunzire kuŵerenga. Madzulo, ndinali kuima ndi kumvetsera pazenera la nyumba ina mmene ana ena anali kuphunzitsidwa ndi mphunzitsi wawo. Munali mu 1940 mmenemo pamene ndinali ndi zaka ngati 12 zakubadwa. Atate wa anawo akandiona, anali kukuwa ndi kundipitikitsa. Koma ndinapitirizabe kumabwera. Nthaŵi zina mphunzitsi sanali kubwera, ndipo ndinali kuloŵa mwakazembera ndi kuona ndi anawo m’mabuku awo. Nthaŵi zina anali kundibwereka mabuku awo. Ndimo mmene ndinaphunzirira kuŵerenga.
Ndigwirizana ndi Anthu a Mulungu
M’kupita kwa nthaŵi ndinapeza Baibulo ndipo ndinali kuliŵerenga nthaŵi zonse ndisanagone. Usiku wina ndinaŵerenga Mateyu chaputala 10, pamene pamalongosola kuti ophunzira a Yesu adzadedwa ndi kuzunzidwa ndi anthu.
Ndinakumbukira kuti Mboni za Yehova zinali zitabwera kunyumba kwanga ndipo sindinawalandire bwino. Ndinalingalira kuti ameneŵa ndiwo ayenera kukhala anthu amene Yesu anali kunena. Mboni zitabweranso nthaŵi yotsatira, ndinawombola magazini kwa iwo. Pamene ndinayamba kuyanjana nawo, anthu anayamba kundinyodola. Komabe, pamene anthu oyesa kundiletsa anali kuchuluka, mpamenenso ndinali kukhutira kwambiri ndiponso kusangalala kuti ndapeza chipembedzo choona.
Chimene chinandisangalatsa kwambiri ponena za Mboni nchakuti, mosiyana ndi zipembedzo zina za m’dera lakwathu, iwo sanali kusanganiza kulambira kwawo ndi miyambo ya chipembedzo chakunja chakomweko. Mwachitsanzo, ngakhale kuti banja langa linkaloŵa tchalitchi cha Anglican, atate wanga anali ndi kachisi wa mulungu wotchedwa Ogun wa fuko la Ayoruba.
Atate wanga atamwalira, kachisiyo anayenera kukhala wanga. Ineyo sindinali kumfuna, popeza ndinadziŵa kuti Baibulo limatsutsa kulambira mafano. Ndinapitabe patsogolo mwauzimu mothandizidwa ndi Yehova, ndipo mu December 1954, ndinabatizidwa.
Khate Likantha
Kuchiyambi kwa chakacho, ndinaona kuti mapazi anga ayamba kutupa ndiponso sanali kumva kukhudza kulikonse. Ndikaponda pamakala amoto sindinali kumva kupweteka. Patapita nthaŵi, zilonda zofiira zinaonekera pamphumi ndi pamilomo panga. Ineyo kapena banja langa sitinadziŵe chochititsa; tinaganiza kuti ndi dzikulukuto. Ndinapita kwa anthu 12 odziŵa mankhwala azitsamba pofunafuna machiritso. Pomalizira pake mmodzi wa iwo anatiuza kuti ndi khate.
Zimenezo zinandiopsa chotani nanga! Zinandisautsa mtima ndipo sindinapeze tulo. Ndinali ndi maloto oipa. Koma chidziŵitso changa cha choonadi cha Baibulo ndi kudalira kwanga Yehova zinandithandiza kuyembekezera zamtsogolo mwachidaliro.
Anthu anauza amayi wanga kuti nditapita kwa wansembe kukapereka nsembe, ndingachire. Ndinakana kupitako, podziŵa kuti kuchita zimenezo kungamnyanse Yehova. Atazindikira kuti ndinali wotsimikiza kusachita zimenezo, anzawo a amayi anawauza kuti atenge mtedza wa kola ndi kukhudza nawo pamphumi panga. Kenako angapite ndi mtedzawo kwa wansembe kukaugwiritsira ntchito pondiperekera nsembe. Sindinafune kuchita nawo zimenezo ndipo ndinawauza motero. Pomalizira pake anasiya zofuna kundiloŵetsa m’chipembedzo chachikunja.
Podzafika nthaŵi imene ndinapita kuchipatala, khate linali litafika pachimake. Ndinali ndi zilonda thupi langa lonse. Kuchipatala, anandipatsa mankhwala, ndipo m’kupita kwa nthaŵi khungu langa linakhalanso bwino.
Anaganiza Kuti Ndafa
Koma mavuto anga anali adakalipo. Phazi langa la kulamanja linawonongeka kwambiri ndi matendawo, ndipo mu 1962 analidula. Atandichita opaleshoni, panali zovuta chifukwa cha opaleshoniyo. Madokotala anaganiza kuti ndidzafa. Wansembe wachiyera anabwera kudzapereka mapemphero omalizira. Ndinali wofooka kwambiri moti sindinathe kulankhula, koma nesi anamuuza kuti ndine mmodzi wa Mboni za Yehova.
Wansembeyo anandifunsa kuti: “Kodi ukufuna kusintha kuti ukhale Mkatolika kotero kuti upite kumwamba?” Zimenezo zinandiseketsa mumtima. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andipatse nyonga yoti ndiyankhe. Nditayesayesa mwamphamvu ndinatha kunena kuti, “Ayi!” Wansembeyo anatembenuka nachoka.
Ndinadwala kwambiri moti antchito a m’chipatala anaganiza kuti ndafa. Anaphimba nkhope yanga ndi nsalu. Komano sanandipereke kunyumba yachisoni chifukwa chakuti dokotala kapena nesi anafunikira kusaina choyamba kuti ndafa. Kunalibe dokotala amene anali kugwira ntchito, ndipo manesi onse anali atapita kuphwando. Choncho anandisiya m’chipinda cha odwalacho mpaka mmaŵa mwake. Pamene dokotala anali kuona odwala mmaŵawo, palibe amene anabwera pabedi langa chifukwa chakuti ndinali ndidakali wophimbidwa kumaso akumayesa kuti ndine wakufa. Kenaka, winawake anaona kuti “mtembo” wophimbidwa ndi nsaluwo ukugwedera!
Ndinakhala bwino, ndipo mu December 1963 anandisamutsira kumudzi wa akhate kuchipatala chotchedwa Abeokuta Leprosy Hospital Settlement kummwera chakumadzulo kwa Nigeria. Ndakhala komweko kuchokera pamenepo.
Kutsutsa Kulalikira Kwanga
M’mudzimu munali akhate ngati 400 pamene ndinafika, ndipo ndine ndekha amene ndinali Mboni. Ndinalembera Sosaite, ndipo anandiyankha mwamsanga mwa kuuza Mpingo wa Akomoje kudzaonana nane. Choncho sindinasiye kuonana ndi abale.
Nditangofika pamudziwu, ndinayamba kulalikira. Pasitala wakuno sizinamkondweretse, ndipo anandinenera kwa ofisala wosamalira zosoŵa zathu amene anali kuyang’anira mudziwu. Ofisalayo anali mwamuna wachikulire wochokera ku Germany. Iye anandiuza kuti ndilibe mphamvu yophunzitsa Baibulo chifukwa chakuti sindinapite kusukulu ndiponso ndilibe setifiketi yochitira zimenezo; popeza kuti ndinalibe ziyeneretso, ndingamaphunzitse anthu zinthu zolakwika. Ngati ndilimbikira kutero, ndidzathamangitsidwa m’mudziwo ndipo adzandimana mankhwala. Sanandilole kuyankha kalikonse.
Kenako anapereka lamulo lakuti palibe amene ayenera kuphunzira nane Baibulo. Choncho, awo amene anali atasonyeza chidwi anasiya kubwera kwa ine.
Nkhaniyo ndinaipereka kwa Yehova m’pemphero, kupempha nzeru ndi chitsogozo. Lamlungu lake, ndinapita kutchalitchi cha Baptist cha m’mudziwo, ngakhale kuti sindinalambire nawo. Panali nthaŵi pamapempheropo pamene opezekapo anali ndi mwayi wofunsa mafunso. Ndinakweza dzanja langa ndi kufunsa kuti: “Ngati anthu onse abwino adzapita kumwamba ndiponso anthu onse oipa adzapita kumalo ena ake, kodi nchifukwa chiyani Yesaya 45:18 amanena kuti Mulungu anapanga dziko lapansi kuti anthu akhalemo?”
Munali kung’ung’udza kwambiri mumpingomo. Pomalizira pake, pasitala mmishonaleyo ananena kuti njira za Mulungu sitingazimvetse. Pomwepo, ndinayankha funso langa mwa kuŵerenga malemba osonyeza kuti anthu 144,000 adzapita kumwamba, kuti oipa adzatha psiti, ndi kuti olungama adzakhala kosatha padziko lapansi.—Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 14:1, 4.
Onse anaomba mmanja poyamikira yankho limenelo. Kenako pasitalayo anati: “Ombani m’manja kachiŵiri chifukwa munthuyu amalidziŵadi Baibulo.” Mapempherowo atatha, ena anabwera kwa ine ndi kunena kuti: “Umadziŵa zambiri kuposa a pasitala!”
Apitirizabe Kusonkhezera kuti Andichotse
Zimenezo zinachepetsa kwambiri chizunzocho, ndipo anthu anagwirizananso nane kuti aphunzire Baibulo. Komabe, otsutsa anatsala amene anakakamiza ofisalayo kuti andichotse. Patapita mwezi umodzi kuchokera pamene ndinapita kutchalitchi kuja, iye anandiitana nanena kuti: “Nchifukwa chiyani ukupitiriza kulalikira? Kudziko lakwathu, anthu samazikonda Mboni za Yehova, ndipo ndi mmenenso zinthu zilili kuno. Undivutitsiranji? Kodi sudziŵa kuti ndingakuchotse?”
Ndinayankha kuti: “Bambo, ndimakulemekezani pazifukwa zitatu. Choyamba, chifukwa chakuti ndinu wamkulu ndi ine, ndipo Baibulo limanena kuti tiyenera kulemekeza aimvi. Chifukwa chachiŵiri chimene ndimakulemekezerani nchakuti munasiya dziko lakwanu kudzatithandiza kuno. Chifukwa chachitatu nchakuti ndinu wachifundo, wooloŵa manja, ndipo mumathandiza ovutika. Koma kodi mukuyesa kuti mungandichotse mwa mphamvu ziti? Pulezidenti wa dziko lino sachotsa Mboni za Yehova. Mfumu ya dera lino siimatichotsa. Ngakhale mutandichotsa m’mudzi uno, Yehova adzandisamalirabe.”
Ndinali ndisanalankhulepo mosapita mbali choncho kwa iye, ndipo ndinaona kuti zinamloŵa mumtima. Anangochoka popanda kunena kalikonse. Pambuyo pake, winawake atakadandaula za ine, iye anayankha mokalipa kuti: “Sindikufunanso kuloŵa m’nkhani imeneyo. Ngati muli ndi vuto ndi kulalikira kwake, kalankhuleni naye!”
Kalasi Lophunzitsa Kuŵerenga ndi Kulemba
Amene anali kupita kutchalitchi cha Baptist cha m’mudziwo anapitirizabe kutsutsa kulalikira kwanga. Kenako ndinadziŵa chochita. Ndinapita kwa ofisalayo ndi kufunsa ngati ndingayambitse kalasi lophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba. Atandifunsa ndalama zimene ndingafune kumalipiridwa, ndinanena kuti ndidzaphunzitsa kwaulere.
Anandipatsa chipinda, bolodi, ndi choko, choncho ndinayamba kuwaphunzitsa kuŵerenga anzanga ena. Tinali kuphunzira masiku onse. Mphindi zoyambirira 30 ndinali kuphunzitsa kuŵerenga, kenako ndinali kusimba ndi kufotokoza nkhani ya m’Baibulo. Kenako, tinali kuŵerenga nkhaniyo m’Baibulo.
Wophunzira wina anali mkazi wotchedwa Nimota. Anali wokonda kwambiri zinthu zauzimu ndipo anali kufunsa mafunso okhudzana ndi zachipembedzo kutchalitchi ndi kumzikiti komwe. Kumeneko mafunso ake sanayankhidwe, choncho anali kubwera kudzandifunsa. M’kupita kwa nthaŵi, anapatulira moyo wake kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Mu 1966 tinakwatirana.
Ambiri mumpingo mwathu lerolino anaphunzira kuŵerenga ndi kulemba m’kalasi limenelo lophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba. Kuyambitsa kalasilo sikunali chifukwa cha nzeru zanga. Ndithudi linali dalitso la Yehova. Pambuyo pake palibe amene anayesa kundiletsa kulalikira.
Nyumba ya Ufumu m’Mudzi wa Akhate
Podzafika nthaŵi imene ineyo ndi Nimota tinakwatirana, tinalipo anayi amene tinali kusonkhana mokhazikika ndi kuchitira pamodzi phunziro la Nsanja ya Olonda. Kwa chaka chimodzi, tinali kusonkhanira m’chipinda chotsukiramo zilonda zakhate. Kenako ofisala wosamalira zosoŵa zathu, amene tsopano anali bwenzi langa, anandiuza kuti: “Si bwino kuti Mulungu wanu muzimlambirira m’chipinda cha odwala.”
Iye anatiuza kuti tingamasonkhanire m’nyumba yopaliramo matabwa imene sanali kuigwiritsira ntchito. M’kupita kwa nthaŵi, nyumba imeneyo tinaisandutsa Nyumba ya Ufumu. Mu 1992, mothandizidwa ndi abale a kutauni, tinamaliza kuikonza. Monga momwe mungaonere pachithunzi patsamba 24, nyumba yathu imeneyo ndi nyumba yabwino—ya pulasitala ndiponso yopakidwa utoto, ya pansi pasimenti ndiponso ya denga labwino.
Kulalikira kwa Anthu Akhate
Kwa zaka 33 gawo langa lakhala mudzi wa anthu akhate. Kodi zimakhala bwanji polalikira akhate? Muno mu Afirika anthu ambiri amakhulupirira kuti zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu. Choncho pamene akanthidwa ndi khate, iwo amakhulupirira kuti Mulungu ayenera kuti ndiye amachititsa. Ena amachita tondovi kwambiri ndi mkhalidwe wawo. Ena amakalipa ndipo amati: “Usatilankhule za Mulungu wachikondi ndi wachifundo. Ngati zimenezo nzoona, matendawa akanatha!” Choncho timaŵerenga ndi kukambitsirana Yakobo 1:13, amene amati: ‘Mulungu sayesa munthu ndi zoipa.’ Kenako timafotokoza chifukwa chimene Yehova amalolera anthu kukanthidwa ndi matenda, ndipo timafotokoza za lonjezo lake la dziko lapansi la paradaiso mmene palibe munthu amene adzadwala.—Yesaya 33:24.
Ambiri alabadira uthenga wabwino. Chibwerere m’mudzi muno, Yehova wandigwiritsira ntchito kuthandiza anthu oposa 30 kuti adzipatulire ndi kubatizidwa, onse akhate. Ambiri abwerera kumakwawo atachira, ndipo angapo anamwalira. Tsopano tili ndi ofalitsa Ufumu 18, ndipo anthu pafupifupi 25 amafika pamisonkhano mokhazikika. Aŵiri mwa ife tikutumikira monga akulu, ndipo tili ndi mtumiki wotumikira mmodzi ndi mpainiya wokhazikika mmodzi. Ndili wachimwemwe chotani nanga kuona ambiri tsopano akutumikira Yehova mokhulupirika m’mudzi uno! Pamene ndinabwera kuno, ndinali ndi mantha akuti ndidzakhala ndekha, koma Yehova wandidalitsa m’njira yosangalatsa kwambiri.
Chimwemwe cha Kutumikira Abale Anga
Ndinamwa mankhwala a khate kuyambira mu 1960 mpaka zaka ngati zisanu zapitazo. Tsopano ndinachiriratu, monganso ena mumpingo mwathu. Khatelo linasiya chizindikiro chake—anandidula mwendo, ndipo sinditha kuwongola mikono yanga—koma matendawo anatha.
Popeza kuti ndinachira, ena afunsa chifukwa chimene sindikuchokera m’mudzi wa akhate ndi kubwerera kwathu. Pali zifukwa zambiri zimene sindikuchokera, koma chifukwa chachikulu nchakuti ndikufuna kupitirizabe kuthandiza abale anga kuno. Chimwemwe chakudza chifukwa cha kusamalira nkhosa za Yehova chimaposa chilichonse chimene banja langa lingandipatse nditabwerera kwa iwo.
Ndili wokondwa kwambiri kuti ndinadziŵa Yehova ndisanadziŵe kuti ndili ndi khate. Chikhala sizinali choncho mwina bwenzi nditadzipha. Pakhala mavuto ambiri pazaka zonsezi, koma chimene chinandilimbikitsa si mankhwala—anali Yehova. Ndikakumbukira zakumbuyo, ndimasangalala; ndipo ndikaganizira zamtsogolo mu Ufumu wa Mulungu, ndimasangalala koposa.
[Bokosi patsamba 25]
Choonadi Ponena za Khate
Kodi Khate Nchiyani?
Khate lamakono ndi matenda ochititsidwa ndi kachilombo ka bacillus komwe kanapezedwa mu 1873 ndi Armauer Hansen. Poyamikira ntchito yake, madokotala amatchanso khate kuti Hansen’s disease (matenda a Hansen).
Kachilombo kameneko kamawononga minyewa, mafupa, maso, ndi ziŵalo zina. Makamaka manja ndi miyendo imasiya kumva kalikonse. Popanda mankhwala, matendawa angapundule kwambiri nkhope, manja, ndi mapazi. Nthaŵi zambiri sakupha.
Kodi Mankhwala Ake Alipo?
Anthu okhala ndi mitundu ya khate yosakhala yamphamvu kwambiri amachira popanda mankhwala alionse. Matenda aakulu kwambiri angachiritsidwe ndi mankhwala.
Mankhwala oyamba ochiritsira khate, amene anayamba kuwagwiritsira ntchito m’zaka za m’ma 1950 anali kugwira ntchito pang’onopang’ono ndipo anayamba kulephera kugwira ntchito chifukwa chakuti mankhwalawo sanali kuchita kanthu ku kachilombo ka khateko. Mankhwala atsopano anapangidwa, ndipo kuchokera kuchiyambi cha zaka za m’ma 1980, Multi-Drug Therapy (MDT) (Machiritso Ogwiritsira Ntchito Mankhwala Osiyanasiyana) anakhala machiritso ovomerezeka kuzungulira dziko lonse lapansi. M’machiritso ameneŵa amagwiritsira ntchito msanganizo wa atatu—Dapsone, Rifampicin, ndi Clofazimine. Pamene kuli kwakuti machiritso a MDT amapha kachilomboko, iwo samakonza zimene zawonongedwa kale.
Machiritso a MDT ngamphamvu kwambiri pochiritsa matendawa. Motero, chiŵerengero cha anthu odwala khate chatsika kwambiri kuchokera pa 12 miliyoni mu 1985 kufika pafupifupi 1.3 miliyoni chapakati pa 1996.
Kodi Anthu Amapatsirana Mosavuta?
Anthu samapatsirana khate mosavuta; ambiri ali ndi matupi olimba moti sangatenge matenda ameneŵa. Ngati apatsirana, nthaŵi zambiri zimachitika kwa anthu amene amakhala pafupi kwambiri ndi akhate kwa nthaŵi yaitali.
Madokotala sakudziŵa bwino lomwe mmene kachilomboka kamaloŵera m’thupi, koma akuganiza kuti kamaloŵera pakhungu kapena m’mphuno.
Ziyembekezo Zamtsogolo
Khate akufuna “kulithetsa monga nthenda yovutitsa anthu” podzafika chaka cha 2000. Zimenezi zikutanthauza kuti chiŵerengero cha anthu odwala khate kulikonse sichidzaposa pa munthu mmodzi mwa anthu 10,000. Mu Ufumu wa Mulungu khate lidzatheratu.—Yesaya 33:24.
Kumene zachokera: World Health Organization; International Federation of Anti-Leprosy Associations; ndi Manson’s Tropical Diseases, 1996 Edition.
[Bokosi patsamba 27]
Kodi Khate Lamakono Likufanana ndi la m’Nthaŵi za Baibulo?
Mabuku amakono olongosola mankhwala amalongosola khate mwatsatanetsatane; dzina lasayansi la kachilombo komwe kamalichititsa ndilo Mycobacterium leprae. Komano, Baibulo si buku lolongosola mankhwala. Mawu achihebri ndi achigiriki otembenuzidwa kuti “khate” m’mabaibulo ambiri ali ndi matanthauzo ambiri. Mwachitsanzo, khate lotchulidwa m’Baibulo linali kusonyeza zizindikiro zoonekera osati mwa anthu okha komanso m’zovala ndi m’nyumba, chinthu chimene kachilomboko sikamachita.—Levitiko 13:2, 47; 14:34.
Ndiponso, zizindikiro zosonyeza khate mwa munthu lerolino sizikufanana kwenikweni ndi mafotokozedwe a khate la m’nthaŵi za Baibulo. Ena amanena kuti mwina chochititsa ndi choonadi chakuti mkhalidwe wa matenda umasintha m’kupita kwa nthaŵi. Ena amakhulupirira kuti khate lotchulidwa m’Baibulo ndilo matenda osiyanasiyana, amene angaphatikizepo kapena sangaphatikizepo matenda ochititsidwa ndi M. leprae.
Theological Dictionary of the New Testament imanena kuti mawu a m’Chigiriki ndi m’Chihebri momwe nthaŵi zambiri otembenuzidwa kuti khate “amanena nthenda imodzimodziyo, kapena gulu limodzi la matenda . . . Nzokayikitsa kunena kuti matenda ameneŵa ndiwo amene tsopano timawatcha kuti khate. Koma malongosoledwe olunjika a matendawa sakusintha mmene timaonera nkhani za kuchiritsa [akhate kwa Yesu ndi ophunzira ake].”
[Chithunzi patsamba 24]
Mpingo panja pa Nyumba ya Ufumu imene ili m’mudzi wa akhate
[Chithunzi patsamba 26]
Isaiah Adagbona ndi mkazi wake, Nimota